Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Kabukuka kakonzedwa kuti kakuthandizeni kukhala ndi luso lowerenga pagulu, lolankhula komanso lophunzitsa.
Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Timaphunzitsa anthu mfundo zofunika kwambiri kuposa mfundo zina zonse.
PHUNZIRO 2
Kulankhula Mokambirana ndi Anthu
Kulankhula mokambirana kumathandiza anthu kuti amasuke komanso atsatire zimene mukunena.
PHUNZIRO 3
Kugwiritsa Ntchito Mafunso
Muzifunsa mafunso abwino kuti anthu achite chidwi komanso kuti mutsindike mfundo zikuluzikulu.
PHUNZIRO 4
Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba
Onani mmene mungathandizire anthu kukonzekera kumva mfundo yapalemba.
PHUNZIRO 5
Kuwerenga Molondola
Kuwerenga molondola kumathandiza kuti anthu adziwe zoona zokhudza Yehova.
PHUNZIRO 6
Kufotokoza Bwino Malemba
Thandizani anthu kuti aone kugwirizana pakati pa lemba limene mwawerenga ndi mfundo imene mukufotokoza.
PHUNZIRO 7
Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima
Mukamalankhula zoona komanso zofika pamtima anthu amakhulupirira zimene mukunena.
PHUNZIRO 8
Mafanizo Abwino
Muzigwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva kuti muzifika anthu pamtima komanso kuwathandiza kumvetsa mfundo zofunika.
PHUNZIRO 9
Kugwiritsa Ntchito Bwino Zinthu Zooneka
Muzigwiritsa ntchito zinthu zooneka n’cholinga choti anthu azikumbukira mfundo zanu.
PHUNZIRO 10
Kusinthasintha Mawu
Pena muzilankhula mofulumira, pena mwapang’onopang’ono, pena mokweza, pena motsitsa komanso pena muzilankhula ndi mawu aakulu, pena aang’ono. Muzichita zimenezi n’cholinga choti muzifika anthu pamtima n’kuwathandiza kuti azitsatira zimene akuphunzira.
PHUNZIRO 11
Kulankhula ndi Mtima Wonse
Mukamalankhula ndi mtima wonse mumasonyeza kuti nkhaniyo yakufikani pamtima ndipo zimathandiza kuti anthu azimvetsera mwachidwi.
PHUNZIRO 12
Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima
Mukamalankhula mochokera mumtima mumasonyeza anthu kuti mumawakonda.
PHUNZIRO 13
Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
Muzithandiza anthu kumvetsa mmene nkhaniyo imakhudzira moyo wawo komanso mmene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzira.
PHUNZIRO 14
Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu
Muziwathandiza kuti azitsatira bwinobwino nkhani yanu ndipo aziona kugwirizana pakati pa mfundo yaikulu iliyonse ndi cholinga komanso mutu wa nkhani yanu.
PHUNZIRO 15
Kulankhula Motsimikiza
Muzilankhula motsimikiza. Muzisonyeza kuti mumaona kuti zimene mukunena n’zofunika kwambiri.
PHUNZIRO 16
Kulankhula Molimbikitsa
Muzilankhula zinthu zothandiza osati zokhumudwitsa. Muzifotokoza mfundo zosangalatsa za m’Mawu a Mulungu.
PHUNZIRO 17
Kulankhula Zomveka
Muzithandiza anthu kuti amvetse mfundo zanu. Muzifotokoza mosavuta kumva mfundo zikuluzikulu.
PHUNZIRO 18
Nkhani Yophunzitsadi Anthu
Muzithandiza anthu kuganiza ndiponso kumva kuti aphunzira mfundo zothandiza.
PHUNZIRO 20
Mawu Omaliza Abwino
Mawu omaliza abwino amathandiza anthu kukhulupirira zimene aphunzira komanso kuzitsatira.
Zimene Inuyo Mwachita
Muzilemba zimene mwachita poyesetsa kuwerenga ndiponso kuphunzitsa mwaluso.