MOYO WATHU WACHIKHRISTU Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani YAMBANI Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Kuvutitsidwa ndi anthu ena kungachititse kuti tizimva kupweteka komanso tisamasangalale. Kungachititsenso kuti ubwenzi wathu ndi Yehova usokonekere ngati tikuopsezedwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu. Kodi mungatani kuti anzanu asamakuvutitseni? Kudalira Yehova kwathandiza atumiki ambiri kuti akwanitse kupirira pamene anzawo akuwavutitsa. (Sl 18:17) Mwachitsanzo, Esitere analankhulapo kuti aulule mapulani oipa a Hamani. (Est 7:1-6) Asanachite zimenezi anasala kudya posonyeza kuti ankadalira Yehova. (Est 4:14-16) Yehova anamudalitsa komanso anamuteteza limodzi ndi anthu a mtundu wake. Achinyamatanu, ngati anthu ena amakuvutitsani, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni ndipo muziuza munthu wina wachikulire, mwachitsanzo makolo anu. Mungakhale otsimikiza kuti Yehova akuthandizani ngati mmene anathandizira Esitere. Kodi mungachitenso chiyani anzanu akamakuvutitsani? ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WANGA WACHINYAMATA—NDINGATANI NGATI ANZANGA AMANDIVUTITSA?, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA: Kodi achinyamata angaphunzirepo chiyani kwa Charlie ndi Ferin? Yankho Kodi makolo angaphunzire chiyani zokhudza kuthandiza ana awo kuchokera pa zimene Charlie ndi Ferin ananena? Yankho Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU–NDANDANDA YA MISONKHANO Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani Chinenero Chamanja cha ku Malawi Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/202023327/univ/art/202023327_univ_sqr_xl.jpg mwb23.9 8