Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

“Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”—AHEBERI 6:12.

1, 2. (a) Kodi woyang’anira dera wina ankawaona bwanji anthu otchulidwa m’Baibulo? (b) Kodi tingapindule bwanji ngati anthu otchulidwa m’Baibulo atakhala anzathu?

MLONGO wina atamvetsera nkhani imene woyang’anira dera wina wachikulire anakamba anati: “M’baleyu amafotokoza za anthu otchulidwa m’Baibulo ngati kuti ndi anzake akalekale.” Mlongoyu ananenadi zoona chifukwa woyang’anira derayu wakhala akuphunzira Mawu a Mulungu komanso kuphunzitsa kwa nthawi yaitali moti amuna ndi akazi achikhulupiriro otchulidwa m’Baibulo amangokhala ngati anali anzake.

2 Kodi sizingakhale bwino kuti anthu amenewa tiziwaonadi ngati anzathu? Kodi ndi mmene inuyo mumawaonera? Ganizirani mmene zingakhalire ngati mutakhala ndi mwayi woyenda ndiponso kucheza ndi anthu monga Nowa, Abulahamu, Rute, Eliya ndiponso Esitere. Malangizo amene angakupatseni komanso mawu olimbikitsa omwe angakuuzeni, zikhoza kukuthandizani kwambiri pa moyo wanu.—Werengani Miyambo 13:20.

3. (a) Kodi kuphunzira za anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo kungatithandize bwanji? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 N’zoona kuti pa nthawi ya “kuuka kwa olungama” zidzakhala zotheka kucheza ndi anthu amenewa. (Mac. 24:15) Komabe ngakhale panopa tikhoza kupindula ndi chikhulupiriro cha amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Mtumwi Paulo ananena mfundo yothandiza yakuti: “Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.” (Aheb. 6:12) Tisanayambe kukambirana nkhani zokhudza amuna ndi akazi achikhulupiriro amene atchulidwa m’bukuli, tiyeni tikambirane kaye mafunso amene tikhoza kukhala nawo chifukwa cha zimene Paulo ananenazi. Funso loyamba ndi lakuti, kodi chikhulupiriro n’chiyani, nanga n’chofunika bwanji kwa ife? Lachiwiri ndi lakuti, kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo?

Kodi Chikhulupiriro N’chiyani, Nanga N’chofunika Bwanji?

4. Kodi anthu ena amaganiza kuti chikhulupiriro n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tingati zimenezi si zoona?

4 Chikhulupiriro ndi khalidwe losangalatsa ndipo amuna ndi akazi amene tikambirane m’bukuli ankaona kuti khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri. Anthu ambiri masiku ano amaona kuti chikhulupiriro si chofunika chifukwa amaganiza kuti munthu akakhala ndi chikhulupiriro ndiye kuti amangokhulupirira zilizonse popanda umboni woti zinthuzo ndi zoona. Koma zimene amaganizazi si zoona. Chikhulupiriro sichitanthauza kumangovomereza kapena kutsatira zinthu m’chimbulimbuli. Munthu wachikhulupiriro chenicheni amakhulupirira zinthu pambuyo poti wazimvetsa ndipo wakhutira kuti n’zoona. Kukhulupirira zinthu m’chimbulimbuli n’koopsa chifukwa munthu wotero sachedwa kusintha maganizo. Komanso kungokhulupirira kuti kuli Mulungu sikokwanira chifukwa “ziwanda nazonso zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera.”—Yak. 2:19.

5, 6. (a) Kodi chikhulupiriro chathu chimakhudza kwambiri zinthu ziwiri ziti zomwe sitingazione? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti pamafunika umboni wotsimikizirika kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni?

5 Baibulo limatiuza tanthauzo lenileni la chikhulupiriro. (Werengani Aheberi 11:1.) Paulo anafotokoza kuti chikhulupiriro chimakhudza kwambiri zinthu ziwiri zomwe sitingazione. Choyamba, chimakhudza zinthu zenizeni zomwe “n’zosaoneka.” Sitingathe kuona zinthu zakumwamba monga Yehova Mulungu, Mwana wake kapenanso Ufumu wa Mulungu umene ukulamulira kumwambako. Chachiwiri, chimakhudza “zinthu zoyembekezeredwa,” kapena kuti zimene sizinachitike. Sitingathe kuona dziko latsopano limene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Ndiye kodi zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zosaoneka komanso zimene tikuyembekezera zilibe umboni?

6 Ayi, chifukwa Paulo anafotokoza kuti munthu wachikhulupiriro chenicheni amakhala ndi umboni wa zimene akukhulupirirazo. Ponena kuti chikhulupiriro ndi “chiyembekezo chotsimikizika,” anagwiritsa ntchito mawu amene angatanthauzenso “chikalata chaumboni chosonyeza mwini wake wa chinthu.” Kuti timvetse zimenezi, tiyerekeze kuti munthu akufuna kukupatsani nyumba. Munthuyo angakupatseni chikalata chaumboni woti malowo ndi ake n’kukuuzani kuti, “Nyumba imene ndakupatsani ndi iyi.” Apa sikuti iye angakhale akutanthauza kuti muzikhala papepalapo. Koma akungotanthauza kuti chikalatacho ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti nyumbayo ndi yanudi ndipo kukhala ndi chikalatacho n’chimodzimodzi n’kukhala ndi nyumbayo. Mofanana ndi zimenezi, umboni wa zinthu zimene timazikhulupirira ndi wamphamvu komanso wotsimikizirika moti timangoona ngati zinthuzo zachitika kale.

7. Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro chenicheni?

7 Choncho munthu wachikhulupiriro chenicheni amakhala ndi umboni wodalirika wa zimene akukhulupirirazo komanso amadalira kwambiri Yehova Mulungu. Chikhulupiriro chimatichititsa kuti tiziona kuti Yehova ndi Atate wathu wachikondi komanso kuti tisamakayikire zoti adzakwaniritsa zonse zomwe walonjeza. Koma chikhulupiriro chenicheni chimafunikanso kuchisamalira kuti chikhalepobe. Kuti chisafe, tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro.—Yak. 2:26.

8. Kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji?

8 Kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji? Tingapeze yankho la funso limeneli pa zimene Paulo analemba. (Werengani Aheberi 11:6.) Ngati tilibe chikhulupiriro sitingathe kupemphera kwa Yehova kapena kumukondweretsa. Choncho chikhulupiriro n’chofunika kuti tithe kukhala pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova, komanso kuti tithe kumutamanda. Zinthu zimenezi n’zimene munthu aliyense komanso angelo ayenera kuchita.

9. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amadziwa zoti timafunika kukhala ndi chikhulupiriro?

9 Yehova amadziwa kuti anthufe timafunika kukhala ndi chikhulupiriro, choncho watipatsa zitsanzo zomwe zingatithandize kudziwa mmene tingalimbitsire ndiponso kusonyezera chikhulupiriro chathu. Komanso mumpingo muli akulu omwe amatitsogolera ndipo ponena za akuluwo, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Tsanzirani chikhulupiriro chawo.” (Aheb. 13:7) Kuwonjezera pamenepa, Paulo analemba za “mtambo wa mboni waukulu” womwe ndi amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo amene anatisiyira chitsanzo chachikhulupiriro. (Aheb. 12:1) Mu chaputala 11 cha Aheberi, Paulo anatchula mayina a amuna ndi akazi amenewa koma palinso ena ambiri. M’Baibulo muli nkhani zambiri za amuna ndi akazi, ana ndi akulu omwe, amene anasonyeza chikhulupiriro ndipo kutsanzira chikhulupiriro chawo, kungatithandize m’dziko lopanda chikhulupiriroli.

Kodi Tingatsanzire Bwanji Chikhulupiriro cha Anthu Otchulidwa M’Baibulo?

10. Kodi tingatani kuti kuphunzira patokha kuzitithandiza kutsanzira chikhulupiriro cha anthu otchulidwa m’Baibulo?

10 Sitingathe kutsanzira munthu pokhapokha titaonetsetsa zochita za munthuyo. Mukamawerenga bukuli, muona kuti tinayesetsa kufufuza zinthu zambiri n’cholinga chofuna kukuthandizani kuti muwadziwe bwino anthu achikhulupirirowa. Tikukulimbikitsani kuti mukamaphunzira bukuli panokha, nanunso muzifufuza mfundo zina ndi zina pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zomwe muli nazo. Mukamasinkhasinkha zimene mwaphunzira, yesani kuganizira mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, malo amene zinachitikira komanso zimene zinachititsa zinthuzo. Yerekezerani kuti mukuona malo amene zikuchitikira komanso mukumva fungo kapena phokoso lomwe lili pamalopo. Ndipo chofunika kwambiri, yesetsani kuganizira mmene anthu otchulidwa m’nkhaniyo ankamvera. Mukamachita zimenezi, mudzawadziwa bwino anthu amenewa ndipo mudzayamba kuwaona ngati anzanu akalekale.

11, 12. (a) Kodi mungatani kuti Abulamu ndi Sarai muziwaona ngati anzanu apamtima? (b) Kodi chitsanzo cha Hana, Eliya kapena Samueli chingakuthandizeni bwanji?

11 Mukawadziwa bwino anthu amenewa, mudzayamba kufuna kuwatsanzira. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti gulu lakupatsani utumiki watsopano. Mwina mwapemphedwa kuti musamukire kudera komwe kukufunikira ofalitsa ambiri, kapena mwapemphedwa kuyesa njira zina zolalikirira zomwe inuyo mukuona kuti n’zovuta. Pamene mukuganizira za utumiki umenewu komanso kupempherera nkhaniyi, mungachite bwino kusinkhasinkha za chitsanzo cha Abulamu. Iye ndi mkazi wake Sarai analolera kusiya moyo wabwino womwe anali nawo ku Uri ndipo anadalitsidwa kwambiri pamapeto pake. Mukamayesetsa kutsatira chitsanzo chawo, mudzaona kuti mwayamba kuwadziwa bwino kwambiri kuposa mmene munkawadziwira poyamba.

12 Nanga bwanji ngati mnzanu kapena wachibale wanu atamakuchitirani nkhanza komanso chipongwe ndipo zikukuchititsani kusafuna kupita kumisonkhano? Kuganizira chitsanzo cha Hana komanso mmene anayesetsera kuti azilambirabe Yehova ngakhale kuti ankachitidwa chipongwe ndi Penina, kungakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru. Zimenezi zingachititsenso kuti muyambe kumuona Hana ngati mnzanu wapamtima. Ngati mukumakhala wofooka chifukwa chodziona ngati wachabechabe, mungachite bwino kuwerenga chitsanzo cha Eliya n’kuganizira mavuto amene anakumana nawo komanso mmene Yehova anamulimbikitsira. Ndipo achinyamata omwe nthawi zambiri amakhala ndi anzawo a kusukulu akhalidwe loipa, angachite bwino kuphunzira mmene Samueli anayesetsera kuti asatengere khalidwe loipa la ana a Eli pamene ankatumikira kuchihema. Kuganizira chitsanzo cha Samueli kungawathandize kuti ayambe kumuona ngati mnzawo.

13. Kodi Yehova angakuoneni kuti ndinu wopanda chikhulupiriro cholimba chifukwa choti mukutsanzira chikhulupiriro cha anthu otchulidwa m’Baibulo? Fotokozani.

13 Kodi Yehova angakuoneni kuti ndinu wopanda chikhulupiriro cholimba chifukwa choti mukutsanzira chikhulupiriro cha anthu otchulidwa m’Baibulo? Ayi. Paja Mawu a Yehova amatilimbikitsa kuti tizitsanzira anthu achikhulupiriro. (1 Akor. 4:16; 11:1; 2 Ates. 3:7, 9) Ndipotu anthu ena amene tiphunzire m’bukuli nawonso anatsanzira chikhulupiriro cha ena omwe anakhalapo iwo asanabadwe. Mwachitsanzo, m’Mutu 17 wa bukuli tiona kuti zinthu zina zimene Mariya ananena zinali zimene Hana analankhula pa nthawi ina. Izi zikusonyeza kuti Mariya ankaona kuti Hana ndi chitsanzo chake. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mariya analibe chikhulupiriro cholimba? Ayi. Chitsanzo cha Hana chinamuthandiza Mariya kukhala ndi chikhulupiriro cholimba moti Yehova Mulungu ankamuona kuti nayenso ndi munthu wachikhulupiriro.

14, 15. Tchulani zinthu zina zimene zili m’bukuli, komanso mmene tingazigwiritsire ntchito.

14 Bukuli lalembedwa m’njira yoti likuthandizeni kulimbikitsa chikhulupiriro chanu. Mitu ya m’bukuli yachokera pa nkhani zakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” zimene zinatuluka mu Nsanja ya Olonda kuyambira 2008 mpaka 2013. Komabe tawonjezeramo zina ndi zina. Mwachitsanzo, taikamo mafunso kuti tiziwagwiritsa ntchito pophunzira bukuli komanso kuti atithandize kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za mu nkhanizi. Tawonjezeranso zithunzi zokongola zothandiza kumvetsa mfundo za m’nkhanizi ndipo zina zomwe zinalipo kale, tazikulitsa ndi kuzikonzanso. Taikamonso zinthu zina zothandiza, monga mapu komanso tchati chosonyeza nthawi imene zinthu zinachitika. Buku la Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo lakonzedwa kuti litithandize pophunzira patokha, pophunzira ngati banja komanso pa phunziro la mpingo. Mabanja angasangalalenso kumawerenga limodzi mokweza nkhani za m’bukuli.

15 Tikukhulupirira kuti bukuli likuthandizani kutsanzira chikhulupiriro cha atumiki a Yehova akale. Tikukhulupiriranso kuti likuthandizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndi kuyandikira Atate wanu wakumwamba, Yehova.