PHUNZIRO 19 Kuwafika Pamtima Anthu YAMBANI Kuwafika Pamtima Anthu Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Miyambo 3:1 MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kumvetsa zimene mukunena komanso kuzigwiritsa ntchito. MMENE MUNGACHITIRE: Muzithandiza anthu kuti azidzifufuza. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kudzifufuza mumtima. Muzithandiza anthu kukhala ndi zolinga zabwino. Thandizani anthu kudzifufuza kuti adziwe chifukwa chimene amachitira zinthu zabwino. Athandizeni kuti azichita zinthu chifukwa chokonda Yehova, anzawo komanso Mawu a Mulungu. Muzikambirana ndi anthu osati kuwauza zochita. Nkhani yanu ikamatha, anthu azikhala atalimbikitsidwa osati atachititsidwa manyazi. Azifunitsitsa kuchita zonse zimene angathe. Muzithandiza anthu kuganizira za Yehova. Nkhani yanu izithandiza anthu kuona kuti malamulo komanso mfundo za m’Baibulo zimasonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi. Muzithandiza anthu kudziwa kuti zochita zawo zimakhudza Yehova ndipo azifunitsitsa kumusangalatsa. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kuwafika Pamtima Anthu KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kuwafika Pamtima Anthu Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kuwafika Pamtima Anthu https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/f62df3bf2a/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 19