Kuti Mutsanzire Yesu Muyenera . . .

Kuti Mutsanzire Yesu Muyenera . . .

KUMVERA ENA CHISONI

Chifukwa chakuti Yesu anali munthu wopanda uchimo sankakumana ndi mavuto amene anthu ena ankakumana nawo. Komabe ankawamvera chisoni. Yesu ankalolera kusiya zimene akuchita kuti awathandize ndipo nthawi zina ankachita zambiri kuposa zimene ankayenera kuchita. Iye ankachita zonsezi chifukwa choti ankamvera chisoni anthuwo. Onani zitsanzo zimene zikupezeka m’Mutu 32, 37, 57, 99.

KUKHALA WOCHEZEKA

Anthu amisinkhu yonse, achinyamata ndi achikulire omwe, ankakhala omasuka kucheza ndi Yesu chifukwa sanali wonyada komanso sankadziona ngati wapamwamba. Anthuwo ankaona kuti Yesu ankachita nawo chidwi ndipo zimenezi zinkachititsa kuti azimasuka akakhala naye. Kuti muone mmene Yesu ankachitira zinthu ndi anthu, werengani Mutu 25, 27, 95.

KUKONDA KUPEMPHERA

Yesu ankapemphera kwa Atate ake kuchokera pansi pa mtima akakhala payekha komanso akakhala ndi otsatira ake okhulupirika. Ankapemphera pa zochitika zosiyanasiyana osati nthawi ya chakudya yokha. Ankapemphera kuti athokoze Atate ake, kuti awalemekeze komanso ankapempha kuti amuthandize asanasankhe zinthu zofunika kwambiri. Onani zitsanzo m’Mutu 24, 34, 91, 122, 123.

KUKHALA WOSADZIKONDA

Nthawi zina, Yesu ankalephera kupumula komanso kucheza n’cholinga choti athandize anthu ena. Iye sankachita zinthu zodzikonda. Pamenepanso anatipatsa chitsanzo chabwino chimene tiyenera kutsanzira. Werengani Mutu 19, 41, 52 kuti muone mmene Yesu anasonyezera khalidwe limeneli.

KUKHULULUKIRA ENA

Sikuti Yesu ankangophunzitsa anthu kuti azikhululukirana koma nayenso ankasonyeza khalidweli pochita zinthu ndi ophunzira ake komanso anthu ena. Onani zitsanzo zimene zikupezeka m’Mutu 26, 40, 64, 85, 131 ndipo ganizirani zimene mungachite kuti muzisonyeza khalidwe limeneli.

KUKHALA WODZIPEREKA

Malemba ananeneratu kuti Ayuda ambiri adzakana Mesiya ndiponso kuti adani ake adzamupha. Zimenezi zikanachititsa kuti Yesu asachite zinthu zambiri pothandiza anthu mwauzimu. Komabe iye anadzipereka pothandiza anthu kuti azilambira m’njira imene Mulungu amaivomereza. Choncho Yesu ndi chitsanzo chabwino kwa otsatira ake onse kuti ayenera kukhalabe odzipereka pamene akukumana ndi mavuto kapena anthu akamawatsutsa. Werengani Mutu 16, 72, 103 kuti muone mmene Yesu anasonyezera kuti anali wodzipereka.

KUKHALA WODZICHEPETSA

Yesu anali wapadera m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ankadziwa zinthu zambiri komanso anali ndi nzeru kuposa munthu wina aliyense. Chifukwa chakuti Yesu analibe uchimo ankatha kuganiza komanso kuchita zinthu kuposa aliyense. Koma chifukwa chakuti anali wodzichepetsa ankatumikira anthu ena. Mukhoza kuona mmene Yesu anasonyezera khalidwe limeneli m’Mutu 10, 62, 66, 94, 116.

KULEZA MTIMA

Nthawi zonse Yesu ankaleza mtima ndi atumwi ake komanso anthu ena akalephera kutsatira chitsanzo chake kapena kuchita zimene wawauza. Ankabwereza zimene wawaphunzitsa moleza mtima n’cholinga choti athe kuyandikira kwa Yehova. Werengani Mutu 74, 98, 118, 135 kuti muone mmene Yesu anasonyezera kuleza mtima.