MUTU 17

“Ndinetu Kapolo wa Yehova!”

“Ndinetu Kapolo wa Yehova!”

1, 2. (a) Kodi mlendo amene anabwera kwa Mariya anamulonjera bwanji? (b) Kodi Mariya ankafunika kusankha pa nkhani yofunika iti?

MARIYA anayang’ana modabwa kwambiri pamene mlendo ankalowa m’nyumba mwawo. Mlendoyu sanafunse za makolo ake chifukwa anabwerera a Mariyayo. Ndipo Mariya anadziwiratu kuti mlendoyu sanali wa mumzinda womwewo wa Nazareti. Popeza kuti mzindawu unali waung’ono, zinali zosavuta kuzindikira munthu wachilendo. Koma mlendo uyu ankaoneka wosiyana kwambiri ndi anthu. Komanso malonje amene iye anauza Mariya anali achilendo kwambiri. Iye anati: “Mtendere ukhale nawe, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.”—Werengani Luka 1:26-28.

2 Umu ndi mmene Baibulo limayambira kutiuza za Mariya, mwana wa Heli, yemwe ankakhala mumzinda wa Nazareti ku Galileya. Pa nthawi imeneyi n’kuti Mariya akufunika kusankha chochita pa nkhani yofunika kwambiri pa moyo wake. Iye anali pa chibwenzi ndi mmisiri wa matabwa Yosefe, yemwe sanali munthu wolemera koma anali wokhulupirika kwa Mulungu. Choncho, Mariya ayenera ankayembekezera kuti banja lawo silidzakhala lolemera komabe anakonzekera kuti azidzathandizana ndi mwamuna wake, Yosefe, kulera ana awo. Koma mosayembekezereka, kunyumba kwawo kunabwera mlendoyu amene anamuuza uthenga wonena za ntchito imene Mulungu ankafuna kum’patsa. Ntchito imeneyi inali yoti idzasintha moyo wake wonse.

3, 4. Kuti timudziwe bwino Mariya, kodi ndi zinthu ziti zomwe tikufunika kusaziganizira kwambiri, nanga ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuziganizira?

3 Anthu ambiri amadabwa kuona kuti Baibulo silinena zambiri zokhudza Mariya. Mwachitsanzo, silinena zambiri za mmene analeredwera ndiponso kuti anali munthu wotani. Silinenanso n’komwe zokhudza maonekedwe ake. Komabe, zimene Mawu a Mulungu amanena za iye zimatithandiza kudziwa zambiri za moyo wake.

4 Kuti tidziwe bwino za Mariya, tiyenera kuiwala kaye zikhulupiriro zambirimbiri zongopeka zimene zipembedzo zosiyanasiyana zimaphunzitsa. Motero, tiyeni tichotse m’maganizo mwathu zithunzi ndi ziboliboli zonse za Mariya zomwe zipembedzo zimajambula kapena kuumba. Komanso, tisaganizire za zinthu zovuta kumvetsa zimene zipembedzo zimaphunzitsa zokhudza mayi ameneyu, zomwe zachititsa kuti apatsidwe mayina monga “Mayi wa Mulungu” ndiponso “Mfumukazi Yakumwamba.” M’malomwake, tiyeni tione zimene Baibulo limanena zokhudza Mariya. Zimenezi zitithandiza kudziwa kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso zitithandiza kuona zimene tingachite pomutsanzira.

Mariya Analandira Mlendo

5. (a) Kodi zimene Mariya anachita mngelo atamuuza kuti ndi ‘wodalitsidwa koposa,’ zikutiuza chiyani za Mariyayo? (b) Kodi tingaphunzire chiyani kwa Mariya?

5 Mlendo amene anafika kwa Mariyayu sanali munthu wamba koma anali mngelo Gabirieli. Iye atatchula Mariya kuti “wodalitsidwa koposawe,” Mariyayo ‘anadabwa kwambiri,’ moti anayamba kusinkhasinkha za moni wamtundu umenewu. (Luka 1:29) Kodi pamenepa mngeloyu ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti Mariya wadalitsidwa ndi Yehova Mulungu. Ngakhale kuti Mariya ankadziwa kuti kudalitsidwa ndi Yehova Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri, sankadzikweza. Ifenso ngati tikufuna kuti Mulungu atidalitse, sitiyenera kuganiza modzikweza kuti Mulungu amatikonda ndipo wayamba kale kutidalitsa. Tikatero tidzaphunzira mfundo yofunika kwambiri imene Mariya ankaidziwa bwino yoti: Mulungu amatsutsa odzikweza, koma amakonda ndi kuthandiza anthu odzichepetsa.—Yak. 4:6.

Mariya sankadzikweza

6. Kodi mngelo anapatsa Mariya ntchito yapadera iti?

6 Mariya anafunikadi kukhala wodzichepetsa chonchi chifukwa ntchito imene mngeloyu anabwera kudzam’patsa inali yapadera kwambiri. Mngeloyo anamuuza kuti adzabereka mwana amene adzakhale wofunika kwambiri kuposa anthu onse. Iye anati: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32, 33) Mosakayikira, Mariya ankadziwa zimene Mulungu analonjeza Davide zaka zoposa 1,000 zimenezi zisanachitike. Lonjezolo linali lakuti mmodzi mwa mbadwa zake adzalamulira kwamuyaya. (2 Sam. 7:12, 13) Choncho mwana wakeyo anali kudzakhala Mesiya amene anthu a Mulungu ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali.

Ntchito imene mngelo Gabirieli anabwera kudzam’patsa Mariya inali yapadera kwambiri

7. (a) Kodi funso limene Mariya anafunsa linasonyeza chiyani? (b) Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Mariya?

7 Kuwonjezera pamenepo, mngeloyo anamuuza kuti mwana wakeyo “adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.” Kodi zingatheke bwanji kuti munthu abereke Mwana wa Mulungu? Ndipo zikanatheka bwanji kuti Mariya akhale ndi mwana, popeza ngakhale kuti anali pa chibwenzi ndi Yosefe, anali asanagonanepo? Mariya anafunsa mngeloyo funso limeneli mosapita m’mbali kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo ndi mwamuna?” (Luka 1:34) Taonani kuti Mariya sanachite manyazi kutchula kuti anali asanagonanepo ndi mwamuna ndipo ankanyadira kuti anali namwali. Koma masiku ano, achinyamata ambiri saona vuto lililonse kugonana asanalowe m’banja, ndipo amanyoza anzawo omwe sanagonanepo ndi wina aliyense. Dzikoli lasintha kwambiri, koma Yehova sanasinthe. (Mal. 3:6) Mofanana ndi mmene zinalili m’masiku a Mariya, Mulungu amasangalala ndi anthu amene amatsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino.—Werengani Aheberi 13:4.

8. Ngakhale kuti Mariya anali munthu wopanda ungwiro, kodi zikanatheka bwanji kuti abereke mwana wangwiro?

8 Ngakhale kuti Mariya anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, anali wopanda ungwiro ngati ife tomwe. Ndiyeno zikanatheka bwanji kuti abereke Mwana wangwiro wa Mulungu? Gabirieli anati: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Kukhala “woyera” kumatanthauza “kusadetsedwa” kapena “kukhala wopatulika.” Mwachibadwa, anthu amapatsira ana awo kupanda ungwiro. Koma pa nkhani ya Mariya, mngelo anasonyeza kuti Yehova adzachita chozizwitsa chapadera kwambiri. Anasonyeza kuti Yehova adzasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wake ‘kuphimba’ Mariya, kuti mwanayo asatengere uchimo. Kodi Mariya anakhulupirira zimene mngeloyo anamuuzazi? Nanga kodi anayankha bwanji?

Zimene Mariya Anayankha Gabirieli

9. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu amene amakayikira nkhani ya Mariya amalakwitsa? (b) Kodi Gabirieli analimbitsa bwanji chikhulupiriro cha Mariya?

9 Anthu ena, kuphatikizapo akatswiri a maphunziro a zaumulungu m’Matchalitchi Achikhristu, sakhulupirira kuti nkhani imeneyi inachitikadi chifukwa amaona kuti mtsikana yemwe sanagonepo ndi mwamuna sangabereke mwana. Ngakhale kuti anthuwa ndi ophunzira kwambiri, amalephera kumvetsa mfundo yosavuta imene Gabirieli ananena. Iye ananena kuti, “zimene Mulungu wanena, sizilephereka.” (Luka 1:37) Mariya sanakayikire zimene Gabirieli ananena chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe izi sizikutanthauza kuti Mariya anali m’gulu la anthu omwe amangokhulupirira zilizonse. Mofanana ndi munthu wina aliyense woganiza bwino, Mariya anafuna umboni wa zomwe anauzidwazi. Ndipo Gabirieli anam’patsadi umboniwo. Anam’fotokozera za m’bale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe anali wokalamba ndipo ankadziwika kuti anali wosabereka. Koma pa nthawiyi Mulungu anachititsa kuti Elizabeti akhale woyembekezera.

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito imene Mariya anapatsidwa sinali yophweka?

10 Kodi pamenepa Mariya akanatani? Iye anali atapatsidwa ntchito yoti achite ndipo anali ndi umboni wakuti Mulungu adzachita zonse zimene Gabirieli ananena. Ngakhale kuti unali mwayi waukulu kupatsidwa ntchito imeneyi, tisaganize kuti inali yophweka kapena kuti yopanda mavuto alionse. Musaiwale kuti iye anali pa chibwenzi ndi Yosefe. Kodi Yosefe akanam’kwatirabe akanadziwa kuti ndi woyembekezera? Komanso n’kutheka kuti Mariya ankaona kuti ntchitoyi sinali yamasewera chifukwa anali kudzakhala ndi pakati pa Mwana wokondedwa kwambiri wa Mulungu, yemwe ndi wamtengo wapatali pa zolengedwa zonse. Ndipo akanafunika kum’samalira ali wakhanda ndiponso kumuteteza ku dziko loipali. Kunena zoona, imeneyi inalidi ntchito yovuta kwambiri.

11, 12. (a) Kodi anthu ena anatani atapatsidwa ntchito ndi Mulungu, ngakhale kuti anali okhulupirika? (b) Kodi zimene Mariya anayankha Gabirieli zikusonyeza kuti anali munthu wotani?

11 Baibulo limasonyeza kuti ngakhale anthu achikhulupiriro cholimba kwambiri nthawi zina anakaikira ngati angakwanitse ntchito imene Mulungu wawapatsa. Mwachitsanzo, Mose ananena kuti sangakhale wolankhulira Mulungu chifukwa chakuti ankavutika kulankhula. (Eks. 4:10) Yeremiya ananena kuti anali “mwana” moti sangakwanitse ntchito imene Mulungu anam’patsa. (Yer. 1:6) Nayenso Yona anathawa Yehova atam’patsa ntchito. (Yona 1:3) Kodi Mariya anayankha chiyani?

12 Zimene iye anayankha zikusonyeza kuti anali wodzichepetsa kwambiri ndiponso womvera. Mariya anauza Gabirieli kuti: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” (Luka 1:38) Kapolo anali mtumiki wotsika kwambiri ndipo moyo wake wonse unkalamulidwa ndi mbuye wake. Choncho, Mariya ankadziona kuti anali kapolo wa Yehova. Ankadziwa kuti ndi wotetezeka m’manja mwake ndiponso kuti Yehova amakhala wokhulupirika kwa anthu okhulupirika kwa iye. (Sal. 18:25) Ankadziwanso kuti Yehova adzam’dalitsa ngati atayesetsa kugwira ntchito yomwe wapatsidwa.

Mariya ankadziwa kuti ndi wotetezeka m’manja mwa Yehova Mulungu, yemwe ndi wokhulupirika

13. Kodi chitsanzo cha Mariya chingatithandize bwanji ngati tikuona kuti ntchito imene Mulungu watipatsa ndi yovuta kapenanso yosatheka?

13 Nthawi zina Mulungu angatiuze kuti tichite zinthu zinazake zimene ifeyo tingaone kuti n’zovuta kapenanso n’zosatheka n’komwe. Komabe, kudzera m’Mawu ake, iye watipatsa zifukwa zomveka zom’khulupirira ndiponso kum’dalira ndi moyo wathu wonse ngati mmene Mariya anachitira. (Miy. 3:5, 6) Tikamadalira Yehova, iye adzatidalitsa ndipo adzatithandiza kuti tizimukhulupirira kwambiri.

Mariya Anapita Kukacheza kwa Elizabeti

14, 15. (a) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Mariya pamene anapita kunyumba kwa Elizabeti ndi Zakariya? (b) Kodi mawu a Mariya opezeka pa Luka 1:46-55 akutiuza chiyani za Mariyayo?

14 Mariya anaona kuti zimene Gabirieli anamuuza zokhudza Elizabeti zinali zofunika kwambiri. Iye ankadziwa kuti palibe munthu wina aliyense amene akanamvetsa bwino zimene zinamuchitikirazi kuposa Elizabeti. Nthawi yomweyo, iye anayamba ulendo wopita kwa Elizabeti ku Yuda. Derali linali lamapiri ndipo mwina ulendowu unatenga masiku atatu kapena anayi. Atafika kunyumba kwa Elizabeti, mkazi wa Zakariya, Yehova anapatsanso Mariya umboni wina womwe unalimbitsa chikhulupiriro chake. Elizabeti atangomva mawu a Mariya, nthawi yomweyo mwana amene anali m’mimba mwake analumpha ndi chisangalalo. Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anatchula Mariya kuti “mayi wa Mbuye wanga.” Mulungu anathandiza Elizabeti kudziwa kuti mwana wa Mariya adzakhala Mbuye wake komanso Mesiya. Ndiponso mouziridwa ndi mzimu, iye anayamikira Mariya chifukwa cha kumvera ndiponso kukhulupirika kwake. Iye anati: “Ndiwe wodala pakuti unakhulupirira.” (Luka 1:39-45) Zoonadi, zonse zimene Yehova anam’lonjeza Mariya zinali zoti zidzakwaniritsidwa.

Ubwenzi wa Mariya ndi Elizabeti unathandiza kwambiri azimayi awiri onsewa

15 Kenako Mariya analankhula mawu omwe amapezeka m’Baibulo. (Werengani Luka 1:46-55.) Pa mawu onse opezeka m’Baibulo amene Mariya analankhula, mawu amenewa ndiye aatali kwambiri ndipo amatithandiza kum’dziwa bwino Mariyayo. Mawuwa amasonyeza kuti iye anali ndi mtima woyamikira, chifukwa anatamanda Yehova pom’patsa mwayi wokhala mayi wa Mesiya. Amasonyezanso kuti Mariya anali ndi chikhulupiriro champhamvu chifukwa iye anafotokoza kuti Yehova amatsitsa anthu odzikweza ndi amphamvu ndipo amakweza odzichepetsa amene amafuna kum’tumikira. Komanso mawuwa akusonyeza kuti Mariya ankadziwa Malemba kwambiri. Zikuoneka kuti iye anatchula mawu opezeka m’Malemba Achiheberi maulendo oposa 20. *

16, 17. (a) Kodi Mariya komanso Yesu anatipatsa chitsanzo chotani? (b) Kodi zimene zinachitika Mariya atapita kwa Elizabeti zikutikumbutsa za kufunika kwa chiyani?

16 Apa n’zoonekeratu kuti Mariya ankadziwa kwambiri Mawu a Mulungu. Ngakhale zinali choncho, iye anadzichepetsa ndipo analankhula mawu amene anali kale m’Malemba m’malo mofotokoza za m’maganizo mwake. Mwana amene anali m’mimba mwake anadzasonyezanso mtima ngati womwewu. Pa nthawi ina Yesu anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.” (Yoh. 7:16) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi inenso ndimalemekeza Mawu a Mulungu chonchi, kapena pophunzitsa ndimangonena maganizo anga?’ Mariya ankalemekeza kwambiri mawu a Mulungu ndipo sankanena za m’maganizo mwake.

17 Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi pafupifupi itatu ndipo mosakayikira iwo analimbikitsana kwambiri pa nthawiyi. (Luka 1:56) Zimenezi zimatikumbutsa kufunika kokhala ndi mabwenzi. Tikakhala ndi anzathu omwe amakondadi Yehova, tidzakula mwauzimu ndiponso tidzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulunguyo. (Miy. 13:20) Kenako Mariya anaganiza zobwerera kwawo. Koma kodi Yosefe anatani atamva kuti Mariya ndi woyembekezera?

Zomwe Zinachitika Mariya Atakumana ndi Yosefe

18. Kodi Mariya anamuuza chiyani Yosefe, nanga iye anatani atamva zimenezi?

18 Mariya sanadikire kuti anthu ayambe kumudabwa kuti ndi woyembekezera. Iye anaona kuti ayenera kumuuza yekha Yosefe. Koma ayenera kuti ankada nkhawa kuti Yosefe, yemwe anali munthu wokhulupirika ndiponso woopa Mulungu, atani akamva za nkhaniyi. Komabe, iye analimba mtima n’kumuuza zonse zimene zinachitika. Nkhani imeneyi inam’vutitsa maganizo kwambiri Yosefe. Ngakhale kuti Yosefe sankamukayikira bwenzi lakeyu, anayamba kuona kuti mwina wamuyenda pansi. Baibulo silinena zimene Yosefe ankaganiza pa nthawiyi. Koma limanena kuti ataganizira za nkhaniyi, anakonza zom’sudzula. Pa nthawi imeneyo, anthu omwe ali pa chibwenzi ankaonedwa ngati okwatirana. Komabe, iye sanafune kum’chititsa manyazi kapena kumuyalutsa, motero anasankha zomusudzula mwamseri. (Mat. 1:18, 19) Ziyenera kuti zinam’pweteka kwambiri Mariya kuona bwenzi lake, yemwe anali munthu wokoma mtima, akuvutika maganizo chifukwa cha nkhaniyi. Komabe Mariya sanamukhumudwire Yosefe chifukwa chosakhulupirira zimene iye anafotokoza.

19. Kodi Yehova anathandiza bwanji Yosefe kudziwa kuti sakuyenera kuthetsa chibwenzi ndi Mariya?

19 Yehova anathandiza Yosefe kudziwa kuti sakuyenera kuthetsa chibwenzicho. Mngelo wa Mulungu anauza Yosefe kudzera m’maloto kuti Mariya anatengadi pathupipo mozizwitsa. Zimenezi ziyenera kuti zinamukhazika mtima pansi ndipo anatsatira malangizo a Yehova ngati mmene Mariya anachitira. Iye anakwatira Mariya ndipo anali wokonzekera kugwira ntchito yapadera yosamalira Mwana wa Yehova.—Mat. 1:20-24.

20, 21. Kodi anthu amene ali pa banja komanso amene akukonzekera kulowa m’banja angaphunzire chiyani kwa Mariya ndi Yosefe?

20 Anthu omwe ali pa banja ndiponso amene akufuna kulowa m’banja ayenera kuphunzirapo kanthu pa zimene Yosefe ndi Mariya anachitazi. Pamene Yosefe ankaona kuti mkazi wake akusamalira bwino banja lake, mosakayikira ankathokoza kuti mngelo wa Yehova uja anam’patsa malangizo abwino. Zimenezi ziyenera kuti zinam’thandiza kwambiri kuona ubwino wodalira Yehova posankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. (Sal. 37:5; Miy. 18:13) Monga mutu wa banja, iye ayenera kuti anapitirizabe kuchita zinthu mosamala ndiponso mwachifundo.

21 Nanga kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Mariya anachita pololera kuti akwatiwe ndi Yosefe? Ngakhale kuti poyamba Yosefe anavutika kuti akhulupirire zimene Mariya anamuuza, Mariya anadekha n’kudikirabe kuti Yosefe asankhe zochita pa nkhaniyi. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti Yosefe ndi amene adzakhale mutu wa banja lawo. Zimenezi zinam’thandiza kwambiri Mariya ndipo ndi chitsanzo chabwino kwa akazi achikhristu masiku ano. Mosakayikira, nkhani zimenezi zinathandiza Yosefe ndi Mariya kuona kufunika kolankhulana momasuka komanso moona mtima.—Werengani Miyambo 15:22.

22. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yosefe ndi Mariya anayala maziko abwino a banja lawo, nanga anali ndi udindo wotani?

22 Yosefe ndi Mariya anayala maziko abwino a banja lawo. Onse ankakonda Yehova Mulungu ndipo ankafunitsitsa kum’sangalatsa mwa kuchita zinthu monga makolo achikondi ndiponso osamalira bwino ana awo. Ngakhale kuti iwo anadalitsidwa m’njira zosiyanasiyana, analinso ndi udindo waukulu wolera Yesu yemwe anali wofunika kwambiri kuposa wina aliyense padziko lonse lapansi.

^ ndime 15 Mawu ena amene Mariya anatchula ayenera kuti ndi amene ananenedwanso ndi Hana, mayi wokhulupirika, amenenso Yehova anamuthandiza kuti akhale ndi mwana.—Onani bokosi lakuti “Mapemphero Awiri Ogwira Mtima,” lomwe lili m’Mutu 6.