PHUNZIRO 7

Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima

Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima

Luka 1:3

MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito maumboni odalirika kuti anthu amene mukukambirana nawo adziwe zoona.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzigwiritsa ntchito maumboni odalirika. Zolankhula zanu zizikhala zochokera m’Mawu a Mulungu ndipo ngati n’zotheka muzichita kuwerenga m’Baibulo. Ngati mukufuna kupereka umboni wochokera kwa asayansi, nyuzi, kapena zinthu zina muzitsimikizira kuti n’zodalirika komanso zolondola.

  • Muzigwiritsa ntchito bwino maumboniwo. Zimene mukufotokoza pa lemba zizikhala zogwirizana ndi nkhani yonse ya lembalo, Baibulo lonse komanso zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wafalitsa. (Mat. 24:45) Ngati mukugwiritsa ntchito umboni wina muzionetsetsa kuti ukugwirizana ndi nkhani yonse komanso cholinga cha wolembayo.

  • Fotokozani m’njira yogwira mtima. Mukawerenga lemba kapena kutchula umboni winawake, muzifunsa mafunso abwino kapena kupereka chitsanzo chothandiza anthu kuzindikira zimene mukutanthauza.