PHUNZIRO 14 Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu YAMBANI Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Aheberi 8:1 MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kuti azitsatira nkhani yanu komanso aziona kugwirizana pakati pa mfundo zazikulu ndi mutu wa nkhani yonseyo. MMENE MUNGACHITIRE: Muzikhala ndi cholinga. Muzidzifunsa kuti, Kodi cholinga cha nkhaniyi n’chiyani? Kodi ndi kuphunzitsa, kuthandiza anthu kuti asinthe maganizo kapena kuwalimbikitsa kuchita zinazake? Ndiyeno mfundo zikuluzikulu zizikuthandizani kukwaniritsa cholingacho. Muzitsindika mutu wa nkhani yanu. Munkhani yanu yonse muzitsindika mutu potchula mawu ofunika kwambiri a m’mutuwo kapena kugwiritsa ntchito mawu ofanana nawo. Muzithandiza anthu kuona mfundo zazikulu m’njira yosavuta. Muzisankha mfundo zikuluzikulu zimene zikugwirizana ndi mutu wa nkhani komanso zimene mungazifotokoze bwino popanda kudya nthawi. Mfundo zikuluzikulu zizikhala zochepa, muzitchula mfundo iliyonse momveka, muzipuma mukamachoka pa mfundo ina kupita pa ina kuti musawasiye anthu m’malere. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 14