Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

Njira Yoyenera Yolambirira Mulungu

Njira Yoyenera Yolambirira Mulungu

1. Kodi ndi ndani angatiuze njira yoyenera yolambirira Mulungu?

MATCHALITCHI ambiri amanena kuti amaphunzitsa anthu zoona zokhudza Mulungu. Komatu zimenezi si zoona, chifukwa iwo amaphunzitsa zinthu zosiyana kwambiri pa nkhani yoti Mulungu ndi ndani komanso pa nkhani ya mmene anthu ayenera kumulambirira. Koma kodi tingadziwe bwanji njira yoyenera yolambirira Mulungu? Yehova yekha ndi amene angatiuze mmene tiyenera kumulambirira.

2. Kodi tingadziwe bwanji njira yoyenera yolambirira Mulungu?

2 Yehova anatipatsa Baibulo n’cholinga choti litithandize kudziwa njira yoyenera yomulambirira. Choncho, muyenera kuphunzira Baibulo ndipo Yehova adzakuthandizani kupindula ndi zimene mukuphunzirazo chifukwa amakukondani kwambiri.—Yesaya 48:17.

3. Kodi Mulungu amafuna kuti tizichita chiyani?

3 Anthu ena amanena kuti Mulungu amavomereza zipembedzo zonse koma zimenezi n’zosiyana ndi zimene Yesu ananena. Iye anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga.” Choncho tiyenera kudziwa zimene Mulungu amafuna n’kumazichita. Nkhani imeneyi sitiyenera kuiona mopepuka chifukwa Yesu anasonyeza kuti “anthu osamvera malamulo” a Mulungu amakhala akupalamula mlandu.—Mateyu 7:21-23.

4. Kodi Yesu ananena chiyani pa nkhani yochita zimene Mulungu amafuna?

4 Yesu anatichenjezeratu kuti tidzakumana ndi mavuto tikamayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Iye anati: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Msewu wopanikiza, womwe ukuimira njira yoyenera yolambirira Mulungu, ndi umene ungathandize munthu kudzapeza moyo wosatha. Msewu waukulu, womwe ukuimira njira yosavomerezeka yolambirira Mulungu, ukupita ku imfa. Komatu Yehova safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. Choncho amapereka mwayi kwa aliyense woti amudziwe.—2 Petulo 3:9.

NJIRA YOYENERA YOLAMBIRIRA MULUNGU

5. Kodi mungadziwe bwanji anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera?

5 Yesu ananena kuti tikhoza kuwadziwa anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera. Tingawadziwe ngati titaona zimene amachita komanso zimene amakhulupirira. Iye anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” Kenako ananenanso kuti: “Mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino.” (Mateyu 7:16, 17) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera salakwitsa chilichonse. Komabe nthawi zonse atumiki a Mulungu amayesetsa kuchita zinthu zoyenera. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zimene zingatithandize kuzindikira anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera amatsatira mfundo za m’Baibulo? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

6 Zimene amachita polambira zimachokera m’Baibulo. Baibulo limati: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Mtumwi Paulo analembera Akhristu kuti: “Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Choncho anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera amatsatira mfundo za M’mawu a Mulungu, Baibulo. Iwo sayendera maganizo a anthu, miyambo kapena zinthu zina zilizonse.

7 Zonse zimene Yesu ankaphunzitsa zinkachokera m’Mawu a Mulungu. (Werengani Yohane 17:17.) Nthawi zambiri iye ankagwira mawu a m’Malemba. (Mateyu 4:4, 7, 10) Atumiki oona a Mulungu amatengera chitsanzo cha Yesu ndipo zonse zimene amaphunzitsa zimachokera m’Baibulo.

8. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani pa nkhani ya kulambira Yehova?

8 Amalambira Yehova yekha. Lemba la Salimo 83:18 limati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Yesu ankafuna kuti anthu amudziwe bwino Mulungu woona n’chifukwa chake ankawaphunzitsa za dzina la Mulunguyo. (Werengani Yohane 17:6.) Iye anati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Choncho atumiki a Mulungu amatsatira chitsanzo cha Yesu. Iwo amalambira Yehova yekha, amagwiritsa ntchito dzina lake komanso amaphunzitsa ena za dzina la Mulungu ndiponso zimene adzachitire anthu.

9, 10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu ena?

9 Amakonda anthu ndi chikondi chenicheni. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azikondana, ndipo ifenso timachita chimodzimodzi. (Werengani Yohane 13:35.) Timakondana posatengera kuti ndife osiyana kochokera, chikhalidwe komanso kuti ndife olemera kapena osauka. Chikondi chimatithandiza kuti tizionana ngati anthu a banja limodzi. (Akolose 3:14) Sitipita kukamenya nawo nkhondo komanso sitipha anthu ena. Baibulo limanena kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake.” Limanenanso kuti: “Tizikondana, osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha m’bale wake.”—1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21.

10 Timagwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso chuma chathu pothandizira abale athu komanso kulimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Timayesetsa ‘kuchitira onse zabwino.’—Agalatiya 6:10.

11. N’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Yesu ndi njira ya Mulungu yopulumutsira anthu?

11 Amakhulupirira kuti Yesu ndi njira ya Mulungu yopulumutsira anthu. Baibulo limati: “Chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) M’Mutu 5 tinaphunzira kuti Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake dipo lowombolera anthu. (Mateyu 20:28) Ndiponso Yehova anasankha Yesu kuti adzalamulire dziko lapansi. N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti tiyenera kumamvera Yesu kuti tidzapeze moyo wosatha.—Werengani Yohane 3:36.

12. N’chifukwa chiyani sitilowerera m’nkhani zandale?

12 Salowerera nkhani zandale. Yesu sankachita nawo zandale. Nthawi ina akuimbidwa mlandu, anauza wolamulira wina wachiroma, dzina lake Pilato kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Werengani Yohane 18:36.) Mofanana ndi Yesu, ndife okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu ndipo chifukwa cha zimenezi, sitilowerera m’nkhani zandale. Komabe Baibulo limatilamula kuti tizimvera “olamulira akuluakulu,” omwe ndi maboma a anthu. (Aroma 13:1) Timamvera malamulo am’dziko limene timakhala. Koma ngati malamulowo akusemphana ndi malamulo a Mulungu, timatsanzira atumwi, omwe ananena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:29; Maliko 12:17.

13. Kodi timalalikira zotani zokhudza Ufumu wa Mulungu?

13 Amalalikira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse padzikoli. Yesu ananena kuti “uthenga wabwino . . . wa ufumu” uyenera kulalikidwa padziko lonse lapansi. (Werengani Mateyu 24:14.) Palibe boma lililonse la anthu limene lingakwanitse kutichitira zinthu zimene Ufumu wa Mulungu udzatichitire. (Salimo 146:3) Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera Ufumu wa Mulungu pamene ananena kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Baibulo limatiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzawononga maboma onse a anthu ndipo “udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.

14. Kodi inuyo mukuona kuti ndi ndani amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera?

14 Pambuyo pokambirana mfundo zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi anthu achipembedzo chiti amene amaphunzitsa zinthu zochokera m’Baibulo zokhazokha? Ndi anthu ati amene amauza ena za dzina la Mulungu? Kodi ndi ndani amene amasonyezana chikondi chenicheni ndiponso amakhulupirira kuti Mulungu anatumiza Yesu kuti adzatipulumutse? Kodi ndi ndani amene salowerera nawo m’nkhani zandale? Nanga ndi ndani amene amalalikira zoti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto a anthu?’ A Mboni za Yehova okha ndi amene amachita zimenezi.—Yesaya 43:10-12.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu?

15 Kungokhulupirira kuti kuli Mulungu sikokwanira chifukwa ngakhale ziwandanso zimakhulupirira kuti kuli Mulungu koma sizimumvera. (Yakobo 2:19) Ngati tikufuna kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu, tiyenera kumamumvera.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kutuluka m’chipembedzo chonyenga?

16 Kuti Mulungu azivomereza kulambira kwathu, tiyeneranso kutuluka m’chipembedzo chonyenga. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Chokani pakati pake! Khalani oyera.” (Yesaya 52:11; 2 Akorinto 6:17) Malinga ndi zimenezi, tiyenera kupewa chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chonyenga.

17, 18. Kodi “Babulo Wamkulu” n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anthu ayenera kutulukamo mwamsanga?

17 Chipembedzo chonyenga ndi chipembedzo chilichonse chimene chimaphunzitsa zinthu zosiyana ndi zimene zili m’Mawu a Mulungu. Baibulo limatchula zipembedzo zonse zonyenga kuti ndi “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5) Kodi anazipatsa dzina limeneli chifukwa chiyani? Pambuyo pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa, anthu a mumzinda wa Babulo anayamba kuphunzitsa zinthu zambiri zabodza. Zinthu zimene ankaphunzitsazo zinayamba kufalikira padziko lonse lapansi. Mwachitsanzo, anthu a ku Babulo ankalambira milungu imene inkakhala itatuitatu. Masiku anonso, matchalitchi ambiri amaphunzitsa zoti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Komatu Baibulo limaphunzitsa kuti pali Mulungu woona mmodzi yekha, Yehova, ndipo Yesu ndi Mwana wake. (Yohane 17:3) Anthu a ku Babulo ankakhulupiriranso kuti munthu akafa pali chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo ndipo chimene chimatsalacho chimatha kukazunzika kumoto. Komatu zimenezi si zoona.—Onani Mawu Akumapeto 14, 17, ndi 18.

18 Mulungu ananeneratu kuti zipembedzo zonse zonyenga ziwonongedwa posachedwapa. (Chivumbulutso 18:8) N’chifukwa chake muyenera kutuluka mwamsanga m’chipembedzo chonyenga. Yehova Mulungu akufuna kuti mutuluke m’chipembedzochi nthawi idakalipo.—Chivumbulutso 18:4.

Mukamatumikira Yehova limodzi ndi anthu ake mudzalowa m’banja lapadziko lonse

19. Kodi Yehova adzakusamalirani bwanji mukasankha kumutumikira?

19 Pamene mwasankha kutuluka m’chipembedzo chonyenga n’kuyamba kutumikira Yehova, anzanu ena komanso achibale anu sangasangalale nazo ndipo akhoza kuyamba kukuvutitsani. Koma Yehova sadzakusiyani. Mudzalowa m’banja lapadziko lonse lomwe lili ndi anthu mamiliyoni ambirimbiri amene amakondana. Mudzakhalanso ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. (Maliko 10:28-30) N’kutheka kuti m’tsogolo ena mwa anzanu komanso abale anu amene amakuvutitsani chifukwa choti munasankha kutumikira Yehova angadzayambe kuphunzira Baibulo.

20. Kodi kulambira Mulungu m’njira yoyenera n’kofunika bwanji?

20 Posachedwapa, Mulungu awononga anthu onse oipa ndipo Ufumu wake udzayamba kulamulira dziko lonse lapansi. (2 Petulo 3:9, 13) Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. Pa nthawi imeneyo anthu onse azidzalambira Yehova m’njira yoyenera ngati mmene mwiniwake amafunira. Choncho panopa ndi nthawi yabwino yoti muyambe kutumikira Mulungu m’njira yoyenera.