PHUNZIRO 6 Kufotokoza Bwino Malemba YAMBANI Kufotokoza Bwino Malemba Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Yohane 10:33-36 MFUNDO YAIKULU: Musamangoti kuwerenga lemba ili, basi kupita pa lemba lina. Muzithandiza anthu kuona kugwirizana pakati pa lemba limene mwawerenga ndi nkhani imene mukukamba. MMENE MUNGACHITIRE: Sankhani mawu ofunika. Mukawerenga lemba, muzisankhapo mawu amene akugwirizana kwambiri ndi mfundo yaikulu yamunkhani yanu. Mungabwereze kutchula mawuwo, kapena kufunsa funso limene lingachititse anthu kuganizira mawuwo. Tsindikani mfundo. Ngati munatchula chifukwa chowerengera lemba, mukaliwerenga muzisonyeza mmene mawu amulembalo akuperekera chifukwacho. Fotokozani mwachidule mmene tingagwiritsire ntchito. Pewani kunena zambirimbiri pa mawu amene sakugwirizana ndi mfundo yanu yaikulu. Ganizirani zimene anthu akudziwa kale pa lembalo. Kenako fotokozani mwachidule mmene anthu angagwiritsire ntchito mfundoyo. Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kufotokoza Bwino Malemba KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kufotokoza Bwino Malemba Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kuwerenga ndi Kuphunzitsa—Kufotokoza Bwino Malemba https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/1add6d1d93/images/syn_placeholder_sqr.png th phunziro 6