Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?

Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?

1. Kodi ndi buku liti limene lingatithandize kudziwa zam’tsogolo?

KODI nthawi inayake mutamvetsera nkhani pa wailesi kapena kuonera pa TV, munakhalapo ndi funso loti, ‘Kodi dzikoli likulowera kuti?’ Masiku ano anthu akukumana ndi mavuto ambiri komanso kukuchitika zinthu zambiri zankhanza moti anthu ena amaona kuti umenewu ndi umboni wakuti dzikoli latsala pang’ono kutha. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Kodi pali chimene chingatithandize kudziwa zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo? Inde, chilipo. Anthu sangathe kuneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo, koma Yehova Mulungu akhoza kuchita zimenezi. Iye amatiuza kudzera m’Baibulo mmene zinthu zidzakhalire pa moyo wathu komanso zimene zidzachitikire dziko lapansili.—Yesaya 46:10; Yakobo 4:14.

2, 3. Kodi ophunzira a Yesu ankafuna kudziwa chiyani, nanga iye anawayankha bwanji?

2 Baibulo likamanena zoti dziko lidzatha, silitanthauza kuti dziko lapansili ndi limene lidzathe, koma zinthu zoipa. Yesu ankaphunzitsa anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lapansili. (Luka 4:43) Ophunzira ake ankafuna kudziwa kuti Ufumuwo udzabwera liti, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Yesu sanawauze tsiku lenileni, koma anawauza zinthu zimene zidzachitike dzikoli likadzatsala pang’ono kutha. Zinthu zimene Yesu anafotokoza zikuchitika masiku ano.

3 M’mutu umenewu tikambirana zinthu zimene zikusonyeza kuti panopa dzikoli latsala pang’ono kutha. Choyamba, tikufunika kudziwa za nkhondo imene inachitika kumwamba. Zimenezi zitithandiza kumvetsa chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri.

NKHONDO IMENE INACHITIKA KUMWAMBA

4, 5. (a) Kodi n’chiyani chinachitika kumwamba Yesu atangokhala Mfumu? (b) Kodi lemba la Chivumbulutso 12:12 linaneneratu kuti chidzachitike ndi chiyani Satana akadzaponyedwa padziko lapansi?

4 M’Mutu 8 tinaphunzira kuti Yesu anakhala Mfumu kumwamba m’chaka cha 1914. (Danieli 7:13, 14) Buku la Chivumbulutso limatiuza zimene zinachitika nthawi imeneyo. Limati: “Kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [kutanthauza Yesu] ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka [Satana]. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo.” * Satana ndi ziwanda zake anagonja pa nkhondoyo ndipo anaponyedwa padziko lapansi. Taganizirani mmene angelo anasangalalira Satana atachotsedwa kumwamba. Koma kodi zimenezi zinakhudza bwanji anthu a padziko lapansi? Baibulo linaneneratu kuti kugwetsedwa kwa Satana kudzachititsa kuti anthu akumane ndi mavuto ambiri. Choncho mavutowa akuchuluka chifukwa Satana ndi wokwiya kwambiri “podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 12:7, 9, 12.

5 Panopa Satana akuyesetsa kuyambitsa mavuto ambiri padzikoli. Iye ndi wokwiya kwambiri chifukwa “wangotsala ndi kanthawi kochepa” kuti awonongedwe. Tiyeni tikambirane zimene Yesu ananena kuti zidzachitika m’masiku otsiriza.—Onani Mawu Akumapeto 24.

MASIKU OTSIRIZA

6, 7. Kodi nkhondo komanso njala zafika pati masiku ano?

6 Nkhondo. Yesu ananena kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Anthu amene amaphedwa pa nkhondo masiku ano ndi ochuluka kwambiri kuposa anthu amene anaphedwa m’mbuyomu. Lipoti la bungwe lina linanena kuti anthu amene aphedwa pa nkhondo kuyambira m’chaka cha 1914, ndi oposa 100 miliyoni. Chiwerengero cha anthu amene anafa pa nkhondo m’zaka 100, zoyambira m’chaka cha 1900 kufika chaka cha 2000, ndi chochuluka kuwirikiza katatu kuposa chiwerengero cha anthu amene anaphedwa m’zaka 1,900 za m’mbuyo mwa nthawi imeneyi. (Worldwatch Institute) Ndiye tangoganizirani chisoni chimene achibale komanso anzawo a anthu ophedwawa amakhala nacho.

7 Njala. Yesu ananena kuti: “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Ngakhale kuti masiku ano padzikoli pamakhala chakudya chochuluka, anthu ambiri sakhala ndi chakudya chokwanira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti sakhala ndi ndalama zokwanira zogulira chakudyacho komanso sakhala ndi malo okwanira olimapo. Anthu oposa 1 biliyoni a m’mayiko osauka amapeza ndalama yochepa kwambiri patsiku. Malinga ndi Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, ana mamiliyoni ambiri amafa chaka chilichonse chifukwa chosowa chakudya chokwanira chimene chingawathandize kuti azikhala ndi moyo wathanzi.

8, 9. N’chiyani chikusonyeza kuti maulosi amene Yesu ananena okhudza zivomezi ndi matenda akukwaniritsidwa?

8 Zivomezi. Yesu ananeneratu kuti: “Kudzachitika zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Masiku ano padziko lapansili pamachitika zivomezi zambiri zamphamvu chaka chilichonse. Kuchokera m’chaka cha 1900, anthu oposa 2 miliyoni anafa chifukwa cha zivomezi. Ndipo ngakhale kuti panopa akatswiri a sayansi apeza njira zabwino zowathandiza kudziwa mwamsanga zoti dera linalake kuchitika chivomezi, anthu ambiri akumaphedwabe ndi zivomezi.

9 Matenda. Yesu ananeneratu kuti “kudzakhala miliri.” Zimenezi zikusonyeza kuti kudzakhala matenda oopsa komanso osachedwa kufalikira omwe adzaphe anthu ambiri. (Luka 21:11) Ngakhale kuti panopa madokotala aphunzira njira zochizira matenda ambiri, padakali matenda ena omwe amalephera kuwachiza. Ndipotu lipoti lina linafotokoza kuti chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amamwalira chifukwa cha matenda a TB, malungo ndiponso kolera. Kuwonjezera pamenepo, madokotala atulukira matenda ena atsopano pafupifupi 30, ndipo ena mwa matendawa alibe mankhwala.

MAKHALIDWE A ANTHU A M’MASIKU OTSIRIZA

10. Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

10 Pa 2 Timoteyo 3:1-5, Baibulo limanena kuti: “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” Kenako mtumwi Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu ambiri adzakhale nawo m’masiku otsiriza. Ananena kuti anthu adzakhala . . .

  • odzikonda

  • okonda ndalama

  • osamvera makolo

  • osakhulupirika

  • osakonda achibale awo

  • osadziletsa

  • oopsa

  • okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu

  • ooneka ngati amakonda Mulungu koma amakana kumumvera

11. Malinga ndi Salimo 92:7, kodi n’chiyani chidzachitikire anthu oipa?

11 Kodi zimenezi ndi zimene anthu ambiri am’dera lanu amachita? Anthu ambiri ali ndi makhalidwe amenewa padziko lonse lapansi. Koma Mulungu athetsa zimenezi posachedwapa. Iye analonjeza kuti: “Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, amatero kuti awonongeke kwamuyaya.”—Salimo 92:7.

ZINTHU ZABWINO ZIMENE ZIKUCHITIKA M’MASIKU OTSIRIZA

12, 13. Kodi Yehova watithandiza kudziwa zinthu ziti m’masiku otsiriza ano?

12 Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza padziko lapansi padzakhala mavuto ambiri. Koma limanenanso kuti pa nthawi imeneyi padzachitika zinthu zina zabwino.

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mateyu 24:14

13 Kumvetsa mfundo za m’Baibulo. Pofotokoza zimene zidzachitike m’masiku otsiriza, mneneri Danieli ananena kuti anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” (Danieli 12:4) Mulungu adzathandiza atumiki ake kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo kuposa mmene ankazimvera poyamba. Yehova wathandiza atumiki ake kumvetsa mfundozi, makamaka kuyambira m’chaka cha 1914. Mwachitsanzo, watithandiza kudziwa kufunika kwa dzina lake, kudziwa chifukwa chake analenga dziko lapansili, kudziwa zoona zokhudza nsembe ya Yesu, zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso kudziwa kuti akufa adzauka. Taphunziranso kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto onse a anthu. Yehova watithandizanso kudziwa zimene zingatithandize kuti tizikhala osangalala ndiponso kuti tizichita zimene Mulungu amasangalala nazo. Koma kodi atumiki a Mulungu amatani akadziwa zimenezi? Pali ulosi wina umene umatithandiza kupeza yankho la funso limeneli.—Onani Mawu Akumapeto 21 ndi 25.

14. Kodi uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa m’mayiko angati, nanga ndi ndani amene akulalikira uthengawu?

14 Ntchito yolalikira ikuchitika padziko lonse. Pamene ankanena za masiku otsiriza, Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:3, 14) Panopa uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa m’mayiko oposa 230, m’ziyankhulo zoposa 700. Padziko lonse lapansi a Mboni za Yehova ochokera “fuko lililonse, [ndi] mtundu uliwonse” akuthandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani ndiponso zimene Ufumuwu udzachitire anthu. (Chivumbulutso 7:9) Ndipotu amachita zimenezi kwaulere. Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri adzadana nawo komanso kuwazunza, komabe zimenezi sizingalepheretse ntchito yolalikirayi.—Luka 21:17.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA

15. (a) Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti panopa tili m’masiku otsiriza? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu omwe amamvera Yehova ndiponso amene samumvera?

15 Kodi inuyo mumakhulupirira kuti panopa dzikoli latsala pang’ono kutha? Maulosi ambiri a m’Baibulo onena za masiku otsiriza akukwaniritsidwa masiku ano. Posachedwapa Yehova aimitsa ntchito yolalikira uthenga wabwino ndipo kenako “mapeto” afika. (Mateyu 24:14) Baibulo likamanena za mapeto limakhala likunena za nkhondo ya Aramagedo. Pa nkhondoyi Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu komanso angelo okhulupirika kuti achotse zinthu zonse zoipa komanso kuwononga anthu onse amene safuna kumvera Yehovayo komanso Yesu. (2 Atesalonika 1:6-9) Zimenezi zikadzachitika, Satana limodzi ndi ziwanda zake sadzasocheretsanso anthu. Anthu onse amene amamvera Mulungu ndiponso amafuna kulamuliridwa ndi Ufumu wake, adzasangalala ndi zinthu zonse zabwino zimene Mulungu analonjeza.—Chivumbulutso 20:1-3; 21:3-5.

16. Popeza mapeto ayandikira, kodi muyenera kuchita chiyani?

16 Dziko la Satanali litha posachedwapa. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi panopa ndiyenera kuchita chiyani?’ Yehova akufuna kuti muphunzire mokwanira mfundo za m’Baibulo. Choncho muyenera kumaona kuphunzira Baibulo kukhala kofunika kwambiri. (Yohane 17:3) A Mboni za Yehova amakhala ndi misonkhano mlungu uliwonse ndipo cholinga chake n’kuthandiza anthu kumvetsa mfundo za m’Baibulo. Mungachite bwino kumapezeka pa misonkhanoyi nthawi zonse. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Ngati zimene mwaphunzira zakupangitsani kuona kuti mukufunika kusiya khalidwe linalake, muyenera kuchita zimenezo mwamsanga. Mukayamba kusintha makhalidwe anu, Mulungu adzayamba kukuonani ngati mnzake.—Yakobo 4:8.

17. N’chifukwa chiyani kuwonongedwa kwa anthu oipa kudzakhale kodzidzimutsa kwa anthu ambiri?

17 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti kuwonongedwa kwa anthu oipa kudzayamba modzidzimutsa ngati mmene mbala imafikira usiku. (1 Atesalonika 5:2) Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri adzanyalanyaza mwadala umboni woti tikukhala m’masiku otsiriza. Iye anati: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu [kapena kuti masiku otsiriza] kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.

18. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani?

18 Yesu anatichenjeza kuti tisatanganidwe ndi “kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.” Ananena kuti mapeto a dzikoli adzafika modzidzimutsa ngati “msampha.” Ananenanso kuti tsikulo “lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.” Ndiyeno kenako anawonjezera kuti: “Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera [kapena kuti mochonderera] nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera chenjezo la Yesu limeneli? Chifukwa chakuti posachedwapa dziko la Satanali liwonongedwa. Anthu amene Yehova komanso Yesu amawaona kuti amachita zabwino ndi amene adzapulumuke ndipo adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi latsopano.—Yohane 3:16; 2 Petulo 3:13.

^ ndime 4 Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Khristu. Kuti mumve zambiri, werengani Mawu Akumapeto 23.