MUTU 14

Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo

Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo

“Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—AHEBERI 13:18.

1, 2. Kodi Yehova amamva bwanji tikamayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo?

TIYEREKEZERE kuti kamnyamata kena kakuchokera kusukulu ndipo katola kachikwama ka ndalama. M’malo mongosunga kachikwamako, mnyamatayo akukapereka kwa mwiniwake. Amayi ake a mwanayo atamva zimenezi akusangalala kwambiri podziwa kuti mwana wawoyo wachita zinthu mwachilungamo.

2 Makolo ambiri amasangalala akaona kuti ana awo amachita zinthu mwachilungamo. Atate wathu wakumwamba ndi “Mulungu wachoonadi” ndipo amasangalala tikamachita zinthu mwachilungamo. (Salimo 31:5) Nafenso timafuna kumusangalatsa ndipo timayesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Tiyeni tikambirane mbali 4 zofunika kwambiri pa moyo wathu, zimene tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu zonse mwachilungamo. Kenako tikambirana ubwino wochita zinthu mwachilungamo.

TISAMADZINAMIZE

3-5. (a) Kodi munthu angadzinamize bwanji? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tisamadzinamize?

3 Kuti tizitha kuchitira ena zinthu mwachilungamo, tiyenera kupewa kudzinamiza tokha. Kuchita zimenezi sikophweka. Mu nthawi ya atumwi, abale a ku Laodikaya ankadzinamiza kuti akusangalatsa Mulungu. (Chivumbulutso 3:17) Nafenso titapanda kusamala tingathe kumadzinamiza kuti tikuchita zabwino.

4 Mtumwi Yakobo analemba kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” (Yakobo 1:26) Kungakhale kudzinamiza kuganiza kuti ngati timachita zabwino, ndiye kuti Mulungu sangakhumudwe nafe ngakhale titamanama kapena kulankhula mwamwano. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamadzinamize?

5 Tikayang’ana pagalasi timaona mmene tikuonekera kunja. Koma tikamawerenga Baibulo timazindikira mmene mtima wathu ulili. Baibulo lingatithandize kudziwa zimene timachita bwino ndi zimene timalakwitsa. Limatithandizanso kudziwa zimene tikufunika kusintha pa zimene timaganiza, kuchita komanso kulankhula. (Werengani Yakobo 1:23-25.) Koma tikamadzinamiza kuti palibe chimene timalakwitsa, sitingakonze zolakwikazo. Tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo kuti tidziwe kuti ndife munthu wotani. (Maliro 3:40; Hagai 1:5) Pemphero nalonso lingatithandize. Tingapemphe Yehova kuti atifufuze ndiponso atithandize kudziwa zomwe timalakwitsa, n’cholinga choti tisinthe. (Salimo 139:23, 24) Tizikumbukira kuti “munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”​—Miyambo 3:32.

MUZICHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO M’BANJA

6. N’chifukwa chiyani mwamuna komanso mkazi ayenera kuchita zinthu mwachilungamo m’banja?

6 Kuchita zinthu mwachilungamo n’kofunika kwambiri m’banja. Mwamuna ndi mkazi wake akamalankhulana momasuka, aliyense amakhulupirira mnzake ndipo amaona kuti ndi wotetezeka. Pali zinthu zambiri zimene zingasonyeze kuti munthu sakuchita zinthu mwachilungamo m’banja. Mwachitsanzo, munthu wapabanja angayambe kukopana ndi munthu wina, kuonera zolaula kapena kuyamba chibwenzi. Koma munthu wina amene analemba nawo Masalimo anati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” (Salimo 26:4) Ngati simuchita zinthu mwachilungamo m’banja, ngakhale pa zimene mumaganiza, banja lanu lingathe kusokonekera.

Muzipewa chilichonse chomwe chingasokoneze banja lanu

7, 8. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji Baibulo pophunzitsa ana anu kuti azichita zinthu mwachilungamo?

7 Nawonso ana ayenera kuphunzira kuti kuchita zinthu mwachilungamo n’kofunika. Makolo angagwiritse ntchito Baibulo pophunzitsa ana awo zimenezi. M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene sanachite zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, Akani anaba, Gehazi ananama kuti apeze ndalama komanso Yudasi ankaba ndalama ndipo kenako anagulitsa Yesu ndi ndalama zasiliva 30.​—Yoswa 6:17-19; 7:11-25; 2 Mafumu 5:14-16, 20-27; Mateyu 26:14, 15; Yohane 12:6.

8 M’Baibulo mulinso zitsanzo za anthu amene anachita zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, Yakobo anauza ana ake kuti akabweze ndalama, Yefita ndi mwana wake anakwaniritsa zomwe anamulonjeza Mulungu komanso Yesu ankachita zinthu mwachilungamo ngakhale pamene zinthu sizinali bwino. (Genesis 43:12; Oweruza 11:30-40; Yohane 18:3-11) Zitsanzo zimenezi zingathandize ana kuti amvetse ubwino wochita zinthu mwachilungamo.

9. Makolo akamachita zinthu mwachilungamo, kodi zimathandiza bwanji ana awo?

9 Makolo angaphunzire zambiri pa mfundo ya m’Baibulo iyi: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikira kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?” (Aroma 2:21) Ngati makolo amaphunzitsa ana awo zina koma iwo n’kumachita zina, anawo amadziwa. Ngati timauza ana athu kuti azichita zinthu mwachilungamo koma ifeyo sitichita zimenezo, anawo amasokonezeka. Mwachitsanzo, ana akaona kuti makolo awo amanama, ngakhale pa zinthu zazing’ono, nawonso amayamba kuchita chimodzimodzi. (Werengani Luka 16:10.) Koma makolo akamachita zinthu mwachilungamo, ana awo akakula amadzakhalanso makolo achilungamo.​—Miyambo 22:6; Aefeso 6:4.

MUZICHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO MUMPINGO

10. Kodi tingatani kuti tizichita zinthu mwachilungamo mumpingo?

10 Tiyeneranso kuchita zinthu mwachilungamo ndi abale ndi alongo athu. N’zosavuta kuti nkhani zimene timakambirana tsiku ndi tsiku zisinthe n’kukhala miseche. Ngati tikuuza munthu wina nkhani zimene tamva kwa wina koma sitikudziwa ngati zilidi zoona, tingapezeke kuti tikufalitsa zinthu zabodza. Choncho ndi bwino kuti ‘tizilamulira milomo yathu.’ (Miyambo 10:19) Koma kuchita zinthu mwachilungamo sikutanthauza kuti tiyenera kuuza ena chilichonse chimene tikuganiza, tikudziwa kapena tamva. Ngakhale zitakhala kuti zimene tikufuna kunenazo ndi zoona, ndi bwino osanena ngati sizikutikhudza, ngati palibe chifukwa chozinenera, kapena ngati kuzinena kungakhale kupanda chikondi. (1 Atesalonika 4:11) Anthu ena amalankhula mwamwano ndipo amaganiza kuti palibe vuto bola ngati zimene akunenazo zili zoona. Koma atumiki a Yehovafe timayesetsa kuti nthawi zonse mawu athu azikhala achisomo komanso okoma mtima.​—Werengani Akolose 4:6.

11, 12. (a) Kodi pangakhale mavuto otani ngati munthu amene wachita tchimo sanafotokozere akulu mwachilungamo? (b) Ngati tadziwa kuti mnzathu wachita tchimo lalikulu, kodi tiyenera kupewa maganizo ati, ndipo n’chifukwa chiyani? (c) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife achilungamo m’gulu la Yehova?

11 Yehova anapatsa akulu udindo woti azitithandiza. Koma zimakhala zosavuta kuti akulu atithandize ngati tawafotokozera zinthu mwachilungamo. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati mwadwala ndipo mwapita kuchipatala, kodi mungabisire dokotala zina mwa zizindikiro za matenda anu? N’zodziwikiratu kuti ngati mutachita zimenezi, dokotalayo sangakuthandizeni bwinobwino. N’chimodzimodzinso ngati tachita tchimo lalikulu. Sitiyenera kuuza akulu zabodza zokhudza tchimo lathulo. M’malomwake, tiyenera kuwafotokozera zoona zokhazokha. (Salimo 12:2; Machitidwe 5:1-11) Nanga bwanji ngati mwadziwa kuti mnzanu wachita tchimo lalikulu? (Levitiko 5:1) Kodi mungaganize kuti: “Ngati ndilidi mnzake, ndikuyenera kumusungira chinsinsi?” Kapena kodi mungakumbukire kuti akulu ayenera kudziwa za nkhaniyo kuti amuthandize kukonzanso ubwenzi wake ndi Yehova?​—Aheberi 13:17; Yakobo 5:14, 15.

12 Komanso tiyenera kuchita zinthu mwachilungamo m’gulu la Yehova tikamalemba malipoti a mu utumiki kapena malipoti ena. Tiyeneranso kulemba zoona zokhazokha tikamalemba fomu yofunsira upainiya kapena utumiki wina uliwonse.​—Werengani Miyambo 6:16-19.

13. Kodi tingasonyeze bwanji chilungamo ngati tinalemba kapena kulembedwa ntchito ndi Mkhristu mnzathu?

13 Akhristu sayenera kuphatikiza nkhani zamalonda ndi zolambira. Mwachitsanzo, sitiyenera kuchita malonda pa Nyumba ya Ufumu kapena mu utumiki. Komanso tikalemba ntchito Mkhristu mnzathu kapena Mkhristu mnzathu akatilemba ntchito sitiyenera kupezerapo mwayi. Mwachitsanzo, ngati mwalemba ntchito m’bale kapena mlongo, muyenera kumulipira pa nthawi yake, kumupatsa ndalama zonse zimene munagwirizana komanso kumuchitira zonse zimene malamulo a boma amafuna. Izi zingaphatikizepo inshulansi ya kuchipatala ndiponso masiku a holide. (1 Timoteyo 5:18; Yakobo 5:1-4) Komanso ngati mwalembedwa ntchito ndi m’bale kapena mlongo, musamayembekezere kuti azikukonderani. (Aefeso 6:5-8) Muzionetsetsa kuti mukugwira ntchito yonse komanso mukugwira maola onse amene munagwirizana.​—2 Atesalonika 3:10.

14. Kodi Akhristu ayenera kuchita chiyani asanayambe kuchitira limodzi bizinesi?

14 Nanga bwanji ngati mukufuna kuchita bizinesi ndi m’bale kapena mlongo? Izi zingaphatikizepo kukongozana ndalama. Pa zinthu ngati zimenezi, ndi bwino kutsatira mfundo ya m’Baibulo iyi: Muyenera kulemba zonse zimene mwagwirizana. Mneneri Yeremiya atagula munda, analemba zikalata ziwiri zofotokoza zomwe anagwirizana, anapeza mboni zoti zisaine chikalata chinacho ndipo kenako anasunga zikalata zonsezo. (Yeremiya 32:9-12; onaninso Genesis 23:16-20) Anthu ena amaganiza kuti kulemba zimene agwirizana kungasonyeze kuti akumukayikira m’bale wawoyo. Koma zimenezi si zoona. Kulemba zimene mwagwirizana kungathandize kuti pasadzakhale kusamvana, kukhumudwitsana komanso mikangano. Ngakhale pa nkhani za bizinezi muzikumbukira kuti mtendere wa mumpingo ndi wofunika kwambiri kuposa kupeza ndalama.​—1 Akorinto 6:1-8; onani Mawu Akumapeto 30.

TIZICHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO NDI ANTHU A M’DZIKOLI

15. Kodi Yehova amamva bwanji anthu akamachita zachinyengo pa malonda?

15 Tiyenera kumachitira aliyense chilungamo kuphatikizapo anthu omwe si a Mboni. Yehova amafuna kuti tizichita zinthu mwachilungamo. “Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova, koma mwala woyezera, wolemera mokwanira, umam’sangalatsa.” (Miyambo 11:1; 20:10, 23) Kale anthu ankagwiritsa ntchito kwambiri masikelo pochita malonda. Koma amalonda ena ankagwiritsa ntchito masikelo achinyengo ndipo ankabera makasitomala awo. Masiku anonso amalonda ambiri amachita chinyengo. Yehova ankadana ndi chinyengo kalelo ndipo amadana nachobe masiku ano.

16, 17. Kodi ndi zinthu zachinyengo ziti zomwe tiyenera kupewa?

16 Tonsefe timakumana ndi zinthu zina zomwe zingatipangitse kuti tisachite zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, kodi timatani tikamafunsira ntchito, tikamalemba mafomu a boma kapena tikamalemba mayeso? Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto kunama, kukokomeza zinthu kapena kupereka mayankho opangitsa munthu kumva zina osati zomwe tikutanthauza. Koma zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza ano anthu adzakhala ‘odzikonda, okonda ndalama komanso osakonda zabwino.’​—2 Timoteyo 3:1-5.

17 Nthawi zina zimaoneka ngati anthu omwe amachita zachinyengo zinthu zimawayendera bwino. (Salimo 73:1-8) Mkhristu akhoza kuchotsedwa ntchito, kuberedwa ndalama kapena kuchitiridwa zinthu zoipa pa ntchito chifukwa chakuti amayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Komabe kuchita zinthu mwachilungamo kuli ndi ubwino wake. N’chifukwa chiyani tikutero?

UBWINO WOCHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO

18. N’chifukwa chiyani kukhala ndi mbiri yabwino n’kofunika kwambiri?

18 Kukhala ndi mbiri yakuti ndife odalirika, okhulupirika komanso achilungamo, ndi chinthu cha mtengo wapatali kwambiri ndipo ndi anthu ochepa m’dzikoli omwe ali ndi mbiri imeneyi. Tonsefe tikhoza kuyesetsa kuti tikhale ndi mbiri yabwino. (Mika 7:2) Anthu ena akhoza kumakusekani komanso kukunenani kuti ndinu wopusa chifukwa choti mumayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Komabe anthu ena angaone zomwe mumachita ndipo angayambe kukukhulupirirani. Padziko lonse a Mboni za Yehova amadziwika kuti amachita zinthu mwachilungamo. Anthu ena amakonda kulemba ntchito a Mboni chifukwa chakuti amadziwa kuti ndi okhulupirika. Nthawi zina mabwana amachotsa ntchito anthu onse chifukwa cha kusakhulupirika n’kungosiya a Mboni okha.

Tikamagwira ntchito molimbika anthu amalemekeza Yehova

19. Kodi mukamayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo, zimakhudza bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?

19 Kuchita zinthu zonse mwachilungamo kungakuthandizeni kuti muzikhala ndi chikumbumtima chabwino komanso mtendere wa mumtima. Mungafanane ndi Paulo yemwe analemba kuti: “Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona.” (Aheberi 13:18) Koma chofunika kwambiri ndi chakuti Atate wanu wakumwamba, Yehova, amaona kuti mukuyesetsa kuchita zinthu zonse mwachilungamo ndipo amayamikira.​—Werengani Salimo 15:1, 2; Miyambo 22:1.