Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu

Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu

“Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi” amafuna kumva mapemphero athu.—Salimo 115:15

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero?

DZIKO lapansi ndi laling’ono kwambiri tikaliyerekezera ndi zinthu zambirimbiri zimene zili m’chilengedwechi. Ndipo Yehova akamayang’ana padzikoli, amaona mitundu yonse ya anthu ngati kadontho ka madzi kochokera mumtsuko. (Salimo 115:15; Yesaya 40:15) Ngakhale kuti anthufe ndife aang’ono kwambiri tikayerekezera ndi zinthu zambirimbiri zimene zili m’chilengedwechi, lemba la Salimo 145:18, 19 limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi. Ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Yehova akufunitsitsa kuti akhale nafe pa ubwenzi ndipo ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero athu ngakhale kuti iye ndi Mlengi Wamphamvuyonse. Choncho mwayi wopemphera kwa Yehova umene tili nawo ndi mphatso yamtengo wapatali imene iye wapereka kwa wina aliyense.

2 Koma kuti Yehova azimva mapemphero athu, tiyenera kumapemphera m’njira imene amafuna. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPEMPHERA KWA YEHOVA?

3. N’chifukwa chiyani muyenera kumapemphera kwa Yehova?

3 Yehova amafuna kuti muzipemphera kapena kuti kulankhulana naye. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Mawu amene ali pamavesiwa ndi ochititsa chidwi. Wolamulira wa chilengedwe chonsechi amakukondani ndipo akufuna kuti muzimuuza mavuto amene mukukumana nawo komanso mmene mukumvera.

4. Kodi kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kungalimbitse bwanji ubwenzi wanu ndi iye?

4 Pemphero limatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova. Anthu amene ndi mabwenzi akamalankhulana pafupipafupi, kuuzana mavuto amene akukumana nawo ndiponso mmene akumvera amayamba kugwirizana kwambiri. N’chimodzimodzi ndi kupemphera kwa Yehova. Kudzera m’Baibulo, Mulungu amatiuza maganizo ake komanso mmene akumvera pa nkhani inayake. Amatiuzanso zimene adzachite m’tsogolo. Kupemphera kwa Mulungu nthawi zonse kumakupatsani mwayi womufotokozera mmene mukumvera mumtima mwanu. Mukamachita zimenezi, ubwenzi wanu ndi Yehova umalimba kwambiri.—Yakobo 4:8.

KODI TIYENERA KUCHITA CHIYANI KUTI MULUNGU AZIMVA MAPEMPHERO ATHU?

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova samvetsera mapemphero onse?

5 Kodi Yehova amamvetsera mapemphero onse? Ayi. M’nthawi ya mneneri Yesaya, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mukatambasula manja anu, ndimakubisirani maso anga. Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Choncho ngati titapanda kusamala, tikhoza kuchita zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova, zomwe zingachititse kuti asamamvetsere tikamapemphera.

6. Kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji? Nanga mungasonyeze bwanji kuti muli ndi chikhulupiriro?

6 Ngati tikufuna kuti Yehova azimvetsera mapemphero athu, tiyenera kumukhulupirira. (Maliko 11:24) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Komatu kungonena kuti tili ndi chikhulupiriro sikokwanira. Tiyenera kumvera Yehova tsiku lililonse kuti tisonyeze kuti tilidi ndi chikhulupiriro.—Werengani Yakobo 2:26.

7. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa komanso aulemu tikamapemphera kwa Yehova? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti mapemphero athu ndi ochokera pansi pa mtima?

7 Tiyenera kudzichepetsa komanso kusonyeza ulemu tikamapemphera kwa Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera mwaulemu komanso modzichepetsa? Ngati tikufuna kulankhula ndi mfumu kapena pulezidenti, tingayesetse kulankhula mwaulemu. Yehova ndi Mulungu wamphamvuyonse, choncho tikamalankhula naye tiyenera kudzichepetsa komanso kumusonyeza ulemu waukulu kuposa mmene tingachitire ndi mfumu kapena pulezidenti. (Genesis 17:1; Salimo 138:6) Tiyeneranso kulankhula zinthu zimene zilidi mumtima mwathu, osati kumangobwereza mawu omweomwewo nthawi zonse.—Mateyu 6:7, 8.

8. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikapempherera zinthu zinazake?

8 Ndipo chomaliza, tikapempha Yehova kuti atithandize pa vuto linalake, tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti tipeze zimene tikufunazo. Mwachitsanzo, ngati tapempha Yehova kuti atithandize kupeza zinthu zofunikira pa moyo wathu, monga chakudya ndi zovala, sitifunika kukhala aulesi n’kumangoyembekezera kuti Yehova azitipangira chilichonse, pamene tili ndi mphamvu zoti n’kugwira ntchito. Tiyenera kugwira ntchito mwakhama komanso kuvomera ntchito iliyonse imene yapezeka yomwe tingakwanitse kugwira. (Mateyu 6:11; 2 Atesalonika 3:10) Kapena ngati tapemphera kwa Yehova kuti atithandize kuti tisiye khalidwe linalake loipa, tiyenera kupewa zinthu zimene zingapangitse kuti tichitenso khalidwelo. (Akolose 3:5) Tsopano tiyeni tikambirane mafunso okhudza pemphero amene anthu ambiri amakhala nawo.

MAFUNSO OKHUDZA PEMPHERO AMENE ANTHU AMBIRI AMAKHALA NAWO

9. Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani? Kodi lemba la Yohane 14:6 limatiphunzitsa chiyani zokhudza pemphero?

9 Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani? Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti ayenera kumapemphera kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Ananenanso kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Choncho tiyenera kupemphera kwa Yehova yekha koma kudzera mwa Yesu. Kodi kupemphera kudzera mwa Yesu kumatanthauza chiyani? Kuti Yehova ayankhe mapemphero athu, tiyenera kusonyeza kuti timayamikira udindo wapadera umene anapereka kwa Yesu. Monga tinaphunzirira kale, Yesu anabwera padziko lapansi kuti adzatipulumutse ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aroma 5:12) Yehova anasankhanso Yesu kuti akhale Mkulu wa Ansembe ndiponso Woweruza.—Yohane 5:22; Aheberi 6:20.

Mukhoza kupemphera kwa Yehova nthawi ina iliyonse

10. Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake yapadera tikamapemphera? Fotokozani.

10 Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake yapadera tikamapemphera? Ayi, Yehova satiuza kuti tizigwada, kukhala pansi kapena kuimirira tikamapemphera. Baibulo limatiuza kuti tikhoza kulankhula ndi Yehova titakhala mwanjira iliyonse imene ingasonyeze kuti tikumulemekeza. (1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25) Zimene Yehova amayang’ana kwambiri tikamapemphera si mmene takhalira kapena kuimira, koma zimene zili mumtima mwathu. Tingapemphere motulutsa mawu kapena chamumtima, pamalo alionse ndiponso nthawi iliyonse, kaya masana kapena usiku. Tikamapemphera tiyenera kukhulupirira kuti Yehova akumva zomwe tikunena, ngakhale zitakhala kuti sizikumveka kwa anthu ena.—Nehemiya 2:1-6.

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingatchule tikamapemphera kwa Yehova?

11 Kodi tiyenera kupempherera zinthu ziti? Tingapempherere zinthu zilizonse zomwe Yehova amaona kuti n’zoyenera. Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Koma kodi ndi bwino kuti tizipempherera mavuto athu komanso zinthu zina zimene ifeyo tikufuna? Inde. Tiyenera kupemphera kwa Yehova momasuka ngati mmene tingachezere ndi mnzathu wapamtima. Tikhoza kumufotokozera Yehova chilichonse chimene chili mumtima mwathu. (Salimo 62:8) Tingamupemphe kuti atipatse mzimu woyera kuti uzitithandiza kuchita zoyenera. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atipatse nzeru zotithandiza kusankha zinthu mwanzeru komanso kuti atipatse mphamvu kuti tipirire mavuto athu. (Yakobo 1:5) Tiyeneranso kupempha Yehova kuti azitikhululukira machimo athu. (Aefeso 1:3, 7) Tizipemphereranso anthu ena, kuphatikizapo achibale athu ndiponso abale ndi alongo mumpingo mwathu.—Machitidwe 12:5; Akolose 4:12.

12. Kodi nkhani zofunika kwambiri kutchula tikamapemphera ndi ziti?

12 Kodi ndi nkhani ziti zimene ndi zofunika kwambiri kumazitchula m’mapemphero athu? Nkhani zokhudza Yehova ndi chifuniro chake. Tiyenera kumuyamikira mochokera pansi pa mtima chifukwa cha zinthu zonse zimene watichitira. (1 Mbiri 29:10-13) Tikudziwa kuti zimenezi n’zofunika chifukwa Yesu ali padziko lapansi pano anaphunzitsa ophunzira ake mmene angapempherere. (Werengani Mateyu 6:9-13.) Iye ananena kuti ayenera choyamba kupemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, kapena kuti lizionedwa kukhala lopatulika. Kenako Yesu anasonyeza kuti tiyenera kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere ndiponso kuti chifuniro chake chichitike padziko lonse lapansi. Yesu atamaliza kutchula zinthu zofunikazi, m’pamene ananena kuti tingathe kupempha zimene ifeyo tikufuna. Tikayamba ndi kupempherera dzina la Yehova komanso chifuniro chake, timasonyeza kuti timaona kuti zinthu zimenezi n’zofunika kwambiri.

13. Kodi mapemphero athu ayenera kukhala aatali bwanji?

13 Kodi mapemphero athu ayenera kumakhala aatali bwanji? Baibulo silinena. Mapemphero athu akhoza kukhala aafupi kapena aatali, malinga ndi mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, tikhoza kupereka pemphero lalifupi tisanayambe kudya koma tingapemphere pemphero lalitali tikakhala patokha ndipo tikufuna kumuthokoza Yehova pa zimene watichitira kapena kumuuza mavuto athu. (1 Samueli 1:12, 15) Sitiyenera kupemphera mapemphero aatali pongofuna kudzionetsera kwa ena, ngati mmene ankachitira anthu ena m’nthawi ya Yesu. (Luka 20:46, 47) Yehova sasangalala ndi mapemphero ngati amenewo. Zimene Yehova amafuna n’zoti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima.

14. Kodi tiyenera kupemphera kangati pa tsiku, nanga kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?

14 Kodi tiyenera kupemphera kangati pa tsiku? Yehova amatiuza kuti tizipemphera kwa iye nthawi zonse. Baibulo limanena kuti: “Pempherani kosalekeza,” “limbikirani kupemphera,” ndiponso “muzipemphera mosalekeza.” (Mateyu 26:41; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Nthawi zonse Yehova amakhala wokonzeka kumvetsera mapemphero athu. Tiyenera kumamuthokoza tsiku lililonse chifukwa cha chikondi chake komanso chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatichitira. Tingamupemphenso kuti azititsogolera, kutipatsa mphamvu komanso kutilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. Ngati timayamikira mwayi wamtengo wapatali umene tili nawo wopemphera kwa Yehova, tidzayesetsa kumapemphera kwa iye nthawi zonse.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kunena kuti “ame” pamapeto pa pemphero?

15 N’chifukwa chiyani tiyenera kunena kuti “ame” pamapeto pa pemphero? Mawu akuti “ame” amatanthauza kuti “zoonadi” kapena kuti “zikhaledi choncho.” Kunena kuti “ame” kumatanthauza kutsimikizira kuti zimene zatchulidwa m’pempherolo ndi zimene zili mumtima mwathu. (Salimo 41:13) Baibulo limatiuza kuti tiyenera kunena kuti “ame,” chamumtima kapena mokweza mawu, pamapeto pa pemphero la pagulu posonyeza kuti zimene zanenedwazo tikugwirizana nazo.—1 Mbiri 16:36; 1 Akorinto 14:16.

MMENE MULUNGU AMAYANKHIRA MAPEMPHERO ATHU

16. Kodi Yehova amayankhadi mapemphero athu? Fotokozani.

16 Kodi Yehova amayankhadi mapemphero athu? Inde, amayankha. Baibulo limanena kuti iye ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Yehova amamvetsera komanso kuyankha mapemphero ochokera pansi pa mtima amene anthu ambirimbiri amapereka ndipo amachita zimenezi m’njira zosiyanasiyana.

17. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji angelo komanso atumiki ake a padziko lapansi poyankha mapemphero athu?

17 Yehova amagwiritsa ntchito angelo komanso atumiki ake a padziko lapansi poyankha mapemphero athu. (Aheberi 1:13, 14) Pali zitsanzo zambiri za anthu amene anapemphera kuti Mulungu awathandize kumvetsa mfundo za m’Baibulo ndipo pasanapite nthawi, a Mboni za Yehova anafika n’kuyamba kuphunzira nawo Baibulo. Baibulo limasonyeza kuti angelo amagwira nawo ntchito yolengeza “uthenga wabwino” padziko lonse lapansi. (Werengani Chivumbulutso 14:6.) Komanso mwina ambirife tinayamba tapemphapo Yehova kuti atithandize pa vuto linalake kapena kuti atithandize kupeza zinthu zinazake zofunika ndipo kenako tinathandizidwa ndi Mkhristu mnzathu.—Miyambo 12:25; Yakobo 2:16.

Yehova angayankhe mapemphero athu pogwiritsa ntchito Akhristu ena

18. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mzimu woyera komanso Baibulo poyankha mapemphero athu?

18 Yehova amagwiritsanso ntchito mzimu woyera poyankha mapemphero athu. Tikapempha kuti atithandize kupirira vuto linalake, iye akhoza kutipatsa mzimu wake woyera kuti utitsogolere ndiponso kutithandiza kupirira. (2 Akorinto 4:7) Nthawi zina Yehova amagwiritsanso ntchito Baibulo poyankha mapemphero athu ndiponso kutithandiza kusankha zinthu mwanzeru. Tikamawerenga Baibulo, tingapeze lemba linalake limene likhoza kutithandiza. Yehova angachititsenso m’bale kapena mlongo wina kupereka ndemanga pamisonkhano, imene ingatithandize pa vuto lathu. Angachititsenso mkulu kuti atiuze mfundo inayake ya m’Baibulo yomwe ingatithandize.—Agalatiya 6:1.

19. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingaoneke ngati Yehova sakuyankha mapemphero athu?

19 Komabe mwina nthawi zina tikhoza kumadzifunsa kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani Yehova sakuyankha pemphero langa mpaka pano?’ Kumbukirani kuti iye amadziwa nthawi komanso njira yoyenera yoyankhira mapemphero athu. Iye amadziwa zinthu zimene tikufunikira. Koma timafunikira kupitirizabe kupemphera kwa kanthawi posonyeza kuti zimene tapemphazo tikuzifunadi ndiponso kuti timamukhulupirira kwambiri Yehova. (Luka 11:5-10) Nthawi zina Yehova amayankha mapemphero athu m’njira yosiyana ndi imene timaganizira. Mwachitsanzo, tikhoza kupemphera kuti atithandize pa vuto linalake koma m’malo motichotsera vutolo akhoza kungotithandiza kuti tilipirire.—Werengani Afilipi 4:13.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kumapemphera kwa Yehova nthawi zonse?

20 Mfundo zimene takambirana m’nkhaniyi, zikusonyeza kuti pemphero ndi mwayi wamtengo wapatali kwambiri. Tisamakayikire zoti Yehova amamva mapemphero athu. (Salimo 145:18) Ndipotu tikamapemphera kwa Yehova pafupipafupi komanso mochokera pansi pa mtima, ubwenzi wathu ndi iye udzakhala wolimba kwambiri.