Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 2

Kodi Mungatani Kuti Muphunzire za Mulungu?

“Buku la Chilamulo ili lisachoke pakamwa pako. Uziliwerenga ndi kuganizira mozama masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo. Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.”

Yoswa 1:8

“Iwo anapitiriza kuwerenga bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga Chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokoza momveka bwino ndi kumveketsa tanthauzo lake. Choncho anathandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene ankawerenga.”

Nehemiya 8:8

“Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa, . . .  koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku. . . . Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.”

Salimo 1:​1-3

“Filipo anathamanga nʼkumayenda mʼmbali mwa galetalo ndipo anamumva akuwerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti: ‘Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?’ Iye anayankha kuti: ‘Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?’”

Machitidwe 8:​30, 31

“Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.”

Aroma 1:​20

“Uziganizira mozama zinthu zimenezi ndipo uzizichita modzipereka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”

1 Timoteyo 4:​15

“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino. Tisasiye kusonkhana pamodzi.”

Aheberi 10:24, 25

“Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu ndipo adzamupatsa, chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.”

Yakobo 1:5