MUTU 22
Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
1, 2. Pamene Yesu anali ku Kaperenao, kodi Petulo ankayembekezera chiyani, koma chinachitika n’chiyani?
PA NTHAWI ina Yesu akuphunzitsa anthu m’sunagoge ku Kaperenao, Petulo anayang’anitsitsa anthuwo mwachidwi. Petulo anali wochokera m’tauni imeneyi ndipo pa nthawi ina ankachita bizinezi yake ya nsomba m’tauni yomweyi, kufupi ndi gombe la nyanja ya Galileya. M’derali munali anzake ambiri, abale ake komanso anthu amene ankachita nawo malonda. N’zosakayikitsa kuti pa nthawiyi, Petulo ankayembekezera kuti anthu a m’tauni yakwawoyi nawonso asangalala kuphunzira za Ufumu wa Mulungu kuchokera kwa Mphunzitsi waluso kwambiriyu. Koma zimene zinachitika zinali zosiyana ndi zimene iye ankayembekezerazi.
2 Anthu ambiri anali atasiya kumvetsera Yesu ndipo ena anayamba kung’ung’udza chifukwa chosagwirizana ndi zimene ankaphunzitsa. Koma zimene Petulo anakhumudwa nazo kwambiri ndi zimene ena mwa ophunzira a Yesu anachita. Nkhope zawo zinayamba kusonyeza kuti asiya kusangalala ndi zimene Yesu akuphunzitsa ndipo alibe chidwi chophunzira zinthu zatsopano ndiponso choonadi kuchokera kwa Yesu. Ankaonekanso kuti asokonezeka maganizo ndiponso akwiya. Ena anayamba kulankhula mokweza kuti zimene Yesu ananena zinali zozunguza. Iwo sanafunenso kupitiriza kumvetsera, choncho anatuluka m’sunagogemo ndipo anasiyiratu kutsatira Yesu.—Werengani Yohane 6:60, 66.
3. Kodi chikhulupiriro cha Petulo chinamuthandiza bwanji kangapo konse?
3 Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa Petulo ndi atumwi anzake. Nayenso sanamvetse tanthauzo la zimene Yesu anaphunzitsa pa tsikuli. Petulo ayenera kuti ankaona kuti mawu amene Yesu analankhula akhoza kukhumudwitsadi munthu ngati sanatanthauziridwe. Ndiye kodi iye anatani? Aka sikanali koyamba kapena komaliza kuti Petulo akumane ndi zinthu zimene zikanam’pangitsa kuti asiye kutsatira Yesu. Tiyeni tione mmene chikhulupiriro cha Petulo chinamuthandizira kuthana ndi mavuto amenewa n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika.
Anakhalabe Wokhulupirika Ena Atasiya Kutsatira Yesu
4, 5. Kodi Yesu anachita zinthu ziti zomwe zinali zosiyana ndi zomwe anthu ankayembekezera?
4 Nthawi zambiri, Petulo ankadabwa ndi zimene Yesu ankachita komanso kunena. Kawirikawiri Yesu ankachita ndiponso kulankhula zinthu zosiyana ndi zimene anthu ankayembekezera. Mwachitsanzo, dzulo lake Yesu anali atadyetsa anthu ambirimbiri mozizwitsa. Chifukwa cha zimenezi, anthuwo anaganiza zomulonga ufumu. Koma iye anadabwitsa anthu ambiri chifukwa anachoka pamalowa ndipo anauza ophunzira ake kuti akwere boti kupita ku Kaperenao. Ophunzira ake akuyendetsa boti usiku wa tsiku limeneli panyanja ya Galileya, Yesu anachitanso chinthu china chomwe chinawadabwitsa kwambiri. Iwo anamuona akubwera poteropo, akuyenda panyanja koma osamira ngakhale kuti panyanjapo panali mafunde. Usiku umenewu, iye anathandizanso Petulo kudziwa kufunika kokhala ndi chikhulupiriro.
5 M’mawa mwake, iwo anaona kuti khamu la anthu lija lawatsatira. Koma zikuoneka kuti ankawatsatira ndi cholinga chakuti Yesu awapatsenso chakudya china mozizwitsa, osati ndi cholinga chakuti awaphunzitse zinthu zauzimu. Motero, Yesu anawadzudzula chifukwa cha mtima wokonda zinthu zakuthupiwu. (Yoh. 6:25-27) Atafika m’sunagoge ku Kaperenao, Yesu anapitiriza nkhani ya chakudya ija, ndipo anawauza zinthu zimene sankayembekezera. Cholinga chake chinali choti awaphunzitse mfundo yofunika kwambiri ngakhale kuti inali yovuta kumva.
6. Kodi Yesu anafotokoza fanizo lotani, nanga omvera ake anatani atamva fanizolo?
6 Yesu sankafuna kuti anthuwa azimutsatira n’cholinga choti awapatse chakudya. Koma ankafuna kuti anthuwo adziwe kuti iyeyo anatumidwa ndi Mulungu n’cholinga choti adzawafere kuti adzapeze moyo wosatha. Choncho Yesu anadziyerekezera ndi mana, chakudya chochokera kumwamba chomwe anthu ankadya m’nthawi ya Mose. Anthu ena atasonyeza kuti sakugwirizana ndi zimene ananenazi, iye anafotokoza fanizo loti anthu ayenera kudya thupi lake ndi kumwa magazi ake kuti apeze moyo. Atanena zimenezi, ena mwa anthuwo anakwiya kwambiri ndipo anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?” Ndipo, ambiri mwa ophunzira ake anaganiza zosiya kuyenda naye. *—Yoh. 6:48-60, 66.
7, 8. (a) Kodi Petulo anali asanamvetse mfundo iti yokhudza Yesu? (b) Kodi Petulo anayankha bwanji funso limene Yesu anafunsa atumwi?
7 Koma kodi Petulo anachita chiyani? Iyenso ayenera kuti anasokonezeka maganizo ndi zimene Yesu ananenazi. Pa nthawiyi Petulo sankadziwa kuti Yesu ankayenera kufa kuti akwaniritse cholinga cha Mulungu. Koma kodi nayenso anasiya kutsatira Yesu ngati mmene anachitira enawo? Ayi, chifukwa Petulo anali ndi khalidwe linalake limene anthu enawo analibe.
8 Yesu anayang’ana atumwi ake n’kuwafunsa kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” (Yoh. 6:67) Funsoli ankafunsa atumwi ake onse 12 koma Petulo ndi amene anayankha. Nthawi zambiri Petulo ndi amene ankakonda kuyankha Yesu akafunsa funso. N’kutheka kuti iye ndi amene anali wamkulu pagulu lonselo. Kaya zimenezi n’zimene zinkachititsa kuti azikonda kuyankha mafunso, mfundo ndi yakuti Petulo anali wokonda kulankhula ndipo kawirikawiri sankaopa kulankhula zimene zinali m’maganizo mwake. Poyankha funso la Yesu lija, Petulo analankhula mawu osaiwalika akuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”—Yoh. 6:68.
9. Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika?
9 Mawu amenewa ndi ogwira mtima kwambiri. Petulo ankakhulupirira kwambiri Yesu ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti asasiye kumutsatira. Petulo anadziwa kuti palibenso Mpulumutsi wina kupatulapo Yesu komanso kuti zimene ankaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu n’zothandiza kuti anthu adzapulumuke. Petulo ankadziwanso kuti ngakhale kuti panali zinthu zimene sankazimvetsa, panalibe kwina kumene akanapita kuti apeze moyo wosatha ndiponso kuti Mulungu apitirize kumukonda.
Tiyenera kutsatira mfundo za Yesu ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zimene timayembekezera komanso zimene tingakonde
10. Kodi tingatsanzire bwanji kukhulupirika kwa Petulo?
10 Kodi inunso muli ndi maganizo ofanana ndi a Petulowa? N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri masiku ano amanena kuti amakonda Yesu koma sasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa iye. Ngati tikufunadi kukhala okhulupirika kwa Yesu tiyenera kukonda mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa ngati mmene Petulo ankachitira. Tiyenera kuphunzira, kumvetsa ndiponso kutsatira mfundozo ngakhale zitakhala kuti n’zosiyana ndi zimene timayembekezera komanso zimene tingakonde. Tidzapeza moyo wosatha umene Yesu analonjeza, pokhapokha ngati tili okhulupirika.—Werengani Salimo 97:10.
Anakhalabe Wokhulupirika Atadzudzulidwa
11. Kodi Yesu anapita kuti ndi otsatira ake? (Onaninso mawu a m’munsi.)
11 Zimenezi zitachitika, Yesu ndi atumwi ake komanso ophunzira ena anayamba ulendo wautali wolowera chakumpoto. Iwo akuyenda, anayamba kuona phiri la Herimoni chakumpoto kwenikweni kwa Dziko Lolonjezedwa. Nthawi zina, munthu akakhala kunyanja ya Galileya, ankatha kuona phirili, lomwe nthawi zambiri linkakutidwa ndi chipale chofewa. Phirili linayamba kuoneka lalitali kwambiri pamene ankaliyandikira ndipo kenako anafika m’midzi yapafupi ndi Kaisareya wa Filipi. * Ali m’dera lokongolali, akayang’ana kum’mwera, ankaona mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. Kenako Yesu anafunsa atumwi ake funso lofunika kwambiri.
12, 13. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa zimene anthu ena ankaganiza ponena za iye? (b) Kodi mawu amene Petulo anauza Yesu anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro chenicheni?
12 Pa nthawiyi Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthuwa akumati ine ndine ndani?” Tingathe kuona m’maganizo mwathu Petulo akumuyang’anitsitsa Yesu, n’kuganizira za kukoma mtima komanso nzeru za Mbuye wakeyo. Yesu ankafunitsitsa kudziwa zimene anthu ankaganiza kuchokera pa zimene anaona ndi kumva za iye. Ophunzirawo anayankha funsoli pobwereza zina mwa zinthu zolakwika zimene anthu ambiri ankanena zokhudza Yesu. Koma iye ankafuna kudziwa ngati ophunzira akewo nawonso anali ndi maganizo olakwikawa. Choncho, anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?”—Luka 9:18-20.
13 Apanso Petulo sanachedwe kuyankha. Iye anayankha momveka komanso molimba mtima zinthu zimenenso zinali m’maganizo a anthu ambiri amene anali pamalopo. Iye anati: “Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesu ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi Petulo chifukwa cha yankho lake ndipo anamuyamikira. Iye anauza Petulo kuti Yehova Mulungu, osati munthu, ndi amene anam’thandiza kudziwa mfundo ya choonadi imeneyi. Apa Petulo anathandizidwa kudziwa imodzi mwa mfundo zofunika kwambiri za choonadi zimene anthu ambiri anali asanazidziwe. Iye anadziwa kuti Yesu ndi Mesiya, kapena kuti Khristu, amene Mulungu analonjeza kalekale.—Werengani Mateyu 16:16, 17.
14. Kodi Yesu anapatsa Petulo ntchito yofunika iti?
14 Khristu ameneyu ndi amene aneneri analosera kalekale kuti ndi mwala umene udzakanidwe ndi amisiri omanga nyumba. (Sal. 118:22; Luka 20:17) Yesu ankaganizira ulosi umenewu pamene ananena kuti Yehova adzakhazikitsa mpingo pamwala umenewu kapena kuti thanthwe, lomwe Petulo anali atangolitchula kumene. Kenako Yesu anapereka kwa Petulo udindo wofunika kwambiri pampingo. Zimenezi sizikutanthauza kuti Petulo anasankhidwa kukhala wapamwamba kuposa atumwi ena, monga mmene anthu ena amaganizira, koma anangopatsidwa ntchito yowonjezera. Yesu anapatsa Petulo “makiyi a ufumu.” (Mat. 16:19) Zimenezi zinatanthauza kuti Petulo adzatsegula khomo lakuti magulu atatu a anthu alowe mu Ufumu wa Mulungu. Maguluwa ndi Ayuda, Asamariya ndiponso anthu amitundu ina.
15. Kodi Yesu ananena mawu otani amene anakhumudwitsa Petulo, nanga Petuloyo anauza Yesu mawu ati?
15 Komabe, nthawi ina Yesu ananena kuti amene apatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunidwa kwa iwo, ndipo mawu amenewa ndi oona tikaganizira za Petulo. (Luka 12:48) Yesu anapitiriza kuuza ophunzira ake mfundo zofunika kwambiri za choonadi zokhudza iyeyo monga Mesiya, kuphatikizapo mfundo yakuti ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kuzunzidwa ndi kuphedwa. Koma Petulo atamva zimenezi anakhumudwa kwambiri ndipo anatengera Yesu pambali n’kumuuza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye; musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.”—Mat 16:21, 22.
16. Kodi Yesu anadzudzula bwanji Petulo, nanga tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu amenewa?
16 Petulo ayenera kuti ananena zimenezi chifukwa choti ankafunira zabwino Yesu, choncho n’kutheka kuti anadabwa ndi zomwe Yesu anayankha. Yesu atamva zimene Petulo ananena, anatembenuka n’kuyang’ana komwe kunali atumwi ena aja, omwe mwina analinso ndi maganizo ngati a Petulo. Kenako anati: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mat. 16:23; Maliko 8:32, 33) Zimene Yesu ananenazi n’zothandizanso kwa ife chifukwa nafenso tikhoza kuyamba kutsatira maganizo a anthu m’malo motsatira zimene Mulungu akufuna. Ngakhale titakhala ndi maganizo ofuna kuthandiza ena, tikamatsatira maganizo a anthu, tingakhale tikupititsa patsogolo zolinga za Satana mosadziwa. Koma kodi Petulo anatani atadzudzulidwa?
17. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza Petulo kuti ‘apite kumbuyo kwake’?
17 Petulo ankadziwa kuti Yesu sankatanthauza kuti iyeyo ndi Satana Mdyerekezi weniweni. Ndipotu, zimene Yesu ananena kwa Petulo sizinali zofanana ndi zimene anauza Satana nthawi ina m’mbuyomo. Tikutero chifukwa polankhula ndi Satana, Yesu anati: “Choka”, pamene polankhula ndi Petulo anati: “Pita kumbuyo kwanga.” (Mat. 4:10) Choncho sikuti Yesu ankadana ndi Petulo, mtumwi yemwe ankamuona kuti ali ndi makhalidwe ambiri abwino. Iye anangofuna kumudzudzula kuti asiye kuganiza molakwika pa nkhaniyi. Ankatanthauza kuti Petulo anafunika kukhala kumbuyo monga wotsatira wake wothandiza kwambiri, osati kukhala patsogolo n’kumapunthwitsa Mbuye wakeyo.
Tikalandira uphungu modzichepetsa n’kuphunzira pa zimene tinalakwitsa, ubwenzi wathu ndi Yesu Khristu ndiponso Yehova Mulungu, umalimba
18. Kodi Petulo anasonyeza bwanji kukhulupirika, ndipo tingamutsanzire bwanji?
18 Kodi Petulo anatsutsana ndi Yesu, n’kukwiya kapena kusiya kulankhula naye? Ayi, analandira uphunguwo modzichepetsa. Mwa kuchita zimenezi, kachiwirinso Petulo anasonyeza kuti ndi wokhulupirika. Anthu onse amene amatsatira Khristu, nthawi zina amafunika kudzudzulidwa. Tikalandira uphunguwo modzichepetsa n’kuphunzira pa zimene tinalakwitsazo, ubwenzi wathu ndi Yesu Khristu ndiponso Yehova Mulungu, umalimba.—Werengani Miyambo 4:13.
Anadalitsidwa Chifukwa cha Kukhulupirika Kwake
19. Kodi Yesu ananena mawu odabwitsa ati, nanga Petulo ayenera kuti anali ndi maganizo otani atamva mawuwo?
19 Pa nthawi imeneyi, Yesu analankhulanso mawu ena odabwitsa. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.” (Mat. 16:28) N’zosakayikitsa kuti Petulo anali ndi chidwi chofuna kudziwa tanthauzo la mawu amenewa. Mwina Petulo anaganiza kuti sadzalandira nawo madalitsowa chifukwa chakuti anali atangodzudzulidwa kumene ndi Yesu.
20, 21. (a) Fotokozani masomphenya amene Petulo anaona. (b) Kodi zinthu zimene anthu a m’masomphenyawo ankakambirana ndi Yesu zinathandiza bwanji Petulo kuzindikira kuti ankaganiza molakwika?
20 Komabe, patapita mlungu umodzi, Yesu anatenga Yakobo, Yohane, ndi Petulo n’kukwera nawo “m’phiri lalitali.” Phirili mwina linali la Herimoni, lomwe linali pafupi ndi kumene iwo anali. Zikuoneka kuti unali usiku chifukwa atumwi atatuwo anali ndi tulo. Koma Yesu atayamba kupemphera, panachitika chinachake chimene chinachititsa kuti tulo tonse timene atumwiwo anali nato tibalalike.—Mat. 17:1; Luka 9:28, 29, 32.
21 Yesu anayamba kusandulika iwo akuona. Nkhope yake inayamba kuwala mpaka kuoneka ngati dzuwa. Zovala zakenso zinayamba kunyezimira kwambiri. Kenako pafupi ndi Yesu panaoneka anthu awiri, mmodzi wooneka ngati Mose ndipo winayo ngati Eliya. Iwo ankakambirana naye “za mmene adzachokere m’dzikoli, ku Yerusalemu.” Zimenezi zikutanthauza kuti ankakambirana za kufa ndi kuuka kwake. Choncho, zinali zoonekeratu kuti Petulo analakwitsa poganiza kuti Yesu sankayenera kudzakumana ndi mavuto ngati amenewa.—Luka 9:30, 31.
22, 23. (a) Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti anali ndi mtima wodzipereka komanso wofuna kuthandiza ena? (b) Kodi Petulo, Yakobo ndi Yohane anadalitsidwanso motani usiku umenewu?
22 Ataona masomphenya amenewa Petulo anafunitsitsa kuti athandizepo kuti masomphenyawo asathe msanga. Moti zitaoneka kuti Mose ndi Eliya akufuna azipita, Petulo anati: “Mlangizi, ndi bwino kuti ife tizikhala pano. Choncho timange mahema atatu, limodzi lanu, limodzi la Mose ndi lina la Eliya.” Komabe, anthu ooneka ngati atumiki a Mulungu omwe anali atafa kalekale amenewa sankafunikira mahema. Choncho, pamenepa Petulo sankadziwa zimene ankanena. Komabe, kodi simukuchita chidwi ndi mtima wake wodzipereka komanso wofuna kuthandiza ena?—Luka 9:33.
23 Petulo, Yakobo ndi Yohane anadalitsidwanso usiku umenewu. Paphiripo panabwera mtambo womwe unawaphimba. Kenako anamva mawu a Yehova Mulungu ochokera mumtambomo, akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndinam’sankha. Mumvereni.” Kenako masomphenyawo anatha ndipo atumwiwo anangotsala ndi Yesu yekha paphiripo.—Luka 9:34-36.
24. (a) Kodi masomphenya a ulemerero wa Yesu anathandiza bwanji Petulo? (b) Kodi ifeyo tingatani kuti tipindule ndi masomphenya amenewa?
24 Masomphenya amenewa anali othandiza kwambiri kwa Petulo ndipo ndi othandizanso kwa ifeyo. Patapita zaka zambiri, Petulo analemba za mwayi wapadera umene anali nawo usiku umenewu, wokhala mmodzi wa anthu amene ‘anaona ndi maso ulemerero’ wa Yesu. Anakhala ngati aona Yesu ali Mfumu kumwamba. Masomphenya amenewa anali umboni wakuti maulosi a m’Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa ndipo analimbitsa chikhulupiriro cha Petulo komanso anamuthandiza kuti adzathe kupirira mayesero amene anali kutsogolo kwake. (Werengani 2 Petulo 1:16-19.) Nafenso masomphenya amenewa angatithandize ngati titapitirizabe kukhala okhulupirika kwa Mbuye wathu, Yesu Khristu, yemwe Yehova wamusankha. Tiyeneranso kuphunzira kwa iye, kutsatira uphungu wake, ndiponso kutsatira mapazi ake modzichepetsa tsiku ndi tsiku.
^ ndime 6 Umboni woti anthuwa anali osachedwa kusintha maganizo umaoneka tikayerekezera zimene iwo ananena pa nthawiyi ndi zimene ananena dzulo lake, pamene ananena mosangalala kuti Yesu ndi mneneri wa Mulungu.—Yoh. 6:14.
^ ndime 11 Kuchokera kugombe la nyanja ya Galileya, gululi linayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 45. Iwo anachoka kugombe lotsika kwambiri ndipo anadutsa m’dera lokongola kukafika kumalo okwera kwambiri.
Nkhani Zina
Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Amuna ndi Akazi Otchulidwa M’Baibulo Kukhulupirira Mulungu Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—MavidiyoMwina Mungakondenso Kudziwa Izi
TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO
Petulo—Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira
Nthawi zina kukayikira zinthu kumakhala koipa kwambiri. Koma Petulo anathetsa mantha komanso mtima wokayikira potsatira chitsanzo cha Yesu.
TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO
Petulo—Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani Petulo pa nkhani ya kukhululuka? Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza kuti anakhululukira Petulo?
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA
Zokuthandizani Pophunzira Baibulo
Sankhani zinthu zokuthandizani pophunzira Baibulo zimene zingapangitse kuphunzira kukhala kopindulitsa komanso kosangalatsa.
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA
Yambani kuphunzira Baibulo
Phunzirani Baibulo kwaulere, mochita kukambirana ndi mphunzitsi wanu.
TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO