Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 19

Musasiyane ndi Yehova

Musasiyane ndi Yehova

1, 2. Kodi tiyenera kumadalira ndani tikakumana ndi mavuto?

TAYEREKEZANI kuti mukuyenda mumsewu ndipo kunja kwayamba kusintha. Mitambo yamvula yayamba kusonkhana moti kunja kwayamba kuoneka mdima, mphenzi zayamba kung’anima, ndiponso mabingu ayamba kugunda. Kenako chimvula champhamvu chayamba kugwa. Nthawi yomweyo mukuyamba kufufuza malo oti mubisalepo. Tikukhulupirira kuti mungasangalale kwambiri ngati mutapeza malo abwino komanso ouma.

2 Panopa tikukumana ndi mavuto ambiri omwe ali ngati chimvula champhamvu. Zinthu zikungoipiraipirabe m’dzikoli. Moti mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndithawire kuti?’ Wolemba masalimo anati: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo, Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.’” (Salimo 91:2) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yehova akhoza kutithandiza pa mavuto athu panopa, ndiponso angatithandize kuti tidzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo.

3. Kodi tingatani kuti Yehova akhale malo athu obisalapo?

3 Koma kodi Yehova amatiteteza bwanji? Akhoza kutithandiza kuthana ndi mavuto alionse amene tingakhale nawo ndiponso ali ndi mphamvu zambiri kuposa munthu aliyense amene angafune kutivulaza. Ndipo ngakhale titavulazidwa, Yehova angatithandize kuti zinthu zidzakhalenso bwino m’tsogolo. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.” (Yuda 21) Tiyenera kusasiyana ndi Yehova kuti azitithandizabe pa mavuto athu. Koma kodi tingatani kuti tisasiyane ndi Yehova?

MULUNGU AMAKUKONDANI

4, 5. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda?

4 Kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kuzindikira kuti iye amatikonda kwambiri. Taganizira za zinthu zonse zimene Yehova amatichitira. Watipatsa dziko lapansi lokongola ndipo anaikamo zinyama ndi zomera zochititsa chidwi. Anatipatsanso chakudya chokoma ndiponso madzi abwino oti tizimwa. Pogwiritsa ntchito Baibulo, Yehova anatiphunzitsanso dzina lake ndiponso makhalidwe ake osangalatsa. Ndipo umboni waukulu woti amatikonda anausonyeza pamene anatumiza Mwana wake wokondedwa, Yesu, padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake n’cholinga choti atipulumutse. (Yohane 3:16) Nsembe imeneyi imatipatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wabwino kwambiri m’tsogolo.

5 Yehova anakhazikitsa Ufumu wa Mesiya, womwe ndi boma lakumwamba limene posachedwapa lidzathetse mavuto onse amene anthu akukumana nawo. Ufumuwu udzakonza dziko lonse kuti likhale paradaiso, mmene anthu azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala mpaka kalekale. (Salimo 37:29) Yehova wasonyezanso kuti amatikonda potiphunzitsa zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wabwino panopa. Amatilimbikitsanso kuti tizipemphera kwa iye ndipo nthawi zonse amakhala wokonzeka kumva mapemphero athu. Zimenezi ndi umboni wakuti Yehova amakonda munthu aliyense.

6. Kodi tiyenera kutani chifukwa cha chikondi chimene Yehova amatisonyeza?

6 Tiyenera kusonyeza kuti timayamikira chikondi chimene Yehova amatisonyeza. Yehova watichitira zinthu zambiri, koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sayamikira. Zimenezi ndi zomwe zinachitikanso pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi. Nthawi ina Yesu anachiritsa anthu 10 omwe anali ndi khate, koma mmodzi yekha ndi amene anathokoza. (Luka 17:12-17) Tiyenera kukhala ngati munthu amene anathokozayu. Nthawi zonse tiyenera kumayamikira zimene Yehova amatichitira.

7. Kodi tizimukonda bwanji Yehova?

7 Nafenso tiyenera kukonda Yehova. Yesu anauza ophunzira ake kuti ayenera kukonda Yehova ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse komanso maganizo awo onse. (Werengani Mateyu 22:37.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

8, 9. Kodi tingamusonyeze bwanji Yehova kuti timamukonda?

8 Kodi kungonena kuti timakonda Yehova n’kokwanira? Ayi. Zochita zathu ndi zimene zingasonyeze kuti timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndiponso maganizo athu onse. (Mateyu 7:16-20) Baibulo limanena momveka bwino kuti ngati timakonda Mulungu, tiyenera kumvera malamulo ake. Kodi kuchita zimenezi ndi kovuta? Ayi, chifukwa “malamulo akewo ndi osalemetsa.”—Werengani 1 Yohane 5:3.

9 Tikamamvera Yehova, timakhala osangalala. (Yesaya 48:17, 18) Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? Tiyeni tione.

PITIRIZANI KULIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova?

10 Kodi paja ndi zinthu ziti zimene munachita kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova? Kuphunzira kwanu Baibulo kwakuthandizani kuti mumudziwe bwino Yehova ndiponso kuti muyambe kukhala naye pa ubwenzi. Ubwenzi wanu ndi Yehova uli ngati moto umene umafunika kuusonkhezera kuti usazime. Moto umafuna nkhuni kuti upitirize kuyaka, kutinso ubwenzi wanu ndi Yehova ukhale wolimba mumafunika kupitiriza kuphunzira za iye.—Miyambo 2:1-5.

Ubwenzi wanu ndi Yehova uli ngati moto umene umafunika kuusonkhezera kuti usazime

11. Kodi zimene timaphunzira m’Baibulo zingakukhudzeni bwanji?

11 Mukapitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadziwa mfundo zimene zidzakufikeni pamtima. Taganizirani mmene ophunzira awiri a Yesu anamvera Yesu akuwafotokozera ulosi wa m’Baibulo. Iwo ananena kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?”—Luka 24:32.

12, 13. (a) Kodi n’chiyani chingachitike ngati munthu sakupitiriza kuphunzira za Mulungu? (b) Kodi tingatani kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhalebe wolimba?

12 Mofanana ndi mmene ophunzira aja anakhudzidwira atamvetsa mfundo za m’Malemba, inunso muyenera kuti munamva chimodzimodzi pamene munayamba kudziwa mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zinakuthandizani kuti mumudziwe Yehova komanso muyambe kumukonda. Tikukhulupirira kuti simungafune kuti chikondi chimenechi chithe.—Mateyu 24:12.

13 Mukakhala pa ubwenzi ndi Mulungu, mumayenera kuyesetsa kuusamalira kuti upitirizebe kukhala wolimba. Muyenera kupitiriza kuphunzira za iye ndiponso za Yesu komanso muziganizira za zinthu zimene mumaphunzira n’kuona mmene mungazigwiritsire ntchito pa moyo wanu. (Yohane 17:3) Mukamawerenga kapena kuphunzira Baibulo, muyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndawerengazi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova Mulungu? N’chifukwa chiyani ndiyenera kumukonda ndi mtima wanga wonse komanso ndi moyo wanga wonse?’—1 Timoteyo 4:15.

14. Kodi pemphero lingathandize bwanji kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba?

14 Mukakhala ndi mnzanu amene mumakondana naye kwambiri, mumayesetsa kuti nthawi zonse muzilankhulana. Zimenezi zimathandiza kuti ubwenzi wanuwo ukhale wolimba. N’chimodzimodzinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikamalankhulana naye m’pemphero nthawi zonse, ubwenzi wathu ndi iye umapitirizabe kukhala wolimba. (Werengani 1 Atesalonika 5:17.) Pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali imene Atate wathu wakumwamba anatipatsa. Nthawi zonse tiyenera kumamuuza zimene zili mumtima mwathu. (Salimo 62:8) Sitiyenera kumangobwereza mapemphero omweomwewo kapena kumapereka mapemphero ongoloweza, koma azikhala ochokera pansi pa mtima. Kuphunzira Baibulo ndiponso kupemphera mochokera pansi pa mtima, kungathandize kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba.

MUZIUZA ENA ZA YEHOVA

15, 16. Kodi inuyo mumaona bwanji ntchito yolalikira?

15 Pali chinthu chinanso chimene tiyenera kuchita ngati tikufuna kukhalabe pa ubwenzi ndi Yehova. Tiyenera kumauza ena zimene timakhulupirira. Ndipotu kuuza ena za Yehova ndi mwayi wamtengo wapatali. (Luka 1:74) Komanso Yesu anapereka ntchito imeneyi kwa Akhristu onse oona. Choncho tonsefe tiyenera kumagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Kodi inuyo munayamba kale kuchita zimenezi?—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

16 Mtumwi Paulo ankaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri moti anaitchula kuti ndi “chuma.” (2 Akorinto 4:7) Palibe ntchito yofunika kwambiri kuposa ntchito youza anthu za Yehova ndiponso cholinga chake. Mukamachita zimenezi mumakhala mukutumikira Yehova ndipo iye amayamikira kwambiri. (Aheberi 6:10) Kugwira ntchito yolalikira kungathandize kuti inuyo komanso anthu amene akumvetsera uthenga wanu mukhale pa ubwenzi ndi Yehova ndiponso kuti mudzapeze moyo wosatha. (Werengani 1 Akorinto 15:58.) Palibe ntchito ina yaphindu komanso yosangalatsa ngati imeneyi.

17. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwamsanga?

17 Panopa ntchito yolalikirayi ikufunika kugwiridwa mwamsanga. Tiyenera kugwira ntchito yolalikirayi “modzipereka.” (2 Timoteyo 4:2) Anthu akufunikira kumva za Ufumu wa Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” Mapeto “sadzachedwa.” (Zefaniya 1:14; Habakuku 2:3) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova awononga dziko la Satanali posachedwapa. Koma zimenezi zisanachitike, anthu ayenera kuchenjezedwa kuti asankhe ngati akufuna kuyamba kutumikira Yehova.

18. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumalambira Yehova limodzi ndi Akhristu oona?

18 Yehova amafuna kuti tizimulambira limodzi ndi Akhristu oona. Baibulo limati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheberi 10:24, 25) Tiyenera kuyesetsa kumapezeka pamisonkhano yonse. Tikakhala pamisonkhano timakhala ndi mwayi wolimbikitsana.

19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikonda abale ndi alongo athu achikhristu?

19 Mukapita kumisonkhano mumakapeza anthu amene angakhale anzanu enieni ndipo angamakulimbikitseni kulambira Yehova. Mumakumananso ndi abale ndi alongo osiyanasiyana omwe nawonso amayesetsa kutumikira Yehova. Mofanana ndi inuyo, anthu amenewa amakhala kuti nawonso ndi opanda ungwiro ndipo amalakwitsa zinthu zina. Ngati atalakwitsa zinazake, muyenera kukhala wokonzeka kuwakhululukira. (Werengani Akolose 3:13.) Nthawi zonse muziyesetsa kuona makhalidwe abwino amene abale ndi alongo anu ali nawo chifukwa kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muziwakonda komanso kuti mukhalebe pa ubwenzi ndi Yehova.

MOYO WENIWENI

20, 21. Kodi ‘moyo weniweni’ ndi uti?

20 Yehova amafuna kuti anthu onse amene ndi mabwenzi ake azikhala ndi moyo wabwino kwambiri. Baibulo limafotokoza kuti m’tsogolo muno, moyo wathu udzakhala wosiyana kwambiri ndi umene tili nawo panopo.

Yehova amafuna kuti mudzasangalale ndi ‘moyo weniweni’

21 Pa nthawi imeneyo tidzakhala ndi moyo mpaka kalekale, osati zaka 70 kapena 80 zokha. Tidzasangalala ndi “moyo wosatha” m’paradaiso wokongola ndipo tizidzakhala mwamtendere, mosangalala komanso sitizidzadwala. Umenewu ndi umene Baibulo limanena kuti ndi ‘moyo weniweni.’ Yehova akufuna kutipatsa moyo weniweniwo komabe ifeyo tiyenera kuyesetsa kuti ‘tiugwire mwamphamvu.’—1 Timoteyo 6:12, 19.

22. (a) Kodi tingatani kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo’? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti moyo umenewu sitichita wogula?

22 Kodi tingatani kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo’? Tiyenera ‘kumachita zabwino’ ndiponso kukhala “olemera pa ntchito zabwino.” (1 Timoteyo 6:18) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumatsatira zimene tikuphunzira m’Baibulo. Komatu sizikutanthauza kuti tikamachita zimenezi ndiye kuti tagula moyo weniweniwo. Moyo umenewu ndi mphatso yaulere imene Yehova amapereka kwa atumiki ake okhulupirika ndipo amaipereka chifukwa cha “kukoma mtima kwakukulu.” (Aroma 5:15) Atate wathu wakumwamba amafunitsitsa kupereka mphatso imeneyi kwa atumiki ake okhulupirika.

23. N’chifukwa chiyani muyenera kusankha zinthu mwanzeru panopa?

23 Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimalambira Mulungu m’njira imene iye amafuna?’ Ngati mutaona kuti mukufunikira kusintha zinthu zina, muyenera kusintha mwamsanga. Ngati titamayesetsa kumvera Yehova ndiponso kumudalira, iye adzakhala malo athu obisalapo. Iye adzatetezera anthu ake okhulupirika m’masiku otsiriza a dziko la Satanali. Kenako Yehova adzatipatsa mwayi wokhala ndi moyo m’Paradaiso mpaka kalekale, ngati mmene analonjezera. Ngati mutasankha zinthu mwanzeru, mukhoza kukhala ndi mwayi wodzakhala ndi moyo weniweni.