Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

1, 2. Kodi anthu ambiri amakhala ndi funso liti?

NTHAWI zina zimatheka madzi kusefukira n’kuwonongeratu mudzi wonse. Kapena chigawenga kuwombera anthu m’tchalitchi n’kupha komanso kuvulaza anthu ambirimbiri. Nthawi zinanso matenda a khansa amatha kupha mayi n’kusiya ana opanda owasamalira.

2 Mavuto ngati amenewa akachitika, anthu ambiri amadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani zimenezi zachitika?” Anthu ambiri amafuna kudziwa zimene zikuchititsa kuti padziko lapansili pazichitika mavuto ambiri. Kodi nanunso munayamba mwakhalapo ndi funso limeneli?

3, 4. (a) Kodi Habakuku anafunsa mafunso ati? (b) Nanga kodi Yehova anamuyankha bwanji?

3 Nkhani zimene timawerenga m’Baibulo zimasonyeza kuti anthu ena amene ankakhulupirira kwambiri Mulungu anafunsanso mafunso ngati amenewa. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anafunsa Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?”—Habakuku 1:3.

4 Pa lemba la Habakuku 2:2, 3, timapezapo yankho la Mulungu pa mafunso amene Habakuku anafunsa ndipo anamulonjeza kuti athetsa mavutowo. Yehova amakonda kwambiri anthu. Baibulo limati: “Amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Ndipotu Mulungu amadana ndi mavuto kuposa mmene ifeyo timachitira. (Yesaya 55:8, 9) Malinga ndi zimenezi, tiyeni tikambirane funso lakuti: Kodi n’chifukwa chiyani panopa m’dzikoli mukuchitika mavuto ambiri?

ZIMENE ZACHITITSA KUTI MAVUTO ACHULUKE PADZIKOLI

5. Kodi atsogoleri ambiri achipembedzo amanena kuti tikukumana ndi mavuto chifukwa chiyani? Nanga Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

5 Atsogoleri azipembedzo nthawi zambiri amanena kuti ndi chifuniro cha Mulungu kuti anthu azikumana ndi mavuto. Ena amanena kuti chilichonse chimene chimachitika pa moyo wa munthu, kuphatikizapo tsoka lililonse, zimakhala zoti Mulungu anachita kukonzeratu ndipo sitingamvetse chifukwa chake. Pamene ena amanena kuti anthu, kuphatikizapo ana aang’ono, amamwalira n’cholinga choti apite kumwamba kukakhala ndi Mulungu. Komatu zimenezi si zoona. Yehova sachititsa zinthu zoipa. Baibulo limanena kuti: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.

6. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu ndi amene akuchititsa mavuto omwe ali padzikoli?

6 Anthu ambiri amanena kuti Mulungu ndi amene akuchititsa kuti anthu azivutika chifukwa iwo amaganiza kuti Mulunguyo ndi amene akulamulira dzikoli. Koma monga mmene tinaphunzirira m’Mutu 3, amene akulamulira dzikoli ndi Satana Mdyerekezi.

7, 8. Kodi n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi?

7 Baibulo limatiuza kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Wolamulira wa dzikoli, Satana, ndi waukali komanso wankhanza ndipo “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu ambiri padzikoli amatengera makhalidwe ake. Chimenechi ndi chifukwa chimodzi chimene chikuchititsa kuti anthu ambiri m’dzikoli azifalitsa nkhani zabodza, azidana komanso kuchitirana nkhanza.

8 Palinso zifukwa zina zimene zimachititsa kuti mavuto achuluke padzikoli. Adamu ndi Hava atachimwa, anapatsira ana awo uchimowo. Ndiye chifukwa cha uchimowo, anthu ena amachititsa kuti anzawo azikumana ndi mavuto. Nthawi zambiri anthu amafuna kuti azioneka apamwamba kuposa ena. Amachita ndewu, kumenya nkhondo ndiponso kuvutitsa anzawo. (Mlaliki 4:1; 8:9) Nthawi zina anthu amakumana ndi mavuto chifukwa cha “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka.” (Mlaliki 9:11) Anthu amatha kuchita ngozi kapena kukumana ndi mavuto ena chifukwa choti anali pamalo olakwika, pa nthawinso yolakwika.

9. Kodi n’chiyani chikutichititsa kuona kuti Yehova ali ndi chifukwa chomveka chololera kuti mavutowa azipitirira?

9 Yehova si amene amachititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto. Iye sachititsa kuti anthu azimenya nkhondo, aziphwanya malamulo, komanso kuti azivutitsa anzawo. Mulungu sachititsa ngozi monga zivomezi, mphepo zamkuntho, kapena kusefukira kwa madzi. Koma mukhoza kumadzifunsa kuti, ‘Ngati Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, n’chifukwa chiyani sachitapo chilichonse n’cholinga choti zinthu zoipazi zisamachitike?’ Tikudziwa kuti Mulungu zimamukhudza kwambiri zinthu zimene anthufe zimatichitikira, choncho ayenera kuti ali ndi chifukwa chomveka chimene akulolera kuti mavuto azipitirirabe padzikoli.—1 Yohane 4:8.

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU AMALOLA KUTI ANTHU AZIVUTIKA?

10. Kodi Satana ananena zotani?

10 Satana anapusitsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Anawauza kuti Mulungu ndi wolamulira wankhanza ndipo ankawamana zinthu zabwino kwambiri. Satana ankafuna kuti Adamu ndi Hava aziganiza kuti iyeyo akhoza kukhala wolamulira wabwino kuposa Yehova ndiponso kuti anthu sakufunikira kumatsogoleredwa ndi Mulungu.—Genesis 3:2-5; onani Mawu Akumapeto 27.

11. Kodi ndi funso liti limene tiyenera kupeza yankho lake?

11 Adamu ndi Hava sanamvere Yehova ndipo anasiya kutsatira zimene Mulungu amafuna. Iwo ankaona kuti ali ndi ufulu wosankha okha zimene akuona kuti ndi zoipa kapena zabwino. Koma funso ndi lakuti, kodi Yehova anapeza njira yotani yosonyezera kuti iyeyo ndi amene amadziwa zinthu zimene zingatithandize moti ndi amene ayenera kutitsogolera?

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu sanaphe Adamu ndi Hava nthawi yomweyo? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti Satana alamulire dzikoli komanso kuti anthu azidzilamulira okha?

12 Yehova sanawononge Adamu ndi Hava nthawi yomweyo. M’malomwake, anawalola kuti abereke ana. Kenako Yehova anapereka mwayi kwa anawo wosankha amene akufuna kuti aziwatsogolera. Zimene Yehova ankafuna zinali zoti padziko lapansili padzaze ndi anthu angwiro, ndipo zimenezi zinali zoti zidzatheka ngakhale Satana atayesetsa kusokoneza.—Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11.

13 Satana anaderera ulamuliro wa Yehova pamaso pa angelo ena ambirimbiri. (Yobu 38:7; Danieli 7:10) Chifukwa cha zimenezi, Yehova anam’patsa Satana nthawi yokwanira yoti asonyeze ngati zimene ankanenazo zinalidi zoona. Anthu anawapatsanso nthawi yoti akhazikitse maboma osiyanasiyana motsogoleredwa ndi Satana kuti adzionere okha ngati zili zotheka kumakhala bwinobwino popanda kuthandizidwa ndi Mulungu.

14. Kodi zaka zimene anthu akhala akudzilamulira okha zasonyeza chiyani?

14 Kwa zaka zambiri anthu ayesetsa kudzilamulira okha koma alephera. Zimenezi zasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Anthu amafunikira kuthandizidwa ndi Mulungu. Mneneri Yeremiya ananena zoona pamene anati: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU SAKUTHETSABE MAVUTOWA MPAKA PANO?

15, 16. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova walola kuti mavuto apitirirebe mpaka pano? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sakukonza mavuto amene Satana akuyambitsa?

15 Kodi n’chifukwa chiyani Yehova walola kuti mavuto apitirirebe mpaka pano? N’chifukwa chiyani salepheretsa zinthu zoipa kuti zisachitike? Chifukwa panafunikira nthawi yokwanira kuti aliyense atsimikizire kuti ulamuliro wa Satana walephera. Anthu ayesa njira zosiyanasiyana za ulamuliro, koma zonsezo sizinathandize. Ngakhale kuti anthu awonjezera luso lawo pa nkhani zasayansi, zinthu monga kupanda chilungamo, umphawi, uchigawenga ndiponso nkhondo zawonjezereka kuposa kale. Uwu ndi umboni wakuti anthufe sitingadzilamulire tokha bwinobwino popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu.

16 Komanso Yehova sanafune kukonza mavuto amene Satana wayambitsa, chifukwa kuchita zimenezo kukanakhala ngati akuthandiza Satana kulamulira. Mulungu sangachite zimenezi ngakhale pang’ono. Kuchita zimenezi kukanapangitsanso anthu kuyamba kuganiza kuti akutha kudzilamulira bwinobwino. Komatu ndi bodza kuganiza kuti anthu akhoza kudzilamulira okha bwinobwino, ndiye Yehova sangathandize anthu pa bodza lawolo chifukwa iye sanama.—Aheberi 6:18.

17, 18. Kodi Yehova adzakonza bwanji zinthu zimene Satana wawononga?

17 Koma kodi Yehova akhoza kukonza zinthu zimene zinawonongeka chifukwa cha kuukira ulamuliro wake kumene Satana ndi anthu anachita? Inde. Mulungu sangalephere kuchita chilichonse chomwe akufuna. Yehova akadzaona kuti zimene Satana ananena zatsimikizika kuti ndi zabodza, adzayamba kukonza dzikoli kuti likhale Paradaiso ngati mmene linalili poyamba. Anthu onse amene ali “m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Pa nthawi imeneyo anthu sadzadwalanso kapena kumwalira. Yesu adzakonza zinthu zonse zimene Satana wawononga. Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu kuti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa choleza mtima kuti tikhale ndi mwayi womudziwa ndiponso womusankha kuti akhale Wolamulira wathu. (Werengani 2 Petulo 3:9, 10.) Ndipo tikakumana ndi mavuto, iye amatithandiza kuti tipirire.—Yohane 4:23; werengani 1 Akorinto 10:13.

18 Yehova satikakamiza kuti timusankhe kukhala Wolamulira wathu. Iye anapatsa anthu ufulu wosankha okha zimene akufuna kuchita. Tiyeni tikambirane mmene tingagwiritsire ntchito mphatso yamtengo wapatali imeneyi.

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO UFULU WOSANKHA ZINTHU

19. Kodi Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali iti, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kwambiri mphatso imeneyi?

19 Mphatso yapadera imene Yehova anatipatsa yotha kusankha tokha zimene tikufuna kuchita imatipangitsa kukhala osiyana kwambiri ndi zinyama. Zinyama zimangochita zinthu mwachibadwa, pamene ife timachita kusankha zinthu zomwe tikufuna kuchita pa moyo wathu komanso timachita kusankha ngati tikufuna kuti tizichita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo. (Miyambo 30:24) Komanso sanatipange ngati mashini omwe saganiza, koma amangochita zimene anawakonzera kuti azichita. Ifeyo tili ndi ufulu wosankha makhalidwe amene tikufuna kukhala nawo, anthu amene tikufuna kuti akhale anzathu, ndiponso zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu. Yehova anachita dala zimenezi chifukwa amafuna kuti tizisangalala ndi moyo.

20, 21. Kodi ndi chinthu chanzeru chiti chimene tiyenera kuchita panopo?

20 Yehova amafuna kuti tizimukonda. (Mateyu 22:37, 38) Ali ngati bambo amene angasangalale kumva mwana wawo akuwauza kuti amawakonda. Iwo angasangalale ngati mwanayo wangonena yekha zimenezi osati chifukwa choti wachita kukakamizidwa kuti anene. Yehova anatipatsa ufulu wosankha kumutumikira kapena ayi. Satana, Adamu komanso Hava anasankha kuti asamatumikire Yehova. Ndiye kodi inuyo mudzagwiritsa ntchito bwanji mphatso yanu yotha kusankha nokha zochita?

21 Mungachite bwino kusankha kutumikira Yehova. Pali anthu ambirimbiri amene anasankha kuchita zimene Mulungu amafuna ndipo safuna kuti Satana aziwalamulira. (Miyambo 27:11) Kodi panopa muyenera kuchita chiyani kuti mudzakhale nawo m’dziko latsopano pa nthawi imene Mulungu adzachotse mavuto onse? Funso limeneli liyankhidwa m’mutu wotsatirawu.