PHUNZIRO 18 Nkhani Yophunzitsadi Anthu YAMBANI Nkhani Yophunzitsadi Anthu Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu 1 Akorinto 9:19-23 MFUNDO YAIKULU: Muzithandiza anthu kuganiza mpaka kufika pozindikira kuti aphunziradi mfundo zothandiza. MMENE MUNGACHITIRE: Ganizirani zimene anthu akudziwa kale. M’malo mongofotokoza zimene anthu akuzidziwa kale, athandizeni kuiganizira nkhaniyo m’njira yatsopano. Muzifufuza komanso kuganizira kwambiri nkhaniyo. Ngati n’zotheka, muzigwiritsa ntchito mfundo zimene anthu sakuzidziwa kwambiri kapena nkhani zimene zangochitika kumene pofotokozera mfundo zikuluzikulu. Muziganizira kwambiri nkhani yanu n’kumaona ngati mfundo zimene mukufuna kugwiritsa ntchito zikugwirizanadi ndi nkhaniyo. Muzithandiza anthu kuona kuti nkhaniyo ndi yofunika kwambiri. Muzifotokoza mmene Malemba angathandizire anthu pa moyo wawo. Muzifotokoza mfundo zogwirizana ndi zimene zimachitikira anthu, zimene anthu amachita komanso zimene anthu amaganiza. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Nkhani Yophunzitsadi Anthu KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Nkhani Yophunzitsadi Anthu Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Nkhani Yophunzitsadi Anthu https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 18