Muzithandiza ana anu kuti azichita nawo zinthu zosiyanasiyana monga kuyeretsa pa Nyumba ya Ufumu kapena kucheza ndi abale ndi alongo achikulire a mumpingo mwanu
Kuthandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kumafuna khama, ndipo nthawi zina kungaoneke ngati kovuta kwambiri. Komabe mukhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova akuthandizani.—Yes 40:29.