Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Abale ndi Alongo Athu Okondedwa:

Kuyambira ndi Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008, yomwe inali Nsanja ya Olonda yogawira yoyamba, m’magaziniwa mwakhala mukutuluka nkhani zatsopano zochititsa chidwi za mutu wakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo.” Nkhanizi zinkatuluka pambuyo pa miyezi itatu iliyonse.

Kodi anthu amene awerengapo nkhani zimenezi afotokoza zotani? Munthu wina atamaliza kuwerenga nkhani ya Marita analemba kuti: “Nkhaniyi inandiseketsa kwambiri chifukwa nanenso ndili ndi vuto ngati la Marita. Nthawi zambiri ndimatanganidwa ndi kuchereza alendo moti nthawi zina ndimaiwala kufunika kodzipatsa mpata wocheza ndi alendowo.” Wachinyamata wina ananena mawu otsatirawa atawerenga nkhani ya Esitere: “Titapanda kusamala, tikhoza kutanganidwa ndi kutchena komanso kupeza zovala zimene zangotuluka kumene. Ndi zoona kuti tiyenera kuoneka bwino, komabe tifunika kusamala kuti tisamangoganizira kwambiri za maonekedwe athu. Yehova amayang’ana kwambiri zimene zili mumtima mwathu, osati mmene tikuonekera.” Ndipo mlongo wina atawerenga nkhani yonena za mtumwi Petulo anati: “Mmene ndinkawerenga nkhaniyi, ndinkangomva ngati ndikuona zinthuzo zikuchitika. Ndinkatha kumva fungo komanso phokoso la zinthu zosiyanasiyana zofotokozedwa m’nkhaniyo.”

Anthu amenewa, komanso ena ambiri amene analemba makalata oyamikira nkhanizi, akutsimikizira mfundo imene mtumwi Paulo analemba yakuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Yehova anaona kuti nkhani zimenezi n’zofunika kulembedwa m’Baibulo kuti zitiphunzitse mfundo zofunika. Nkhani zimenezi n’zothandiza kwa tonsefe, ngakhale amene akhala m’choonadi kwa zaka zambiri.

Tikukulimbikitsani kuwerenga bukuli mwamsanga. Mungachite bwino kuliphunzira pa Kulambira kwa Pabanja ndipo ana adzalikonda kwambiri. Tikadzayamba kuliphunzira kumpingo pa Phunziro la Baibulo la Mpingo, mudzayesetse kusajomba kumisonkhano, ngakhale mlungu umodzi. Liwerengeni mofatsa komanso mosafulumira kuti mulimvetse bwino. Pamene mukuwerenga, yerekezerani kuti zinthuzo zikuchitika inu muli pomwepo ndipo muziganizira mmene zinthu zotchulidwa m’nkhaniyo zinkaonekera, kumvekera komanso fungo lake. Yesetsani kuganizira mmene anthu otchulidwa m’nkhaniyo ankamvera zinthuzo zikamachitika. Ganizirani zomwe anthuwo anachita ndipo muziyerekeze ndi zimene inuyo mukanachita zikanakhala kuti zinthuzo zachitikira inuyo.

Ndife osangalala kutulutsa bukuli ndipo tikukhulupirira kuti likuthandizani inuyo komanso banja lanu. Dziwani kuti timakukondani kwambiri ndipo tikukufunirani zabwino zonse,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova