MUTU 8

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Anakumana ndi Mavuto

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Anakumana ndi Mavuto

1. N’chifukwa chiyani anthu a ku Silo anali ndi chisoni kwambiri?

SAMUELI anadziwa kuti anthu a ku Silo ali ndi chisoni chachikulu. Zinkaoneka kuti anthu m’tauni yonseyi ankalira maliro. Sitikudziwa kuti panali azimayi ndi ana angati amene ankalira chifukwa cha chisoni ndi imfa ya abambo awo, amuna awo, ana awo ndi achibale amene anaphedwa kunkhondo. Chomwe tikudziwa ndi choti pa nthawiyi amuna pafupifupi 30,000 anali ataphedwa pa nkhondo yoopsa yomenyana ndi Afilisiti. Ndipo zimenezi zinachitika pasanathe nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli enanso 4,000 anaphedwa pa nkhondo ina.—1 Sam. 4:1, 2, 10.

2, 3. Kodi ndi zinthu ziti zochititsa manyazi ndiponso zomvetsa chisoni zimene zinachitika ku Silo?

2 Komatu limeneli linali vuto limodzi chabe mwa mavuto ambirimbiri amene Aisiraeli anakumana nawo. Mwachitsanzo, pa nthawi ina likasa la Yehova linalandidwa. Mkulu wa Ansembe Eli anali ndi ana aamuna awiri oipa kwambiri. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinehasi ndipo iwo ananyamula likasa lopatulika la pangano kuchokera ku Silo. Likasa limeneli linkakhala m’malo opatulika m’chihema chomwe chinali kachisi wooneka ngati tenti, ndipo chinali chizindikiro chakuti Mulungu ali pamalowo. Aisiraeli anatenga Likasalo n’kupita nalo kunkhondo poganiza kuti likakhala ngati chithumwa chowateteza. Komatu pamenepa sanaganize bwino chifukwa Afilisiti analanda Likasalo ndipo anapha Hofeni ndi Pinehasi.—1 Sam. 4:3-11.

3 Kwa zaka zambiri anthu ankalemekeza chihema chopatulika chimene chinali ku Silo chifukwa chakuti m’chihemacho munali Likasa. Koma tsopano Likasali linali litalandidwa. Eli, amene pa nthawiyi anali ndi zaka 98, atamva kuti Likasa lalandidwa anagwa pampando chagada ndipo anafa. Mpongozi wake, yemwe anali mkazi wake wa Pinehasi, nayenso anamwalira akubereka. Mayiyu asanamwalire ananena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.” Zimenezi zinalidi zoona chifukwa zinthu zinali zitasinthiratu ku Silo.—1 Sam. 4:12-22.

4. Kodi tikambirana chiyani m’mutu uno?

4 Kodi Samueli anatani kuti apirire mavuto aakulu amenewa? Kodi iye anali ndi chikhulupiriro cholimba moti akanatha kuthandiza anthu amenewa, omwe Yehova anali atasiya kuwateteza ndiponso kuwakonda? Masiku ano tonsefe nthawi zina timakumana ndi mavuto ndiponso zokhumudwitsa zimene zimayesa chikhulupiriro chathu. Choncho tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Samueli.

“Anachita Chilungamo”

5, 6. Kodi Baibulo limafotokoza zinthu ziti zimene zinachitika pa zaka 20 zomwe silitchula za Samueli, nanga Samueli ankagwira ntchito yotani pa nthawiyi?

5 Pambuyo pofotokoza za kulandidwa kwa Likasa lopatulika, Baibulo silipitiriza kunena za Samueli. M’malomwake limafotokoza za Likasalo ndiponso zimene Afilisiti anakumana nazo chifukwa cholanda Likasa, zomwe zinachititsa kuti akakamizike kukalibweza. Pamene Baibulo likunenanso za Samueli, n’kuti patapita zaka 20. (1 Sam. 7:2) Kodi Samueli ankachita chiyani pa zaka zimenezi? Baibulo limatithandiza kudziwa zimene ankachita.

Kodi Samueli akanathandiza bwanji Aisiraeli kupirira imfa ya abale awo komanso mavuto ena?

6 Baibulo limasonyeza kuti nthawi imeneyi isanafike, “Samueli anapitiriza kulankhula ndi Aisiraeli onse.” (1 Sam. 4:1) Limasonyezanso kuti pambuyo pa zaka 20 zimenezi, Samueli ankayendera mizinda itatu ya Isiraeli, ndipo ankazungulira m’maderawa chaka chilichonse kuweruza Aisiraeli. Akayendera madera amenewa, ankabwerera kwawo ku Rama. (1 Sam. 7:15-17) Zimenezi zikusonyeza kuti Samueli anali munthu wotanganidwa kwambiri ndipo pa zaka 20 zimenezi anali ndi zochita zambiri.

Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zinthu zimene Samueli ankachita pa zaka 20 kuchokera pamene likasa linalandidwa, tikukhulupirira kuti pa zaka zimenezi iye anali wotanganidwa kwambiri kutumikira Yehova

7, 8. (a) Kodi Samueli anauza anthu uthenga wotani atagwira ntchito mwakhama kwa zaka 20? (b) Kodi anthuwo anatani atamva zimene Samueli anawauza?

7 Chinyengo ndiponso khalidwe lachiwerewere la ana a Eli linasokoneza chikhulupiriro cha anthu. Zikuoneka kuti anthu ambiri anayamba kulambira mafano. Komabe Samueli atatha zaka 20 akugwira mwakhama ntchito yolimbikitsa anthuwo, anawauza kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu. Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti, ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina, ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”—1 Sam. 7:3.

8 Aisiraeli ankavutika kwambiri chifukwa chokhala “m’manja mwa Afilisiti.” Popeza asilikali a Isiraeli anali atagonjetsedwa, Afilisiti ankaona kuti anali ndi ufulu wonse wozunza anthu a Mulunguwo. Koma Samueli anawatsimikizira kuti ngati atabwerera kwa Yehova, zinthu zikhoza kusintha. Kodi Aisiraeli analidi okonzeka kubwerera kwa Yehova? Samueli anasangalala kwambiri kuona kuti iwo asiyadi mafano awo “n’kuyamba kutumikira Yehova yekha.” Kenako Samueli anaitanitsa msonkhano ku Mizipa, tauni ya kumapiri imene inali chakumpoto kwa Yerusalemu. Aisiraeli anasonkhanadi kumeneko ndipo anasala kudya komanso analapa machimo awo ndipo anasiya kulambira mafano.—Werengani 1 Samueli 7:4-6.

Afilisiti atamva kuti Aisiraeli asonkhana ku Mizipa, anaona kuti ndi mwayi woti akamenyane nawo

9. Kodi Afilisiti anaganiza zochita chiyani atamva zoti Aisiraeli asonkhana ku Mizipa, nanga anthu a Mulungu anatani atamva zimenezi?

9 Koma Afilisiti anamva kuti Aisiraeli asonkhana ku Mizipa ndipo anaona kuti umenewu unali mwayi woti akamenyane nawo. Choncho anatumiza gulu lawo lankhondo ku Mizipa kuti likawononge anthu a Yehova. Aisiraeli atamva kuti Afilisiti akubwera, anachita mantha kwambiri ndipo anapempha Samueli kuti awapempherere. Samueli anachitadi zimenezi ndipo anaperekanso nsembe. Mwambo wapaderawu uli mkati, gulu lankhondo la Afilisiti linafika ku Mizipa. Kenako Yehova anayankha pemphero la Samueli. Ndipo posonyeza mkwiyo wake, Yehova “anachititsa mabingu amphamvu kwambiri pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.”—1 Sam. 7:7-10.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mabingu amene Yehova anachititsa anali osiyana ndi mabingu a nthawi zonse? (b) Kodi chinachitika n’chiyani pambuyo pa nkhondo ya ku Mizipa?

10 Koma tisaganize kuti Afilisiti anali ngati ana amene akangomva kulira kwa mabingu amathamangira kwa amayi awo kuti akabisale chifukwa cha mantha. Iwo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo. Koma mabingu amenewa anali asanawamvepo chiyambire chifukwa kugunda kwake kunali kwamphamvu kwambiri, ankachitika kumwamba kulibe mtambo ngakhale umodzi komanso phokoso lake linkamveka kuchokera kumapiri ndipo linali logonthetsa m’khutu. Choncho, Afilisiti anasokonezeka ndipo anaopa kwambiri. Chifukwa cha kusokonezekaku, zinthu zinasintha mofulumira. Afilisiti, omwe anabwera kudzaukira Aisiraeli, anatheratu mphamvu. Asilikali a Isiraeli anabwera kuchokera ku Mizipa ndipo anagonjetsa Afilisiti n’kuwathamangitsa mpaka kum’mwera chakumadzulo kwa Yerusalemu.—1 Sam. 7:11.

11 Nkhondo imeneyi inali chiyambi cha kusintha kwa zinthu pakati pa anthu a Mulungu. Pa nthawi yonse imene Samueli anali woweruza, Afilisiti ankaopa kumenyana ndi Aisiraeli. Pang’ono ndi pang’ono anthu a Mulungu anayamba kulandanso mizinda yawo imene inali m’manja mwa Afilisiti.—1 Sam. 7:13, 14.

12. Kodi n’chifukwa chiyani tingati Samueli “anachita chilungamo”? Nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti apitirize kuthandiza anthu?

12 Patapita zaka zambiri mtumwi Paulo anatchula Samueli pa mndandanda wa oweruza ndiponso aneneri okhulupirika amene “anachita chilungamo.” (Aheb. 11:32, 33) Samueli anathandizadi kwambiri kuti anthu achite zabwino ndiponso zoyenera pamaso pa Mulungu. Iye anatha kuchita zimenezi chifukwa chakuti anayembekezera Yehova moleza mtima ndipo anapitirizabe kugwira ntchito yake mokhulupirika ngakhale kuti panali mavuto osiyanasiyana. Samueli analinso ndi mtima woyamikira moti Aisiraeli atapambana nkhondo ya ku Mizipa, iye anaimika mwala wachikumbutso kuti azikumbukira mmene Yehova anathandizira anthu ake.—1 Sam. 7:12.

13. (a) Kuti titsanzire Samueli, kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati? (b) Kodi nthawi yabwino yoyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene Samueli anali nawo ndi iti?

13 Kodi nanunso mumalakalaka ‘mutamachita chilungamo’? Ngati ndi choncho, mungaphunzire zambiri pa kuleza mtima, kudzichepetsa komanso mtima woyamikira umene Samueli anali nawo. (Werengani 1 Petulo 5:6.) Ndipo tonsefe tifunika kukhala ndi makhalidwe amenewa. Samueli anaphunzira makhalidwe amenewa ali mwana, ndipo izi zinamuthandiza kupirira mavuto ambiri amene anakumana nawo atakula.

“Ana Ako Sakutsatira Chitsanzo Chako”

14, 15. (a) Kodi Samueli anakumana ndi vuto lalikulu liti “atakalamba”? (b) Kodi Samueli anali bambo wolekerera ngati Eli? Fotokozani.

14 Nthawi yotsatira pamene Baibulo limanenanso za Samueli, n’kuti “atakalamba.” Pa nthawiyi Samueli anali ndi ana amuna awiri akuluakulu, Yoweli ndi Abiya ndipo anawasankha kuti azimuthandiza pa ntchito yoweruza. Koma n’zomvetsa chisoni kuti iye sanasankhe bwino. Ngakhale kuti Samueli anali woona mtima ndiponso wachilungamo, ana akewa anagwiritsa ntchito molakwa udindo wawo. Iwo sankaweruza mwachilungamo ndiponso ankalandira ziphuphu.—1 Sam. 8:1-3.

15 Tsiku lina akulu a mu Isiraeli anapita kwa mneneri wokalambayu ndipo anamudandaulira kuti: “Ana ako sakutsatira chitsanzo chako.” (1 Sam. 8:4, 5) Koma kodi Samueli ankadziwa zimene ana akewa ankachita? Baibulo silinena ngati ankadziwa kapena ayi. Koma mosiyana ndi Eli, Samueli sanali bambo wolekerera. Yehova anadzudzula komanso kulanga Eli chifukwa ankalephera kulangiza ana ake oipa ndiponso chifukwa iye ankalemekeza ana akewo kuposa Mulungu. (1 Sam. 2:27-29) Koma Yehova anaona kuti Samueli anali wosiyana ndi Eli.

Kodi Samueli anapirira bwanji vuto la kukhala ndi ana osamvera?

16. Kodi makolo amene ali ndi ana osamvera amamva bwanji, nanga chitsanzo cha Samueli chingawathandize bwanji?

16 Kodi Samueli anachita manyazi, kuda nkhawa ndiponso kukhumudwa atauzidwa za khalidwe loipa la ana akewa? Baibulo silifotokoza mmene anamvera. Koma makolo ambiri angamvetse mmene iye anamvera chifukwa masiku anonso m’dziko lovutali, ana ambiri samvera malangizo a makolo awo. (Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.) Makolo amene akuvutika maganizo chifukwa chakuti ana awo analowerera, angalimbikitsidwe ndiponso kupeza malangizo poganizira chitsanzo cha Samueli. Iye sanalole kuti kusakhulupirika kwa ana ake kusinthe khalidwe lake labwino ngakhale pang’ono. Ndipo musaiwale kuti ngakhale mwana wanu atapanda kusintha pambuyo poti mwamudzudzula kapena kum’patsa malangizo, nthawi ina akhoza kudzasintha chifukwa choona khalidwe lanu labwino. Komanso mofanana ndi Samueli, makolo nthawi zonse ayenera kuchita zinthu zimene zingasangalatse Atate wawo, Yehova Mulungu.

“Tikufuna Kuti Utiikire Mfumu”

17. Kodi akulu a mu Isiraeli anamuuza chiyani Samueli, nanga iye anamva bwanji?

17 Ana a Samueli sanaganizire n’komwe za mavuto amene angabwere chifukwa cha khalidwe lawo ladyera komanso lodzikonda. Akulu a mu Isiraeli anauza Samueli kuti: “Tikufuna kuti utiikire mfumu yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.” N’kutheka kuti pamenepa Samueli anaona kuti anthuwo akumukana iyeyo. Samueli anali atagwira ntchito yoweruza Aisiraeli m’malo mwa Yehova kwa zaka zambiri. Koma tsopano Aisiraeli ananena kuti akufuna mfumu yoti iziwalamulira, osati mneneri chabe ngati Samueli. Mitundu yonse yowazungulira inali ndi mafumu awo, choncho Aisiraeli anafuna kuti nawonso akhale ndi mfumu. Kodi Samueli anamva bwanji? Baibulo limati: “Zimenezi zinamuipira” Samueli.—1 Sam. 8:5, 6.

18. Kodi Yehova anamulimbikitsa bwanji Samueli, komabe kodi mawu akewo anasonyeza bwanji kuti Aisiraeli anachimwira Yehova popempha mfumu?

18 Koma tamvani zimene Yehova anayankha Samueli atamuuza nkhaniyi m’pemphero. Yehova anati: “Mvera zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe, pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.” Mawu a Yehova amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Samueli. Komabe mawuwa anasonyezanso kuti anthuwo anachitira Mulungu Wamphamvuyonse chipongwe chachikulu. Yehova anauza mneneri Samueli kuti achenjeze Aisiraeli za kuipa kokhala ndi munthu woti aziwalamulira ngati mfumu yawo. Koma Samueli atawachenjeza, iwo anaumirirabe kuti: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira.” Popeza nthawi zonse Samueli ankamvera Mulungu, iye anapita kukadzoza mfumu imene Yehova anasankha.—1 Sam. 8:7-19.

19, 20. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Samueli anamvera malangizo a Yehova oti adzoze Sauli kuti akhale mfumu ya Isiraeli? (b) Kodi Samueli anapitiriza bwanji kuthandiza anthu a Yehova?

19 Komano kodi Samueli anamvera Mulungu mochokera pansi pa mtima? Kapena kodi iye anachita zinthu moipidwa ndiponso monyinyirika? Kodi iye analola kuti mavuto amenewa aipitse mtima wake, n’kumangokhala wokhumudwa nthawi zonse? Anthu ambiri akanachita zimenezo, koma Samueli sanatero. Iye anadzoza Sauli kukhala mfumu ndipo anavomereza kuti anali munthu amene Yehova wamusankha. Anamupsompsona posonyeza kusangalala naye ndiponso kumugonjera monga mfumu yatsopano. Ndiyeno anauza anthuwo kuti: “Kodi mwaona amene Yehova wam’sankha, kuti palibe aliyense pakati pa anthu onse wofanana naye?”—1 Sam. 10:1, 24.

20 Samueli sanaganizire kwambiri zolakwa za Sauli koma anaganizira za makhalidwe abwino a Sauliyo. Ndiponso Samueli anaganizira kwambiri za kukhulupirika kwake kwa Mulungu, osati zakuti anthu osakhulupirikawo azimukonda. (1 Sam. 12:1-4) Komanso anagwira mokhulupirika ntchito imene Mulungu anamupatsa yolangiza Aisiraeli pa mavuto amene ankakumana nawo ndipo anawalimbikitsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Anthuwo anakhudzidwa kwambiri ndi malangizowo ndipo anamupempha kuti awapempherere. Iye anawayankha mawu olimbikitsa akuti: “N’zosatheka kuti ineyo ndichimwire Yehova mwa kusiya kukupemphererani. Ndipo ndiyenera kukulangizani za njira yabwino ndi yolondola.”—1 Sam. 12:21-24.

Chitsanzo cha Samueli chikutiphunzitsa kuti sitiyenera kukhala ndi mkwiyo kapena maganizo ansanje mumtima mwathu

21. Kodi chitsanzo cha Samueli chingakuthandizeni bwanji ngati mwakhumudwa chifukwa choti munthu wina wapatsidwa udindo kapena zochita zinazake?

21 Kodi munayamba mwakhumudwapo chifukwa chakuti munthu wina wasankhidwa kapena kupatsidwa mwayi winawake? Chitsanzo cha Samueli chikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti sitiyenera kukhala ndi mkwiyo kapena maganizo ansanje mu mtima mwathu. (Werengani Miyambo 14:30.) Nthawi zonse Mulungu amadalitsa mtumiki wake aliyense ndiponso kumupatsa zochita.

“Kodi Ulirira Sauli Mpaka Liti?”

22. N’chifukwa chiyani Samueli sanalakwitse kuyembekezera kuti Sauli achita zinthu zabwino?

22 Samueli sanalakwitse kuyembekezera kuti Sauli achita zinthu zabwino chifukwa Sauli anali munthu wapadera kwambiri. Iye anali wamtali, wooneka bwino, wolimba mtima, wodziwa zambiri ndipo poyamba anasonyeza kuti anali wodzichepetsa ndiponso wosachita zinthu modzionetsera. (1 Sam. 10:22, 23, 27) Koma Sauli analinso ndi ufulu wosankha. Akanatha kusankha kuti akhala munthu wotani ndiponso kusankha yekha zimene akufuna kuchita. (Deut. 30:19) Komano kodi Sauli anagwiritsa ntchito bwino ufulu umenewu?

23. Kodi Sauli anachita khalidwe loipa liti ndipo anasonyeza bwanji kuti sanasiye khalidweli?

23 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amati akapatsidwa udindo waukulu, amayamba kudzikweza. Moti pasanapite nthawi, Sauli anayamba kudzikuza. Iye anasiya kumvera malamulo a Yehova amene Samueli ankamupatsa. Tsiku lina Sauli analephera kudikira ndipo anapereka nsembe yomwe ankayenera kupereka ndi Samueli. Samueli anadzudzula kwambiri Sauli ndipo anamuuziratu kuti ufumu sudzapitiriza kukhala m’banja lake. Koma m’malo moti aphunzirepo kanthu pa zimene Samueli anamuuza, Sauli anapitiriza kuchita zinthu zosamvera.—1 Sam. 13:8, 9, 13, 14.

24. (a) Pa nkhondo imene Sauli anamenyana ndi Aamaleki, kodi anasonyeza bwanji kusamvera Yehova? (b) Kodi Sauli anatani atapatsidwa malangizo, ndipo maganizo a Yehova anali otani pa nkhaniyi?

24 Nthawi ina kudzera mwa Samueli, Yehova anauza Sauli kuti akamenyane ndi Aamaleki. Limodzi mwa malangizo amene Yehova anapatsa Sauli linali lakuti aphe Agagi yemwe anali mfumu yoipa ya Aamaleki. Koma Sauli sanaphe Agagi ndiponso sanawononge zinthu zabwino zimene analanda kunkhondoko ngakhale kuti Yehova analamula kuti ziwonongedwe. Samueli atapita kukamuuza Sauli za kuipa kwa zimene anachitazo, Sauli anasonyezeratu kuti anali atasintha kwambiri. M’malo modzichepetsa n’kuvomereza kuti walakwa, Sauli anayamba kunena zinthu zambiri zodziikira kumbuyo, kupereka zifukwa zimene anachitira zimenezi, kudzilungamitsa, kusafuna kuti akambiranebe nkhaniyo komanso kuloza chala anthu. Sauli anayamba kupeputsa ndiponso kukana malangizo ponena kuti zina mwa zinthu zimene analanda kunkhondoko zinali zoti akazipereke nsembe kwa Yehova. Pamenepo Samueli anamuuza mawu amene anthu ambiri amawadziwa masiku ano akuti: “Kumvera kuposa nsembe.” Samueli anadzudzula Sauli molimba mtima ndipo anamuuza maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Anamuuza kuti ufumu udzachotsedwa kwa Sauliyo n’kuperekedwa kwa munthu wina woyenera kuposa iyeyo. *1 Sam. 15:1-33.

25, 26. (a) N’chifukwa chiyani Samueli analirira Sauli, ndipo Yehova anamulangiza bwanji mwachikondi? (b) Kodi Samueli anaphunzira chiyani atapita kunyumba ya Jese?

25 Samueli anakhumudwa kwambiri ndi zochita za Sauli. Iye anachezera usiku wonse akupemphera kwa Yehova za nkhaniyi. Samueli anafika mpaka polirira Sauli kwambiri. Poyamba Samueli ankaona kuti Sauli angathe kuchita bwino pa zinthu zambiri, koma zonse zimene ankayembekezera zinathera pompo. Munthu amene poyamba ankamudziwa kuti anali wabwino uja anali atasinthiratu. Iye anali atasiya kusonyeza makhalidwe ake abwino ndiponso kutsatira malangizo a Yehova. Chifukwa cha chisoni, Samueli anakana kuonananso ndi Sauli. Koma patapita nthawi, Yehova analangiza Samueli mwachikondi kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli? Thira mafuta m’nyanga yako ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”—1 Sam. 15:34, 35; 16:1.

26 Kuti Yehova akwaniritse cholinga chake sadalira anthu opanda ungwiro omwe nthawi zina amakhala osakhulupirika. Munthu wina akasiya kukhala wokhulupirika kwa iye, Yehova amagwiritsa ntchito wina kuti akwaniritsebe zolinga Zake. Choncho Samueli anasiya kulirira Sauli. Potsatira malangizo a Yehova, Samueli anapita ku Yerusalemu, kunyumba kwa Jese komwe anakapeza ana aamuna angapo a Jese ooneka bwino. Koma Yehova anali atamuuza kuti asakopeke ndi maonekedwe. (Werengani 1 Samueli 16:7.) Kenako Samueli anaona Davide, yemwe anali wamng’ono pa ana onse a Jese, ndipo anazindikira kuti ameneyu ndi amene Yehova anamusankha.

Samueli anaona kuti palibe mavuto omwe ndi akulu kwambiri moti Yehova sangathe kuwathetsa kapena kuwasandutsa madalitso

27. (a) N’chiyani chinathandiza Samueli kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba? (b) Kodi mukumva bwanji mukaganizira chitsanzo cha Samueli?

27 Chakumapeto kwa moyo wake, Samueli anaona kuti Yehova anachita bwino kusankha Davide kuti alowe m’malo mwa Sauli. Sauli anayamba nsanje kwambiri moti ankafuna kupha Davide komanso anayamba mpatuko. Koma Davide anali ndi makhalidwe abwino kwambiri. Iye anali wolimba mtima, wokhulupirika komanso anali ndi chikhulupiriro cholimba. Pamene Samueli ankakalamba, chikhulupiriro chake chinkalimbanso kwambiri. Iye anaona kuti palibe mavuto omwe ndi akulu kwambiri moti Yehova sangathe kuwathetsa kapena kuwasandutsa madalitso. Kenako Samueli anamwalira ndipo anasiya mbiri yabwino yomwe inakhalapobe kwa zaka zambiri. N’chifukwa chake ndi zosadabwitsa kuti Aisiraeli onse anamulira munthu wokhulupirika ameneyu. Masiku anonso atumiki a Yehova angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikutsanzira chikhulupiriro cha Samueli?’

^ ndime 24 Samueli anapha Agagi. Mfumu imeneyi ngakhalenso anthu a m’banja lake sankafunika kuchitiridwa chifundo. Ziyenera kuti patapita zaka zambiri, mbadwa za Agagi zinaphatikizapo “Hamani Mwagagi” yemwe ankafuna kupha atumiki onse a Mulungu.—Esitere 8:3; onani Mutu 15 ndi 16 m’buku lino.