Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlozera wa Zithunzi

Mlozera wa Zithunzi

Potengera Masamba a M’bukuli

  • Pazikuto: Paulo, Tabita, Galiyo, Luka, msilikali wapakachisi ali ndi atumwi, Msaduki, Paulo akumuperekeza ku Kaisareya, kulalikira masiku ano, galimoto yokhala ndi zokuzira mawu ndiponso galamafoni.

  • Tsamba 1 Paulo atamangidwa maunyolo ali ndi Luka m’ngalawa yonyamula katundu yopita ku Roma.

  • Masamba 2, 3 M’bale J. E. Barr ndi M’bale T. Jaracz a m’Bungwe Lolamulira, akuyang’ana mapu a dziko lapansi.

  • Tsamba 11 Yesu akupereka ntchito kwa atumwi 11 okhulupirika ndi otsatira ake ena paphiri ku Galileya.

  • Tsamba 14 Yesu akukwera kumwamba. Atumwi akumuyang’anitsitsa.

  • Tsamba 20 Pa Pentekosite, ophunzira akulankhula ndi alendo m’zilankhulo za alendowo.

  • Tsamba 36 Atumwi aimirira pamaso pa Kayafa amene wakwiya kwambiri. Asilikali apakachisi ndi okonzeka kumanga atumwiwo ngati atauzidwa ndi oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda.

  • Tsamba 44 M’munsi: Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, khoti lina la ku East Germany linagamula molakwa kuti Mboni za Yehova ndi akazitape a dziko la America.​—Neue Berliner Illustrierte, October 3, 1950.

  • Tsamba 46 Sitefano akuimbidwa mlandu m’Khoti Lalikulu la Ayuda. Asaduki olemera ali chakumbuyo ndipo Afarisi otsatira miyambo ya chipembedzo chawo monyanyira ali kutsogolo.

  • Tsamba 54 Petulo waika dzanja lake pa wophunzira watsopano. Simoni wanyamula kathumba ka ndalama.

  • Tsamba 75 Petulo ndi anzake amene ankayenda naye akulowa m’nyumba ya Koneliyo. Koneliyo wapachika chinsalu paphewa lake lakumanzere chosonyeza udindo wake monga kapitawo wa asilikali a Chiroma.

  • Tsamba 83 Petulo akutulutsidwa m’ndende ndi mngelo. N’kutheka kuti ndendeyi inali mu Nsanja ya Antoniya.

  • Tsamba 84 M’munsi: Anthu achiwawa pafupi ndi ku Montreal, ku Quebec, mu 1945.​—Weekend Magazine, July 1956.

  • Tsamba 91 Paulo ndi Baranaba awaponya kunja kwa mzinda wa Antiokeya wa ku Pisidiya. Chakumbuyo, kuli ngalande zatsopano za madzi. Mwina ngalandezi zinamangidwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 100 C.E.

  • Tsamba 94 Paulo ndi Baranaba akuletsa anthu kuti asawalambire ku Lusitara. Anthu akamapereka nsembe, kawirikawiri ankavala zovala zokongola n’kumaimba nyimbo mokweza kwambiri.

  • Tsamba 100 Pamwamba: Sila ndi Yudasi akulimbikitsa mpingo ku Antiokeya wa ku Siriya. (Machitidwe 15:30-32) M’munsi: Woyang’anira dera akukamba nkhani pampingo ku Uganda.

  • Tsamba 107 Mpingo wa ku Yerusalemu wasonkhana m’nyumba ya Mkhristu wina.

  • Tsamba 124 Paulo ndi Timoteyo ali m’ngalawa ya ku Roma yonyamula katundu. Chakutsogoloko kukuoneka nsanja yokhala ndi nyale yotsogolera oyendetsa ngalawa.

  • Tsamba 139 Paulo ndi Sila ali m’bwalo lotchingidwa ndi geti, ndipo akuthawa anthu achiwawa.

  • Tsamba 155 Galiyo akukalipira anthu amene akuimba Paulo mlandu. Iye wavala zovala zogwirizana ndi udindo wake. Wavala mkanjo woyera wachifumu wokhala ndi mpendero wofiirira ndi nsapato yooneka ngati jombo.

  • Tsamba 158 Demetiriyo akulankhula ndi amisiri osula siliva m’malo awo ogwirira ntchito ku Efeso. Amisiriwa amagulitsa tiakachisi tasiliva ta Atemi kwa alendo.

  • Tsamba 171 Paulo ndi anzake akukwera ngalawa. Chakumbuyo kukuoneka chipilala chotchedwa Great Harbor, chimene chinamangidwa m’zaka za m’ma 100 B.C.E.

  • Tsamba 180 M’munsi: Mabuku a Mboni za Yehova ataletsedwa ku Canada m’ma 1940, wa Mboni wachinyamata wabweretsa mozemba mabuku ofotokoza za m’Baibulo. (Zongoyerekezera.)

  • Tsamba 182 Paulo wamvera zimene akulu amupempha. Luka ndi Timoteyo akhala pansi chakumbuyoko, ndipo akukonzekera kukagawa zopereka.

  • Tsamba 190 Mwana wa mlongo wake wa Paulo akulankhula ndi Kalaudiyo Lusiya mu Nsanja ya Antoniya kumene mwina Paulo anaikidwa m’ndende. Kachisi wa Herode akuoneka chakumbuyoko.

  • Tsamba 206 Paulo akupempherera anthu otopa apaulendo amene anakwera ngalawa yonyamula katundu.

  • Tsamba 222 Paulo ali mkaidi ndipo amumangirira kwa msilikali wachiroma. Iwo akuyang’ana mbali ina ya mzinda wa Roma.