MUTU 2

Muzikhala Okhulupirika

Muzikhala Okhulupirika

“Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Maliko 10:9

Yehova amafuna kuti tizikhala okhulupirika. (Aefeso 4:24) Kukhala okhulupirika n’kofunika kwambiri m’banja chifukwa popanda zimenezi mumangokayikirana. Koma kuti munthu akonde kwambiri mwamuna kapena mkazi wake ayenera kumukhulupirira.

Masiku ano, anthu ambiri sakhala okhulupirika m’banja. Choncho muyenera kuchita zinthu ziwiri kuti muteteze banja lanu.

1 MUZIONA KUTI BANJA LANU NDI LOFUNIKA KWAMBIRI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Dziwani kuti banja lanu ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu. Choncho muyenera kuliika patsogolo pochita zinthu.

Yehova amafuna kuti muziganizira kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu n’kumasangalala naye. (Mlaliki 9:9) Iye safuna kuti muzimunyalanyaza koma muziyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa. (1 Akorinto 10:24) Zochita zanu zizithandiza mnzanuyo kudziona kuti ndi wofunika kwambiri.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muziyesetsa kupeza nthawi yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndipo muzimumvetsera akamalankhula

  • Musiye kuchita zinthu mmene munkachitira muli nokha

2 MUZITETEZA MTIMA WANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Ngati munthu wapabanja amalakalaka anthu ena tinganene kuti ndi wosakhulupirika.

Yehova amanena kuti tiyenera ‘kuteteza mtima wathu.’ (Miyambo 4:23; Yeremiya 17:9) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kudziletsa kuti tisayang’anitsitse zinthu zosayenera. (Mateyu 5:29, 30) Tiyenera kutsanzira Yobu amene anachita pangano ndi maso ake kuti asayang’anitsitse akazi ena n’kuyamba kuwalakalaka. (Yobu 31:1) Muyeneranso kutsimikiza mumtima mwanu kuti musaonere zolaula. Komanso muzipeweratu kukopana ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Anthu asamachite kukayikira ngati mumakondadi mwamuna kapena mkazi wanu

  • Muziganizira maganizo a mwamuna kapena mkazi wanu ndipo muzisiyiratu kucheza ndi munthu amene angachititse mnzanu kuyamba nsanje