Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

Kodi Ufumu Wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu Wa Mulungu N’chiyani?

1. Kodi tikambirana zokhudza pemphero liti lodziwika bwino?

ANTHU ambiri amadziwa pemphero lotchuka kwambiri lotchedwa Pemphero la Atate Wathu, kapena Pemphero la Ambuye. Yesu ananena pemphero limeneli pamene ankaphunzitsa ophunzira ake kupemphera. Kodi iye anapempha zinthu zotani? Nanga pemphero limeneli ndi lofunika bwanji kwa ifeyo?

2. Kodi Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera zinthu zitatu ziti?

2 Yesu ananena kuti: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.’” (Werengani Mateyu 6:9-13.) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera zinthu zitatu zimenezi?—Onani Mawu Akumapeto 20.

3. Kodi tiyenera kudziwa chiyani za Ufumu wa Mulungu?

3 Taphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Komanso takambirana chifukwa chimene Mulungu analengera anthu komanso dziko lapansi. Koma kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Ufumu wanu ubwere”? Tikambirana kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani, zimene udzachite, komanso mmene udzachititsire kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe.

KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI?

4. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?

4 Yehova anakhazikitsa boma kumwamba ndipo anasankha Yesu kuti akhale Mfumu yake. Baibulo limanena kuti boma limeneli ndi Ufumu wa Mulungu. Yesu ndi “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye.” (1 Timoteyo 6:15) Yesu ndi wolamulira wabwino kuposa wolamulira aliyense, ndipo ali ndi mphamvu zambiri kuposa zimene olamulira onse ali nazo.

5. Kodi Ufumu wa Mulungu uzidzalamulira uli kuti, nanga udzalamulira chiyani?

5 Patadutsa masiku 40 kuchokera pamene anaukitsidwa, Yesu anabwerera kumwamba. Patapita nthawi, Yehova anamusankha kukhala Mfumu ya Ufumu wake. (Machitidwe 2:33) Boma la Mulungu limeneli lili kumwamba koma lidzalamulira dziko lapansi. (Chivumbulutso 11:15) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu ndi “ufumu . . . wakumwamba.”—2 Timoteyo 4:18.

6, 7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri kuposa mafumu onse?

6 Baibulo limanena kuti Yesu ndi woposa mafumu onse a anthu chifukwa “ali ndi moyo wosakhoza kufa.” (1 Timoteyo 6:16) Anthu onse amamwalira, kuphatikizapo anthu amene amalamulira anzawo, koma Yesu sadzamwalira. Yesu adzapitiriza kutichitira zinthu zabwino mpaka kalekale.

7 Ulosi wa m’Baibulo umanena kuti Yesu adzakhala Mfumu yachilungamo komanso yachifundo. Ulosiwu umati: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziwa zinthu ndi woopa Yehova. Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova. Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka [kapena kuti, osauka].” (Yesaya 11:2-4) Kodi simungakonde kukhala ndi mfumu ngati imeneyi?

8. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu sadzalamulira yekha?

8 Mulungu anasankha anthu ena kuti akalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi mtumwi Paulo, moti anauza Timoteyo kuti: “Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso limodzi ndi iye monga mafumu.” (2 Timoteyo 2:12) Koma kodi anthu amene adzalamulire ndi Yesu alipo angati?

9. Kodi ndi anthu angati amene adzalamulire limodzi ndi Yesu? Nanga Mulungu anayamba liti kusankha anthu amenewa?

9 Monga tinaphunzirira m’Mutu 7, mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza Yesu akulamulira monga Mfumu kumwamba limodzi ndi mafumu enanso okwana 144,000. Kodi anthu 144,000 amenewa ndi ndani? Yohane anafotokoza kuti anthu amenewa analembedwa “dzina [la Yesu] ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.” Ananenanso kuti: “Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu.” (Werengani Chivumbulutso 14:1, 4.) Anthu 144,000 amenewa ndi Akhristu okhulupirika amene Mulungu anawasankha kuti akhale “mafumu olamulira dziko lapansi” limodzi ndi Yesu. Anthu amenewa akamwalira, amaukitsidwa n’kupita kumwamba. (Chivumbulutso 5:10) Kuyambira m’nthawi ya atumwi, Yehova wakhala akusankha Akhristu okhulupirika oti adzakhale m’gulu la mafumu 144,000 amenewa.

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova anasonyeza chikondi pokonza zoti Yesu ndi anthu okwana 144,000 adzalamulire anthu?

10 Yehova amatiganizira kwambiri moti anasankha anthu ena kuti adzalamulire ndi Yesu. Yesu adzakhala wolamulira wabwino chifukwa amatidziwa bwino. Iye anakhalapo munthu ndipo kuvutika amakudziwa. Paulo ananena kuti Yesu ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu’ ndipo “anayesedwa m’zonse ngati ifeyo.” (Aheberi 4:15; 5:8) Nawonso anthu 144,000 amene adzalamulire ndi Yesu anakhalapo anthu ndipo anavutikapo ndi matenda komanso mavuto ena obwera chifukwa cha uchimo. Choncho tisamakayikire kuti Yesu ndi a 144,000 adzatithandiza kwambiri chifukwa akudziwa mavuto amene tikukumana nawo.

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACHITA ZOTANI?

11. N’chifukwa chiyani Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba?

11 Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba? Tinaphunzira m’Mutu 3 kuti Satana Mdyerekezi anaukira ulamuliro wa Yehova. Satana atayamba kuukira ulamuliro wa Mulungu, Yehova analola kuti iye pamodzi ndi ziwanda akhalebe kumwamba kwa kanthawi. Choncho pa nthawi imeneyo, si onse kumwambako amene ankachita chifuniro cha Mulungu. M’Mutu 10, tidzaphunzira zambiri zokhudza Satana ndi ziwanda.

12. Kodi lemba la Chivumbulutso 12:10 likufotokoza za zinthu ziwiri zofunika kwambiri ziti?

12 Baibulo limanena kuti Yesu akadzangoikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzamenya nkhondo yolimbana ndi Satana. (Werengani Chivumbulutso 12:7-10.) Vesi 10 limafotokoza zinthu ziwiri zofunika kwambiri zomwe zinayenera kuchitika. Likufotokoza za kuyamba kulamulira kwa Yesu monga Mfumu ndiponso kuchotsedwa kwa Satana kumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi. Zimene tiphunzire zikusonyeza kuti zinthu zimenezi zinachitika kale.

13. Kodi chinachitika n’chiyani Satana atachotsedwa kumwamba?

13 Baibulo limafotokoza mmene angelo okhulupirika anasangalalira Satana ndi ziwanda zake atachotsedwa kumwamba. Timawerenga kuti: “Kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!” (Chivumbulutso 12:12) Panopa kumwamba kuli mtendere ndi mgwirizano chifukwa aliyense kumwambako amachita zimene Mulungu amafuna.

Padzikoli pakhala pakuchitika mavuto osiyanasiyana kungoyambira pamene Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba. Mavuto amenewa atha posachedwapa

14. Kodi chinachitika n’chiyani Satana ataponyedwa padziko lapansi?

14 Koma umu si mmene zinthu zilili padziko lapansi pano. Anthu akukumana ndi mavuto ambiri “chifukwa Mdyerekezi watsikira” padziko lapansi pano, komanso chifukwa “ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa anathamangitsidwa kumwamba ndipo akudziwa kuti awonongedwa posachedwapa. Iye akuyesetsa kuyambitsa mavuto osiyanasiyana padziko lonse lapansi.

15. Kodi Mulungu anali ndi maganizo otani pamene ankalenga dziko lapansili?

15 Koma Mulungu sanasinthe maganizo amene anali nawo pa nthawi imene ankalenga dziko lapansi. Iye amafunabe dzikoli litakhala lokongola kwambiri komanso kuti anthu azikhalamo mosangalala mpaka kalekale. (Salimo 37:29) Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani kuti zimenezi zitheke?

16, 17. Kodi lemba la Danieli 2:44 limatiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?

16 Ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Kodi ulosi umenewu ukutiphunzitsa chiyani?

17 Choyamba, ukutiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira “m’masiku a mafumu amenewo.” Zimenezi zikutanthauza kuti maufumu ena apadziko lapansi adzakhala alipobe pa nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira. Chachiwiri, ukutiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzalowedwa m’malo ndi boma lina. Chachitatu, ukutiuza kuti padzakhala nkhondo pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maufumu a dziko lapansi. Ufumu wa Mulungu udzapambana pa nkhondoyi ndipo ndi umene uzidzalamulira dziko lonse lapansi. Pa nthawi imeneyo anthu azidzalamuliridwa ndi boma labwino kwambiri kuposa maboma onse.

18. Kodi nkhondo yomalizira ya pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi olamulira a dziko lapansili imatchedwa chiyani?

18 Koma kodi Ufumu wa Mulungu udzayamba bwanji kulamulira dziko lonse lapansi? Nkhondo yomaliza, yotchedwa Aramagedo isanayambe, ziwanda zidzasocheretsa “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Zimenezi zikusonyeza kuti olamulira a padziko lapansili adzamenyana ndi Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 16:14, 16; onani Mawu Akumapeto 10.

19, 20. N’chifukwa chiyani tikufunikira kulamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu?

19 Kodi n’chifukwa chiyani tikufunikira kulamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu? Pali zifukwa zitatu. Choyamba, ndife ochimwa n’chifukwa chake timadwala komanso timafa. Koma Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira anthu azidzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

20 Chifukwa chachiwiri n’chakuti m’dzikoli muli anthu ambiri oipa, omwe amanama, kuchita zachinyengo ndiponso chiwerewere. Palibe zomwe tingachite kuti tichotse anthu amenewa, koma Mulungu adzawachotsa. Anthu amene amachita zoipa adzawonongedwa pa nthawi ya Aramagedo. (Werengani Salimo 37:10.) Chifukwa chachitatu n’chakuti olamulira amasiku ano alibe mphamvu, ndi ankhanza, komanso achinyengo. Olamulira amenewa safuna kuthandiza anthu kuti azimvera Mulungu. Baibulo limanena kuti “munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

21. Kodi Ufumu wa Mulungu udzapangitsa bwanji kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi?

21 Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti zimene Mulungu amafuna zizichitika padziko lonse lapansi. Mwachitsanzo, udzachotsa Satana ndi ziwanda zake. (Chivumbulutso 20:1-3) M’kupita kwa nthawi, anthu sadzadwalanso kapena kumwalira. Nsembe ya Yesu idzathandiza kuti anthu okhulupirika akhale ndi mwayi wokhala m’Paradaiso mpaka kalekale. (Chivumbulutso 22:1-3) Ufumuwu udzayeretsa dzina la Mulungu. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti boma la Mulungu likamadzalamulira dziko lapansi, anthu onse azidzalemekeza dzina la Mulungu.—Onani Mawu Akumapeto 21.

KODI YESU ANAKHALA LITI MFUMU?

22. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu sanayambe kulamulira pa nthawi imene anali padziko lapansi pano kapena atangoukitsidwa kumene?

22 Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” Zimenezi zikusonyeza kuti pa nthawi imene Yesu ankanena mawu amenewa n’kuti Ufumu wa Mulungu usanabwere. Yehova anafunika kukhazikitsa kaye Ufumuwu ndiponso kuika Yesu kuti akhale Mfumu yake. Koma kodi Yesu anakhala Mfumu atangobwerera kumwamba? Ayi, anadikira kaye. Patapita nthawi kuchokera pamene Yesu anaukitsidwa, Petulo ndi Paulo ananena kuti ulosi umene uli pa Salimo 110:1 unkanena za Yesu ndipo zomwe iwo anafotokoza zimasonyeza kuti Yesu anayenera kudikira kaye. Mu ulosiwu Yehova ananena kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.” (Machitidwe 2:32-35; Aheberi 10:12, 13) Kodi Yesu anayenera kudikira kwa nthawi yaitali bwanji asanapatsidwe Ufumuwu?

Ufumu wa Mulungu udzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chikuchitika padziko lapansi

23. (a) Kodi Yesu anayamba liti kulamulira ngati Mfumu ya boma la Mulungu? (b) Kodi tidzakambirana zotani m’nkhani yotsatira?

23 Kudakali zaka zambiri kuti chaka cha 1914 chifike, gulu la Akhristu okhulupirika linazindikira kuti chaka chimenechi chidzakhala chapadera chifukwa ulosi winawake wa m’Baibulo udzakwaniritsidwa. Zinthu zimene zakhala zikuchitika padziko lonse lapansi kuyambira mu 1914 zimasonyeza kuti ankanena zoona. M’chaka chimenechi Yesu anayamba kulamulira ngati Mfumu. (Salimo 110:2) Patangopita nthawi yochepa, Satana anaponyedwa padziko lapansi ndipo panopa “wangotsala ndi kanthawi kochepa” kuti awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12) M’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zambiri zimene zikutitsimikizira kuti Satana watsala pang’ono kuwonongedwa. Tidzakambirananso kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzaonetsetsa kuti zimene Mulungu amafuna zikuchitika padziko lapansi.—Onani Mawu Akumapeto 22.