Mawu Omaliza

Mawu Omaliza

“Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”—AHEBERI 6:12.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu panopa? Perekani chitsanzo.

CHIKHULUPIRIRO ndi mawu omwe amanena za khalidwe losangalatsa kwambiri. Koma tikamva mawuwa tiyenera kuganiziranso za mawu ena akuti: “Changu.” Chifukwatu ngati tilibe chikhulupiriro, tikufunika kuyesetsa panopa kuti tikhale nacho. Ndipo ngati tili nacho kale, inoyo ndiye nthawi yoyenera kuyesetsa kuchitetezera ndiponso kuchisamalira. N’chifukwa chiyani tikufunika kuchita zimenezi?

2 Tiyerekeze kuti mukudutsa m’chipululu chachikulu ndipo muli ndi ludzu kwambiri. Mutapeza madzi, mungayesetse kuwatetezera kuti asatenthe ndi dzuwa komanso mungamawawonjezere n’cholinga choti akakufikitseni kumene mukupita. M’dziko limene tikukhalali anthu ambiri alibe chidwi ndi kulambira Yehova, choncho chikhulupiriro chenicheni n’chosowa kwambiri ngati madzi m’chipululu. Motero tiyenera kuteteza chikhulupiriro chathu komanso kuchilimbitsa kuti chisathe. Anthufe sitingathe kukhala ndi moyo popanda madzi. Mofanana ndi zimenezi, sitingathenso kukhala pa ubwenzi ndi Yehova popanda chikhulupiriro.—Aroma 1:17.

3. Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti zotithandiza kulimbikitsa chikhulupiriro chathu, nanga tiyenera kukumbukira chiyani?

3 Yehova amadziwa kuti tikufunika kukhala ndi chikhulupiriro ndipo amadziwanso kuti masiku ano n’zovuta kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. N’chifukwa chake watipatsa zitsanzo za anthu achikhulupiriro kuti tizitsanzira. Iye anauzira mtumwi Paulo kulemba kuti: “Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.” (Aheb. 6:12) N’chifukwa chakenso gulu la Yehova limatilimbikitsa kutsatira zitsanzo za amuna ndi akazi akale okhulupirika ngati amene takambirana m’bukuli. Ndiye kodi pamenepa tiyenera kuchita chiyani? Tifunika kukumbukira mfundo ziwiri izi: (1) Tiyenera kupitirizabe kulimbitsa chikhulupiriro chathu; (2) nthawi zonse tizikumbukira zinthu zimene Mulungu watilonjeza.

4. Kodi Satana wachita chiyani posonyeza kuti ndi mdani wa chikhulupiriro, komabe n’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti n’zosatheka kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?

4 Pitirizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Satana, yemwenso ndi wolamulira wa dzikoli, ndi mdani wamkulu wa chikhulupiriro chathu. Iye wachititsa dzikoli kukhala malo ovuta kuti munthu akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba. Satana ndi wamphamvu kwambiri kuposa anthufe. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti n’zosatheka kukhala ndi chikhulupiriro cholimba? Ayi, chifukwa Yehova ndi Bwenzi lalikulu la anthu onse amene akuyesetsa kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni. Iye amatilonjeza kuti ali kumbali yathu ndipo adzatithandiza kutsutsa zofuna za Mdyerekezi mpaka Mdyerekeziyo adzatithawa. (Yak. 4:7) Timachita zimenezi tikamayesetsa kupeza nthawi yolimbitsa chikhulupiriro chathu tsiku lililonse. Koma kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?

5. Fotokozani chimene chinathandiza amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo kuti akhale ndi chikhulupiriro.

5 Monga taonera, anthu achikhulupiriro otchulidwa m’Baibulo sikuti anabadwa ali kale ndi chikhulupiriro. Koma zimene anachita pa moyo wawo ndi umboni wakuti chikhulupiriro ndi khalidwe limene mzimu woyera wa Yehova umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Iwo ankapemphera kwa Yehova kuti awathandize ndipo iye ankalimbitsa chikhulupiriro chawo. Nafenso tiyeni tizichita chimodzimodzi ndipo tisamaiwale kuti anthu amene amamupempha n’kumachita mogwirizana ndi zomwe apemphazo, Yehova amawapatsa mzimu wake mowolowa manja. (Luka 11:13) Koma palinso zina zimene tiyenera kuchita.

6. Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri tikamaphunzira nkhani za m’Baibulo?

6 M’bukuli tangokambirana zitsanzo zochepa za anthu amene anali ndi chikhulupiriro cholimba, koma pali enanso ambiri. (Werengani Aheberi 11:32.) Tingaphunzirenso zambiri kwa anthu amenewa omwe nkhani zawo sizinaikidwe m’bukuli. Kuti tilimbitse kwambiri chikhulupiriro chathu tiyenera kuphunzira nkhani za anthu amenewa mofatsa, osati mothamanga. Tiyeneranso kufufuza mokwanira mmene zinthu zinalili pa nthawiyo komanso chimene chinachititsa zinthuzo. Tikamakumbukira kuti amenewa anali anthu “monga ife tomwe,” zitsanzo zawo zidzatilimbikitsa kwambiri. (Yak. 5:17) Tingathe kuganizira mmene ankamvera akakumana ndi mavuto ofanana ndi amene ifenso timakumana nawo.

7-9. (a) Kodi mukuganiza kuti amuna ndi akazi achikhulupiriro otchulidwa m’Baibulo akanamva bwanji akakhala kuti ankalambira Yehova m’njira imene ife timalambirira masiku ano? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro?

7 Zochita zathu zingathandizenso kuti chikhulupiriro chathu chilimbe. Ndipotu Baibulo limanena kuti “chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yak. 2:26) Taganizirani mmene anthu amene takambirana m’bukuli akanasangalalira akanapatsidwa ntchito yolalikira imene Yehova watipatsa ife masiku ano.

8 Mwachitsanzo, kodi mukuganiza kuti Abulahamu akanamva bwanji akanauzidwa kuti azilambira Yehova, osati paguwa, koma m’Nyumba ya Ufumu ndi pa misonkhano ikuluikulu ngati mmene ife timachitira? Pamalo amenewa timaphunzira za malonjezo amene iye ‘ankangowaonera patali.’ (Werengani Aheberi 11:13.) Nanga kodi Eliya akanamva bwanji akanauzidwa kuti ntchito imene wapatsidwa si yopha aneneri a Baala, koma youza anthu mwamtendere uthenga wolimbikitsa komanso wopatsa chiyembekezo? N’zodziwikiratu kuti anthu achikhulupiriro otchulidwa m’Baibulo akanasangalala kwambiri akanakhala ndi mwayi wolambira Yehova m’njira imene timachitira masiku ano.

9 Choncho, tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba. Tingachite zimenezi mwa kutsanzira chikhulupiriro cha anthu otchulidwa m’Mawu a Mulungu. Monga tinafotokozera m’mawu oyamba aja, zimenezi zingachititse kuti tiyambe kuwaona ngati anzathu apamtima. Ndipotu posachedwapa anthu amenewa adzakhaladi anzathu enieni.

10. Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zomwe tidzachite m’Paradaiso?

10 Nthawi zonse tizikumbukira zinthu zimene tikuyembekezera. Anthu okhulupirika akale ankalimbikitsidwa akaganizira malonjezo a Mulungu. Kodi inunso mumatero? Mwachitsanzo, taganizirani mmene mudzasangalalire kucheza ndi atumiki a Mulungu omwe adzaukitsidwe pa “kuuka kwa olungama.” (Werengani Machitidwe 24:15.) Kodi mungakonde kudzawafunsa mafunso ati?

11, 12. M’dziko latsopano, kodi ndi mafunso ati amene mungakonde kudzamufunsa (a) Abele? (b) Nowa? (c) Abulahamu? (d) Rute? (e) Abigayeli? (f) Esitere?

11 Mukadzakumana ndi Abele, mwina mungafune kudzamufunsa kuti makolo ake anali otani. Mwinanso mungadzamufunse kuti: “Kodi munalankhulanapo ndi akerubi amene ankalondera munda wa Edeni aja?” Nanga ndi mafunso ati amene mungakonde kudzamufunsa Nowa? Mwina mungafune kudzamufunsa kuti: “Kodi nanunso munkachita mantha mukakumana ndi Anefili? Nanga munakwanitsa bwanji kusamalira nyama zonse zimene zinali m’chingalawa?” Mukadzakumana ndi Abulahamu mwina mungadzamufunse kuti: “Kodi munkadziwana ndi Semu? Ndani anakuphunzitsani za Yehova? Nanga munamva bwanji Mulungu atakuuzani kuti muchoke mumzinda wa Uri?”

12 Ndiyeno ganizirani mafunso amene mungakonde kudzafunsa akazi okhulupirika akale akadzaukitsidwa. Mwina Rute mungadzamufunse kuti: “N’chiyani chinakuchititsani kuti muyambe kulambira Yehova?” Abigayeli mwina mungadzamufunse kuti: “Kodi munkachita mantha kumuuza Nabala za zinthu zimene munamupatsa Davide?” Mwina Esitere mungadzam’funse kuti: “Kodi inuyo ndi Moredekai zinthu zinakuyenderani bwanji nkhani imene inafotokozedwa m’Baibulo ija itatha?”

13. (a) Kodi ndi mafunso ati amene mwina anthu akale angadzakufunseni akadzaukitsidwa? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira zodzakumana ndi anthu okhulupirika akale?

13 N’zodziwikiratu kuti nawonso anthu akale adzakhala ndi mafunso ambirimbiri oti akufunseni. Zidzakhalatu zosangalatsa kuwafotokozera zokhudza masiku otsiriza komanso mmene Yehova wadalitsira anthu ake pa nthawi yovuta imeneyi. N’zosakayikitsa kuti adzasangalala kwambiri akadzamva mmene Yehova anakwaniritsira malonjezo ake onse. Popeza anthu okhulupirika amenewa tidzakhala nawo m’Paradaiso, nthawi imeneyo tidzadziwa zonse zokhudza anthuwa zomwe panopa timangoyerekezera. Choncho panopa yesetsani kuphunzira zambiri za anthu amenewa kuti muziwaona ngati anzanu. Pitirizani kutsanzira chikhulupiriro chawo. Mukatero mudzasangalala kutumikira nawo limodzi mpaka kalekale ngati anzanu apamtima.