PHUNZIRO 16

Kulankhula Molimbikitsa

Kulankhula Molimbikitsa

Yobu 16:5

MFUNDO YAIKULU: M’malo mongotchula mavuto okhaokha, muzifotokoza njira yothetsera mavutowo komanso mfundo zimene zingalimbikitse anthu.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muziona kuti anthu amene mukulankhula nawo ali ndi mtima wabwino. Muziona kuti Akhristu anzanu amafuna kusangalatsa Yehova. Ngakhale pamene mukufuna kuwapatsa malangizo, muziyamba ndi kuwayamikira kuchokera pansi pa mtima.

  • Chepetsani mfundo zosalimbikitsa. Zinthu zina zosalimbikitsa mukhoza kuzitchula ngati mukufuna kutsimikizira mfundo inayake. Koma nkhani yanu yonse iyenera kukhala yolimbikitsa.

  • Muzigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu. Thandizani anthu kuganizira zimene Yehova wachita m’mbuyomu, zimene akuchita panopa, ndiponso zimene adzachite m’tsogolo. Thandizani anthu kukhala ndi chiyembekezo komanso kuti alimbe mtima.