A7-D
Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi—Utumiki Waukulu wa Yesu MʼGalileya (Gawo 2)
NTHAWI |
MALO |
ZIMENE ZINACHITIKA |
MATEYU |
MALIKO |
LUKA |
YOHANE |
---|---|---|---|---|---|---|
31 kapena 32 |
Dera la Kaperenao |
Yesu anafotokoza mafanizo a Ufumu |
||||
Nyanja ya Galileya |
Analetsa mphepo ali mʼngalawa |
|||||
Dera la Gadara |
Anatumiza ziwanda munkhumba |
|||||
Mwina ku Kaperenao |
Anachiritsa mayi wamatenda otaya magazi; Anaukitsa mwana wa Yairo |
|||||
Kaperenao (?) |
Anachiritsa wosaona ndi wosalankhula |
|||||
Nazareti |
Anakanidwanso mumzinda wakwawo |
|||||
Galileya |
Ulendo wachitatu wa ku Galileya; anatumiza atumwi kukalalikira |
|||||
Tiberiyo |
Herode anapha Yohane Mʼbatizi; Anathedwa nzeru atamva za Yesu |
|||||
32, Pasika atayandikira (Yoh. 6:4) |
Kaperenao (?); Pafupi ndi Nyanja ya Galileya |
Atumwi anabwera kuchokera kolalikira; Yesu anadyetsa amuna 5,000 |
||||
Pafupi ndi Nyanja ya Galileya; Genesareti |
Ankafuna kuveka Yesu ufumu; anayenda panyanja; anachiritsa anthu |
|||||
Kaperenao |
Anati iye ndi “chakudya chopatsa moyo”; ambiri anasiya kumutsatira |
|||||
32, Pambuyo pa Pasika |
Mwina ku Kaperenao |
Anawadzudzula chifukwa cha miyambo |
||||
Foinike; Dekapoli |
Anachiritsa mwana wa mayi wa ku Foinike; anadyetsa amuna 4,000 |
|||||
Magadani |
Anapereka chizindikiro cha Yona |