MUTU 13
Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali
1. Kodi ndi ndani amene anatipatsa moyo?
YEHOVA “ndi Mulungu wamoyo.” (Yeremiya 10:10) Iye ndi amene anatilenga, moti moyowu anatipatsa ndi iyeyo. Pofotokoza za Yehova, Baibulo limanena kuti: “Munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Lemba limeneli likusonyeza kuti Yehova ankafuna kuti tikhale ndi moyo, choncho anatipatsa mphatso yamtengo wapatali imeneyi.—Werengani Salimo 36:9.
2. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu?
2 Yehova amatipatsa chakudya, madzi komanso zinthu zina zofunika kuti tipitirizebe kukhala ndi moyo. (Machitidwe 17:28) Kuwonjezera pamenepo, iye amafuna kuti tizikhala ndi moyo wosangalala. (Machitidwe 14:15-17) Koma kuti zinthu zitiyendere bwino, tiyenera kumamvera malamulo a Mulungu.—Yesaya 48:17, 18.
MMENE MULUNGU AMAONERA MOYO
3. Kodi Yehova anachita chiyani Kaini atapha Abele?
3 Baibulo limatiuza kuti Yehova amaona kuti moyo wathu komanso wa anthu ena ndi wamtengo wapatali kwambiri. Mwachitsanzo, pamene mwana wa Adamu ndi Hava dzina lake Kaini anakwiyira kwambiri mng’ono wake Abele, Yehova anamuchenjeza kuti asapitirize kukwiyako. Koma Kaini sanamvere. M’malomwake anapitiriza kupsa mtima kwambiri mpaka “anam’kantha Abele m’bale wake n’kumupha.” (Genesis 4:3-8) Yehova anamulanga Kaini chifukwa chopha Abele. (Genesis 4:9-11) Zimenezi zikusonyeza kuti kupsa mtima komanso kudana ndi munthu wina n’koopsa chifukwa kungatipangitse kukhala achiwawa kapena ankhanza. Munthu amene ali ndi makhalidwe amenewa sangadzapeze moyo wosatha. (Werengani 1 Yohane 3:15.) Ngati tikufuna kusangalatsa Yehova, tiyenera kuyesetsa kumakonda anthu onse.—1 Yohane 3:11, 12.
4. Kodi lamulo lina limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli limasonyeza bwanji kuti Mulungu amaona kuti moyo ndi wofunika?
4 Patadutsa zaka zambiri zimenezi zitachitika, Yehova anasonyeza kuti amaona moyo kuti ndi wamtengo wapatali pamene anapereka Malamulo 10 kwa Mose. Limodzi mwa malamulowo linali lakuti: “Usaphe munthu.” (Deuteronomo 5:17) Ngati munthu wapha mnzake mwadala nayenso ankafunika kuphedwa.
5. Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani yochotsa mimba?
5 Nanga kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani yochotsa mimba? Iye amaona kuti moyo wa mwana, ngakhale amene asanabadwe, ndi wamtengo wapatali. Malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, ananena kuti ngati munthu wavulaza mayi wapakati mpaka kupha mwana wosabadwayo, munthuyo amayenera kuphedwa. (Werengani Ekisodo 21:22, 23; Salimo 127:3.) Zimenezi zikusonyeza kuti kuchotsa mimba n’kulakwa.—Onani Mawu Akumapeto 28.
6, 7. Kodi tingamusonyeze bwanji Yehova kuti timaona moyo kukhala wamtengo wapatali?
6 Kodi tingamusonyeze bwanji Yehova kuti timaona kuti moyo wathu komanso wa anthu ena ndi wamtengo wapatali? Tingasonyeze zimenezi ngati titamapewa chilichonse chomwe chingaike pangozi moyo wathu kapena wa anthu ena. Choncho sitingasute fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo chifukwa kuchita zimenezi kungawononge moyo wathu komanso kukhoza kutipha.
7 Mulungu ndi amene anatipatsa moyo ndi thupi, choncho tiyenera kuzigwiritsa ntchito mmene iyeyo amafunira. Tiyenera kumasamalira thupi lathu chifukwa ngati titapanda kutero Mulungu sangatione kukhala anthu oyera. (Aroma 6:19; 12:1; 2 Akorinto 7:1) Ngati sitiona moyo kukhala wamtengo wapatali, n’zosatheka kutumikira Mulungu yemwe anatipatsa moyowo. Ngakhale kuti zingakhale zovuta kusiya makhalidwe oipa amene takhala tikuchita kwa nthawi yaitali, Yehova angatithandize ngati tikuyesetsa kuti tiwasiye.
8. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisaike pangozi moyo wathu kapena wa anthu ena?
8 Taphunzira kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali ndipo Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kupewa kuchita zinthu zimene zingaike pangozi moyo wathu komanso wa anthu ena. Tingachite zimenezi poonetsetsa kuti tikuyendetsa mosamala galimoto kapena njinga. Tiyeneranso kupewa masewera oopsa kapena achiwawa. (Salimo 11:5) Tiziyesetsanso kuti pakhomo pathu pasamakhale zinthu zimene zingachititse ngozi. Yehova analamula Aisiraeli kuti: “Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.”—Deuteronomo 22:8.
9. Kodi tizichita bwanji ndi zinyama?
9 Yehova amaonanso moyo wa zinyama kuti ndi wofunika. Iye amatilola kupha nyama kuti tidye kapena tipeze zikopa zopangira zovala ndiponso ngati tikuona kuti nyamayo ikhoza kutivulaza. (Genesis 3:21; 9:3; Ekisodo 21:28) Choncho sitiyenera kuchitira nkhanza nyama kapena kuzipha pongofuna kusewera.—Miyambo 12:10.
MUZIONA KUTI MOYO NDI WOPATULIKA
10. Kodi tikudziwa bwanji kuti magazi amaimira moyo?
10 Yehova amaona kuti magazi ndi opatulika chifukwa amaimira moyo. Kaini atapha m’bale wake Abele, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.” (Genesis 4:10) Palembali magazi akuimira moyo wa Abele ndipo Yehova analanga Kaini chifukwa chopha m’bale wake. Pambuyo pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa, Yehova anasonyezanso kuti magazi amaimira moyo. Iye analoleza Nowa ndi anthu a m’banja lake kuti akhoza kumadya nyama. Anawauza kuti: “Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu. Komanso ndikukupatsani zamasamba zonse kuti zikhale chakudya chanu.” Komabe, Yehova anawaletsa kudya chinthu chimodzi. Anati: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.”—Genesis 1:29; 9:3, 4.
11. Kodi Mulungu anapereka lamulo lotani kwa Aisiraeli pa nkhani ya magazi?
11 Patapita zaka pafupifupi 800 kuchokera pamene Yehova anauza Nowa kuti asamadye magazi, Iye anauzanso anthu ake kuti: “Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithira magazi ake pansi ndi kuwafotsera ndi dothi.” Kenako anawauza kuti: “Musamadye magazi.” (Levitiko 17:13, 14) Yehova ankafuna kuti anthu ake azionabe kuti magazi ndi opatulika. Ankawalola kudya nyama koma osati magazi. Akapha nyama kuti adye, ankafunika kuthira magazi ake pansi.
12. Kodi Akhristu amawaona bwanji magazi?
12 Patapita zaka zingapo Yesu atamwalira, atumwi ndi akulu amene ankatsogolera mpingo wachikhristu ku Yerusalemu anakumana kuti akambirane malamulo amene anaperekedwa kwa Aisiraeli omwe ankagwirabe ntchito kwa Akhristu. (Werengani Machitidwe 15:28, 29; 21:25.) Yehova anawathandiza kudziwa kuti iye amaonabe kuti magazi ndi amtengo wapatali moti Akhristuwo ankafunikanso kuwaona kuti ndi opatulika. Akhristu oyambirira sankayenera kudya kapena kumwa magazi ndiponso kudya nyama imene sinakhetsedwe magazi bwinobwino. Kuchita zimenezi kunali kofanana ndi tchimo la chiwerewere kapena kulambira mafano. Kuyambira nthawi imeneyo, Akhristu onse oona amapewa kumwa kapena kudya magazi. Yehova amafunabe kuti tiziona magazi kukhala opatulika.
13. N’chifukwa chiyani Akhristu salola kupatsidwa magazi kuchipatala?
13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akhristu ayeneranso kupewa kupatsidwa magazi kuchipatala? Inde, chifukwa Yehova anatilamula kuti tisamadye kapena kumwa magazi. Kodi dokotala atakuuzani kuti musiye kumwa mowa, mukhoza Mawu Akumapeto 29.
kumangodziika dilipi ya mowawo? Ayi. Mofanana ndi zimenezi, lamulo loletsa kudya kapena kumwa magazi likutanthauza kuti sitiyenera kulola kupatsidwa magazi kuchipatala.—Onani14, 15. Kodi kulemekeza moyo ndiponso kumvera Yehova n’kofunika bwanji kwa Mkhristu?
14 Koma nanga bwanji ngati dokotala atakuuzani kuti mufa ngati simulandira magazi? Munthu aliyense ayenera kusankha ngati akufuna kumvera malamulo a Mulungu pa nkhaniyi kapena ayi. Monga Akhristu timalemekeza kwambiri mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa ndipo timayesetsa kufufuza thandizo loyenerera kuti tipitirize kukhala ndi moyo. Koma sitingalole kupatsidwa magazi.
15 Timayesetsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhale ndi moyo wathanzi koma popeza moyo ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu sitilola kupatsidwa magazi. Timaona kuti kumvera Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa kuyesa kutalikitsa moyo wathu pochita zinthu zimene amaletsa. Yesu ananena kuti: “Aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.” (Mateyu 16:25) Choncho timamvera malamulo a Yehova chifukwa timamukonda komanso timaona kuti amadziwa zimene timafunikira pa moyo wathu. Timaonanso kuti moyo ndi wamtengo wapatali ndiponso wopatulika ngati mmene iyeyo amaonera.—Aheberi 11:6.
16. N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amamvera malamulo ake?
16 Atumiki okhulupirika a Mulungu amayesetsa kumvera malamulo a Mulungu okhudza magazi. Iwo sadya kapena kumwa magazi ndiponso sangalole kupatsidwa magazi kuchipatala. * Komabe akhoza kulola njira zina zimene madokotala angagwiritse ntchito pofuna kupulumutsa moyo wawo. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu yemwe analenga moyo ndi magazi amadziwa zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu. Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Mulungu amadziwa zinthu zimene zili zabwino kwa inu?
KUGWIRITSA NTCHITO MAGAZI KOMWE YEHOVA ANAVOMEREZA
17. M’nthawi ya Aisiraeli, kodi ndi njira iti yokha yogwiritsa ntchito magazi imene Yehova ankavomereza?
17 Limodzi mwa malamulo amene anali m’Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Mose kuti auze Aisiraeli, linali lakuti: “Moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho popeza magazi ndiwo amaphimba machimo, chifukwa moyo uli m’magaziwo.” (Levitiko 17:11) Aisiraeli akachimwa ndipo akafuna kuti Yehova awakhululukire, ankatha kupereka nsembe za nyama ndipo wansembe ankathira ena mwa magazi a nyamayo paguwa la nsembe. Imeneyi ndi njira yokhayo yomwe Mulungu analola Aisiraeli kuti azigwiritsa ntchito magazi.
18. Kodi nsembe ya Yesu inachititsa kuti zikhale zotheka kudzapeza chiyani?
18 Yesu atabwera padziko lapansi, anapereka moyo wake, kapena kuti magazi ake, monga dipo n’cholinga choti Mulungu azitha kutikhululukira machimo athu. Nsembe imeneyi inalowa mmalo mwa nsembe za nyama zimene Aisiraeli ankapereka. (Mateyu 20:28; Aheberi 10:1) Moyo wa Yesu unali wamtengo wapatali kwambiri moti ataukitsidwa n’kubwerera kumwamba, Yehova anapereka mwayi kwa anthu onse wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale.—Yohane 3:16; Aheberi 9:11, 12; 1 Petulo 1:18, 19.
19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ‘oyera pa mlandu wa magazi a anthu onse’?
19 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa Ezekieli 3:17-21) Tikachita zimenezi, tidzatha kunena mawu amene mtumwi Paulo ananena akuti: “Ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro chonse cha Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Tingasonyeze kuti timalemekeza kwambiri moyo komanso magazi ngati titamauza ena za Yehova komanso zoti iye amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali.
moyo womwe ndi mphatso yamtengo wapatali. Ndipo tiyenera kuuza anthu ena kuti akhoza kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale ngati angakhulupirire Yesu. Timakonda anthu ndipo tidzachita zilizonse zomwe tingathe kuti tiwaphunzitse zimene zingawathandize kuti adzapeze moyo. (^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kuikidwa magazi, onani tsamba 77-79 m’buku lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.