MUTU 9

Anachita Zinthu Mwanzeru

Anachita Zinthu Mwanzeru

1-3. (a) N’chiyani chinabweretsa mavuto pa nyumba ya Abigayeli? (b) Kodi tiphunzira zotani zokhudza mzimayi wochititsa chidwiyu?

TSIKU lina Abigayeli anaona mmodzi wa anyamata ake akubwera kudzaonana naye ali ndi mantha kwambiri, ndipo zinali zomveka chifukwa moyo wawo unali pangozi. Nthawi imeneyo n’kuti asilikali 400 ali m’njira kudzapha munthu aliyense wamwamuna pakhomo pa Nabala, amene anali mwamuna wa Abigayeli. Komano n’chifukwa chiyani asilikaliwo ankafuna kudzachita zimenezi?

2 Zonsezi zinayambika chifukwa cha Nabala yemwe anali wakhalidwe loipa kwambiri. Iye anali wankhanza ndiponso wamwano. Koma pa nthawiyi anaputa munthu wolakwika. Iye anaputa mtsogoleri wa asilikali odziwa nkhondo kwambiri. Komabe, mmodzi wa anyamata a Nabala, yemwe mwina anali m’busa, anauza Abigayeli zimene zinachitikazo. Anachita zimenezi chifukwa ankakhulupirira kuti Abigayeli akhoza kuganizira njira inayake yowapulumutsira. Komano kodi mzimayi mmodzi akanakwanitsa kulimbana ndi gulu la asilikali?

Kodi mzimayi mmodzi akanakwanitsa kulimbana ndi gulu la asilikali?

3 Choyamba tiyeni tikambirane kaye za mzimayi wochititsa chidwi ameneyu. Kodi Abigayeli anali ndani? Nanga kodi mavutowa anayambika bwanji? Ndipo ifeyo tingaphunzirepo chiyani pa chikhulupiriro cha mayiyu?

Mkazi “Wanzeru Kwambiri Ndi Wokongola”

4. Kodi Nabala anali munthu wotani?

4 Abigayeli ndi Nabala anali osayenerana. Abigayeli anali wakhalidwe labwino kwambiri koma anakwatiwa ndi mwamuna wachabechabe. Mwamunayu anali wolemera ndipo ankadziona kuti anali munthu wofunika kwambiri. Koma kodi anthu ena ankamuona bwanji? M’Baibulo lonse, palibe munthu amene amatchulidwa ndi mayina oipa kuposa Nabala. Ndipo dzina lakuti Nabala limatanthauza “Wopanda nzeru” kapena “Wopusa.” Kodi makolo ake ndi omwe anam’patsa dzinali kapena anachita kupatsidwa ndi anthu ena chifukwa cha khalidwe lake loipa? Sizikudziwika, koma dzinali linali logwirizana kwambiri ndi khalidwe lake chifukwa iye “anali wouma mtima ndi wokonda kuchita zinthu zoipa.” Analinso chidakwa komanso wankhanza moti anthu ambiri ankamuopa kwambiri ndipo sankagwirizana naye.—1 Sam. 25:2, 3, 17, 21, 25.

5, 6. (a) Kodi Abigayeli anali ndi makhalidwe osiririka ati? (b) Kodi ziyenera kuti Abigayeli anakwatiwa ndi Nabala chifukwa chiyani?

5 Koma Abigayeli anali wosiyana kwambiri ndi mwamuna wake. Dzina lake limatanthauza kuti, “Bambo Anga Asangalala.” Abambo ambiri amasangalala akabereka mwana wamkazi wokongola, koma anzeru amasangalala kwambiri mwana wawoyo akakhalanso ndi khalidwe labwino. Ndipo nthawi zambiri, munthu wokongola kwambiri amaiwala kuti chofunika kwambiri ndi kukhala ndi makhalidwe monga kuganiza bwino, nzeru, kulimba mtima kapenanso chikhulupiriro. Koma zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi Abigayeli, chifukwa Baibulo limasonyeza kuti ngakhale anali wokongola kwambiri, analinso wanzeru.—Werengani 1 Samueli 25:3.

6 Ena angadabwe kuti, n’chifukwa chiyani mkazi wanzeru ngati ameneyu analola kukwatiwa ndi Nabala, munthu wachabechabe? Kumbukirani kuti kale makolo ambiri ankasankhira ana awo munthu woti akwatirane naye. Ngakhale munthu atasankha yekha womanga naye banja, komabe makolo ndi amene ankapereka chilolezo choti mwana wawoyo akwatirane ndi munthuyo. Kodi mwina makolo a Abigayeli ndi amene anakonza zoti mwana wawo akwatiwe ndi Nabala chifukwa choti Nabalayo anali munthu wotchuka komanso wachuma? Ngati makolo ndi amene anakonza zoti iye akwatiwe ndi Nabala, n’kutheka kuti anachita zimenezi chifukwa anali osauka. Komabe mfundo ndi yakuti, ndalama sizinachititse Nabala kukhala mwamuna wabwino.

7. (a) Kodi makolo ayenera kupewa chiyani kuti athandize ana awo kuona kuti ukwati ndi wopatulika? (b) Kodi Abigayeli ankayesetsa kuchita chiyani?

7 Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo kuti aziona kuti ukwati ndi wopatulika. Choncho, salimbikitsa anawo kuti akwatiwe ndi winawake chifukwa choti munthuyo ndi wolemera. Ndiponso sakakamiza ana awo kuti ayambe chibwenzi asanakhwime moti n’kukwaniritsa maudindo a m’banja. (1 Akor. 7:36) Komabe popeza Abigayeli anali atakwatiwa kale, zinali zosatheka kuti aganizire mfundo zimenezi. Kaya iye anakwatiwa ndi Nabala pa zifukwa zotani, koma chodziwika n’choti ankayesetsa kupirira mavuto a m’banja.

“Mbuyanga Walalatira Nthumwizo”

8. Kodi Nabala ananyoza ndani, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti pamenepa analakwitsa kwambiri?

8 Nabala anachita zinthu zoipa zimene zinavutitsa kwambiri Abigayeli. Iye ananyoza kwambiri Davide, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Komanso Davide anali atadzozedwa ndi mneneri Samueli kuti adzalowe m’malo mwa Mfumu Sauli mogwirizana ndi mmene Mulungu anafunira. (1 Sam. 16:1, 2, 11-13) Davide anali atathawa Sauli, amene anali mfumu yansanje komanso yoopsa kwambiri, ndipo anakakhala m’chipululu ndi asilikali ake okwana 600.

9, 10. (a) Kodi Davide ndi anthu ake ankakumana ndi mavuto otani? (b) N’chifukwa chiyani Nabala ankayenera kuyamikira zimene Davide ndi anthu ake ankachita? (Onaninso mawu a m’munsi a pa ndime 10.)

9 Nabala anali ndi nkhosa zokwana 3,000 ndipo ankakhala m’mudzi wa Maoni koma zikuoneka kuti anali ndi malo ena ku Karimeli, komwe ankagwirako ntchito. * Dera limeneli linali lokwera ndipo kunkapezeka msipu wobiriwira. Choncho antchito a Nabala ankadyetsa nkhosa zake m’derali. Komabe, derali linali losalimidwa ndipo chakum’mwera kwake kunali chipululu chachikulu cha Parana. Chakum’mawa kwake, kufupi ndi Nyanja Yamchere, kunali dera lokhala ndi zigwembe ndiponso mapanga. Davide ndiponso anthu amene anali nawo ankavutika kwambiri kudera limeneli kuti apeze chakudya komanso ankakumana ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri iwo ankakumana ndi anyamata omwe ankaweta nkhosa za Nabala.

10 Kodi asilikaliwa ankatani akakumana ndi abusawo? Zinali zosavuta kuti aziba nkhosa za Nabala, koma iwo sankachita zimenezi. M’malomwake, iwo ankateteza nkhosazo ndiponso abusawo. (Werengani 1 Samueli 25:15, 16.) Abusa pamodzi ndi nkhosa zawo ankakumana ndi mavuto ambirimbiri chifukwa kuderali kunkapezeka zilombo zambiri zolusa. Komanso derali linali pafupi kwambiri ndi malire akum’mwera a dziko la Isiraeli, moti akuba ochokera m’madera ena ankabwera kuderali pafupipafupi. *

11, 12. (a) Kodi Davide anasonyeza bwanji nzeru komanso ulemu potumiza uthenga kwa Nabala? (b) N’chifukwa chiyani tingati Nabala sanayankhe bwino pempho la Davide?

11 Davide ayenera kuti anali ndi udindo waukulu kwambiri wopezera chakudya anthu ake, omwe anali nawo m’chipululumo. Motero tsiku lina anatumiza anyamata ake 10 kuti akapemphe chakudya kwa Nabala. Nthawi imene Davide anatumiza anyamatawa inali yabwino chifukwa inali nthawi yometa ubweya wankhosa ndiponso yamadyerero. Pa nthawiyi anthu ankakonda kugawana zinthu. Komanso Davide anasankha bwino mawu oti anyamata ake akalankhule kwa Nabala ndipo anawauza kuti akalankhule naye mwaulemu kwambiri. Anawalangiza anyamatawo kukanena kuti ‘mwana wanu Davide’ ndi amene akupempha zinthuzi ndipo mwina anachita zimenezi posonyeza kuti ankazindikira zoti Nabala ndi munthu wamkulu. Koma kodi Nabala anatani?—1 Sam. 25:5-8.

12 Iye anakwiya kwambiri moti mnyamata wake, yemwe watchulidwa kumayambiriro kwa nkhani ino, pouza Abigayeli za nkhaniyi ananena kuti “mbuyanga walalatira nthumwizo.” Nabala anali munthu womana kwambiri moti anauza anyamatawo kuti sangawononge nyama, madzi ndiponso mkate wake kupatsa Davide ndi anyamata ake. Iye ananyoza Davide ponena kuti anali wachabechabe ndiponso anali ngati kapolo amene wathawa mbuye wake. N’kutheka kuti Nabala ankaona Davide mofanana ndi mmene Sauli, yemwe ankadana ndi Davideyo, ankamuonera. Nabala ndi Sauli sankaona Davide ngati mmene Yehova ankamuonera. Mulungu ankakonda kwambiri Davide ndipo ankamuona kuti ndi mfumu ya m’tsogolo ya Isiraeli, osati ngati kapolo wothawa mbuye wake.—1 Sam. 25:10, 11, 14.

13. (a)  Kodi Davide anachita chiyani atanyozedwa ndi Nabala? (b) Kodi mfundo yopezeka pa Yakobo 1:20 ikutiphunzitsa chiyani tikaganizira zimene Davide ankafuna kuchita?

13 Ndiyeno Davide atauzidwa ndi anyamata ake zimene Nabala ananena, anapsa mtima kwambiri. Nthawi yomweyo analamula asilikali ake kuti: “Aliyense amange lupanga lake m’chiuno!” Davide pamodzi ndi asilikali ake 400 ananyamula zida ndipo anayamba ulendo wopita kukapha Nabala. Iwo anakonza zokaseseratu munthu aliyense wamwamuna pakhomo pa Nabala. (1 Sam. 25:12, 13, 21, 22) Zinali zomveka kuti Davide akwiye koma zimene ankafuna kuchita chifukwa cha kukwiyako zinali zolakwika. Baibulo limati: “Mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:20) Komano kodi Abigayeli akanatani kuti apulumutse anthu a m’banja mwake?

“Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako”

14. (a) Kodi Abigayeli anachita chiyani posonyeza kuti ankafuna kukonza zimene Nabala anali atalakwitsa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira kusiyana kwa Nabala ndi Abigayeli? (Onaninso mawu a m’munsi.)

14 Zimene Abigayeli anachita pomvetsera zimene mnyamata uja anamuuza zinasonyeza kuti akufuna kukonza zimene mwamuna wake anali atalakwitsa. Mosiyana ndi Nabala, Abigayeli anali wofunitsitsa kumvetsera. Ponena za Nabala, mnyamatayo anati: “Mbuye wathu ndi munthu wopanda pake, sitingathe kulankhula naye.” * (1 Sam. 25:17) N’zomvetsa chisoni kuti Nabala anali wonyada kwambiri moti zimenezi zinamuchititsa kuti asamamve za ena. N’chimodzimodzinso masiku ano, anthu ambiri safuna kumva za ena. Koma mnyamatayo ankadziwa kuti Abigayeli anali munthu wabwino kwambiri, ndipo n’chifukwa chake anaganiza zomuuza nkhaniyi.

Mosiyana ndi Nabala, Abigayeli ankamva zonena za ena

15, 16. (a) Kodi Abigayeli anasonyeza bwanji kuti anali mkazi wabwino ngati amene anatchulidwa m’buku la Miyambo? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Abigayeli anachita sikunali kusagonjera mwamuna wake monga mutu?

15 Abigayeli anaiganizira kwambiri nkhaniyi ndipo anaona kuti ayenera kuchitapo kanthu. Baibulo limati: “Nthawi yomweyo, Abigayeli anafulumira.” M’nkhaniyi, mawu onena za mzimayiyu akuti “anafulumira” amapezeka kanayi. Iye anakonza mphatso zokapatsa Davide ndi anthu ake. Zina mwa mphatsozo zinali mikate, vinyo, nkhosa, tirigu wokazinga, mphesa zouma zoumba pamodzi ndiponso nkhuyu zouma zoumba pamodzi. N’zoonekeratu kuti Abigayeli ankadziwa bwino zinthu zimene anali nazo ndiponso ankadziwa kuyendetsa bwino zinthu m’banja lake mofanana ndi mkazi wanzeru wotchulidwa m’buku la Miyambo. (Miy. 31:10-31) Abigayeli anatumiza anyamata ake kuti atsogole ndi mphatsozo ndipo iye anatsatira pambuyo ali yekha. Baibulo limati: “Koma mwamuna wake Nabala sanamuuze kalikonse.”—1 Sam. 25:18, 19.

16 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Abigayeli sankagonjera mwamuna wake monga mutu wa banjalo? Ayi si choncho. Nabala anali atachita zinthu zoipa kwa mtumiki wodzozedwa wa Yehova ndipo zimenezi zikanaphetsa anthu ambiri osalakwa a panyumba pake. Komanso Abigayeli akanapanda kuchita chilichonse, akanakhala ngati akugwirizana ndi zimene mwamuna wake anachita. Choncho, iye anaona kuti anayenera kugonjera Mulungu m’malo mogwirizana ndi zinthu zoipa zimene mwamuna wake anachita.

17, 18. Kodi Abigayeli anachita chiyani atakumana ndi Davide, nanga n’chifukwa chiyani mawu ake anali ogwira mtima?

17 Pasanapite nthawi, Abigayeli anakumana ndi Davide ndi asilikali ake. Apanso iye anafulumira kutsika pabulu wake n’kugwada posonyeza kudzichepetsa pamaso pa Davide. (1 Sam. 25:20, 23) Kenako anachonderera Davide mochokera pansi pa mtima kuti achitire chifundo mwamuna wake pamodzi ndi anthu a m’banja lake. N’chifukwa chiyani mawu akewo anali ogwira mtima?

“Chonde, lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu”

18 Abigayeli analankhula ngati kuti walakwitsa ndi iyeyo ndipo anapempha Davide kuti am’khululukire. Iye anavomereza kuti mwamuna wake anali wopanda nzeru, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake. Choncho anapempha Davide, yemwe anali waulemu wake, kuti asalimbane ndi munthu wopanda nzeruyo. Iye analankhula mosonyeza kuti ankadziwa zoti Davide ndi mtumiki wa Yehova ndiponso kuti akumenya “nkhondo za Yehova.” Abigayeli anasonyezanso kuti ankadziwa zoti Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa ufumu. Tikutero chifukwa polankhula ndi Davide, iye anati: “Yehova . . . adzakuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli.” Kenako anapempha Davide kuti asachite chilichonse chimene chingam’chititse kuti akhale ndi mlandu wamagazi kapena zimene ‘zikanavutitsa chikumbumtima’ chake. (Werengani 1 Samueli 25:24-31.) Apa iye analankhuladi mokoma mtima ndiponso mogwira mtima.

19. Kodi Davide anatani atamva mawu a Abigayeli, nanga n’chifukwa chiyani anamuyamikira?

19 Ndiyeno kodi Davide anachita chiyani? Iye analandira zimene Abigayeli anamubweretsera ndipo ananena kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana nane lero! Iwenso udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako. Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi.” Davide anayamikira kwambiri Abigayeli chifukwa cholimba mtima n’kupita mwachangu kukakumana naye ndiponso chifukwa chomuthandiza kuti asachite zinthu zimene zikanachititsa kuti akhale ndi mlandu wamagazi. Kenako Davide anauza Abigayeli kuti: “Pita kunyumba kwako mwamtendere.” Anamuuzanso modzichepetsa kuti: “Ndamvera mawu ako.”—1 Sam. 25:32-35.

“Ine Kapolo Wanu”

20, 21. (a) Kodi n’chifukwa chiyani zili zochititsa chidwi kuti Abigayeli anali wofunitsitsabe kubwerera kwa mwamuna wake? (b) Kodi Abigayeli anasonyeza bwanji kulimba mtima ndiponso nzeru posankha nthawi yabwino yolankhula ndi mwamuna wake?

20 Atanyamuka, Abigayeli ayenera kuti ankaganizirabe zimene anakambirana ndi Davide ndipo anatha kuona kuti Davide anali munthu wokhulupirika ndiponso wokoma mtima mosiyana ndi mwamuna wake yemwe anali wankhanza kwambiri. Komabe sikuti iye ankangokhalira kuganizira zimenezi. Baibulo limati: “Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala.” Izi zikusonyeza kuti iye anabwerera kwa mwamuna wake ndipo anali ndi mtima wofunitsitsa kusamalira banja lake mmene angathere. Komabe anafunika kudziwitsa mwamuna wakeyo za mphatso zimene anapatsa Davide ndi anthu ake, chifukwa monga mutu wabanja, Nabala anayenera kudziwa zimene zinachitika. Abigayeli atafika kunyumba kwake, anafunika kufotokoza yekha zimenezi kwa mwamuna wake kuopera kuti mwamunayo akanachita manyazi akanamva nkhaniyi kwa anthu ena. Komabe, pa nthawiyi zinali zosatheka kumuuza nkhaniyi chifukwa anali paphwando lalikulu ngati la mfumu ndipo anali ataledzera kwambiri.—1 Sam. 25:36.

Abigayeli anafotokozera mwamuna

21 Pamenepanso Abigayeli anasonyeza kuti anali wolimba mtima komanso woganiza bwino chifukwa anadikira mpaka m’mawa kuti alankhule ndi mwamuna wakeyo ali bwinobwino. Anadziwa kuti mwamuna wake angamvetsere bwino atakhala kuti sanaledzere ngakhale kuti pa nthawiyi m’pamene ankakhala woopsa kwambiri. Ngakhale zinali choncho, iye anauzabe mwamuna wakeyo zonse zimene zinachitika. Mwachidziwikire Abigayeli ankayembekezera kuti mwamuna wake alusa kwambiri, mwinanso kufika pomumenya. Koma Nabala atamva zimenezi, anangokhala zii, osatakataka.—1 Sam. 25:37.

22. Kodi n’chiyani chinachitikira Nabala, nanga tikuphunzirapo chiyani?

22 Kodi n’chifukwa chiyani Nabala anangokhala, osatakataka? Baibulo limati: “Mtima wake unaferatu mkati mwake ndipo iye anakhala ngati mwala.” Mwina anadwala matenda a sitiroko chifukwa cha mantha. Iye anamwalira patapita masiku 10, osati chifukwa cha matenda, koma chifukwa choti ‘Yehova anamukantha ndipo anafa.’ (1 Sam. 25:38) Nabala atafa, mavuto amene Abigayeli ankakumana nawo m’banja lakeli anathera pomwepo. Ngakhale kuti masiku ano Yehova sapha anthu ngati mmene anachitira ndi Nabala, nkhaniyi ikutiphunzitsa mfundo yoti Yehova amaona nkhanza komanso zoipa zonse zimene zimachitika m’banja. Pa nthawi yake yoyenerera, iye adzapereka chilango kwa anthu ochita makhalidwe oipawa.—Werengani Luka 8:17.

23. Kodi Abigayeli anapeza madalitso enanso ati, ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti iye sanayambe kudzikweza?

23 Kuwonjezera pa kutha kwa mavuto a m’banja lake, Abigayeli anapezanso madalitso ena. Davide atamva kuti Nabala wafa, anatumiza anthu kuti akamufunsirire ukwati. Abigayeli anayankha kuti: “Ine kapolo wanu ndine wokonzeka kukhala mtumiki wosambitsa mapazi a atumiki a mbuyanga.” N’zoonekeratu kuti iye sanayambe kudzikweza chifukwa choti wapeza mwayi wokhala mkazi wa Davide ndipo ananena kuti anali wokonzeka kukhala mtumiki wa akapolo a Davide. Zitatero, Baibulo limafotokozanso kuti ananyamuka mofulumira kupita kwa Davide.—1 Sam. 25:39-42.

24. Kodi Abigayeli anakumana ndi mavuto otani atakwatirana ndi Davide, koma kodi mwamuna wake komanso Mulungu ankamuona bwanji?

24 Komabe zimenezi sizinatanthauze kuti tsopano moyo wa Abigayeli ukhala wopanda mavuto alionse, chifukwa Davide anali kale ndi mkazi wina dzina lake Ahinowamu. Ngakhale kuti pa nthawiyo Mulungu ankalola mitala, n’zoonekeratu kuti akazi okhulupirika omwe anali pa mitala ankakumana ndi mavuto ambiri. Komanso pa nthawiyi Davide anali asanakhale mfumu ndipo panali mavuto ambiri amene akanakumana nawo asanakhale pa udindowo. Koma Abigayeli ankathandiza ndiponso kulimbikitsa Davide ndi mtima wake wonse ndipo anam’berekera mwana wamwamuna. Abigayeli ankaonanso kuti mwamuna wakeyo ankam’lemekeza, ankam’konda ndiponso ankamuteteza. Ndipotu pa nthawi inayake, Davide anapulumutsa mkazi wakeyu kwa anthu omwe anamuba. (1 Sam. 30:1-19) Choncho, Davide ankatsanzira Yehova Mulungu, yemwe amakonda ndiponso kulemekeza akazi oganiza bwino, olimba mtima ndiponso okhulupirika ngati mmene analili Abigayeli.

^ ndime 9 Karimeli ameneyu si phiri lotchuka lomwe linali kumpoto kwambiri kwa Maoni komwe pambuyo pake mneneri Eliya anakumana ndi aneneri a Baala. (Onani Mutu 10.) Koma unali mudzi womwe unali kufupi ndi chipululu cha Parana.

^ ndime 10 Zikuoneka kuti Davide ankaona kuti kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo kunali kutumikira Yehova Mulungu. Masiku amenewo, Yehova ankafuna kuti mbadwa za Abulahamu, Isake ndi Yakobo zizikhala m’derali. Choncho kuteteza anthu a m’derali ndiponso ziweto zawo unali utumiki wopatulika.

^ ndime 14 Mawu enieni omwe mnyamatayo anagwiritsira ntchito ponena za Nabala ndi akuti “mwana wa beliyali (wachabechabe).” Pavesi limeneli, Mabaibulo ena amati Nabala anali “munthu wosamva za ena,” ndipo “sichinali chinthu chanzeru kulankhula naye.”