MUTU 19

Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

1, 2. (a) Kodi Yosefe ndi banja lake anayenera kuchita chiyani, nanga zimenezi zikanabweretsa mavuto otani? (b) Kodi Yosefe ankafunika kuuza mkazi wake nkhani yovuta iti?

YEREKEZERANI kuti mukuona Yosefe akukweza katundu pabulu. Kenako akusisita buluyo uku akuyang’anitsitsa mudzi wa Betelehemu. Iye akuganizira za ulendo wautali umene ayende wopita ku Iguputo. Kodi iye ndi banja lake akakwanitsa kusintha zinthu pa moyo wawo kuti akagwirizane ndi anthu akumeneko omwe ali ndi chilankhulo komanso miyambo yosiyana ndi yawo?

2 Zinali zovuta kuti Yosefe auze mkazi wake wokondedwa, Mariya, nkhani yomvetsa chisoni imene anauzidwa. Komabe iye analimba mtima n’kumuuza. Anamuuza zimene mngelo wa Mulungu anamufotokozera m’maloto zoti Mfumu Herode ikufuna kupha mwana wawo ndipo iwo akufunika kusamuka mwamsanga. (Werengani Mateyu 2:13, 14.) Mariya anamva chisoni kwambiri ndi zimenezi. Iye anadabwa kuti munthu wina angafune kupha mwana wake wosalakwayo chifukwa chiyani. Zimenezi zinali zovuta kumvetsa komabe iwo anakhulupirira Yehova ndipo anayamba kukonzekera zosamuka.

3. Fotokozani mmene Yosefe ndi banja lake anachokera ku Betelehemu. (Onaninso chithunzi.)

3 Usiku, anthu a ku Betelehemu ali m’tulo, Yosefe, Mariya ndi Yesu anatuluka m’mudzimo. Iwo analowera chakummwera ndipo pamene kumacha, Yosefe ayenera kuti anayamba kuda nkhawa kuti ziwathera bwanji. Popeza kuti iye anali kalipentala wamba, kodi akanakwanitsa bwanji kuteteza banja lake kwa Herode ndi Satana? Kodi akanakwanitsa kupezera banja lake zosowa? Nanga kodi iye akanakwanitsa udindo waukulu umene Yehova Mulungu anamupatsa wosamalira ndi kulera Yesu, yemwe anali mwana wapadera? Yosefe anakwanitsa kuchita zonsezi ndipo nkhaniyi ikusonyeza mmene iye anachitira zimenezi. Kuphunzira zimene iye anachita kuthandiza abambo komanso ena tonsefe kutsanzira chikhulupiriro chake.

Yosefe Ankateteza Banja Lake

4, 5. (a) Kodi Yosefe anakumana ndi zotani? (b) Kodi mngelo anamulimbikitsa bwanji Yosefe kulandira udindo waukulu umene anapatsidwa?

4 Miyezi yambiri izi zisanachitike, m’tauni ya Nazareti, komwe kunali kwawo kwa Yosefe, munachitika zinthu zomwe zinasintha kwambiri moyo wa Yosefeyo. Pa nthawiyi n’kuti iye ali pa chibwenzi ndi Mariya, mwana wa Heli. Yosefe ankaona kuti Mariya anali mtsikana wokhulupirika koma kenako anangomva kuti Mariyayo ali ndi pakati. Atamva zimenezi anakonza zoti amusudzule mwamseri n’cholinga choti Mariyayo asachite manyazi. * Koma asanachite zimenezi mngelo wa Mulungu analankhula naye m’maloto ndipo anamuuza kuti Mariyayo anali ndi pakati mwa mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova. Mngeloyo ananenanso kuti mwana amene adzabadweyo “adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” Komanso anauza Yosefe kuti: “Usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba.”—Mat. 1:18-21.

5 Popeza Yosefe anali munthu wolungama komanso ankamvera Mulungu, anachita zimene mngelo anamuuzazo. Anavomera udindo waukulu kwambiri wolera mwana wosakhala wake koma amene anali wofunika kwambiri kwa Mulungu. Kenako, Yosefe anatenga mkazi wake, yemwe pa nthawiyi anali ndi pakati, n’kupita ku Betelehemu kuti akalembetse m’kaundula. Iye anachita zimenezi pomvera lamulo la boma ndipo kumeneko n’kumene mwana wa Mariya anabadwira.

6-8. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Yosefe ndi banja lake akumanenso ndi mavuto ena? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Satana ndi amene anatumiza nyenyezi imene okhulupirira nyenyezi aja anaitsatira? (Onaninso mawu a m’munsi.)

6 Yosefe sanabwererenso ndi banja lake ku Nazareti. Iye anayamba kukhala ku Betelehemu, kufupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Ngakhale kuti anali wosauka, Yosefe ankayesetsa kuteteza ndi kupezera anthu a m’banja lake zosowa zawo. Kwa kanthawi, iwo ankakhala m’kanyumba kenakake. Kenako, Yesu atakulirapo, mwina atakwanitsa chaka, banja lawo linakumananso ndi mavuto ena.

7 Kunyumba kwa Yosefe ndi Mariya kunabwera amuna okhulupirira nyenyezi ochokera Kum’mawa, omwe mwina anali a ku Babulo. Iwo anatsatira nyenyezi inayake mpaka kukafika kunyumbako ndipo cholinga chawo chinali kukaona mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda. Amunawa anali aulemu kwambiri.

8 Kaya ankadziwa kapena ayi, zimene okhulupirira nyenyeziwa anachita zinamuika Yesu m’mavuto oopsa. M’malo mowatsogolera ku Betelehemu, nyenyezi ija inawalondolera kaye ku Yerusalemu. * Kumeneko amunawa anauza Mfumu Herode, yemwe anali woipa kwambiri, kuti akufufuza mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda. Herode atamva zimenezi anachita nsanje ndipo anakwiya kwambiri.

9-11. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wamphamvu kuposa Herode komanso Satana? (b) Mosiyana ndi zimene mabuku ena amene anawonjezeredwa pa mabuku a m’Baibulo amanena, kodi ulendo wa ku Iguputo unali wotani?

9 Koma mwamwayi, Yehova yemwe ndi wamphamvu kuposa Herode komanso Satana anateteza mwanayo. Kodi iye anachita zimenezi motani? Amuna aja anafikadi kwa Yesu ndipo anabweretsa mphatso zamtengo wapatali zoti banjali silinkayembekezera kuti lingakhale nazo. Iwo anabweretsa “golide, lubani ndi mule.” Amuna okhulupirira nyenyeziwa anali ndi cholinga choti pobwerera kwawo, adzerenso kwa Mfumu Herode kuti akamufotokozere kumene kuli mwanayo. Koma Yehova analowererapo. Kudzera m’maloto, anawauza kuti adutse njira ina.—Werengani Mateyu 2:1-12.

10 Okhulupirira nyenyeziwo atangochoka, mngelo wa Yehova anachenjeza Yosefe kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akukonza zoyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” (Mat. 2:13) Monga taonera koyambirira kwa nkhaniyi, Yosefe sanazengereze kutsatira chenjezolo ndipo anayamba ulendo wopita ku Iguputo. Iye anachita zimenezi chifukwa anaona kuti kuteteza mwanayo kunali kofunika kuposa chilichonse. Chifukwa chakuti okhulupirira nyenyezi aja anawapatsa mphatso zamtengo wapatali, iwo anali ndi zinthu zoti angakagwiritse ntchito kumalo kumene anasamukirako.

Pofuna kuteteza mwana wake, Yosefe anachita zinthu mosazengereza komanso mosonyeza kuganizira ena

11 Ulendowu unali wautali, wovuta komanso wotopetsa. Koma m’mabuku ena amene anawonjezeredwa pa mabuku amene ali m’Baibulo, muli nkhani zopeka komanso nthano zina zomwe zimanena mokometsera ulendo wa banjali wopita ku Iguputo. Nkhanizi zimati ulendowo unali wosapweteka chifukwa chakuti Yesu mozizwitsa anafupikitsa ulendowu, anachititsa kuti anthu achifwamba asawavulaze komanso anachititsa kuti mitengo ya kanjedza iziweramira pansi kuti mayi ake azithyola zipatso zake. *

Yosefe ankagwira ntchito mwakhama kuti azisamalira banja lake

12. Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Yosefe?

12 Makolo angaphunzire zambiri kwa Yosefe. Iye sanaganizire kwambiri za ntchito yake kapena zinthu zina mpaka kulephera kutetezera banja lake. N’zachidziwikire kuti ankaona kuti anali ndi udindo wopatsidwa ndi Yehova wosamalira banja lakelo. Masiku anonso makolo ali ndi udindo waukulu wotetezera ana awo chifukwa m’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zingathe kuwononga khalidwe la ana, mwinanso kuwaphetsa kumene. Komabe n’zosangalatsa kuti makolo ambiri amayesetsa kugwira ntchito mwakhama kuti asamalire komanso ateteze ana awo ngati mmene Yosefe anachitira.

Yosefe Ankasamalira Banja Lake

13, 14. N’chiyani chinachititsa kuti Yosefe ndi Mariya abwerere ku Nazareti?

13 Zikuoneka kuti banjali silinakhalitse ku Iguputo chifukwa pasanapite nthawi mngelo anauza Yosefe kuti Herode wafa. Choncho Yosefe anatenga banja lake n’kuyamba ulendo wobwerera kudziko lakwawo. Ulosi wina unaneneratu kuti Yehova adzaitana Mwana wake “kuti atuluke mu Iguputo.” (Mat. 2:15) Yosefe anathandizira nawo kuti ulosi umenewu ukwaniritsidwe. Koma kodi tsopano iye ndi banja lake akakhala kuti?

14 Ngakhale kuti Herode anali atafa, Yosefe anachita zinthu mosamala chifukwa anamva kuti Arikelao, amene analowa m’malo mwa Herode, nayenso anali wankhanza. Mulungu anatsogolera Yosefe ndi banja lake kuti apite chakumpoto, kutali ndi mzinda wa Yerusalemu, mpaka anafika kwawo ku Nazareti mumzinda wa Galileya. Kumeneko Yosefe ndi Mariya anaberekanso ana ena.—Werengani Mateyu 2:19-23.

15, 16. Fotokozani ntchito imene Yosefe ankagwira, komanso zipangizo zomwe ankagwiritsa ntchito.

15 Iwo ankakhala moyo wosalira zambiri komabe ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti apeze zofunika pa moyo. Baibulo limanena kuti Yosefe anali mmisiri wamatabwa. Mawu amenewa akusonyeza kuti ntchito yake inkaphatikizapo kugwetsa mitengo, kuinyamula komanso kuiumitsa kuti akamangire nyumba ndi milatho ing’onoing’ono. Mitengoyi ankaigwiritsanso ntchito popanga maboti, ngolo, mateyala, magoli ndi zipangizo zosiyanasiyana zaulimi. (Mat. 13:55) Imeneyi sinali ntchito yamasewera. Nthawi zambiri mmisiri wamatabwa ankagwirira ntchito pakhonde pa nyumba yake kapena m’kanyumba komwe ankakamanga moyandikana ndi nyumba yakeyo.

16 Yosefe anali ndi zipangizo zosiyanasiyana ndipo n’kutheka kuti zina mwa zimenezi anapatsidwa ndi bambo ake. Ankagwiritsa ntchito zipangizo monga sikweya, chingwe chowongolera, kankhwangwa, sowo, kasemasema, hamala, tchizulo, zomatira zosiyanasiyana, chobowolera komanso mwina ankakhala ndi misomali ngakhale kuti inali yokwera mtengo.

17, 18. (a) Kodi Yesu anaphunzira chiyani kuchokera kwa Yosefe? (b) N’chifukwa chiyani Yosefe ankafunikira kugwira ntchito mwakhama?

17 Yesu ali wamng’ono ayenera kuti ankakonda kuonerera bambo ake akamagwira ntchito. Ankayang’anitsitsa mwachidwi chilichonse chimene iwo ankachita. Ayenera kuti ankachita chidwi ndi mphamvu komanso luso la bambo akewo. N’kutheka kuti Yosefe ankaphunzitsa mwana wakeyo ntchito zing’onozing’ono monga kusalaza thabwa pogwiritsa ntchito chikopa chouma cha nsomba. Mwinanso anamuphunzitsa kusiyanitsa matabwa a mitengo imene ankagwiritsa ntchito, monga matabwa a mtengo wa mkuyu, wa maolivi ndi mitengo ina.

Yosefe anaphunzitsa mwana wake ntchito ya ukalipentala

18 Yesu ankadziwa kuti ngakhale kuti bambo ake anali ndi manja okhakhala chifukwa cha ntchito imene ankagwira, monga kugwetsa mitengo, kuiwaza komanso kulumikiza matabwa, iwo ankamusisita mwachikondi ndiponso ankamulimbikitsa. Ankachitanso chimodzimodzi ndi mayi ake komanso abale ake. Yosefe ndi Mariya anali ndi banja lalikulu chifukwa m’kupita kwa nthawi anabereka ana ena osachepera 6, kuwonjezera pa Yesu. (Mat. 13:55, 56) Choncho Yosefe ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti azisamalira ndiponso kudyetsa banja lakeli.

Josefe ankaona kuti kusamalira banja lake mwauzimu n’kofunika kwambiri

19. Kodi Yosefe ankasamalira bwanji banja lake mwauzimu?

19 Komabe iye ankadziwa kuti chofunika kwambiri ndi kusamalira banja lake mwauzimu. Choncho ankayesetsa kupeza nthawi yophunzitsa ana ake za Yehova Mulungu ndi malamulo Ake. Nthawi zonse Yosefe ndi Mariya ankatenga ana awo kupita kusunagoge kumene Chilamulo chinkawerengedwa ndiponso kufotokozedwa. N’kutheka kuti Yesu ankakhala ndi mafunso pa zimene wamva kusunagogeko ndipo Yosefe ankayesetsa kumuyankha mafunso akewo. Yosefe ankatenganso banja lake kupita ku zikondwerero zomwe zinkachitika ku Yerusalemu. Kuti akapezeke ku mwambo wa Pasika umene unkachitika chaka chilichonse, iye ndi banja lake ankayenera kuyenda ulendo wa makilomita 110. Ulendo wonsewu unkatenga milungu iwiri.

Nthawi zonse Yosefe ankatenga banja lake kupita nalo ku Yerusalemu

20. Kodi mitu ya mabanja achikhristu ingatsatire bwanji chitsanzo cha Yosefe?

20 Masiku ano, Akhristu omwe ndi mitu ya mabanja amachitanso chimodzimodzi. Amadzipereka kuthandiza ana awo ndipo amaona kuti kuphunzitsa anawo zinthu zauzimu n’kofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi. Iwo amayesetsa kupita ndi ana awo ku misonkhano yonse ya mpingo ngakhalenso yaikuluikulu. Mofanana ndi Yosefe, iwo amadziwa kuti palibe chabwino chimene angapatse ana awo kuposa kuwaphunzitsa zinthu zauzimu.

“Tinada Nkhawa Kwambiri”

21. Kodi Yosefe ndi abale ake ankachita zotani pa nthawi ya Pasika, nanga iye ndi mkazi wake anadziwa nthawi yanji kuti Yesu wasowa?

21 Yesu ali ndi zaka 12, Yosefe anatenganso banja lake kupita ku Yerusalemu. Inali nthawi ya chikondwerero cha Pasika ndipo mabanja akuluakulu anayendera limodzi. Ankayenda ndi nyama zonyamula katundu ndipo anadutsa m’njira zomwe zinali ndi msipu wobiriwira m’mbali mwake. Akuyandikira mzinda wa Yerusalemu, womwe unali pamalo okwera, n’kutheka kuti ambiri anayamba kuimba masalimo a nyimbo zokwerera kumzinda. (Sal. 120 mpaka 134) Pa nthawi ya chikondwererochi, mumzindawo munali anthu piringupiringu. Chikondwererocho chitatha, mabanja onse anayamba ulendo wobwerera kwawo. Mwina chifukwa chotanganidwa, Yosefe ndi Mariya ankaona ngati Yesu ali naye limodzi pa ulendowo ndipo akuyenda ndi achibale ena. Koma atayenda mtunda wa tsiku lathunthu, anazindikira kuti Yesu wasowa.—Luka 2:41-44.

22, 23. Kodi Yosefe ndi Mariya anatani atazindikira kuti mwana wawo wasowa, nanga Mariya ananena chiyani atamupeza?

22 Nthawi yomweyo anayambanso ulendo wobwerera ku Yerusalemu ndipo anam’fufuza m’malo onse amene anadutsa. Taganizirani mmene mzindawo unkaonekera pa nthawiyi, anthu onse atapita, pamene iwo ankayenda kwinaku akuitana Yesu. Kodi iye anali ali kuti? Atafufuza kwa masiku atatu, mwina Yosefe anayamba kuda nkhawa kuti walephera udindo wake umene Yehova anamupatsa. Kenako anapita kukam’fufuza m’kachisi. Iwo anafufuza paliponse mpaka anafika m’chipinda chimene munali aphunzitsi odziwa bwino Chilamulo ndipo mmenemo ndi mmene anam’peza Yesu. Apa n’zoonekeratu kuti mtima wa Yosefe ndi Mariya unakhala m’malo.—Luka 2:45, 46.

23 Yesu ankamvetsera zimene aphunzitsiwo ankanena ndiponso ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo anachita chidwi kwambiri ndi nzeru za mwanayo komanso mayankho amene ankapereka. Koma Mariya ndi Yosefe anadabwa kum’peza ali kumeneko. Baibulo limasonyeza kuti Yosefe sanalankhule kanthu. Koma mawu amene Mariya analankhula akusonyeza maganizo amene makolo onsewo anali nawo. Iye anati: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.”—Luka 2:47, 48.

24. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti kulera mwana si ntchito yamasewera?

24 Pamenepatu Mawu a Mulungu akusonyeza kuti kulera mwana si ntchito yamasewera, ngakhale mwanayo atakhala wangwiro. Zimene zikuchitika m’dzikoli masiku ano zikuchititsa kuti kulera ana kuzipangitsa makolo kukhala ndi ‘nkhawa kwambiri.’ Komabe iwo ayenera kudziwa kuti Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amazindikira mavuto amene akukumana nawo.

25, 26. Kodi Yesu anawayankha zotani makolo ake, nanga Yosefe anamva bwanji Yesu atanena mawu amenewa?

25 N’zosangalatsa kuti Yesu anali pamalo amene ankaona kuti amuthandiza kuyandikira kwambiri kwa Atate wake wakumwamba, Yehova. Iye anali wofunitsitsa kuphunzira zambiri za Atate wake. N’chifukwa chake anayankha makolo ake kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”—Luka 2:49.

26 Yosefe ayenera kuti anaganizira mawu amenewa kambirimbiri. N’kutheka kuti nthawi zina akakumbukira mawuwa ankanyadira popeza anali atayesetsa kumuphunzitsa mwanayu kuti aziona kuti Yehova Mulungu ndi Atate wake. Ngakhale kuti Yesu anali adakali mwana, ankakonda kwambiri Yehova ndipo ankamuona kuti ndi “Atate” wake. Iye anakhala ndi maganizo amenewa chifukwa cha zimene Yosefe ankam’phunzitsa.

27. Ngati ndinu bambo, kodi muli ndi udindo wotani, nanga n’chifukwa chiyani muyenera kukumbukira chitsanzo cha Yosefe?

27 Ngati ndinu bambo, kodi mumazindikira udindo umene muli nawo wothandiza ana anu kuti aziona kuti Yehova ndi Atate wachikondi komanso amateteza anthu ake? N’chimodzimodzinso ngati mumalera ana oti si anu. Muyenera kutengera chitsanzo cha Yosefe ndipo muziona kuti mwana aliyense ndi wofunika. Athandizeni kuyandikira kwa Atate wawo wakumwamba, Yehova Mulungu.Werengani  Aefeso 6:4.

Yosefe Anakhalabe Wokhulupirika

28, 29. (a) Kodi mawu a pa Luka 2:51, 52 akutiuza chiyani za Yosefe? (b) Kodi Yosefe anachita zinthu ziti zimene zinathandiza kuti mwana wake apitirize kukula mwauzimu?

28 M’Baibulo muli nkhani zochepa zokhudza Yosefe komabe nkhani zake ndi zothandiza kwambiri. Baibulo limanena kuti Yesu “anapitiriza kuwamvera” makolo ake. Komanso limanena kuti “Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.” (Werengani Luka 2:51, 52.) Mawu amenewa akutiphunzitsa zambiri zokhudza Yosefe. Choyamba, tikuphunzira kuti Yosefe anapitirizabe kutsogolera banja lake. Tikutero chifukwa Yesu, yemwe anali mwana wangwiro, ankalemekeza komanso kumvera bambo akewo.

29 Chachiwiri, tikuphunzira kuti Yesu anapitiriza kukula mu nzeru. N’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi amene anathandiza kwambiri mwana wakeyu. Pa nthawi imeneyo, panali mwambi umene Ayuda ankakonda kunena. Iwo ankanena kuti anthu omwe sagwira ntchito zolemetsa ndi amene amakhala anzeru koma anthu amene amagwira ntchito zolemetsa monga akalipentala, alimi komanso osula zitsulo “sangaphunzitse ena nzeru ndi chilungamo ndipo anthu oterewa sayenera kupezeka pamene akuluakulu akukamba mawu okuluwika.” Koma nkhani ya Yesu inasonyeza kuti mawu amenewa ndi abodza. Iye ali mnyamata, bambo ake omwe anali kalipentala wamba, anamuphunzitsa “nzeru ndi chilungamo” cha Yehova. Yosefe ayenera kuti anaphunzitsa Yesu zimenezi kambirimbiri.

30. N’chifukwa chiyani tingati Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwa mitu ya mabanja masiku ano?

30 Chinanso chimene chikusonyeza kuti Yosefe ankalera bwino Yesu ndi mmene Yesuyo ankakulira. Yesu anali mwana wosamalidwa bwino ndipo zimenezi zinachititsa kuti atakula akhale munthu wamphamvu komanso wathanzi. Yosefe anaphunzitsanso mwana wakeyu ntchito yamanja imene iye ankagwira. Yesu sankangodziwika kuti anali mwana wa mmisiri wamatabwa koma nayenso ankadziwika kuti anali “mmisiri wamatabwa.” (Maliko 6:3) Izi zikusonyeza kuti Yosefe anamuphunzitsa bwino ntchitoyi. Abambo ambiri amatsatira chitsanzo cha Yosefe ndipo amaganizira za tsogolo la ana awo. Choncho amaonetsetsa kuti akuwaphunzitsa ntchito kuti adzadziimire pa okha akadzakula.

31. (a) Kodi Yosefe ayenera kuti anamwalira liti? ( Onaninso bokosi.) (b) Kodi Yosefe anatisiyira chitsanzo chotani?

31 Kungoyambira pamene Yesu anabatizidwa ali ndi zaka 30, Baibulo silitchulanso za Yosefe. N’kutheka kuti pamene Yesu ankayamba utumiki wake n’kuti Mariya ali mayi wamasiye. (Onani bokosi lakuti  “Kodi Yosefe Anamwalira Liti?”) Komabe zimene Yosefe anachita zinasonyeza kuti iye anali bambo wabwino yemwe ankateteza ndi kusamalira banja lake. Komanso iye anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake. Zimene Yosefe anachita ndi chitsanzo chabwino kwa abambo, amuna okwatira komanso Akhristu onse.

^ ndime 4 M’masiku amenewo, chibwenzi chinkaonedwa mosasiyana kwenikweni ndi ukwati.

^ ndime 8 Imeneyi sinali nyenyezi yeniyeni ndipo sinatumizidwe ndi Mulungu. N’zodziwikiratu kuti Satana anagwiritsa ntchito chinthu chodabwitsachi pofuna kupeza njira yophera Yesu.

^ ndime 11 Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba, kapena kuti “chiyambi cha zizindikiro zake,” atabatizidwa.—Yoh. 2:1-11.