A7-A
Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi—Zimene Zinachitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake
Zochitika za MʼMauthenga Abwino 4, Zondandalikidwa Motsatira Nthawi Imene Zinachitika
Matchati otsatirawa ali ndi mapu osonyeza mmene Yesu anayendera komanso malo omwe analalikirako. Zizindikiro zangati mivi pamapu, sizikusonyeza njira zenizeni zimene anadutsa koma zikungosonyeza madera amene anafikako. Chizindikiro cha “c.” chikutanthauza “cha mʼma.”
Zimene Zinachitika Yesu Asanayambe Utumiki Wake
NTHAWI |
MALO |
ZIMENE ZINACHITIKA |
MATEYU |
MALIKO |
LUKA |
YOHANE |
---|---|---|---|---|---|---|
3 B.C.E. |
Yerusalemu, mʼkachisi |
Mngelo Gabirieli anauza Zekariya za kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi |
||||
c. 2 B.C.E. |
Nazareti; Yudeya |
Mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti adzabereka Yesu; Mariya anapita kukaona Elizabeti |
||||
2 B.C.E. |
Dera lakumapiri la Yudeya |
Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi ndi kupatsidwa dzina; Zekariya analosera; Yohane azidzakhala mʼchipululu |
||||
2 B.C.E., mwina pa 1 Oct. |
Betelehemu |
Kubadwa kwa Yesu; “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama” |
||||
Pafupi ndi Betelehemu; Betelehemu |
Mngelo anauza abusa nkhani yabwino; angelo anatamanda Mulungu; abusa anapita kukaona mwana |
|||||
Betelehemu; Yerusalemu |
Yesu anadulidwa (tsiku la 8); makolo ake anapita naye kukachisi (patatha masiku 40) |
|||||
1 B.C.E. kapena 1 C.E. |
Yerusalemu; Betelehemu; Iguputo; Nazareti |
Okhulupirira nyenyezi anakaona Yesu; banja linathawira ku Iguputo; Herode anapha ana aamuna; banja linabwerera nʼkukhazikika ku Nazareti 2:1-23 |
||||
12 C.E., Pasika |
Yerusalemu |
Yesu ali ndi zaka 12 kukachisi akufunsa aphunzitsi |
||||
Nazareti |
Anabwerera ku Nazareti; anapitiriza kumvera makolo ake; anaphunzira ukalipentala; Mariya anabereka ana ena 4 aamuna komanso ana aakazi (Mat. 13:55, 56; Maliko 6:3) |
|||||
29, kumayambiriro |
Chipululu, Mtsinje wa Yorodano |
Yohane Mʼbatizi anayamba utumiki wake |