MUTU 1
Chikondi cha Mulungu Sichimatha
“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 YOHANE 5:3.
1, 2. N’chifukwa chiyani mumakonda Mulungu?
KODI mumakonda Mulungu? Muyenera kuti mumamukonda kwambiri moti munadzipereka kwa iye. N’kuthekanso kuti mumamuona kuti ndi mnzanu wapamtima. Komatu iye ndi amene anayamba kukukondani inuyo musanayambe kumukonda. Baibulo limati: “Ife timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”—1 Yohane 4:19.
2 Yehova anatisonyeza chikondi m’njira zambiri. Mwachitsanzo, anatipatsa dziko lokongolali komanso zinthu zina zambiri kuti tizisangalala ndi moyo. (Mateyu 5:43-48; Chivumbulutso 4:11) Amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi komanso amatilola kuti tiphunzire za iye. Tikamawerenga Baibulo, timakhala kuti tikumva zimene iye akutiuza ndipo tikamapemphera iye amamvetsera. (Salimo 65:2) Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera potitsogolera ndiponso kutilimbikitsa. (Luka 11:13) Komanso anatumiza Mwana wake wokondedwa kuti adzatimasule ku uchimo ndi imfa.—Werengani Yohane 3:16; Aroma 5:8.
3. Kodi tingatani kuti Yehova apitirize kukhala mnzathu?
3 Taganizirani za mnzanu wapamtima amene amakhala nanu nthawi zonse, kaya zinthu zili bwino kapena ayi. Pamafunika khama kuti ubwenzi woterowo upitirire. Ndi mmene zililinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Yehova angakhale mnzathu wapamtima kuposa aliyense ndipo tikhoza kukhala naye pa ubwenzi mpaka kalekale. Baibulo limati: “Pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.” (Yuda 21) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Yankho la funso limeneli likupezeka pa 1 Yohane 5:3. Lembali limati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”
ZIMENE “KUKONDA MULUNGU” KUMATANTHAUZA
4, 5. Fotokozani zimene zinachitika kuti muyambe kukonda Yehova.
4 Kodi “kukonda Mulungu” kumatanthauza chiyani? Musanayankhe funso limeneli, tayesani kukumbukira nthawi imene munayamba kukonda Yehova.
5 Kodi mukukumbukira mmene munamvera mutaphunzira kuti Yehova amafuna kuti mudzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano? Munazindikira mfundo yoti kuti zimenezi zitheke, Mulungu anatumiza Mwana wake kuti adzatifere. Imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (Mateyu 20:28; Yohane 8:29; Aroma 5:12, 18) Mutaphunzira kuti Yehova amakukondani kwambiri, zinakukhudzani mumtima ndipo nanunso munayamba kumukonda.—Werengani 1 Yohane 4:9, 10.
6. (a) Ngati timakonda munthu wina, kodi timachita chiyani? (b) Kodi inuyo munachita zinthu ziti chifukwa chokonda Yehova?
6 Koma kukonda Yehova chinali chiyambi chabe. Ukakhala ndi mnzako amene umamukonda kwambiri, kungomuuza kuti “ndimakukonda” sikukhala kokwanira. Ngati timakondadi munthu, timayesetsa kuchita zimene zingamusangalatse. Mofanana ndi zimenezi, chikondi chanu pa Yehova chinachititsa kuti muziyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa. Chikondichi chitayamba kukula, muyenera kuti munadzipereka kwa iye n’kubatizidwa. Izi zikutanthauza kuti munamulonjeza kuti mudzamutumikira mpaka kalekale. (Werengani Aroma 14:7, 8.) Ndiye kodi mungatani kuti musunge lonjezo lanuli?
“KUSUNGA MALAMULO AKE”
7. (a) Kodi timachita chiyani ngati timakonda Yehova? (b) Kodi malamulo ena a Mulungu ndi ati?
7 Popeza timakonda Yehova, ‘timasunga malamulo ake.’ Kodi timachita bwanji zimenezi? Timayesetsa kumumvera. M’Baibulo muli mfundo zimene zimatithandiza kudziwa zimene Yehova amadana nazo. Mwachitsanzo, timaphunzira kuti sitiyenera kuledzera, kuba kapena kugonana ndi munthu amene sitinakwatirane naye. Timaphunziranso kuti sitiyenera kulambira chilichonse kapena aliyense, koma Yehova yekha.—1 Akorinto 5:11; 6:18; 10:14; Aefeso 4:28; Akolose 3:9.
8, 9. Kodi tingadziwe bwanji maganizo a Yehova pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake? Perekani chitsanzo.
8 Koma kuti tisangalatse Yehova, pamafunika zambiri osati kumvera malamulo ake kokha. Iye sanatipatse mndandanda wa malamulo okhudza chilichonse. Choncho nthawi zina tingapeze kuti m’Baibulo mulibe lamulo lotiuza zoyenera kuchita pa nkhani inayake. Ndiye kodi tingatani kuti tisankhe zoyenera pa nkhani ngati zimenezi? (Aefeso 5:17) M’Baibulo muli mfundo za makhalidwe abwino zomwe zimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Tikamawerenga Baibulo timayamba kumudziwa bwino Yehova. Timadziwa zimene amakonda komanso zimene amadana nazo.—Werengani Salimo 97:10; Miyambo 6:16-19; onani Mawu Akumapeto 1.
9 Mwachitsanzo, kodi timadziwa bwanji zoyenera kuonera pa TV kapena pa intaneti? Palibe lamulo la Yehova lenileni limene limanena zoyenera kuchita pa nkhaniyi. Koma mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuti tisankhe bwino. Zosangalatsa zambiri masiku ano zimasonyeza zinthu zachiwawa komanso zachiwerewere. Koma Baibulo limanena kuti Yehova “amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa” komanso “adzaweruza adama ndi achigololo.” (Salimo 11:5; Aheberi 13:4) Kodi mfundo zimenezi zingatithandize bwanji kusankha zoyenera? Tikadziwa kuti Yehova amaona kuti khalidwe linalake ndi loipa ndipo amadana nalo, tiyenera kulipewa.
10, 11. N’chifukwa chiyani timamvera Yehova?
10 N’chifukwa chiyani timamvera Yehova? Sitichita zimenezi chifukwa chongopewa kulangidwa kapena kukumana ndi mavuto ayi. (Agalatiya 6:7) Timamvera Yehova chifukwa choti timamukonda. Mofanana ndi ana amene amafuna kusangalatsa bambo awo, ifenso timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Palibe chinthu chosangalatsa kwambiri kuposa kudziwa kuti Yehova akusangalala nafe.—Salimo 5:12; Miyambo 12:2; onani Mawu Akumapeto 2.
11 Komanso sikuti timamvera Yehova pokhapokha tikaona kuti zimene akufuna ndi zosavuta kapena tikaona kuti sitingachitire mwina. Sikutinso timachita kusankha malamulo ndi mfundo zoti tizitsatira. (Deuteronomo 12:32) M’malomwake timayesetsa kumumvera pa chilichonse, ndipo timakhala ndi maganizo ofanana ndi a munthu wina amene analemba nawo masalimo yemwe anati: “Ndidzakondwera ndi malamulo anu, amene ndimawakonda.” (Salimo 119:47; Aroma 6:17) Timafunanso kukhala ngati Nowa amene anasonyeza kuti ankakonda Yehova ndipo ankachita zonse zimene Mulungu ankamuuza. Baibulo limati Nowa “anachitadi momwemo.” (Genesis 6:22) Kodi inunso mumafuna kuti Yehova aziona kuti mumachitadi zonse zimene amafuna?
12. Kodi tingatani kuti tisangalatse Yehova?
12 Kodi Yehova amamva bwanji tikamamumvera? ‘Mtima wake’ umasangalala. (Miyambo 11:20; 27:11) Taganizirani mfundo imeneyi. Tikakhala omvera timasangalatsa Mulungu, yemwe analenga zinthu zonse. Koma ngakhale zili choncho, iye satikakamiza kuti tizimumvera. Anatipatsa ufulu wosankha zochita. Choncho tingathe kusankha kuchita zabwino kapena ayi. Koma Yehova amafuna kuti tizisankha kuchita zabwino chifukwa chomukonda. Amafunanso kuti tizichita zabwino kuti tikhale ndi moyo wosangalala.—Deuteronomo 30:15, 16, 19, 20; onani Mawu Akumapeto 3.
“MALAMULO AKEWO NDI OSALEMETSA”
13, 14. Kodi tikudziwa bwanji kuti malamulo a Yehova si ovuta kwambiri ndipo tingathe kuwatsatira? Perekani chitsanzo.
13 Koma bwanji ngati timaganiza kuti malamulo a Yehova ndi ovuta kwambiri kuwatsatira komanso amatiphera ufulu? Zimenezi si zoona chifukwa Baibulo limati: “Malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Mawu amene anawamasulira kuti ‘kulemetsa’ pavesili, m’malemba ena anawagwiritsa ntchito pofotokoza za malamulo ovuta kapena anthu amene amalamulira anzawo mwankhanza. (Mateyu 23:4; Machitidwe 20:29, 30) Koma malamulo a Mulungu si ovuta kwambiri moti mpaka tingalephere kuwatsatira. Nthawi zonse Yehova amatipatsa malamulo amene akudziwa kuti tingakwanitse kuwatsatira.
14 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuthandiza mnzanu amene akusamuka ndipo walongedza katundu wake m’makatoni. Pali makatoni opepuka komanso osavuta kunyamula, koma palinso ena olemera kwambiri oti angafunike kunyamula anthu awiri. Kodi mnzanuyo angakupempheni kuti munyamule nokha katoni yolemera? N’zodziwikiratu kuti sangachite zimenezo chifukwa akudziwa kuti ingathe kukuvulazani. Mofanana ndi zimenezi, Yehova sangatiuze kuti tichite zinthu zomwe sitingakwanitse. (Deuteronomo 30:11-14) Iye “akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:14.
15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malamulo onse amene Yehova amatipatsa ndi othandiza?
15 Mose anauza Aisiraeli kuti malamulo a Yehova akanawathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino “nthawi zonse.” Anawauzanso kuti kumvera malamulowo kukanawathandiza kuti ‘akhale ndi moyo.’ (Deuteronomo 5:28-33; 6:24) N’chimodzimodzinso masiku ano. Zonse zimene Yehova amafuna kuti tizichita zimatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino. (Werengani Yesaya 48:17.) Iye ali ngati Bambo athu ndipo nthawi zonse amadziwa zimene zingatithandize. (Aroma 11:33) Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Izi zikusonyeza kuti zonse zimene Yehova amanena komanso kuchita, amazichita chifukwa cha chikondi.
16. Kodi tikudziwa bwanji kuti tingathe kumvera Mulungu ngakhale kuti si ife angwiro komanso tikukhala m’dziko loipa?
16 Si nthawi zonse pamene kumvera Mulungu kumakhala kophweka. Tikukhala m’dziko loipa ndipo wolamulira wake ndi Mdyerekezi. Iye amalimbikitsa anthu kuti azichita zoipa. (1 Yohane 5:19) Komanso popeza si ife angwiro, timalimbana ndi maganizo oipa amene angatilepheretse kumvera Mulungu. (Aroma 7:21-25) Koma chifukwa choti timakonda Yehova, timayesetsa kuchita zabwino. Tikamayesetsa kumumvera, iye amaona ndipo amatipatsa mzimu wake woyera kuti uzitithandiza. (1 Samueli 15:22, 23; Machitidwe 5:32) Mzimu woyera umatithandizanso kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tisamavutike kwambiri kumvera Mulungu.—Agalatiya 5:22, 23.
17, 18. (a) Kodi tiphunzira zotani m’bukuli? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani?
17 M’bukuli tiphunzira zimene tingachite kuti tizikhala moyo wosangalatsa Yehova. Tiphunziranso zoyenera kuchita kuti tizitsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. Musaiwale kuti Yehova satikakamiza kuti tizimumvera. Koma tikasankha kumumvera, timakhala ndi moyo wabwino panopa ndiponso tidzapeza madalitso ambiri m’tsogolo. Chofunikanso kwambiri n’chakuti, tikamamvera Mulungu timasonyeza kuti timamukonda.—Onani Mawu Akumapeto 4.
18 Yehova anatipatsa chikumbumtima kuti chizitithandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Ngati titaphunzitsa bwino chikumbumtima chathu, chingatithandize kuti ‘tizisunga malamulo ake.’ Koma kodi chikumbumtima ndi chiyani, nanga tingachiphunzitse bwanji? M’mutu wotsatira tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa.
KODI MUNGATANI KUTI MULUNGU AZIKUKONDANI?