FUNSO 11
Kodi Chimachitika Nʼchiyani Munthu Akamwalira?
“Mpweya wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.”
“Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse . . . Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru.”
“[Yesu] anauza ophunzira akewo kuti: ‘Mnzathu Lazaro ali mʼtulo, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa.’ Apa Yesu ankatanthauza kuti Lazaro wamwalira. Koma iwo ankaganiza kuti akunena za kugona tulo teniteni. Kenako Yesu anawauza mosapita mʼmbali kuti: ‘Lazaro wamwalira.’ ”