MUTU 6

Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima

Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani Hana sankasangalala pamene ankakonzekera ulendo wopita kuchihema? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani ya Hana?

PA NTHAWI ina Hana anali kalikiliki kukonzekera ulendo ndipo zimenezi zinathandiza kuti aiwaleko mavuto ake. Ulendowu unali wosangalatsa kwambiri. Chaka chilichonse, mwamuna wake, Elikana, ankapita ndi banja lake lonse kukalambira kuchihema ku Silo. Yehova ankafuna kuti nthawi imeneyi izikhala yosangalatsa. (Werengani Deuteronomo 16:15.) Choncho Hana ayenera kuti kuyambira ali mwana ankasangalala kukachita nawo misonkhano imeneyi. Koma zinthu pa moyo wake zinali zisakuyenda bwino.

2 Hana anali ndi mwayi kuti mwamuna wake, Elikana, ankamukonda kwambiri. Koma Elikana analinso ndi mkazi wina ndipo dzina lake anali Penina. Zikuoneka kuti mkazi ameneyu ankachita zilizonse zimene angathe kuti azimusowetsa Hana mtendere. Penina anapeza njira yomupweteketsera mtima Hana, ngakhale pazochitika zapadera zapachaka zimenezi. Kodi ankachita bwanji zimenezi? Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi kukhulupirira Yehova kunathandiza bwanji Hana kupirira mavuto amene ankaoneka ngati ovuta kuwapirira? Ngati nanunso mukukumana ndi mavuto amene amakuchititsani kuti musamasangalale ndi moyo, nkhani ya Hana ingakuthandizeni kwambiri.

“N’chifukwa Chiyani Ukupwetekedwa Mtima?”

3, 4. Fotokozani mavuto awiri amene Hana anali nawo.

3 Baibulo limasonyeza kuti Hana anali ndi mavuto akuluakulu awiri. Panali zochepa zimene akanachita ndi vuto loyambalo, koma pa vuto lachiwirilo, panalibiretu chimene akanachita. Vuto loyamba linali lakuti Hana anali pa mitala, ndipo mkazi mnzake ankadana naye kwambiri. Vuto lachiwiri linali lakuti iye anali wosabereka. Zimenezi zimakhala zokhumudwitsa kwa mkazi amene akufuna kukhala ndi ana. Ndipo m’nthawi ya Hana komanso malinga ndi chikhalidwe cha kwawoko, kukhala wosabereka kunali chinthu chopweteka kwabasi. Banja lililonse linkaona kuti kukhala ndi ana n’kofunika kwambiri kuti dzina la banjalo lisafe. Choncho, kukhala wosabereka kunali kochititsa manyazi komanso kunkachititsa kuti munthu azinyozedwa kwambiri.

4 N’kutheka kuti Hana akanapirira vuto lakelo zikanakhala kuti Penina sankamuvutitsa. Mitala si yabwino chifukwa kawirikawiri m’banja lamitala mumakhala kudana, kukangana ndi kupweteketsana mtima. Poyambirira, Mulungu anayambitsa banja la mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Choncho, mitala ndi yosiyana kwambiri ndi zimene Mulungu anayambitsa m’munda wa Edeni. (Gen. 2:24) Baibulo limasonyeza kuti mitala si yabwino, ndipo nkhani yokhudza zimene zinkachitika m’banja la Elikana ndi umboni woonekeratu wa zimenezi.

5. N’chifukwa chiyani Penina ankavutitsa Hana, ndipo ankachita bwanji zimenezi?

5 Elikana ankamukonda kwambiri Hana. Mbiri ya Ayuda imasonyeza kuti Hana anali mkazi woyamba ndipo patapita zaka m’pamene Elikana anakwatira Penina. Mulimonse mmene zinalili, mfundo ndi yakuti, Penina ankamuchitira nsanje kwambiri Hana, ndipo ankachita zoipa zambiri n’cholinga choti mnzakeyo azisowa mtendere. Penina ankapezerapo mwayi chifukwa chakuti Hana ali wosabereka. Penina ankati akabereka mwana m’pamene ankanyoza kwambiri mnzakeyo n’kumadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri. M’malo momumvera chisoni mkazi mnzakeyo chifukwa anali wosabereka, Penina anapezerapo mwayi wosowetsa Hana mtendere. Baibulo limanena kuti Penina ankavutitsa Hana kwambiri “n’cholinga choti amukhumudwitse.” (1 Sam. 1:6) Ndipotu iye ankachita dala zimenezi. Cholinga chake chinali kum’pweteketsa mtima Hana ndipo ndi zimene zinachitikadi.

Hana ankakhala wachisoni kwambiri chifukwa chakuti anali wosabereka ndipo Penina ankachita chilichonse kuti mkazi mnzakeyu asowe mtendere chifukwa cha vuto lakelo

6, 7. (a) Ngakhale kuti Elikana anayesetsa kulimbikitsa Hana, n’chifukwa chiyani Hanayo sanamuuze nkhani yonse? (b) Kodi kusabereka kwa Hana ndi umboni wakuti Yehova sankasangalala naye? Fotokozani. (Onani mawu a m’munsi.)

6 Zikuoneka kuti Penina ankakonda kuvutitsa Hana ikafika nthawi yopita ku Silo. Ndipo chaka china nthawiyi itakwana, Elikana anapatsa ‘ana onse a Penina, aamuna ndi aakazi,’ omwe anali ambiri, magawo a nsembe zoti akapereke kwa Yehova. Zitatere, Penina anayamba kunyoza Hana chifukwa cha vuto lake losabereka. Zimenezi zinachititsa kuti Hana akhumudwe kwambiri moti ankangolira ndipo sankadya. Elikana anazindikira kuti Hana mkazi wake wokondedwa wakhumudwa ndipo sakudya. Choncho anayesetsa kuti amulimbikitse. Iye anamufunsa kuti: “Hana, n’chifukwa chiyani ukulira, ndipo n’chifukwa chiyani sukudya? Komanso n’chifukwa chiyani ukupwetekedwa mtima? Kodi sindine woposa ana aamuna 10 kwa iwe?”​—1 Sam. 1:4-8.

7 Elikana anazindikira kuti Hana anali wokhumudwa chifukwa cha vuto lake losabereka. Hana ayenera kuti anayamikira kwambiri zimene mwamuna wake ananena pofuna kumulimbikitsa. * Koma Elikana sananene chilichonse chokhudza zoipa zimene Penina ankachitira Hana, ndipo nkhaniyi siisonyeza kuti Hana anafotokozera Elikana zoipa zimene Penina ankamuchitira. Mwina Hana anaona kuti kumunenera Penina kukanangowonjezera mavuto ake. Ndipo kodi Hana akanafotokozera Elikana nkhaniyi, sizikanangochititsa kuti Peninayo azidana naye kwambiri? Nanga zimenezi sizikanachititsa kuti ana ndiponso antchito a Penina azidana nayenso kwambiri? Zimenezi zikanapangitsa kuti Hana azingokhala ngati mlendo panyumba pake pomwe.

Pamene Hana ankakumana ndi zokhoma kunyumba kwake, ankadalira Yehova

8. Anthu akamatichitira zinthu zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani ndi bwino kukumbukira kuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo?

8 Kaya Elikana ankadziwa zonse zimene Penina ankachitira Hana kapena ayi, koma Yehova Mulungu ankaona zonse. Tikutero chifukwa Baibulo limafotokoza zonse zimene zinachitika ndipo zimenezi ndi chenjezo kwa onse amene amachitira ena nsanje komanso zinthu zina zoipa, ngakhale zooneka ngati zazing’ono. Komanso, mofanana ndi Hana, anthu osalakwa ndiponso okonda mtendere amalimbikitsidwa podziwa kuti Mulungu, yemwe ndi wachilungamo, amathetsa mavuto pa nthawi imene iye wasankha komanso m’njira imene waona kuti ndi yoyenera. (Werengani Deuteronomo 32:4.) Hana ayenera kuti ankadziwa bwino zimenezi, chifukwa anapempha Yehova kuti amuthandize.

“Sanakhalenso Ndi Nkhawa”

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Hana anachita popitabe ku Silo ngakhale kuti ankadziwa zoti mkazi mnzake azikamunyoza?

9 M’mawa wa tsiku la ulendoli, banja lonse la Elikana, linali pakalikiliki kukonzekera. Banja lalikululi linkakonzekera ulendo wa makilomita oposa 30 wopita ku Silo, kudutsa m’mapiri a ku Efraimu. * Kwa munthu woyenda pansi, ulendowu unali wa tsiku limodzi kapena masiku awiri. Hana ankadziwa kuti mkazi mnzake azikamunyoza, koma anapitabe. Pamenepatu iye anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu olambira Mulungu masiku ano. Si bwino kulola khalidwe loipa la anthu ena kutilepheretsa kulambira Mulungu. Ngati titachita zimenezi zingatilepheretse kulandira madalitso amene angatithandize kupirira mavuto.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani Hana anapita kukachisi atangomaliza kudya? (b) Kodi Hana anafotokoza bwanji mavuto ake kwa Atate wake wakumwamba?

10 Kenako banjali linafika ku Silo. Mzinda wa Silo unali paphiri lozunguliridwa ndi mapiri ena akuluakulu. Akuyandikira, Hana ayenera kuti ankaganizira kwambiri zimene akauze Yehova m’pemphero. Banjali litafika kumeneko, linadya chakudya ndipo Hana atangomaliza kudya, anachoka pagululo n’kukalowa kuchihema cha Yehova. Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe, anali atakhala pafupi ndi khomo la chihemacho. Koma Hana anangomudutsa chifukwa ankaganizira za Mulungu wake basi. Iye anali ndi chikhulupiriro chonse kuti kuchihemako Mulungu akamva pemphero lake. Ankaona kuti mwina palibe munthu amene ankamvetsa mavuto ake, koma ankadziwa kuti Atate wake wakumwamba ankamvetsa. Chisoni chake chitakula, anayamba kulira.

11 Hana anayamba kulankhula ndi Yehova chamumtima, uku akusisima. Milomo yake inkanjenjemera pofotokoza mavuto ake. Anapemphera kwa nthawi yaitali, kuuza Atate wake wakumwamba zakukhosi kwake. Koma sikuti iye anangouza Mulungu kuti akufunitsitsa atakhala ndi mwana. Ngakhale kuti Hana ankafunitsitsa kuti Mulungu amudalitse, analinso wokonzeka kupatsa Mulungu chilichonse. Choncho analonjeza Mulungu kuti akadzabereka mwana wamwamuna, adzamupereka kuti akatumikire Yehova kukachisi.—1 Sam. 1:9-11.

12. Kodi chitsanzo cha Hana chikusonyeza kuti tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya pemphero?

12 Pamenepa Hana anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki onse a Mulungu pa nkhani ya pemphero. Yehova amafuna kuti atumiki ake azipemphera kwa iye momasuka, osakayikira chilichonse. Iye amafuna kuti anthu azimuuza mavuto awo onse monga mmene mwana amachitira popempha chinthu kwa kholo lake limene limamukonda. (Werengani Salimo 62:8; 1 Atesalonika 5:17.) Mtumwi Petulo analemba kuti popemphera kwa Yehova ‘tizimutulira nkhawa zathu zonse, pakuti amatidera nkhawa.’—1 Pet. 5:7.

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani Eli anamunena Hana kuti waledzera? (b) N’chifukwa chiyani zimene Hana anachita ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe?

13 Yehova amamvetsa mavuto athu komanso amatimvera chisoni kuposa mmene anthu amachitira. Hana akulira popemphera, anadzidzimuka kumva munthu akumulankhula. Anali Eli, mkulu wa ansembe, yemwe ankaona zimene Hana ankachita. Iye anafunsa Hanayo kuti: “Kodi ukhala woledzera mpaka liti? Pita kaye, kuledzera kwakoku kuyambe kwatha.” Eli anali ataona kuti milomo ya Hana ikunjenjemera, akusisima ndiponso akuoneka kuti akuvutika kwambiri maganizo. M’malo momufunsa kuti watani, anangofikira kumunena kuti waledzera.—1 Sam. 1:12-14.

14 Ziyenera kuti zinali zowawa kwambiri kwa Hana kuona kuti pa nthawi imene amavutika maganizo chonchi, munthu wina anamunamizira kuti waledzera ngakhale kuti panalibe umboni. Ndipo chomvetsa chisoni kwambiri n’chakuti munthu wakeyo anali mkulu wa ansembe. Koma pamenepanso Hana anasonyeza chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro. Iye sanalole kuti zochita za munthu wina zisokoneze kulambira kwake Yehova. Iye anamuyankha Eli mwaulemu ndipo anamufotokozera vuto lake. Eli anayankha, mwina mozindikira kuti walakwa komanso ndi mawu odekha, kuti: “Pita mu mtendere, ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.”—1 Sam. 1:15-17.

15, 16. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Hana atapita kuchihema komanso atauza Yehova zakukhosi kwake? (b) Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Hana tikamavutika maganizo ndi zinazake?

15 Kodi chinachitika n’chiyani Hana atapita kuchihema komanso atamuuza Yehova zakukhosi kwake? Baibulo limati: “Mkaziyo anachoka ndi kupita kukadya, ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:18) Ndipo Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limati: “Nkhope yake siinakhalanso yachisoni.” Hana atauza Yehova nkhawa zake, mtima wake unakhala m’malo. Zinali ngati ankalemedwa ndi katundu winawake, ndiyeno watulira katunduyo Atate wakumwamba amene ndi wamphamvu kwambiri kuposa iye. (Werengani Salimo 55:22.) Kodi pali vuto limene Mulungu angalephere kulisenza? Ayi, palibe ngakhale limodzi.

16 Tikaona kuti mavuto atikulira, ndi bwino kutsatira chitsanzo cha Hana. Tiyenera kulankhula momasuka kwa Mulungu amene Baibulo limamutchula kuti “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Tikamapemphera tili ndi chikhulupiriro, nafenso tidzaona kuti nkhawa zathu zatha ndipo tapeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afil. 4:6, 7.

“Palibe Thanthwe Lofanana Ndi Mulungu Wathu”

17, 18. (a) Kodi Elikana anasonyeza bwanji kuti anagwirizana ndi zomwe Hana analonjeza? (b) Kodi Penina anazindikira chiyani zokhudza zimene ankachitira Hana?

17 M’mawa mwake, Hana anapitanso kuchihema pamodzi ndi Elikana. Hana ayenera kuti anauza mwamuna wake Elikana za zimene anapempha komanso zimene analonjeza Mulungu. Mwina anachita zimenezi chifukwa Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mwamuna anali ndi ufulu wofafaniza lonjezo la mkazi wake, ngati mkaziyo walonjeza Mulungu zinthu zinazake asanapemphe mwamuna wake. (Num. 30:10-15) Koma mwamuna wokhulupirikayu sanachite zimenezo. M’malomwake, iyeyo ndi Hana analambira Yehova limodzi kuchihema asananyamuke ulendo wobwerera kwawo.

18 Kodi Penina anazindikira liti kuti Hana sakukhumudwanso ndi zimene akumuchitira? Baibulo silinena, koma mawu akuti “sanakhalenso ndi nkhawa” akusonyeza kuti Hana atangopemphera, anayamba kuoneka wosangalala. Mulimonse mmene zinalili, pasanapite nthawi Penina anazindikira kuti zochita zake zofuna kukwiyitsa Hana sizikugwiranso ntchito. Kuyambira pamenepa, Baibulo silitchulanso dzina la Penina.

19. Kodi Hana anadalitsidwa bwanji, nanga anasonyeza bwanji kuti anayamikira Mulungu?

19 Patapita miyezi ingapo, Hana anayamba kuonekeratu kuti ali ndi mtendere wamumtima. Iye anali ndi pakati. Ngakhale kuti anali wosangalala, Hana sanaiwale m’pang’ono pomwe kumene madalitso amenewo anachokera. Mwanayo atabadwa, anamupatsa dzina lakuti Samueli, limene limatanthauza kuti “Dzina la Mulungu.” Zikuoneka kuti tanthauzo la dzinali n’logwirizana ndi zimene Hana anachita popempha Mulungu kuti amuthandize. Samueli atabadwa, Hana sanapite limodzi ndi Elikana komanso banja lake ku Silo kwa zaka zitatu, kufikira mwanayo atasiya kuyamwa. Kenako anayamba kukonzekera tsiku limene adzasiyane ndi mwana wake wokondedwa kwambiriyo.

20. Kodi Hana ndi Elikana anakwaniritsa bwanji lonjezo lawo kwa Yehova?

20 Zinali zovuta kwambiri kuti Hana asiyane ndi mwana wake. Ngakhale kuti Hana ankadziwa zoti Samueli akasamalidwa bwino ku Silo ndi amayi ena amene ankatumikira kuchihemako, mwanayo anali adakali wamng’ono ndipo monga tikudziwira, n’zovuta kwa mayi aliyense kusiyana ndi mwana wake wamng’ono. Komabe Hana ndi mwamuna wake anakapereka mwana wawoyo kuchihema mosangalala. Atafika kuchihemako, anapereka nsembe kwa Mulungu ndipo kenako anapereka Samueli kwa Eli. Pomuperekapo, iwo anakumbutsa Eli za lonjezo limene Hana analonjeza Yehova zaka zingapo zapitazo.

Hana anasonyeza kuti anali mayi wabwino kwambiri

21. Kodi pemphero la Hana limasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba? (Onaninso bokosi lakuti  Mapemphero Awiri Ogwira Mtima.)

21 Kenako Hana anapemphera ndipo Mulungu anaona kuti pemphero limeneli n’lofunika kuti likhale m’Mawu ake ouziridwa. Mukamawerenga mawu a Hana a pa 1 Samueli 2:1-10, mungathe kuona kuti zonse zimene ananena zimasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Iye anatamanda Yehova chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mphamvu zake modabwitsa, amatsitsa anthu odzikweza komanso amathandiza anthu oponderezedwa. Anatamandanso Yehova chifukwa cha mphamvu zake zotha kuchotsa moyo kapena kuukitsa akufa. Iye anatamanda Atate wake wakumwamba chifukwa chakuti ndi woyera kwambiri, wolungama ndiponso wokhulupirika. M’pake kuti Hana ananena kuti: “Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wodalirika kwambiri ndipo sasintha. Choncho, anthu onse oponderezedwa angathawire kwa iye kuti awathandize.

22, 23. (a) Tikudziwa bwanji kuti Samueli ankadziwa kuti makolo ake amamukonda? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova anapitiriza kudalitsa Hana?

22 Samueli anali ndi mwayi kwambiri chifukwa mayi ake ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ngakhale kuti Samueli sankawaona mayi ake pafupipafupi, iye sankaona kuti amuiwala. Chaka chilichonse, Hana akamapita ku Silo ankatenga malaya odula manja amene ankasokera Samueli kuti azikavala potumikira kuchihema. Zimenezi zikusonyeza kuti Hana ankamukonda kwambiri mwana wakeyo. (Werengani 1 Samueli 2:19.) Tingathe kumuona Hana m’maganizo mwathu akumveka mwana wakeyo chovala chatsopanocho, kuchiwongolawongola, n’kumamuyang’ana mosangalala, uku akumulankhula mawu olimbikitsa ndiponso osonyeza kuti amamukonda. Samueli anali ndi mwayi kukhala ndi mayi ngati amenewa. Iye atakula anakhala munthu wodalirika kwa makolo ake ndiponso kwa mtundu wonse wa Isiraeli.

23 Yehova anapitiriza kudalitsa Hana moti anaberekanso ana ena asanu. (1 Sam. 2:21) Komabe mwina Hana ankaona kuti dalitso lalikulu linali ubwenzi wolimba umene anali nawo ndi Atate wake, Yehova, womwe unkapitirizabe kukula. Inunso mungakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngati mutatsanzira chikhulupiriro cha Hana.

^ ndime 7 Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Yehova “anali atatseka mimba” ya Hana, palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu sankasangalala ndi Hana, yemwe anali mkazi wokhulupirika komanso wodzichepetsa. (1 Sam. 1:5) Nthawi zina Baibulo limanena kuti Mulungu wachita chinachake, koma kwenikweni amakhala kuti wangolola kuti chichitike.

^ ndime 9 Mtunda umenewu tikutengera kuti mwina kwawo kwa Elikana kunali ku Rama, komwe m’nthawi ya Yesu kunkadziwika ndi dzina lakuti Arimateya.