PHUNZIRO 12 Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima YAMBANI Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu 1 Atesalonika 2:7, 8 MFUNDO YAIKULU: Mukamalankhula, anthu aziona kuti mumawaganizira komanso mumawafunira zabwino. MMENE MUNGACHITIRE: Muziganizira anthu. Pokonzekera nkhani yanu muziganizira mavuto amene anthu akukumana nawo. Muziganiziranso mmene anthuwo akumvera chifukwa cha mavuto awo. Muzisankha bwino mawu. Cholinga chanu chizikhala kuwalimbikitsa, kuwatonthoza komanso kuwapatsa mphamvu. Pewani kukhumudwitsa anthu, kudzudzula anthu omwe si Mboni kapena kutsutsa kwambiri mfundo zimene anthu ena amazikhulupirira kwambiri. Muzisonyeza kuti mumakonda anthu. Mawu komanso nkhope yanu zizisonyeza kuti mumaganizira anthu. Muzikondanso kumwetulira. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 12