Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

Kodi Mulungu Analenga Anthu Chifukwa Chiyani?

Kodi Mulungu Analenga Anthu Chifukwa Chiyani?

1. Kodi cholinga cha Mulungu polenga anthu chinali chotani?

PAMENE Mulungu ankalenga anthu anali ndi cholinga chabwino kwambiri. Iye analenga Adamu ndi Hava kuti azikhala m’munda wokongola kwambiri. Ankafuna kuti anthu amenewa abereke ana, akonze dziko lonse kuti likhale paradaiso ndiponso kuti azisamalira nyama.—Genesis 1:28; 2:8, 9, 15; onani Mawu Akumapeto 6.

2. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti zimene Mulungu ankafuna polenga anthu zidzachitikadi? (b) Kodi Baibulo limati ndi anthu otani omwe adzakhale ndi moyo wosatha?

2 Kodi inuyo mumaona kuti zimene Mulungu ankafunazi, zoti anthu azikhala m’paradaiso, zidzachitikadi? Yehova ananena kuti: “Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.” (Yesaya 46:9-11; 55:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti chilichonse chimene Mulungu ankafuna chidzachitikadi, ndipo palibe chimene chingamulepheretse. Yehova ananena kuti anali ndi cholinga pamene ankalenga dziko lapansili. Iye “sanalilenge popanda cholinga.” (Yesaya 45:18) Mulungu amafuna kuti anthu achuluke n’kumakhala padziko lonse lapansi. Koma kodi Mulungu amafuna kuti padzikoli pazikhala anthu otani? Nanga anthuwo azikhalapo kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limanena kuti: “Olungama [kapena kuti omvera] adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

3. Kodi anthu amakhala ndi funso lotani chifukwa choona kuti anthu amadwala komanso amamwalira?

3 Komatu masiku ano anthu amadwala ndiponso amamwalira. M’mayiko ambiri anthu amamenyana komanso kuphana. Izi sizimene Mulungu ankafuna kuti zizichitika. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? Baibulo ndi limene lingatiuze zimene zinachitika.

MDANI WA MULUNGU

4, 5. (a) Kodi ndi ndani ankalankhula ndi Hava m’munda wa Edeni pogwiritsa ntchito njoka? (b) Kodi n’chiyani chingachititse kuti munthu yemwe anali wabwinobwino asinthe n’kukhala wakuba?

4 Baibulo limanena kuti pali mdani wa Mulungu yemwe dzina lake ndi “Mdyerekezi ndi Satana.” Satana anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava m’munda wa Edeni. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:1) Satana anapangitsa kuti njokayo izioneka ngati ndi imene ikulankhula.—Onani Mawu Akumapeto 7.

5 Kodi Mulungu ndi amene analenga Satana Mdyerekezi? Ayi. Mngelo wina amene anali kumwamba pamene Mulungu ankalenga dziko lapansi kuti Adamu ndi Hava azikhalamo anasintha n’kukhala Mdyerekezi. (Yobu 38:4, 7) Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Zimene zinachitika n’zofanana ndi zimene zimachitika kuti munthu yemwe anali wabwinobwino asinthe n’kukhala wakuba. Munthuyo sabadwa ali wakuba. Koma amayamba kufunitsitsa, kapena kuti kulakalaka, chinthu chinachake chomwe si chake. Akapitiriza kuganizira za chinthucho, maganizo ake olakwikawo amawonjezeka. Kenako akangopeza mwayi, amaba chinthucho. Pamenepa tingati munthuyo wadzipangitsa yekha kukhala wakuba.—Werengani Yakobo 1:13-15; onani see Mawu Akumapeto 8.

6. Kodi chinachitika n’chiyani kuti mngelo wina akhale mdani wa Mulungu?

6 Izi ndi zimenenso mngeloyu anachita. Yehova atalenga Adamu ndi Hava, anawauza kuti abereke ana ndipo ‘adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:27, 28) Mngelo ameneyu ayenera ankaganiza kuti, ‘Anthu onsewotu akhoza kumalambira ineyo osati Yehova.’ Maganizo amenewa anakula mumtima mwake moti anayamba kusirira ulamuliro wa Yehova. Mngeloyu ankafuna kuti anthu azilambira iyeyo. Iye anauza Hava zinthu zabodza zimene zinachititsa kuti Hava asamvere Mulungu. (Werengani Genesis 3:1-5.) Zimene mngeloyu anachitazi zinapangitsa kuti akhale Satana Mdyerekezi ndiponso mdani wa Mulungu.

7. (a) Kodi Adamu ndi Hava anafa chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani ifenso timakalamba ndi kufa?

7 Adamu ndi Hava sanamvere zimene Mulungu anawauza ndipo anadya chipatso chimene anawaletsa. (Genesis 2:17; 3:6) Iwo anachimwira Yehova ndipo patapita nthawi anamwalira monga mmene Mulungu anawauzira kuti ndi zimene zidzachitike ngati sadzamvera. (Genesis 3:17-19) Ana a Adamu ndi Hava amamwalira chifukwa nawonso ndi ochimwa. (Werengani Aroma 5:12.) Kuti timvetse mmene ana a Adamu ndi Hava anakhalira ochimwa, tiyeni tione chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mukuumba njerwa pogwiritsa ntchito chikombole chopindika. Ndiye kuti njerwa iliyonse izituluka yopindika. Pamene Adamu sanamvere Mulungu, anakhala wochimwa. Popeza ifeyo ndi ana a Adamu, tonse ndife ochimwa. Zimenezi zimachititsa kuti tizikalamba komanso kumwalira.—Aroma 3:23; onani Mawu Akumapeto 9.

8, 9. (a) Kodi Satana ankafuna kuti Adamu ndi Hava aziona kuti Mulungu ndi wotani? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sanaphe oukirawo nthawi yomweyo?

8 Pamene Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava asamvere Mulungu, anayambitsa kagulu koukira ulamuliro wa Mulungu. Ankafuna kuti Adamu ndi Hava aziona ngati Yehova ndi wabodza, salamulira bwino ndipo sawafunira zabwino. Ankaonanso kuti anthu sakufunikira kuti Mulungu aziwauza zochita. M’malomwake Adamu ndi Hava ayenera kumasankha okha zimene akuona kuti ndi zoyenera kapena zosayenera. Ndiye kodi Mulungu anatani? Iye akanatha kungopha oukirawo nthawi yomweyo. Koma kodi zimenezi zikanasonyeza kuti zimene Satana ankanena ndi zabodza? Ayi.

9 N’chifukwa chake Yehova sanaphe oukirawo nthawi yomweyo. Iye anaona kuti ndi bwino papite nthawi anthu akudzilamulira okha. Zimenezi zinapereka mpata wotsimikizira kuti Satana ndi wabodza komanso kuti Yehova ndi amene amadziwa zinthu zimene anthu amafunikira. Tidzamva zambiri za nkhani imeneyi m’Mutu 11. Koma kodi inuyo mukuona kuti zimene Adamu ndi Hava anachitazi zinali zoyenera? Kodi anachita bwino kumvera Satana osati Mulungu? Zinthu zonse zimene Adamu ndi Hava anali nazo zinali zopatsidwa ndi Yehova. Anawapatsa moyo wabwino, malo okongola oti azikhalamo, ndiponso ntchito imene ankasangalala nayo. Koma palibe chilichonse chimene Satana anawachitira.

10. Kodi panopa aliyense akufunika kusankha chiyani?

10 Nafenso timafunika kusankha zinthu zoyenera kuchita ndipo moyo wathu umadalira pa zimene tingasankhezo. Tikhoza kusankha kuti Yehova azitilamulira ndipo zimenezi zingathandize kusonyeza kuti Satana ndi wabodza. Tikhozanso kusankha kuti Satana azitilamulira. (Salimo 73:28; werengani Miyambo 27:11.) Masiku ano pali anthu ochepa kwambiri amene amamvera Mulungu. Ndipotu zimenezi ndi zomveka chifukwa panopa akulamulira dzikoli ndi Satana. Koma kodi zimenezi ndi zimene Baibulo limanena?

KODI AKULAMULIRA DZIKOLI NDI NDANI?

Kodi Satana akanamuuza Yesu kuti amupatsa maufumu onse a dziko lapansi akanakhala kuti si ake?

11, 12. (a) Kodi zimene Satana anachita pomuuza Yesu kuti amupatsa maufumu adziko lapansi, zikusonyeza chiyani? (b) Kodi ndi malemba ati omwe akusonyeza kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli?

11 Yesu ankadziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Pa nthawi ina, Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Ndiyeno anamulonjeza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.” (Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6) Kodi Satana akanamuuza Yesu kuti amupatsa maufumu a dziko lapansi akanakhala kuti si ake? Ayi. Zimenezi zikusonyeza kuti maboma onse a dziko lapansi ali m’manja mwa Satana.

12 Koma mwina mukudabwa kuti, ‘Kodi zingatheke bwanji kuti Satana akhale wolamulira wa dzikoli? Kodi m’mesa Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo ndi amene analenga zinthu zonse?’ (Chivumbulutso 4:11) Zimenezi ndi zoona, komatu Yesu ananena momveka bwino kuti Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Mtumwi Paulo ananenanso kuti Satana Mdyerekezi ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:3, 4) Mtumwi Yohane nayenso analemba kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

MMENE MULUNGU ADZAWONONGERE DZIKO LA SATANALI

13. N’chifukwa chiyani tikufunikira dziko latsopano?

13 Dzikoli likuwonjezeka kuopsa tsiku ndi tsiku. Panopo m’madera ambiri mukuchitika nkhondo komanso tikuona anthu ambiri akuchita zakatangale, zachinyengo komanso zachiwawa. Anthu sangathe kuthetsa mavuto onsewa ngakhale atayesetsa chotani. Koma posachedwapa Mulungu adzawononga dziko loipali pa nkhondo yake ya Aramagedo ndipo adzakhazikitsa dziko latsopano lachilungamo.—Chivumbulutso 16:14-16; onani Mawu Akumapeto 10.

14. (a) Kodi Mulungu anasankha ndani kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake? (b) Kodi Baibulo linaneneratu zotani zokhudza Yesu?

14 Yehova anasankha Yesu Khristu kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake. Zaka masauzande angapo zapitazo, Baibulo linaneneratu kuti Yesu adzalamulira monga “Kalonga Wamtendere” ndipo boma lake silidzatha. (Yesaya 9:6, 7) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera boma limeneli. Iye anawauza kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) M’Mutu 8, tidzaphunzira mmene Ufumu wa Mulungu udzayambire kulamulira m’malo mwa maboma amene alipowa. (Werengani Danieli 2:44.) Kenako Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso wokongola.—Onani Mawu Akumapeto 11.

DZIKO LATSOPANO LAYANDIKIRA

15. Kodi “dziko lapansi latsopano” n’chiyani?

15 Baibulo limalonjeza kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera” ndipo “mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13; Yesaya 65:17) Nthawi zina Baibulo likamanena za “dziko” limakhala likunena za anthu amene amakhala m’dzikoli. (Genesis 11:1) Choncho “dziko lapansi latsopano” likutanthauza anthu onse amene amamvera Mulungu.

16. M’dziko latsopano, kodi ndi mphatso yotani imene Mulungu adzapereke kwa anthu, nanga tiyenera kuchita chiyani kuti tidzalandire mphatso imeneyi?

16 Yesu analonjeza kuti anthu amene adzakhale m’dziko latsopano adzapatsidwa “moyo wosatha.” (Maliko 10:30) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzalandire mphatso imeneyi? Kuti mupeze yankho, werengani Yohane 3:16 ndi 17:3. Tsopano tiyeni tione mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso.

17, 18. Kodi tikudziwa bwanji kuti padziko lonse padzakhala mtendere komanso chitetezo?

17 Nkhondo, kusamvera malamulo, chiwawa ndi zinthu zonse zoipa zidzatha. Padziko lapansi sipadzatsala munthu aliyense woipa. (Salimo 37:10, 11) Mulungu adzathetsa “nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Salimo 46:9; Yesaya 2:4) Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu amene amakonda Mulungu komanso kumumvera. Padziko lapansi padzakhala mtendere mpaka kalekale.—Salimo 72:7.

18 Anthu olambira Yehova adzakhala motetezeka. Kale Aisiraeli akamamvera Mulungu, ankakhala mwamtendere chifukwa iye ankawateteza. (Levitiko 25:18, 19) M’Paradaiso sitidzaopa chilichonse kapena munthu aliyense. Nthawi zonse tidzakhala otetezeka.—Werengani Yesaya 32:18; Mika 4:4.

19. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti m’dziko latsopano mudzakhala zakudya zambiri?

19 Kudzakhala zakudya zambiri. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” (Salimo 72:16) Yehova, yemwe ndi “Mulungu wathu, adzatidalitsa” ndipo “dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.”—Salimo 67:6.

20. Kodi tikudziwa bwanji kuti dziko lonse lidzakhala paradaiso?

20 Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Anthu adzakhala ndi nyumba zokongola komanso minda ya maluwa okongola. (Werengani Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 11:18.) Dziko lonse lapansi lidzakhala lokongola ngati mmene munda wa Edeni unalili. Yehova azidzatipatsa zonse zimene timafunikira. Baibulo limanena kuti Yehova ‘amatambasula dzanja lake ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’—Salimo 145:16.

21. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu azidzakhala mwamtendere ndi zinyama?

21 Anthu azidzakhala mwamtendere ndi zinyama. Zinyama sizidzavulazanso anthu. Ana aang’ono sazidzaopa kusewera ndi nyama zimene panopa ndi zoopsa.—Werengani Yesaya 11:6-9; 65:25.

22. Kodi Yesu adzawachitira chiyani anthu omwe akudwala?

22 Anthu sazidzadwala. Yesu ali padziko lapansi pano, anachiritsa anthu ambiri. (Mateyu 9:35; Maliko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Koma monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachiritsa anthu onse. Pa nthawi imeneyo palibe amene adzanene kuti: “Ndikudwala.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

23. Kodi Mulungu adzawachitira chiyani anthu omwe anamwalira?

23 Anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Mulungu akulonjeza kuti adzaukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira. “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Werengani Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

24. Kodi mumamva bwanji mukaganizira zodzakhala m’Paradaiso?

24 Tonsefe tili ndi ufulu wosankha kuphunzira za Yehova n’kumamutumikira, kapena kumangochita zimene tikufuna. Ngati titasankha kutumikira Yehova, tingayembekezere kuti moyo wathu udzakhala wabwino kwambiri m’tsogolo. Yesu anauza munthu wina amene anapachikidwa pambali pake kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Tiyenera kupitiriza kuphunzira za Yesu Khristu komanso za mmene adzakwaniritsire zinthu zosangalatsa zimene Mulungu anatilonjeza.