MUTU 5
Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana Ndi Dzikoli?
“Simuli mbali ya dzikoli.”—YOHANE 15:19.
1. Kodi Yesu ankadera nkhawa za chiyani kutatsala tsiku limodzi kuti aphedwe?
KUTATSALA tsiku limodzi kuti aphedwe, Yesu ankadziwa kuti watsala pang’ono kusiyana ndi ophunzira ake. Iye ankadera nkhawa za tsogolo la ophunzira akewo. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Kenako anapemphera kwa Atate wake ndipo ponena za ophunzira akewo anati: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?
2. Kodi mawu akuti “dziko” amene Yesu ananena akutanthauza chiyani?
2 Ponena kuti “dziko” Yesu ankatanthauza anthu amene sadziwa Mulungu ndipo amalamuliridwa ndi Satana. (Yohane 14:30; Aefeso 2:2; Yakobo 4:4; 1 Yohane 5:19) Ndiye kodi tingatani kuti tisakhale “mbali ya dziko”? M’mutu uno tikambirana zinthu zingapo zimene tingachite. Zinthu zake ndi izi: Tizikhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu ndipo tisamalowerere ndale, tizipewa mzimu wa dziko, tizivala ndi kudzikongoletsa moyenera, tiziona ndalama moyenera komanso tizinyamula zida zankhondo zimene Mulungu watipatsa.—Onani Mawu Akumapeto 16.
TIZIKHALA OKHULUPIRIKA KU UFUMU WA MULUNGU
3. N’chifukwa chiyani Yesu sankalowerera ndale?
3 Yesu ali padzikoli, ankaona kuti anthu ambiri anali ndi mavuto osiyanasiyana. Iye ankadera nkhawa kwambiri anthuwo ndipo ankafunitsitsa kuwathandiza. Ndiye kodi anakhala mtsogoleri wa ndale? Ayi. Iye ankadziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene ungathandize anthuwo. Ankadziwanso kuti iyeyo ndi amene adzakhale Mfumu ya Ufumu umenewu ndipo nthawi zambiri ankaphunzitsa anthu za Ufumuwu. (Danieli 7:13, 14; Luka 4:43; 17:20, 21) Yesu sankachita ndale ndipo sankatenga mbali pa zochitika za m’dzikoli. Atakaonekera pamaso pa bwanamkubwa wachiroma, dzina lake Pontiyo Pilato, anamuuza kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Ophunzira ake nawonso sankalowerera zochitika za m’dzikoli. Buku lina linanena kuti Akhristu oyambirira “sankakhala ndi udindo uliwonse wandale.” (On the Road to Civilization) Masiku anonso Akhristu oona salowelera ndale. Timakhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu ndipo sitipanga nawo chilichonse chokhudza ndale.—Mateyu 24:14.
4. Kodi Akhristu oona amasonyeza bwanji kuti ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu?
4 Akhristu odzozedwa, omwe akuyembekezera kudzalamulira ndi Khristu kumwamba, ali ngati akazembe. Akazembe amakhala m’dziko lina koma amaimira dziko lawo. Choncho salowerera ndale za m’dziko limene akukhalalo. Paulo analembera Akhristu odzozedwa kuti: “Ndife akazembe m’malo mwa Khristu.” (2 Akorinto 5:20) Odzozedwa amaimira Ufumu wa Mulungu. Choncho salowerera ndale kapena zochitika zilizonse za m’dzikoli. (Afilipi 3:20) M’malomwake amathandiza anthu kuti aphunzire za Ufumu wa Mulungu. A “nkhosa zina,” omwe adzakhale m’dziko latsopano, amathandiza odzozedwa ndipo nawonso salowerera ndale. (Yohane 10:16; Mateyu 25:31-40) Malemba amanena mosapita m’mbali kuti Akhristu oona sayenera kulowerera ndale.—Werengani Yesaya 2:2-4.
5. N’chifukwa chiyani Akhristu samenya nawo nkhondo?
5 Akhristu oona amaona kuti Akhristu anzawo ali ngati anthu a m’banja lawo. Choncho amayesetsa kukhala mogwirizana, mosatengera dziko limene amachokera kapena chikhalidwe chawo. (1 Akorinto 1:10) Sitipita kunkhondo chifukwa timadziwa kuti kuchita zimenezo kungachititse kuti timenyane ndi Akhristu anzathu omwe ndi abale athu amene Yesu anatilamula kuti tiziwakonda. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12) Ndipo Yesu anati tizikonda anthu onse, ngakhale adani athu.—Mateyu 5:44; 26:52.
6. Kodi Akhristu amachita zinthu ziti pomvera boma?
6 Ngakhale kuti Akhristufe sitilowerera ndale, timayesetsa kuti tikhale nzika zabwino. Mwachitsanzo, timasonyeza kuti timamvera boma potsatira malamulo komanso kukhoma misonkho. Komabe timaonetsetsa kuti tikupereka ‘zinthu za Mulungu kwa Mulungu.’ (Maliko 12:17; Aroma 13:1-7; 1 Akorinto 6:19, 20) “Zinthu za Mulungu” ndi monga kumukonda, kumumvera komanso kumulambira. Ndipotu timalolera kufa kusiyana n’kuti tisamvere Yehova.—Luka 4:8; 10:27; werengani Machitidwe 5:29; Aroma 14:8.
TIZIPEWA “MZIMU WA DZIKO”
7, 8. Kodi “mzimu wa dziko” n’chiyani, nanga umapangitsa anthu kukhala ndi makhalidwe ati?
7 Kuti tikhale osiyana ndi dziko la Satanali, tiyenera kuonetsetsa kuti sitikuyendera “mzimu wa dziko.” Tikati mzimu wa dziko tikunena za maganizo komanso makhalidwe ochokera kwa Satana amene anthu omwe satumikira Yehova amasonyeza. Koma Akhristu amayesetsa kupewa mzimu wa dziko. Paulo anati Akhristufe “sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.”—1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2, 3; onani Mawu Akumapeto 17.
8 Mzimu wa dziko umapangitsa anthu kukhala odzikonda, onyada komanso osafuna kuuzidwa zochita. Umawapangitsanso kukhala ndi maganizo akuti sakufunika kumamvera Mulungu. Satana amafuna kuti anthu azichita chilichonse chimene akufuna popanda kuganizira zotsatira zake. Amasangalalanso anthu akakhala ndi maganizo akuti chofunika kwambiri ndi kukwaniritsa zokhumba za mtima wawo. (1 Yohane 2:16; 1 Timoteyo 6:9, 10) Mdyerekezi akuyesetsa kwambiri kuti asocheretse atumiki a Yehova n’cholinga choti aziganiza ngati mmene iyeyo amaganizira.—Yohane 8:44; Machitidwe 13:10; 1 Yohane 3:8.
9. Kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kuyendera mzimu wa dziko?
9 Mofanana ndi mpweya umene timapuma, mzimu wa dziko uli paliponse. Titapanda kusamala, ifenso tingayambe kuyendera mzimu umenewu. (Werengani Miyambo 4:23.) Nthawi zina sitingazindikire n’komwe kuti mzimu wa dziko wayamba kutilowa. Mwachitsanzo, tingayambe kutsanzira maganizo komanso makhalidwe a anthu amene salambira Yehova. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Nthawi zinanso tingayambe mpatuko, kuonera zolaula, kapena kuchita masewera olimbikitsa mtima wa mpikisano.—Onani Mawu Akumapeto 18.
10. Kodi tingapewe bwanji mzimu wa dziko?
10 Kodi tingapewe bwanji mzimu wa dzikoli? Tiyenera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kumalola kuti Mawu ake azititsogolera. Komanso tizimupempha pafupipafupi kuti azitipatsa mzimu wake woyera. Tiyeneranso kutanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira. Yehova ndi wamphamvu kuposa aliyense. Choncho angatithandize kuti tithe kupewa mzimu wa dziko.—1 Yohane 4:4.
TIZIVALA MOYENERA
11. Kodi mzimu wa dzikoli umapangitsa kuti anthu azivala bwanji?
11 Timasonyezanso kuti sitili mbali ya dzikoli tikamavala komanso kudzikongoletsa moyenera. Anthu ambiri m’dzikoli amavala mosayenera n’cholinga choti anthu aziwacheukira kapena pofuna kukopa ena. Enanso amavala zovala zosonyeza kuti ndi oukira ndipo ena amavala modzionetsera n’cholinga choti anthu adziwe kuti ndi andalama. Ndiye pali enanso amene saganizira n’komwe za maonekedwe awo. Amakhala ndi ndevu zosameta, tsitsi lanyankhalala komanso thupi ndi zovala zawo zimakhala zauve. Koma Akhristufe timayesetsa kuti tisatengere maganizo a anthu am’dzikoli pa nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa.
12, 13. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kudziwa zovala zoyenera?
12 Atumiki a Yehovafe nthawi zonse tiyenera kuvala zovala zaukhondo, zabwino komanso zogwirizana ndi kumene tili. Timayesetsa kuvala “mwaulemu ndi mwanzeru” pofuna kusonyeza kuti ‘timalemekeza Mulungu.’—1 Timoteyo 2:9, 10; Yuda 21.
13 Tikamavala moyenera zingachititse kuti anthu azilemekeza Yehova komanso anthu ake. Timafuna kuchita “zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Munthu wodzichepetsa amaganiziranso anthu ena ndipo amapewa kuvala zovala zimene zingawakhumudwitse. Choncho tikamasankha zovala zoti tivale komanso mmene tikufuna kuonekera, tizikumbukira kuti tikapanda kusankha bwino, tingathe kukhumudwitsa ena.—1 Akorinto 4:9; 2 Akorinto 6:3, 4; 7:1.
14. Kodi tizikumbukira mfundo iti tikamasankha zovala zoti tivale kumisonkhano kapena mu utumiki?
14 Kodi timavala bwanji tikamapita kumisonkhano kapena mu utumiki? Kodi timavala n’cholinga choti aliyense azikangoyang’ana ifeyo? Nanga kodi anthu ena amachita manyazi chifukwa cha mmene tavalira? Kodi timaganiza kuti ndi ufulu wathu kuvala zimene tikufuna ndipo ena sizikuwakhudza? (Afilipi 4:5; 1 Petulo 5:6) N’zoona kuti aliyense amafuna kuoneka bwino. Koma tizikumbukira kuti chimene chingachititse kuti anthu azisangalala nafe, ndi makhalidwe athu abwino. Nayenso Yehova amayang’ana makhalidwe amenewa. Makhalidwewa ndi amene amasonyeza kuti ndife munthu wotani kwenikweni, chifukwa amasonyeza “munthu wobisika wamumtima” amene ndi “wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petulo 3:3, 4.
15. N’chifukwa chiyani Yehova sanatipatse mndandanda wa malamulo onena za zovala zoyenera ndi zosayenera?
15 Yehova sanatipatse mndandanda wa malamulo a zoyenera ndi zosayenera kuvala. Koma anatipatsa mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhaniyi. (Aheberi 5:14) Yehova amafuna kuti tizisankha zoyenera, kaya pa nkhani zazikulu kapena zazing’ono. Iye amafuna kuti tizichita zimenezi chifukwa chomukonda komanso chifukwa chokonda anzathu. (Werengani Maliko 12:30, 31.) Padziko lonse lapansi, a Mboni za Yehova amavala mosiyanasiyana mogwirizana ndi chikhalidwe cha kumene amakhala komanso zimene munthu aliyense amakonda. Zimenezi zimathandiza kuti tizisangalala.
TIZIKHALA NDI MAGANIZO OYENERA PA NKHANI YA NDALAMA
16. (a) Kodi mmene anthu am’dzikoli amaonera ndalama n’zosiyana bwanji ndi zimene Yesu anaphunzitsa? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
16 Satana amafuna kuti anthu aziganiza zoti ndalama komanso chuma ndi zimene zingawathandize kukhala osangalala. Koma atumiki a Yehovafe timadziwa kuti zimenezi si zoona. Timakhulupirira mawu a Yesu akuti: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Ndalama sizingatithandize kuti tikhale osangalala. Tikutero chifukwa chakuti ndalama sizingathandize munthu kuti azikhala ndi mtendere wamumtima, akhale ndi anzake enieni kapenanso kuti adzapeze moyo wosatha. N’zoona kuti timafunika ndalama komanso zinthu zina kuti tikhale ndi moyo. Koma Yesu anatiphunzitsa kuti munthu amakhala wosangalala ngati ali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu komanso ngati amaona kuti chofunika kwambiri ndi kulambira Yehova. (Mateyu 5:3; 6:22) Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi ndayamba kuona ndalama ngati mmene anthu am’dzikoli amazionera? Kodi ndimangokhalira kuganizira komanso kulankhula za ndalama?’—Luka 6:45; 21:34-36; 2 Yohane 6.
17. Kodi kupewa mzimu wa dzikoli kungakuthandizeni bwanji?
17 Mtima wathu wonse ukakhala pa kutumikira Yehova n’kumapewa maganizo a anthu am’dzikoli pa nkhani ya ndalama, moyo wathu umakhala waphindu. (Mateyu 11:29, 30) Timakhutira ndi zimene tili nazo ndiponso timakhala ndi mtendere wa mumtima. (Mateyu 6:31, 32; Aroma 15:13) Komanso timachepetsa kuda nkhawa. (Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Timasangalala chifukwa chokhala ndi mtima wopatsa. (Machitidwe 20:35) Komanso timakhala ndi nthawi yambiri yocheza ndiponso kuchita zinthu zina ndi anthu amene timawakonda. Ndiponso timagona tulo tabwino.—Mlaliki 5:12.
TIZINYAMULA “ZIDA ZONSE ZANKHONDO”
18. Kodi Satana akufunitsitsa kuchita chiyani?
18 Satana akufunitsitsa kuti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tiyenera kuyesetsa kuuteteza. Tili pa nkhondo yolimbana ndi “makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Satana ndi ziwanda zake safuna kuti tizisangalala komanso kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. (1 Petulo 5:8) Adani amphamvu amenewa akulimbana nafe kwambiri, koma Yehova angatithandize kuti tipambane.
19. Fotokozani zimene lemba la Aefeso 6:14-18 limanena zokhudza ‘zida zankhondo’ zimene Mulungu watipatsa.
19 Kale asilikali akamapita kunkhondo ankavala ‘zida zankhondo’ pofuna kudziteteza. Ifenso tiyera kuvala ‘zida zankhondo’ zimene Yehova watipatsa chifukwa zingatiteteze. (Aefeso 6:13) Zida zimenezi zatchulidwa pa Aefeso 6:14-18. Lembali limati: “Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi m’chiuno mwanu, mutavalanso chodzitetezera pachifuwa chachilungamo, mapazi anu mutawaveka nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere. Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro, chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Komanso landirani chisoti cholimba chachipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu. Pamene mukutero, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero.”
20. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘zida zankhondo’ zimene Mulungu watipatsa zitithandize?
20 Msilikali akaiwala kuvala chida china, mbali ina ya thupi lake inkakhala yosatetezeka. Zikatero adani ake ankatha kumubaya pamalo osatetezekawo. Ifenso ngati tikufuna kuti titetezeke, tizikumbukira kuvala “zida” zonse. Tizichita zimenezi nthawi zonse komanso tizionetsetsa kuti zida zathu sizakutha. Nkhondo yathu ipitirira mpaka pamene dziko loipali lidzawonongedwe komanso mpaka Satana ndi ziwanda zake adzachotsedwe. (Chivumbulutso 12:17; 20:1-3) Choncho ngati tikulimbana ndi zilakolako zoipa kapena tikuyesetsa kuti tithetse vuto linalake, tisafooke.—1 Akorinto 9:27.
21. Kodi tingatani kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi Mdyerekezi?
21 Patokha sitingapambane pa nkhondo yolimbana ndi Mdyerekezi. Koma Yehova angatithandize kuti tipambane. Kuti tikhalebe okhulupirika, tizipemphera kwa Yehova, tiziphunzira Mawu ake komanso tizisonkhana ndi abale ndi alongo athu. (Aheberi 10:24, 25) Zinthu zimenezi zingatithandize kuti tisasiye kutumikira Yehova mokhulupirika. Zingatithandizenso kuti tizikhala okonzeka kuteteza chikhulupiriro chathu.
TIZIKHALA OKONZEKA KUTETEZA CHIKHULUPIRIRO CHATHU
22, 23. (a) Kodi tingatani kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kuteteza chikhulupiriro chathu? (b) Kodi munkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
22 Tiyenera kukhala okonzeka nthawi zonse kuti tizitha kuteteza chikhulupiriro chathu. (Yohane 15:19) Pa nkhani zina, a Mboni za Yehova amachita zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri akuchita. Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimadziwadi chifukwa chake timachita zimenezi? Kodi ndimakhulupirira kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona? Nanga ndimakhulupirira kuti kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amanena zoona? Kodi ndimanyadira kukhala wa Mboni za Yehova? (Salimo 34:2; Mateyu 10:32, 33) Kodi ndingathe kufotokozera ena zimene ndimakhulupirira?’—Mateyu 24:45; Yohane 17:17; werengani 1 Petulo 3:15.
23 Nthawi zambiri timadziwiratu zoyenera kuchita kuti tisakhale ku mbali ya dzikoli. Koma nthawi zina sizikhala zodziwikiratu. Satana amagwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana n’cholinga choti atikole. Chinthu china chimene amagwiritsa ntchito ndi zosangalatsa. Ndiye kodi tingatani kuti tizisankha mwanzeru zosangalatsa? Munkhani yotsatira tidzakambirana yankho la funso limeneli.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA
Pewani Kutengera Maganizo a M’dzikoli
Tonsefe tiyenera kusamala kuti maganizo a m’dzikoli asatisokoneze. Onani zitsanzo 5 za maganizo a m’dzikoli.
KODI MUNGATANI KUTI MULUNGU AZIKUKONDANI?