PHUNZIRO 10 Kusinthasintha Mawu YAMBANI Kusinthasintha Mawu Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Miyambo 8:4, 7 MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula momveka bwino ndipo muzisinthasintha mawu, pena kukweza pena kutsitsa, pena kulankhula mofulumira pena pang’onopang’ono. MMENE MUNGACHITIRE: Pena muzikweza mawu pena kuwatsitsa. Mungakweze mawu kuti mutsindike mfundo yofunika kapena kuti mulimbikitse anthu kuchita zinazake. Mungachitenso zomwezo powerenga uthenga wachiweruzo wa m’Baibulo. Mungatsitse mawu pothandiza anthu kuyembekezera kumva mfundo inayake kapena pofotokoza zinthu zochititsa mantha kapena zodetsa nkhawa. Pena muzilankhula mawu aakulu pena aang’ono. Ngati n’zololeka m’chilankhulo chanu, muzisintha mawu potsindika mfundo, ponena zinthu zazikulu kapena pofotokoza zinthu zimene zili patali. Muzisinthanso mawu ponena zinthu zomvetsa chisoni kapena zodetsa nkhawa. Pena muzilankhula mofulumira pena pang’onopang’ono. Muzilankhula mofulumira posonyeza kusangalala koma pang’onopang’ono mukamatchula mfundo yofunika kwambiri. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kusinthasintha Mawu KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kusinthasintha Mawu Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kusinthasintha Mawu https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 10