PHUNZIRO 15 Kulankhula Motsimikiza YAMBANI Kulankhula Motsimikiza Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu 1 Atesalonika 1:5 MFUNDO YAIKULU: Muzisonyeza kuti mumakhulupirira kwambiri mfundo za choonadi ndipo simukukayikira kuti mfundo zimene mukunena n’zothandiza. MMENE MUNGACHITIRE: Muzikonzekera bwino. Pokonzekera muzidzifunsa kuti, Kodi mfundo za m’Malemba zingathandize bwanji munthu kufika pozindikira zoona zake pa nkhaniyi? Muzigwiritsa ntchito mawu osavuta pofotokoza mfundo zikuluzikulu. Muziganizira mmene zingathandizire anthu amene mukukambirana nawo. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera. Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kutsimikiza. M’malo monena ndendende mmene mawu anawalembera m’mabuku athu, muzigwiritsa ntchito mawu anuanu. Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti simukukayikira zimene mukunena. Muzilankhula mochokera pansi pa mtima komanso mosakayikira. Mawu anu asakwere kwambiri kapena kutsika kwambiri. Ngati n’zololeka kwanuko, muziyang’ana anthu amene mukukambirana nawo. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kulankhula Motsimikiza KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kulankhula Motsimikiza Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kulankhula Motsimikiza https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 15