MUTU 1

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

Mutuwu ukufotokoza mwachidule nkhani zimene zili m’buku la Machitidwe a Atumwi komanso mmene zimatikhudzira masiku ano

1-6. Fotokozani nkhani imene ikusonyeza kuti a Mboni amalalikira m’madera, m’malo ndiponso pa nthawi zosiyanasiyana.

 MTSIKANA wina wa Mboni za Yehova ku Ghana, dzina lake Rebecca, ankaona kuti kusukulu kumene ankaphunzira ndi malo abwino kulalikirako. Nthawi zonse ankanyamula mabuku ndi magazini m’chikwama chake cha kusukulu. Pa nthawi yopuma, iye ankayesetsa kulalikira kwa ana asukulu anzake ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi ana ambiri a m’kalasi mwake.

2 Ku Madagascar, chilumba chimene chili kum’mawa chakum’mwera kwa Africa, kunali apainiya enaake awiri amene nthawi zonse ankayenda pansi mtunda wa makilomita pafupifupi 25 kupita kumudzi wina wakutali ngakhale kuti dera limeneli ndi lotentha kwambiri. Kumeneko ankaphunzira Baibulo ndi anthu angapo achidwi.

3 A Mboni za Yehova a ku Paraguay limodzi ndi a Mboni enanso ongodzipereka ochokera m’mayiko 15, anakonza zoti azilalikira anthu okhala m’mbali mwa mtsinje wa Paraguay ndi wa Paraná ndipo anakonza boti lalikulu loti anthu 12 akhoza kumakhalamo. Pogwiritsa ntchito boti limeneli, olalikira za Ufumu akhama analalikira uthenga wabwino m’madera amene anali ovuta kufikako.

4 Ku Alaska, a Mboni ankapezerapo mwayi wolalikira m’nyengo yotentha chifukwa kumabwera alendo ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana. M’nyengo yotenthayi, kunkabwera alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana pa sitima, ndipo a Mboni m’derali ankaima padoko atanyamula mabuku ndi magazini ofotokoza nkhani za m’Baibulo, a m’zilankhulo zosiyanasiyana. M’dera lomweli, ofalitsa ena ankagwiritsa ntchito ndege kuti akalalikire m’madera akutali. Zimenezi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikire kwa anthu a mtundu wa Aleut, Athabascan, Tsimshian, ndi Tlingit.

5 Larry wa ku Texas ku U.S.A., anali ndi gawo lapadera limene ankalalikirako, lomwe ndi nyumba yosamalirako anthu okalamba ndi olumala komwe iyeyo ankakhala. Larry amayenda panjinga ya anthu olumala chifukwa chakuti anavulala pangozi, komabe ankalalikira mwakhama. Iye ankauza ena uthenga wa Ufumu komanso zimene Baibulo limalonjeza zoti tsiku lina mu Ufumu umenewo, adzayambiranso kuyenda.​—Yes. 35:5, 6.

6 Gulu lina la a Mboni linayenda ulendo wa masiku atatu pa boti kuchokera mumzinda wa Mandalay, popita kumsonkhano m’dera la kumpoto m’dziko la Myanmar. Chifukwa choti ankafunitsitsa kulalikira uthenga wabwino, anatenga mabuku othandiza pophunzira Baibulo ndipo ankagawira anthu amene anakwera nawo botilo. Botilo likaima patauni kapena pamudzi uliwonse, a Mboniwo ankatsika mofulumira n’kupita m’makomo mwa anthu kukagawira mabukuwo. Iwo akamabwerera, ankapeza kuti m’botimo mwakwera anthu ena ndipo amenewo ankakhala gawo lawo latsopano.

7. Kodi a Mboni amagwiritsa ntchito njira ziti akamalalikira za Ufumu wa Mulungu nanga cholinga chawo n’chiyani?

7 Mofanana ndi abale ndi alongo amene atchulidwa mu zitsanzozi, anthu amene amalambira Yehova mwakhama padziko lonse ‘akuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu.’ (Mac. 28:23) Iwo amalalikira kunyumba ndi nyumba, m’misewu, amalemba makalata komanso amalalikira pa foni. Kaya ali m’basi, kaya ali koyenda kapena pa nthawi yopuma kuntchito, iwo amayesetsa kupeza mpata wolalikira za Ufumu wa Mulungu. Pali njira zosiyanasiyana zolalikirira, koma cholinga chathu n’chimodzi, kulalikira uthenga wabwino kulikonse kumene tingapeze anthu.​—Mat. 10:11.

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani n’zodabwitsa kuti ntchito yolalikira za Ufumu ikupita patsogolo kwambiri? (b) Kodi ndi funso liti limene tiyenera kuliganizira, nanga tikufunika kuchita chiyani kuti tipeze yankho lake?

8 Kodi inuyo, amene mukuwerenga bukuli, muli m’gulu la anthu amene akulengeza mwachangu uthenga wa Ufumu m’mayiko oposa 235? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukhoza kukhala osangalala chifukwa mukuthandiza kuti uthenga wabwino ufikire anthu onse padziko lonse. Zimene zikuchitika pa ntchito imeneyi padziko lonse n’zodabwitsa kwambiri. Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amakumana ndi mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo kuletsedwa ndi boma ndiponso kuzunzidwa, iwo akupitiriza kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu kwa anthu a mitundu yonse.

9 Koma taganizirani izi, ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana komanso Satana akuyesetsa kulepheretsa ntchito yathu yolalikira, n’chifukwa chiyani ntchitoyi ikupitirirabe? Kuti tiyankhe funsoli, tikufunika kuganizira zimene zinachitika m’nthawi ya atumwi. Tikutero chifukwa chakuti a Mboni za Yehovafe masiku ano, tikupitiriza ntchito imene inayamba nthawi imeneyo.

Ntchito Yofunika Kwambiri

10. Kodi Yesu anadzipereka kwambiri pa ntchito iti, nanga ankadziwa chiyani zokhudza ntchitoyo?

10 Yesu Khristu, amene anayambitsa mpingo wa Chikhristu, anadzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndipo iye ankaona kuti imeneyi ndi ntchito yofunika kwambiri pa moyo wake. Pa nthawi ina ananena kuti: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Yesu ankadziwa kuti akuyambitsa ntchito imene payekha sakanaimaliza. Atatsala pang’ono kuphedwa, iye ananeneratu kuti uthenga wa Ufumu udzalalikidwa “kwa anthu amitundu yonse.” (Maliko 13:10) Kodi zimenezi zikanatheka bwanji ndipo ndi ndani akanagwira ntchito imeneyi?

“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.”

11. Kodi ndi ntchito yofunika kwambiri iti imene Yesu anapatsa ophunzira ake, nanga n’chiyani chikanawathandiza pogwira ntchito imeneyi?

11 Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa ophunzira ake ndipo anawapatsa ntchito yofunika kwambiri pamene anawauza kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera, ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani. Ndipo dziwani kuti ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Mawu akuti “ine ndili limodzi ndi inu” anasonyeza kuti Yesu adzathandiza ophunzirawo pa ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Iwo ankafunikiradi thandizo limenelo chifukwa chakuti Yesu anawauziratu kuti ‘mitundu yonse idzadana nawo.’ (Mat. 24:9) Panalinso chinthu china chimene chikanathandiza ophunzirawo. Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba, anawauza kuti mzimu woyera udzawapatsa mphamvu kuti akhale mboni zake ndipo adzalalikira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mac. 1:8.

12. Kodi pali mafunso ofunika ati, nanga kudziwa mayankho ake n’kofunika bwanji?

12 Tsopano ganizirani mafunso ofunika kwambiri akuti: Kodi atumwi a Yesu ndiponso ophunzira ena pa nthawiyo ankaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunikadi? Kodi amuna ndi akazi a Chikhristu ochepawa anachitiradi umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu ngakhale pamene ankazunzidwa kwambiri? Kodi iwo anathandizidwadi ndi Yehova, Yesu, angelo ndiponso mzimu woyera pogwira ntchito yawo yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu? Mafunso amenewa komanso ena ambiri akuyankhidwa m’buku la m’Baibulo la Machitidwe. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti tidziwe mayankho ake? Yesu analonjeza kuti ntchito imene anapatsa ophunzira ake idzapitirira “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Choncho Yesu anapereka ntchito imeneyi kwa Akhristu onse oona, kuphatikizapo ifeyo amene tikukhala m’nthawi ya mapeto. Choncho tili ndi chidwi ndi nkhani zimene zili m’buku la Machitidwe.

Mfundo Zachidule Zomwe Zili M’buku la Machitidwe

13, 14. (a) Kodi ndi ndani amene analemba buku la Machitidwe, nanga zimene analembazo anazidziwa bwanji? (b) Kodi m’buku la Machitidwe muli nkhani zotani?

13 Kodi ndi ndani analemba buku la Machitidwe? Bukuli silitchula amene analilemba, koma mawu oyambirira a m’bukuli amasonyeza kuti amene analemba buku la Machitidwe ndi amenenso analemba buku la Uthenga Wabwino wa Luka. (Luka 1:1-4; Mac. 1:1, 2) Choncho kuyambira kalekale, anthu amakhulupirira kuti Luka, “dokotala wokondedwa” komanso katswiri wolemba mbiri yakale, ndi amene analemba buku la Machitidwe. (Akol. 4:14) Nkhani zimene zili m’bukuli zinachitika kwa zaka pafupifupi 28, kuyambira nthawi imene Yesu anapita kumwamba mu 33 C.E., mpaka cha m’ma 61 C.E., pamene Paulo anatsala pang’ono kumasulidwa pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma. Mawu ena amene ali m’bukuli, amasonyeza kuti nthawi zambiri Luka ankakhalapo pamene zinthu zimene akufotokozazo zinkachitika. (Mac. 16:8-10; 20:5; 27:1) Luka anali munthu wodziwa kufufuza bwino nkhani, ndipo mosakayikira iye analemba buku la Machitidwe atauzidwa nkhaniyo ndi Paulo, Baranaba, Filipo ndiponso anthu ena amene atchulidwa m’bukuli.

14 Kodi m’buku la Machitidwe muli nkhani zotani? Poyambirira, mu Uthenga Wabwino umene Luka analemba, anafotokoza zimene Yesu ananena komanso zimene anachita. Koma m’buku la Machitidwe, Luka anafotokoza zimene otsatira a Yesu ananena ndiponso kuchita. Choncho limafotokoza za anthu amene anagwira ntchito yaikulu yolalikira, ngakhale kuti anthu amene sanali Akhristu ankaona ambiri mwa iwo ngati “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Mwachidule, nkhani youziridwayi imatiuza mmene mpingo wa Chikhristu unayambira ndiponso mmene unakulira. Buku la Machitidwe limasonyeza mmene Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankalalikirira komanso mtima umene anali nawo pogwira ntchitoyi. (Mac. 4:31; 5:42) Limasonyezanso mmene mzimu woyera unathandizira Akhristuwo pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino. (Mac. 8:29, 39, 40; 13:1-3; 16:6; 18:24, 25) Bukuli, mofanana ndi mabuku ena onse a m’Baibulo, limafotokoza kwambiri za nkhani yaikulu imene ili m’Baibulo yomwe ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, pogwiritsa ntchito Ufumu wake womwe wolamulira wake ndi Khristu. Likusonyezanso mmene ntchito yofalitsa uthenga wa Ufumu inapitira patsogolo ngakhale kuti Akhristuwo ankatsutsidwa kwambiri.​—Mac. 8:12; 19:8; 28:30, 31.

15. Kodi kuphunzira buku la Machitidwe kutithandiza bwanji?

15 Kunena zoona, tisangalala kwambiri ndipo chikhulupiriro chathu chilimba tikaphunzira buku la Machitidwe. Sitikukayikira kuti tikaphunzira nkhani za m’bukuli n’kuganizira khama limene Akhristu oyambirira anali nalo polalikira molimba mtima, zitikhudza mtima kwambiri. Tikhala ofunitsitsa kutsanzira chikhulupiriro cha Akhristu anzathu a m’nthawi imeneyo. Ndipo zitithandiza kukhala okonzeka kugwira ntchito imene Yesu anatipatsa kuti ‘tipite kukaphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ Buku limene mukuwerengali lapangidwa kuti likuthandizeni kumvetsa bwino buku la Machitidwe.

Buku Lotithandiza Kuphunzira Baibulo

16. Kodi cholinga chachikulu cha bukuli n’chiyani?

16 Kodi cholinga chachikulu cha bukuli n’chiyani? Cholinga chachikulu cha bukuli tingachigawe mbali zitatu: (1) Kuti tisamakayikire zoti Yehova, pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, akutsogolera ntchito yathu yolalikira za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, (2) kuti tizichita utumiki wathu mwakhama kwambiri potengera chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ndiponso (3) kuti tizilemekeza kwambiri gulu la Yehova komanso abale amene akutsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuyang’anira mipingo.

17, 18. Kodi bukuli lalembedwa m’njira yotani, ndipo lili ndi zinthu ziti zimene zingatithandize pophunzira Baibulo patokha?

17 Kodi bukuli lalembedwa m’njira yotani? Muona kuti lagawidwa m’zigawo 8, ndipo gawo lililonse likufotokoza mbali yochepa ya buku la Machitidwe. Cholinga cha mitu ya kutsogoloku si kufotokoza nkhani za m’buku la Machitidwe vesi ndi vesi, koma kuti tiphunzirepo kanthu pa nkhani zimene zili m’buku la m’Baibulo limeneli ndiponso kuti tione mmene ifeyo patokha tingagwiritsire ntchito zimene taphunzirazo. Kumayambiriro kwa mutu uliwonse kuli mawu amene akufotokoza mwachidule mfundo yaikulu ya mutuwo ndiponso kuli mavesi a m’buku la Machitidwe amene akufotokozedwa m’mutu umenewo.

18 M’bukuli mulinso zinthu zina zimene zingatithandize kwambiri pophunzira Baibulo patokha. Zithunzi zokongola zosonyeza nkhani zosangalatsa za m’buku la Machitidwe zikuthandizani kuona m’maganizo mwanu zimene zinkachitika pa nthawiyo. Mitu yambiri ili ndi mabokosi amene ali ndi mfundo zina zapadera zimene zingakuthandizeninso kwambiri. Mabokosi ena m’bukuli akufotokoza mwachidule mbiri za anthu osiyanasiyana otchulidwa m’Baibulo amene tiyenera kutsanzira chikhulupiriro chawo. Ndipo mabokosi ena akufotokoza mwatsatanetsatane za malo, zochitika, miyambo kapena anthu ena amene atchulidwa m’buku la Machitidwe.

Muzilalikira mwakhama m’gawo limene mwapatsidwa

19. N’chifukwa chiyani tikuyenera kumadzifufuza nthawi ndi nthawi, nanga tingachite bwanji zimenezi?

19 Bukuli lingatithandize kudzifufuza moona mtima pa nkhani yotumikira Yehova. Kaya mwakhala mukufalitsa uthenga wa Ufumu kwa nthawi yaitali bwanji, ndi bwino kumadzifufuza nthawi ndi nthawi kuti muone zinthu zimene mukuziika pamalo oyamba m’moyo wanu komanso mmene mukuonera utumiki wanu wa Chikhristu. (2 Akor. 13:5) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuonabe kuti utumiki wanga ndi wofunika kuuchita mwachangu? (1 Akor. 7:29-31) Kodi ndikulalikira uthenga wabwino mofunitsitsa ndiponso mwakhama? (1 Ates. 1:5, 6) Kodi ndikugwira nawo mokwanira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu?’​—Akol. 3:23.

20, 21. N’chifukwa chiyani tikufunika kugwira mwakhama ntchito yolalikira, ndipo tikhale otsimikiza ndi mtima wonse kuchita chiyani?

20 Nthawi zonse tizikumbukira kuti tapatsidwa ntchito yofunika kwambiri yolalikira ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Pamene mapeto a nthawi ino akuyandikira, ntchitoyi ikufunika kuigwira mwamsanga kwambiri. Panopa anthu ambiri akufunika kuwathandiza kuti asadzawonongedwe. Sitikudziwa kuti ndi anthu angati amaganizo abwino amene angamvetsere uthenga wathu. (Mac. 13:48) Koma ndi udindo wathu kuthandiza anthu amenewo nthawi isanathe.​—1 Tim. 4:16.

21 N’zofunika kwambiri kuti titsanzire Akhristu a m’nthawi ya atumwi amene ankalalikira mwakhama uthenga wa Ufumu. Choncho phunzirani bukuli mofatsa ndipo likuthandizani kuti muzigwira ntchito yolalikira mwakhama komanso molimba mtima. Tiyeni tikhale otsimikiza ndi mtima wonse kuti tipitirize ‘kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu.’​—Mac. 28:23.