Zekariya 9:1-17
9 Uthenga wokhudza dziko la Hadiraki:
“Uwu ndi uthenga wa Yehova wokhudza dziko la Hadiraki,Ndipo makamaka ukupita kumzinda wa Damasiko.+Chifukwa maso a Yehova ali pa anthu,+Komanso pa mafuko onse a Isiraeli.
2 Uthengawu ukupitanso kwa Hamati+ amene anachita naye malire.Komanso kwa Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+
3 Turo anamanga malo okwera omenyerapo nkhondo.
Anadziunjikira siliva wambiri ngati fumbi,Ndiponso golide wambiri ngati dothi lamʼmisewu.+
4 Yehova adzamulanda zinthu zake.Gulu lake lankhondo adzaliponyera mʼnyanja.+Ndipo iye adzatenthedwa ndi moto.+
5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha.Gaza adzamva ululu waukulu.Izi zidzachitikiranso Ekironi chifukwa amene ankamudalira wachititsidwa manyazi.
Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu,Ndipo ku Asikeloni sikudzakhalanso anthu.+
6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu azidzakhala ku Asidodi,Ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+
7 Ndidzachotsa zinthu zamagazi mʼkamwa mwawo,Komanso chakudya chonyansa pakati pa mano awo.Ndipo aliyense amene adzatsale, adzakhala wa Mulungu wathu.Iye adzakhala ngati mtsogoleri mu Yuda,+Ndipo Ekironi adzakhala ngati munthu wa Chiyebusi.+
8 Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+Moti sipadzakhala munthu wolowa kapena kutuluka.Aliyense amene ankawagwiritsa ntchito* sadzadutsanso pakati pawo+Chifukwa ine ndaona ndi maso anga.*
9 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* sangalala kwambiri.
Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu.*
Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe.+
Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso.*Ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu.Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.+
10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku EfuraimuNdiponso mahatchi ku Yerusalemu.
Mauta omenyera nkhondo adzachotsedwa.
Mfumuyo idzalalikira uthenga wamtendere kwa anthu a mitundu ina.+Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja ina.Ndiponso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
11 Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,Ndidzatulutsa akaidi ako mʼdzenje lopanda madzi.+
12 Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo, bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+
Lero ndikukuuza kuti,‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+
13 Ndidzapinda Yuda kuti akhale uta wanga.
Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi.Ndidzadzutsa ana ako, iwe Ziyoni,Kuti aukire ana a Girisi.Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la msilikali.’
14 Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,Ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.
Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga,+Ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho yakumʼmwera.
15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza anthu ake.Adani awo adzawaponyera miyala ndi gulaye,* koma iwo adzawagonjetsa.+
Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.Adzakhala ngati mbale zolowa zodzaza vinyo,Ndiponso ngati magazi amene athiridwa mʼmakona a guwa lansembe.+
16 Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,Zomwe ndi anthu ake.+Popeza iwo adzakhala ngati miyala yamtengo wapatali yapachisoti chachifumu yomwe ikunyezimira mʼdziko lake.+
17 Ubwino wake ndi waukulu kwambiri,+Ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri.
Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata,Ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amene ankawapondereza.”
^ Mwina kutanthauza kuvutika kwa anthu ake.
^ Kapena kuti, “yapambana; yapulumutsidwa.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.