Mutu 10

Yesu Ali ndi Mphamvu Kuposa Ziwanda

Yesu Ali ndi Mphamvu Kuposa Ziwanda

KODI ukukumbukira chifukwa chimene mmodzi wa angelo a Mulungu anakhalira Satana Mdyerekezi?— Chinali chifukwa chakuti anali wodzikonda ndipo analakalaka kuti anthu azimulambira, moti iye anakana Mulungu. Kodi angelo enanso anatsatira Satana?— Inde. Baibulo limawanena kuti ‘angelo a Satana,’ kapena kuti ziwanda.—Chivumbulutso 12:9.

Kodi angelo oipa ameneŵa, kapena kuti ziwanda, amakhulupirira Mulungu?— ‘Ziwanda zimakhulupirira kuti Mulungu aliko,’ limatero Baibulo. (Yakobo 2:19) Koma zimaopa. Zimaopa chifukwa chakuti zimadziŵa kuti Mulungu adzazilanga chifukwa chochita zinthu zoipa. Kodi zachita zoipa zotani?—

Baibulo limanena kuti angelo amenewo anachoka kwawo kumwamba ndi kudzakhala anthu padziko lapansi. Anachita zimenezi chifukwa chakuti anafuna kuti azigonana ndi akazi okongola padziko lapansi pano. (Genesis 6:1, 2; Yuda 6) Tsopano tandiuza, kodi umadziŵapo chiyani za kugonana?—

Kugonana ndi pamene munthu wamwamuna ndi munthu wamkazi akhala pamodzi mwa njira yodabwitsa kwambiri. Akatero mwana amatha kuyamba kukula m’mimba mwa amayi ake. Koma ndi kulakwa kuti angelo agonane ndi aliyense. Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene anakwatirana ndiwo amene azigonana. Ndiye patabadwa mwana, mwamuna ndi mkazi wakeyo akhoza kumusamalira mwanayo.

Kodi angelo aŵa anachita chiyani chimene chinali choipa?

Pamene angelo anakhala anthu ndi kumagonana ndi akazi pano padziko lapansi, anabala ana ndipo anawo atakula anali zianthu zikuluzikulu kwambiri. Anali ankhanza zedi, ndipo anali kuzunza anthu. Motero Mulungu anabweretsa chigumula kuti awononge zianthu zikuluzikuluzo ndi anthu onse oipa. Koma anauza Nowa kuti apange chingalawa, kapena kuti chiboti chachikulu, kuti apulumutse anthu ochepa amene anali kuchita zabwino. Mphunzitsi Waluso ananena kuti tifunika kumakumbukira zimene zinachitika pa Chigumulacho.—Genesis 6:3, 4, 13, 14; Luka 17:26, 27.

Kodi ukudziŵa zimene zinachitikira angelo oipawo Chigumula chitabwera?— Anasiya kugwiritsa ntchito matupi a anthu amene anapangawo ndi kubwereranso kumwamba. Koma iwo sanakhalenso angelo a Mulungu, choncho anakhala angelo a Satana, kapena kuti ziwanda. Nanga ndi chiyani chinachitikira ana awo, zianthu zikuluzikulu zija?— Iwo anafa pa Chigumula. Anafa limodzi ndi anthu onse amene sanamvere Mulungu.

N’chifukwa chiyani masiku ano padziko lapansi pali mavuto ambiri kusiyana ndi kale?

Kuchokera panthaŵi ya Chigumulayo, Mulungu sanalole ziwanda kukhalanso anthu. Koma ngakhale ziwanda sitingazione, izo zimayesetsabe kuti anthu azichita zinthu zoipa kwambiri. Zikuvutitsa anthu kwambiri kusiyana ndi kalelo. Zikuvutitsa chonchi chifukwa zinachotsedwa kumwamba ndi kuponyedwa padziko lapansi.

Kodi ukudziŵa chifukwa chake ziwanda sitingazione?— Ndi chifukwa chakuti ndi zosaoneka. Koma tikutsimikiza kuti ziliko. Baibulo limanena kuti Satana ‘akunyenga anthu padziko lonse,’ ndipo ziwanda zake zimamuthandiza.—Chivumbulutso 12:9, 12.

Kodi nafenso Mdyerekezi ndi ziwanda zake akhoza kutinyenga, kapena kuti kutiputsitsa?— Inde akhoza, ngati sitisamala. Komabe sitifunika kuopa. Mphunzitsi Waluso anati: ‘Mdyerekezi sangandichite kanthu.’ Ngati nthaŵi zonse tiyandikira kwa Mulungu, iye adzatiteteza kwa Mdyerekezi ndi ziwanda zake.—Yohane 14:30.

Tifunika kudziŵa zinthu zoipa zimene ziwanda zimafuna kuti tizichita. Tsono taganiza. Kodi ndi zinthu zoipa ziti zimene ziwanda zinachita pamene zinabwera padziko lapansi?— Chigumula chisanachitike, zinali kugonana ndi akazi. Izitu zinali zosayenera kwa angelo. Ziwanda zimasangalala pamene anthu masiku ano samvera lamulo la Mulungu lonena za kugonana. Nditakufunsa, Kodi ndani amayenera kugonana?— Wayankha bwino, ndi anthu okha amene anakwatirana.

Masiku ano anyamata ndi atsikana ena amagonana, koma zimenezi ndi zoipa. Baibulo limanena za “mpheto” ya mwamuna, kapena kuti chiwalo choberekera cha mwamuna. (Levitiko 15:1-3, NW) Mpheto ya mkazi ndiyo chiwalo chake choberekera. Yehova analenga ziwalo zimenezi za thupi lathu kuti zizigwira ntchito yapadera imene amayenera kuchita anthu okhawo amene anakwatirana. Ziwanda zimasangalala anthu akamachita zinthu zimene Yehova amaletsa. Mwachitsanzo, ziwanda zimakondwera pamene mnyamata ndi mtsikana aseweretsana ziwalo zawo zoberekera. Ife sitifuna kusangalatsa ziwanda, si choncho?—

Pali chinanso chimene ziwanda zimakonda koma Yehova amadana nacho. Kodi ukuchidziŵa?— Chiwawa. (Salmo 11:5) Chiwawa ndi kuchitira anthu ena nkhanza ndi kuwapweteka. Kumbukira kuti zimenezi ndi zimene ana a ziwanda, zianthu zikuluzikulu zija, anali kuchita.

Ziwanda zimakondanso kuopsa anthu. Nthaŵi zina zimayerekeza kukhala anthu amene anamwalira. Ndipo mawu a ziwandazo angamveke ngati mmene anthu akufawo anali kulankhulira. Mwa kuchita zimenezi ziwanda zimapusitsa anthu ambiri kuti azikhulupirira kuti akufa ali moyo ndipo akhoza kulankhula ndi anthu amoyo. Inde, ziwanda zimachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti kuli mizukwa.

Choncho tiyenera kukhala ochenjera kuti Satana ndi ziwanda zake asatipusitse. Baibulo limachenjeza kuti: ‘Satana amadzionetsa ngati mngelo wabwino, ndipo atumiki ake amachitanso chimodzimodzi.’ (2 Akorinto 11:14, 15) Koma zoona zake ndi zakuti ziwanda ndi zoipa. Tiye tione zimene zingachite pofuna kuti ife tifanane nazo.

Kodi anthu amaphunzira bwanji zinthu zambiri zokhudza chiwawa, kugonana kolakwika, mizimu, ndi mizukwa?— Kodi si mwa kuonerera TV ndi mafilimu, kupita ku mavidiyo, kapenanso kugwirizana ndi ana amakhalidwe oipa kusukulu? Kodi ngati tichita zimenezi, tingayandikire kwambiri ndani? Mulungu kapena Mdyerekezi ndi ziwanda zake? Iwe ukuganiza bwanji?—

Kodi chingachitike ndi chiyani ngati tionerera chiwawa?

Kodi ukuganiza kuti ndani amene amafuna kuti tizimvetsera komanso kuonerera zinthu zoipa?— Inde, ndi Satana ndi ziwanda zake. Ndiye kodi iweyo ndi ine tifunika kuchita chiyani?— Tifunika kuŵerenga, kumvetsera, ndi kuonerera zinthu zabwino ndiponso zimene zidzatithandiza kutumikira Yehova. Kodi ungaganizeko zinthu zina zabwino zimene tingachite?—

Kodi ndi chiyani chimene chili chabwino kuchita?

Ngati timachita zabwino, palibe chifukwa choopera ziwanda. Yesu ndi wamphamvu kuposa ziwandazo, ndipo izo zimamuopa. Tsiku lina ziwanda zinadandaula kwa Yesu kuti: ‘Kodi mwabwera kudzatiwononga?’ (Marko 1:24) Kodi sitidzasangalala nthaŵi ikadzafika yakuti Yesu awononge Satana ndi ziwanda zake?— Koma panthaŵi ino tikutsimikiza kuti Yesu adzatiteteza ku ziwanda ngati nthaŵi zonse tiyandikira Yesuyo ndi Atate ake akumwamba.

Tiye tiŵerenge zimene tifunika kuchita, pa 1 Petro 5:​8, 9 ndi Yakobo 4:​7, 8.