Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale Paubwenzi ndi Mulungu?

Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale Paubwenzi ndi Mulungu?

Mutu 35

Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale Paubwenzi ndi Mulungu?

Jeremy anazindikira kufunika kokhala paubwenzi ndi Mulungu chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo. Iye anati: “Pamene ndinali ndi zaka 12, bambo anga anachoka n’kutisiya ndi mayi. Tsiku lina usiku, ndinayamba kupemphera kwa Yehova kuti bambo angawo abwerere.”

Jeremy atathedwa nzeru, anayamba kuwerenga Baibulo, ndipo anakhudzidwa mtima kwambiri atawerenga Salmo 10:14. Ponena za Yehova, vesili limati: “Waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.” Jeremy anati: “Ndinamva ngati Yehova akulankhula nane, kundiuza kuti iye ndiye mthandizi wanga; ndiye Bambo wanga. Ndipo palibe munthu wina aliyense amene angakhale bambo wabwino kwambiri kuposa Yehova.”

KAYA mukukumana ndi mavuto ngati a Jeremy kapena ayi, Baibulo limasonyeza kuti Yehova amafuna kuti mukhale naye paubwenzi. Ndipo limanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobe 4:8) Taganizirani tanthauzo la mawu amenewa: Ngakhale kuti Yehova Mulungu simungamuone, ndipo simungafanane naye ngakhale pang’ono, iye akukupemphani kuti mukhale naye paubwenzi.

Komatu pamafunika khama ndithu kuti mukhale paubwenzi ndi Mulungu. Tiyerekezere kuti mwabzala duwa lam’nyumba. Kodi lingakule lokha popanda kulisamalira? Kuti duwalo likule bwino, mungafunike kulithirira nthawi zonse ndiponso kuliika pamalo abwino. N’chimodzimodzinso ndi kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Kodi mungatani kuti mukhale paubwenzi wolimba?

Kuphunzira Baibulo N’kofunika

Anthu ogwirizana amafunika kulankhulana ndiponso kumvetserana. Ndi zimenenso zimafunika munthu akakhala paubwenzi ndi Mulungu. Tikamawerenga ndiponso kuphunzira Baibulo timakhala tikumvetsera zimene Mulungu akutiuza.—Salmo 1:2, 3.

Mwina inu simukonda kuwerenga. Achinyamata ambiri amaona kuti ndi bwino kuonera TV, kuchita masewera enaake kapena kucheza ndi anzawo m’malo mowerenga. Koma ngati mukufuna kukhala paubwenzi ndi Mulungu, muyenera kuchita zonse zimene iye akufuna kuti mutsatire. Mufunika kumvetsera zimene iye akunena mwa kuphunzira Mawu ake.

Komabe, musadere nkhawa. Kuwerenga Baibulo si ntchito yolemetsa. Ngakhale kuti mwachibadwa mwina simukonda kuwerenga, n’zotheka kuti muzisangalala mukamawerenga Baibulo. Chinthu choyamba chimene muyenera kuchita ndicho kupatula nthawi yoti muziwerenga Baibulo. Mtsikana wina dzina lake Lais anati: “Ndili ndi ndandanda ya zinthu zimene ndiyenera kuchita. Ndimawerenga Baibulo chaputala chimodzi m’mawa uliwonse ndikangodzuka.” Maria, yemwe ali ndi zaka 15, nayenso ali ndi ndandanda yake. Iye anati: “Ndimawerenga Baibulo pang’ono madzulo aliwonse ndisanagone.”

Kuti mukhale ndi ndandanda yanu yophunzirira Baibulo, onani  bokosi limene lili patsamba 292. Ndiyeno, lembani m’munsimu nthawi imene mukuona kuti mungamaphunzire Mawu a Mulungu kwa mphindi pafupifupi 30 kapena kuposerapo.

․․․․․

Kukonza ndandanda ndi chiyambi chabe. Mukayamba kuphunzira Baibulo, mwina mudzaona kuti nkhani zake zina ndi zovuta kuwerenga. N’kutheka kuti mungagwirizane ndi zimene ananena mnyamata wina wazaka 11, dzina lake Jezreel. Iye anati, “Nkhani zina za m’Baibulo n’zovuta kuzimvetsa ndipo n’zosasangalatsa kwenikweni.” Ngakhale mutakhala ndi maganizo oterowo, musasiye kuwerenga Baibulo. Nthawi zonse muziona kuti kuphunzira Baibulo ndi njira imene bwenzi lanu, Yehova Mulungu akukulankhulirani. Mukamachita khama kwambiri, m’pamene mudzaone kuti kuphunzira Baibulo n’kosangalatsa komanso kopindulitsa kwambiri.

Pemphero Ndi Lofunika

Pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri chifukwa ndi njira imene timalankhulira ndi Mulungu. Mungalankhule ndi Yehova Mulungu nthawi iliyonse, kaya masana kapena usiku. Iye ndi wokonzeka kukumvetserani nthawi zonse. Komanso amafunitsitsa kumva zimene mukufuna kunena. N’chifukwa chake Baibulo limakulimbikitsani kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Mogwirizana ndi lembali, pali zinthu zambiri zimene mungafune kuuza Yehova. Zina mwa zinthu zimenezi ndi mavuto amene mukukumana nawo. Mungamuuzenso zinthu zina zimene mumayamikira. Mwachibadwa, anzanu akakuchitirani zabwino mumawayamikira. Choncho mungachitenso zomwezo kwa Yehova, yemwe wakuchitirani zinthu zambiri kuposa mnzanu wina aliyense.—Salmo 106:1.

Lembani pa mizere iyi zina mwa zinthu zimene zimakuchititsani kuthokoza Yehova.

․․․․․

N’zodziwikiratu kuti pali zinthu zosiyanasiyana zimene zimakudetsani nkhawa. Lemba la Salmo 55:22 limati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”

Lembani pa mizere yotsatirayi zinthu zimene zikukudetsani nkhawa zomwe mukufuna kumazitchula m’pemphero.

․․․․․

Zochitika Pamoyo Wanu

Kuti mukhale paubwenzi ndi Mulungu pali chinthu chinanso chimene simuyenera kuchinyalanyaza. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” (Salmo 34:8) Pamene Davide ankalemba Salmo 34 anali atangokumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Panthawi imeneyo ankathawa mfumu yoipa Sauli, ndipo n’zodziwikiratu kuti zimenezi zinali zosokoneza maganizo kwambiri. Koma kenako anakabisala pakati pa Afilisti omwe anali adani ake. Poopa kuphedwa, Davide ananamizira kuti ndi wamisala ndipo anapulumuka.—1 Samueli 21:10-15.

Apatu Davide anapulumukira mkamwa mwa mbuzi. Komabe, sanadzitame kuti anapulumuka chifukwa cha nzeru zake. M’malo mwake, iye anatamanda Yehova kuti ndi amene anam’thandiza. Chakumayambiriro kwa Salmo 34, iye analemba kuti: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Salmo 34:4) Choncho, kuchokera pa zimene zinam’chitikira pamoyo wake, Davide anatha kulimbikitsa anthu ena kuti, “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” *

Kodi mungatchule chinachake chimene chinakuchitikiranipo chosonyeza kuti Yehova amakukondani? Ngati chilipo, chilembeni m’munsimu. Kumbukirani izi: M’posafunika kuti chinthucho chichite kukhala chozizwitsa. Ganizirani zinthu zabwino, ngakhale zooneka ngati zing’onozing’ono, zimene zimachitika pamoyo wanu.

․․․․․

Mwina makolo anu anakuphunzitsani Baibulo. Ngati ndi choncho, amenewo ndi madalitso. Komabe, inuyo panokha muyenera kuchita khama kuti mukhale paubwenzi ndi Mulungu. Ngati panopa simunakhalebe paubwenzi ndi Mulungu, mungathe kugwiritsa ntchito mfundo za m’nkhani ino kuti zikuthandizeni kuchita zimenezo. Yehova adzadalitsa khama lanulo. Baibulo limati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza.”—Mateyo 7:7.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 38 NDI 39

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi zimakuvutani kuuza ena za Mulungu? Onani zimene zingakuthandizeni kuti muzitha kuuza ena zimene mumakhulupirira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 M’Mabaibulo ena, mawu akuti “talawani, ndipo onani” anawamasulira kuti “dzionereni nokha” ndiponso kuti “mudzazindikira zitakuchitikirani.”—Today’s English Version ndi The Bible in Basic English.

LEMBA LOFUNIKA

“Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.

MFUNDO YOTHANDIZA

Werengani Baibulo masamba anayi tsiku lililonse, ndipo mudzalimaliza pasanathe chaka chimodzi.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Yehova amakukondani, ndipo umboni wa zimenezi ndi wakuti mukuwerenga buku lino komanso kutsatira malangizo ochokera m’Baibulo omwe ali m’bukuli.—Yohane 6:44.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndizipindula kwambiri ndikamaphunzira Baibulo ndizichita izi: ․․․․․

Kuti ndizipemphera nthawi zonse ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi mungatani kuti muzisangalala kwambiri pophunzira Baibulo?

● N’chifukwa chiyani Yehova amafunitsitsa kumvetsera mapemphero a anthu opanda ungwiro?

● Kodi mungatani kuti mapemphero anu azikhala ochokera pansi pamtima?

[Mawu Otsindika patsamba 291]

“Ndili mwana, mapemphero anga ankakhala ongobwerezabwereza. Panopa ndikamapemphera ndimayesetsa kutchula zinthu zabwino ndi zoipa zimene zandichitikira patsikulo. Popeza kuti zochitika zatsiku ndi tsiku zimasiyanasiyana, zimenezi zimandithandiza kuti mapemphero anga asamakhale ongobwerezabwereza.”—Anatero Eve

[Bokosi/Chithunzi patsamba 292]

 Phunzirani Baibulo Mozama

1. Sankhani nkhani inayake imene mukufuna kuwerenga m’Baibulo. Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa nkhaniyo.

2. Werengani nkhaniyo mofatsa. Pamene mukuwerenga, yerekezerani kuti munalipo pamene nkhaniyo inkachitika, ndipo mukuona zimene zikuchitika, mukumva mawu a anthu osiyanasiyana otchulidwa m’nkhaniyo, mukumva fungo la zinthu zimene zikutchulidwa ndi zina zotero.

3. Ganizirani zinthu zimene mwawerengazo. Dzifunseni mafunso monga awa:

● N’chifukwa chiyani Yehova anafuna kuti nkhaniyi ilembedwe m’Mawu ake?

● Kodi ndi anthu ati otchulidwa m’nkhaniyi omwe ndi oyenera kuwatsanzira, nanga ndi ati omwe si oyenera kuwatsanzira?

● Kodi m’nkhaniyi ndikuphunziramo chiyani?

● Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa zotani zokhudza Yehova?

4. Pempherani mwachidule kwa Yehova. M’fotokozereni zimene mwaphunzira m’Baibulo komanso zimene mukufuna kuchita pogwiritsa ntchito mfundozo. Nthawi zonse muzithokoza Yehova chifukwa cha mphatso imene wakupatsani imene ndi Mawu ake, Baibulo.

[Chithunzi]

“Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”—Salmo 119:105.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 294]

Muziika Zinthu Zofunika Kwambiri Pamalo Oyamba

Kodi mumalephera kupemphera chifukwa chosowa nthawi? Kodi simupeza nthawi yophunzira Baibulo? Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ndi vuto lolephera kuzindikira zinthu zofunika kwambiri pamoyo.

Chitani izi: Ikani miyala ingapo m’ndowa. Ndiyeno, thiranimo mchenga mpaka kudzaza bwinobwino.

Kenako, khuthulirani mchenga ndi miyalayo pamalo abwino. Tsopano, tengani mchengawo ndi kuuthiranso m’ndowamo ndipo kenako ikanimo miyala ija. N’zachidziwikire kuti miyalayo sikwanamo chifukwa chakuti munayambira mchenga.

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Baibulo limanena kuti: “Mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Mukamaika zinthu zing’onozing’ono, monga zosangalatsa pamalo oyamba, simudzatha kupeza nthawi yochitira zinthu zauzimu, zomwe ndi zofunika kwambiri. Koma mukatsatira malangizo a m’Baibulo, mudzapeza kuti muli ndi nthawi yokwanira yochitira zinthu zauzimu ndiponso zosangalatsa. Kuti muthe kuchita zimenezi, mufunika kuonetsetsa kuti mukuika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba.

[Chithunzi patsamba 290]

Duwa lam’nyumba limafunika kulisamalira kuti likule bwino. N’chimodzimodzinso ndi ubwenzi wanu ndi Mulungu