MUTU 2

Mungatani Kuti Muzikhala Ndi Chikumbumtima Chabwino?

Mungatani Kuti Muzikhala Ndi Chikumbumtima Chabwino?

“Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”​—1 PETULO 3:16.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani timafunika chinthu chotitsogolera tikakhala kumalo achilendo? (b) Kodi Yehova anatipatsa chiyani kuti chizititsogolera?

TIYEREKEZE kuti mukuyenda m’chipululu chachikulu ndipo inuyo n’koyamba kudutsa m’chipululu chimenecho. Kenako kukuyamba kuwomba chimphepo champhamvu chomwe chikupangitsa kuti musokonezeke n’kusowa kolowera. Zimenezi zingachititse kuti musochere. Ndiye kodi mungatani? Mungafunike munthu woti akutsogolereni kapena chinthu chomwe chingakuthandizeni kudziwa koyenera kupita. Zinthu zimene zingakuthandizeni ndi monga kampasi, dzuwa, nyenyezi, mapu kapena GPS. Zimenezi n’zofunika kwambiri chifukwa zingachititse kuti musafere m’chipululumo.

2 Tonsefe timakumana ndi mavuto ndipo nthawi zina tingasokonezeke chifukwa cha mavutowo. Choncho Yehova anatipatsa chikumbumtima kuti chizititsogolera. (Yakobo 1:17) M’mutuwu tikambirana mafunso awa: Kodi chikumbumtima n’chiyani, nanga chimagwira ntchito bwanji? Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu? N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira chikumbumtima cha ena? Nanga kodi kukhala ndi chikumbumtima chabwino n’kothandiza bwanji?

KODI CHIKUMBUMTIMA NDI CHIYANI NANGA CHIMAGWIRA NTCHITO BWANJI?

3. Kodi chikumbumtima n’chiyani?

3 Chikumbumtima ndi mphatso yapadera kwambiri imene Yehova anatipatsa. Chimatithandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chikumbumtima” amatanthauza “kudzidziwa wekha.” Chikumbumtima chathu chikamagwira ntchito bwino, chingatithandize kudzifufuza kuti tidziwe kuti ndife anthu otani. Chingatithandizenso kudziwa bwino zimene timaganiza komanso mmene timamvera. Chikumbumtima chingatithandizenso kuti tizichita zabwino, n’kumapewa zoipa. Chimapangitsanso kuti tizisangalala tikachita zabwino kapena tizidziimba mlandu tikachita zoipa.​—Onani Mawu Akumapeto 5.

4, 5. (a) N’chiyani chinachitika Adamu ndi Hava atanyalanyaza chikumbumtima chawo? (b) Kodi chikumbumtima chimagwira ntchito bwanji? Perekani zitsanzo za m’Baibulo.

4 Munthu aliyense angasankhe kumvera chikumbumtima chake kapena ayi. Adamu ndi Hava sanamvere chikumbumtima chawo ndipo zinachititsa kuti achimwe. Kenako anayamba kudziimba mlandu koma munali m’mbuyo mwa alendo. Tikutero chifukwa chakuti anali atasonyeza kale kuti sanafune kumvera Mulungu. (Genesis 3:7, 8) Ngakhale kuti onse anali ndi chikumbumtima changwiro ndipo ankadziwa kuti kusamvera Yehova n’kulakwa, anasankha kunyalanyaza chikumbumtima chawocho.

5 Koma pali anthu ambiri omwe anasankha kumvera chikumbumtima chawo ngakhale kuti sanali angwiro. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Yobu. Iye ankasankha kuchita zinthu zoyenera, choncho anati: “Mtima wanga sudzandinyoza [kapena kuti kundiimba mlandu] masiku anga onse.” (Yobu 27:6) Pamene Yobu ananena kuti “mtima” ankatanthauza chikumbumtima chake, chomwe chinkamuthandiza kudziwa zabwino ndi zoipa. Pa nthawi ina Davide ananyalanyaza chikumbumtima chake ndipo sanamvere Yehova. Koma kenako anazindikira kuti walakwitsa ndipo “anavutika mumtima mwake.” (1 Samueli 24:5) Apa ndiye kuti chikumbumtima cha Davide chinkamuuza kuti wachita zolakwika. Munthu akamvera chikumbumtima chake chimene chikumuimba mlandu, ulendo wina amapewa kudzachitanso zomwezo.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu onse anapatsidwa chikumbumtima?

6 Ngakhale anthu amene salambira Yehova, nthawi zambiri amadziwa zoyenera ndi zosayenera. Baibulo limati: “Maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomereza.” (Aroma 2:14, 15) Mwachitsanzo, anthu ambiri amadziwa kuti kuba komanso kupha munthu n’kulakwa. Choncho tingati mosadziwa amatsatira chikumbumtima chimene Yehova anawapatsa, chomwe chimawathandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Akamachita zimenezi, amakhalanso kuti mosadziwa akutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene Yehova amatipatsa kuti zizitithandiza kusankha zoyenera.

7. N’chiyani chingapangitse kuti chikumbumtima chathu chitinamize?

7 Koma nthawi zina chikumbumtima chathu chingatinamize. Izi zingachitike ngati chawonongeka ndi maganizo olakwika amene anthu ochimwafe timakhala nawo, ndipo chingamatilole kuchita zolakwika. Komatu chikumbumtima chabwino sichibwera chokha. (Genesis 39:1, 2, 7-12) Timafunika kuchita kuchiphunzitsa. Kuti tithe kuchita zimenezi, Yehova amatipatsa mzimu wake woyera komanso mfundo za m’Baibulo. (Aroma 9:1) Koma kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu?

KODI TINGAPHUNZITSE BWANJI CHIKUMBUMTIMA CHATHU?

8. (a) Kodi maganizo athu amakhudza bwanji chikumbumtima chathu? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti tisanasankhe zochita?

8 Anthu ena amaganiza kuti kumvera chikumbumtima chawo kumatanthauza kumangotsatira zimene mtima wawo ukufuna. Amaganiza kuti angathe kuchita chilichonse chimene akuona kuti n’chabwino. Koma tizikumbukira kuti ndife ochimwa ndipo maganizo athu angathe kutisocheretsa. Komanso kumangotsatira maganizo athu kungachititse kuti chikumbumtima chathu chisamagwire bwino ntchito. Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?” (Yeremiya 17:9) Izi zikusonyeza kuti tingayambe kuganiza kuti zinthu zoipa ndi zabwino. Mwachitsanzo, Paulo asanakhale Mkhristu ankazunza anthu a Mulungu ndipo ankaganiza kuti akuchita zabwino. Chikumbumtima chake sichinkamuuza kuti akuchita zolakwika. Koma kenako anati: “Yehova ndiye amandifufuza.” (1 Akorinto 4:4; Machitidwe 23:1; 2 Timoteyo 1:3) Ataphunzira kuti Yehova sankasangalala ndi zimene ankachitazo, anazindikira kuti akufunika kusintha. Choncho tisanachite chilichonse, tizidzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova angasangalale nditachita chiyani?’

9. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani?

9 Ngati timakonda munthu wina, sitifuna kumukhumudwitsa. Popeza timakonda Yehova, timayesetsa kuti tisamukhumudwitse ndipo zimenezi zimatheka ngati timamuopa. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Nehemiya. “Chifukwa choopa Mulungu,” sankagwiritsa ntchito udindo wake pofuna kulemera. (Nehemiya 5:15) Nehemiya sankafuna kuchita chilichonse chimene chikanakhumudwitsa Yehova. Ifenso tizipewa kuchita zinthu zolakwika zimene zingakhumudwitse Yehova. Tikamawerenga Baibulo timadziwa zimene Yehova amasangalala nazo.​—Onani Mawu Akumapeto 6.

10, 11. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani ya mowa?

10 Mwachitsanzo, Mkhristu angafunike kusankha kumwa mowa kapena ayi. Koma pali mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingamuthandize kusankha zoyenera pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, Baibulo sililetsa kumwa mowa. Ndipotu limati vinyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Salimo 104:14, 15) Komabe Yesu anauza otsatira ake kuti sayenera “kumwa kwambiri.” (Luka 21:34) Komanso Paulo anauza Akhristu kuti azipewa “maphwando aphokoso.” (Aroma 13:13) Ananenanso kuti oledzera “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10.

11 Mkhristu ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti mowa ndi wofunika kwambiri? Kodi ndimasangalala pokhapokha ndikamwa mowa? Nanga ndimafunika kumwa mowa kuti ndichotse manyazi? Kodi ndimatha kudziletsa kuti ndisamwe mowa wambiri kapena kuti ndisamamwe pafupipafupi? * Nanga kodi ndimasangalala kucheza ndi anzanga ngakhale zitakhala kuti palibe mowa?’ Tiyenera kupempha Yehova kuti azitithandiza kusankha bwino zochita. (Werengani Salimo 139:23, 24.) Tikamachita zimenezi timakhala kuti tikuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitsatira mfundo za m’Baibulo. Komabe tiyeneranso kuganizira chikumbumtima cha ena.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUGANIZIRA CHIKUMBUMTIMA CHA ENA?

12, 13. (a) N’chiyani chingachititse kuti anthu azisiyana pa nkhani ya chikumbumtima? (b) Kodi tingatani ngati chikumbumtima chathu chikusiyana ndi cha wina?

12 Anthufe timasiyana pa nkhani ya chikumbumtima. Chikumbumtima chanu chingakuloleni kuchita zinthu zina zimene cha wina sichingamulole. Mwachitsanzo, inuyo mukhoza kusankha kumwa mowa, koma wina angaone kuti sakuyenera kuchita zimenezo. Kodi n’chifukwa chiyani anthufe timaganiza mosiyana pa nkhani ngati zimenezi?

Chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chingakuthandizeni kusankha kumwa mowa kapena ayi

13 Nthawi zina chimakhala chifukwa cha kumene munthuyo anakulira, mmene banja lawo limaonera nkhaniyo komanso zimene wakumana nazo pa moyo wake. Ndipotu anthu ena amene anavutika kwambiri kuti asiye mowa, amasankha kuti asamamwenso ngakhale pang’ono. (1 Mafumu 8:38, 39) Ndiye ngati mwamupatsa munthu wina mowa ndipo wakana, kodi muyenera kuchita chiyani? Kodi muyenera kukhumudwa, kapena kumukakamiza? Kapena kodi muyenera kumuumiriza kuti akuuzeni chifukwa chake akukana? Ayi, muyenera kulemekeza chikumbumtima chake.

14, 15. (a) Kodi ndi nkhani iti yomwe inachitika mu nthawi ya Paulo? (b) Kodi Paulo anapereka malangizo otani?

14 Mu nthawi ya mtumwi Paulo panachitika nkhani ina yomwe imasonyeza kuti anthufe timasiyana pa nkhani ya chikumbumtima. Nyama imene inkatsala akamapereka nsembe kwa mafano inkagulitsidwa pamsika. (1 Akorinto 10:25) Paulo ankaona kuti palibe vuto kugula komanso kudya nyama imeneyo, chifukwa chakudya chilichonse chimachokera kwa Yehova. Koma abale ena amene poyamba ankalambira mafano ankaona kuti n’kulakwa kudya nyama yoteroyo. Kodi Paulo anaganiza kuti, ‘Zawo izo, ine chikumbumtima changa sichikundiletsa kudya nyama imeneyi. Ndili ndi ufulu wodya chilichonse chimene ndikufuna’?

15 Ayi. Iye ankaona kuti abale ake ndi ofunika kwambiri moti analolera kusiya kuchita zinthu zimene anali ndi ufulu wozichita. Paulo ananena kuti sitiyenera “kumadzikondweretsa tokha.” Ananenanso kuti: “Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:1, 3) Choncho mofanana ndi Yesu, Paulo ankaona kuti zofuna za abale ake ndi zofunika kwambiri kuposa zake.​—Werengani 1 Akorinto 8:13; 10:23, 24, 31-33.

16. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza abale athu pa zimene chikumbumtima chawo chikuwalola kuchita?

16 Nanga kodi tingatani ngati chikumbumtima cha wina chikumulola kuchita zinthu zimene ifeyo tikuona kuti n’zolakwika? Tiyenera kusamala kuti tisamuweruze. Sitiyeneranso kuumirira kuti ifeyo ndi amene tikulondola ndipo iye akulakwitsa. (Werengani Aroma 14:10.) Yehova anatipatsa chikumbumtima kuti chizitiweruza ifeyo osati kuti tiziweruzira ena. (Mateyu 7:1) Tizisamala kuti tisagawanitse mpingo chifukwa cha zinthu zimene aliyense amayenera kusankha mogwirizana ndi chikumbumtima chake. M’malomwake tiyenera kuyesetsa kuti tonse mumpingo tizikondana komanso tizigwirizana.​—Aroma 14:19.

KUKHALA NDI CHIKUMBUMTIMA CHABWINO N’KOTHANDIZA

17. Kodi anthu ena ali ndi chikumbumtima chotani?

17 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.” (1 Petulo 3:16) Munthu akapitiriza kunyalanyaza mfundo za Yehova, chikumbumtima chake chimasiya kumuchenjeza akafuna kuchita zosayenera. Paulo ananena kuti chikumbumtima cha munthu wotereyu chimakhala “ngati chipsera chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.” (1 Timoteyo 4:2) Kodi inuyo munayamba mwapsa kwambiri? Munthu akapsa kwambiri amakhala ndi chipsera chomwe sichimva kukhudza kapena kuwawa. Munthu akapitiriza kuchita zolakwika, chikumbumtima chake chimakhala ngati chipsera chimenechi ndipo pakapita nthawi chimasiya kugwira ntchito.

Chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chimatithandiza kuti tizichita zoyenera komanso kuti tikhale ndi mtendere wamumtima

18, 19. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti munthu azidziimba mlandu? (b) Kodi tingatani ngati tikudziimbabe mlandu pa zolakwa zimene tinachita kalekale ndipo tinalapa?

18 Tikamadziimba mlandu ndiye kuti chikumbumtima chathu chimakhala chikutiuza kuti tachita zinazake zolakwika. Izi zingatithandize kuti tizindikire zimene talakwitsazo n’kupeza njira yosinthira. Tiyenera kuphunzirapo kanthu pa zimene talakwitsa n’kuyesetsa kuti tisadzachitenso. Mwachitsanzo, Mfumu Davide atachimwa, chikumbumtima chake chinamuthandiza kuti alape. Anazindikira kuti anachita zoipa kwambiri ndipo anatsimikiza mtima kuti sadzachitanso zimenezo. Ataganizira zimene zinamuchitikira, anati Yehova ndi ‘wabwino ndipo ndi wokonzeka kukhululuka.’​—Salimo 51:1-19; 86:5; onani Mawu Akumapeto 7.

19 Koma anthu ena amadziimbabe mlandu pa zolakwa zimene anachita kalekale ndipo analapa. Izi zingapangitse kuti azidziona kuti ndi achabechabe. Ngati inunso mumamva chonchi nthawi zina, kumbukirani kuti n’zosatheka kusintha zimene zinachitikazo. Komabe kaya munachita zimenezi mwadala kapena ayi, dziwani kuti Yehova anakukhululukirani ndipo anafufuta machimo anuwo. Iye samakuonani kuti ndinu munthu wochimwa ndipo amaona kuti panopa mukuchita zoyenera. Mtima wanu ukhoza kumakuimbanibe mlandu, koma dziwani kuti Baibulo limati: “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (Werengani 1 Yohane 3:19, 20.) Zimenezi zikutanthauza kuti chikondi cha Yehova komanso mtima wake wokhululuka ndi zamphamvu kuposa mtima wathu wodziimba mlandu kapena wochita manyazi chifukwa cha zimene tinalakwitsa. Choncho musamakayikire kuti Yehova anakukhululukirani. Munthu akavomereza kuti Yehova anamukhululukira, amakhala ndi mtendere wamumtima ndipo amayambanso kumutumikira mosangalala.​—1 Akorinto 6:11; Aheberi 10:22.

20, 21. (a) Kodi bukuli ndi lothandiza bwanji? (b) Kodi Yehova anatipatsa ufulu wotani, ndipo tiyenera kuugwiritsa ntchito bwanji?

20 Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kuphunzitsa chikumbumtima chanu. Chikumbumtima choterocho chingamakuchenjezeni mukafuna kuchita zolakwika ndipo chingakutetezeni m’dziko loipali. Chingakuthandizeninso kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo. Koma sikuti m’bukuli muli mndandanda wa malamulo onena za zimene muyenera kuchita pa nkhani iliyonse. Akhristufe timatsatira “chilamulo cha Khristu” chomwe ndi chochokera pa mfundo za Mulungu. (Agalatiya 6:2) M’Baibulo mukakhala kuti mulibe lamulo lachindunji pa nkhani inayake, sitiona kuti ndi chifukwa choti tichitire zolakwika. (2 Akorinto 4:1, 2; Aheberi 4:13; 1 Petulo 2:16) M’malomwake timagwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha, n’kuchita zinthu zosonyeza kuti timakonda Yehova.

21 Tikamaganizira mfundo za m’Baibulo n’kumazitsatira pa moyo wathu, timaphunzira kugwiritsa ntchito ‘mphamvu zathu za kuzindikira.’ Zimenezi zimatithandizanso kuti tiziona zinthu mmene Yehova amazionera. (Aheberi 5:14) Tikatero chikumbumtima chathu chimatithandiza kuti tizichita zoyenera ndipo izi zingachititse kuti Mulungu apitirize kutikonda.

^ ndime 11 Madokotala ambiri amati zidakwa ndi zimene zimavutika kwambiri kudziletsa kuti zisamwe mowa wambiri. Choncho amati njira yabwino kwa anthu oterewa ndi kusiyiratu kumwa mowa.