Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?

Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?

Kodi mungayankhe kuti . . .

  • inde?

  • ayi?

  • mwinamwake?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Zingatilimbikitse pamene wachibale wathu wamwalira.—2 Akorinto 1:3, 4.

Sitingaopenso imfa.—Aheberi 2:15.

Tidzaonananso ndi achibale athu amene anamwalira.—Yohane 5:28, 29.

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:

  • Mulungu ndi amene analenga moyo. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndiye “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9; Machitidwe 17:24, 25) Popeza kuti Mulungu ndi amene anapereka moyo kwa chinthu chilichonse chamoyo, sitingakayikire zoti angathe kuukitsa anthu amene anamwalira.

  • M’mbuyomu Mulungu anaukitsapo anthu. Baibulo limafotokoza nkhani za anthu 8 amene anaukitsidwa. Pa gulu la anthu amenewa panali achinyamata, achikulire, amuna ndiponso akazi. Ena mwa anthuwa anaukitsidwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anamwalira, koma mmodzi anaukitsidwa patatha masiku anayi ali m’manda.—Yohane 11:39-44.

  • Mulungu akufunitsitsa kuchitanso zimenezi. Yehova amadana ndi imfa, moti amaiona kuti ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) Mulungu ‘akulakalaka’ kugonjetsa mdani ameneyu mwa kuukitsa akufa. Iye akukumbukira anthu onse amene ali m’manda ndipo akufunitsitsa kuwaonanso ali ndi moyo padziko lapansili.—Yobu 14:14, 15.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

N’chifukwa chiyani timakalamba n’kufa?

Baibulo limayankha funso limeneli pa GENESIS 3:17-19 ndi pa AROMA 5:12.