MUTU 7

Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu

Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu

“Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako.”—Deuteronomo 6:6, 7

Yehova amafuna kuti makolo azitsogolera ana awo. (Akolose 3:20) Choncho makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azikonda Yehova komanso kuti adzakhale anthu odalirika. (2 Timoteyo 1:5; 3:15) Makolo ayeneranso kudziwa zimene zili mumtima mwa ana awo. Musaiwale kuti ana amatsatira zimene mumachita. Choncho Mawu a Yehova ayenera kukhala mumtima mwanu choyamba kuti muphunzitse bwino ana anu.—Salimo 40:8.

1 ATHANDIZENI KUTI AZIMASUKA NANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Muzithandiza ana anu kuti azimasuka kulankhula nanu. Ana ayenera kudziwa kuti mukhoza kuwamvetsera nthawi iliyonse imene akufuna kukuuzani zinazake. Mukamakhala mwamtendere m’banja mwanu, ana amamasuka kufotokoza maganizo awo. (Yakobo 3:18) Koma sangamasuke akaona kuti mukhoza kukwiya kapena kuwadzudzula akakuuzani zinazake. Muyenera kuwalezera mtima ndipo muziwatsimikizira kuti mumawakonda.—Mateyu 3:17; 1 Akorinto 8:1.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzimvetsera ana anu akafuna kulankhula nanu

  • Muzilankhulana ndi ana anu nthawi zonse osati pakakhala vuto basi

2 MUZIYESETSA KUMVETSA MAGANIZO AWO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino.” (Miyambo 16:20) Nthawi zina mwana akalankhula musamaganizire zimene wanena koma zimene akutanthauza komanso mmene akumvera mumtima mwake. Achinyamata amakonda kukokomeza zinthu kapena kulankhula zina koma akutanthauza zina. Paja Baibulo limati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa.” (Miyambo 18:13) Choncho musamafulumire kukwiya.—Miyambo 19:11.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • aya mwana wanu alankhule zotani, yesetsani kuti musamudule mawu kapena kumupsera mtima

  • Muzikumbukira mmene munkamvera muli msinkhu wakewo komanso zimene munkaona kuti n’zofunika

3 MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.” (Miyambo 1:8) Yehova wapereka udindo wolera ana kwa bambo komanso mayi. Muyenera kuphunzitsa ana anu kuti azikulemekezani ndiponso kukumverani. (Aefeso 6:1-3) Ana amadziwa ngati makolo awo ‘sagwirizana.’ (1 Akorinto 1:10) Ngati simunagwirizane pa nkhani inayake, muziyesetsa kuti ana anu asaone zimenezi chifukwa angasiye kukulemekezani.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muyenera kugwirizana zimene muzichita polangiza ana anu

  • Ngati mukusiyana maganizo pa nkhaniyi, yesetsani kumvetsa zimene mnzanuyo akufuna

4 MUZIGWIRIZANA MMENE MUNGAWAPHUNZITSIRE

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.” (Miyambo 22:6) Sikuti kuphunzitsa bwino ana anu kumangochitika kokha. Koma muyenera kugwirizana zimene muzichita powaphunzitsa ndiponso kuwalangiza. (Salimo 127:4; Miyambo 29:17) Muyenera kuthandiza ana kumvetsa ubwino wa malamulo anu komanso zifukwa zimene mumawalangira. (Miyambo 28:7) Muziwaphunzitsanso kukonda Mawu a Yehova ndiponso kumvetsa mfundo zake. (Salimo 1:2) Zimenezi zingawathandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino.—Aheberi 5:14.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muziyesetsa kuthandiza ana anu kuti adziwe bwino Mulungu n’kumamudalira

  • Muziwathandiza kuzindikira ndiponso kupewa zinthu zoipa zimene zimapezeka pa Intaneti. Muziwaphunzitsanso mmene angapewere ogwirira ana

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera”