MUTU 9
“Thawani Dama”
“Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”—AKOLOSE 3:5.
1, 2. Kodi Balamu anatani pofuna kukopa anthu a Mulungu kuti achite zoipa?
MSODZI akafuna kupha nsomba, amapita kumalo amene akuganiza kuti angapeze mtundu wa nsomba zimene akufunazo. Amasankha nyambo yoyenerera kenako amaponya mbedza m’madzi. Akatero amadikira mpaka nsomba itakodwa kumbedzayo ndipo kenako amaikoka mofulumira.
2 Anthunso akhoza kukodwa mwa njira yomweyi. Mwachitsanzo, Aisiraeli atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa anamanga kaye msasa m’chigwa cha Mowabu. Mfumu ya ku Mowabu inalonjeza munthu wina dzina lake Balamu kuti idzamupatsa ndalama zambiri ngati angatemberere Aisiraeli. Atalephera kuwatemberera, anapeza njira imene ikanachititsa kuti Aisiraeli adzibweretsere okha matemberero. Iye anasankha nyambo yabwino. Anatumiza atsikana a ku Mowabu kuti apite kumene Aisiraeli ankakhala kukakopa amuna.—Numeri 22:1-7; 31:15, 16; Chivumbulutso 2:14.
3. Kodi cholinga cha Balamu chinakwaniritsidwa bwanji?
3 Kodi Aisiraeli anakodwadi ndi nyambo imene Balamu anagwiritsa ntchitoyi? Inde. Amuna ambiri “anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.” Anayambanso kulambira milungu yonyenga, kuphatikizapo Baala wa ku Peori, yemwe anali Mulungu wa zogonana. Zimenezi zinachititsa kuti Aisiraeli 24,000 aphedwe atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Numeri 25:1-9.
4. N’chifukwa chiyani Aisiraeli anachita chiwerewere?
4 Kodi n’chifukwa chiyani Aisiraeli ambiri anachita zimene Balamu ankafuna? Ndi chifukwa choti ankangoganizira zofuna zawo ndipo anaiwala zonse zimene Yehova anawachitira. Komatu panali zifukwa zambiri zowachititsa kukhala okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, anawalanditsa ku ukapolo ku Iguputo, ankawapatsa chakudya m’chipululu komanso anawatsogolera mpaka pa nthawiyi pomwe anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Aheberi 3:12) Koma iwo anaiwala zonsezi n’kuyamba kuchita chiwerewere. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tisamachite dama, mmene ena mwa iwo anachitira dama, [n’kuphedwa].”—1 Akorinto 10:8.
5, 6. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Aisiraeli ali m’chigwa cha Mowabu?
5 Dziko latsopano lili pafupi kwambiri. Choncho tili ngati Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (1 Akorinto 10:11) Masiku ano anthu ambiri a m’dzikoli amakonda kwambiri chiwerewere kuposa mmene zinalili ndi anthu a ku Mowabu, moti n’zosavuta kuti anthu a Mulungu akopeke ndi khalidwe limeneli. Ndipotu chiwerewere ndi nyambo yaikulu imene Mdyerekezi akugwiritsa ntchito masiku ano.—Numeri 25:6, 14; 2 Akorinto 2:11; Yuda 4.
6 Choncho muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi bwino kuti ndisangalale kwa nthawi yochepa ndi khalidwe lachiwerewere m’malo modzasangalala kwamuyaya m’dziko latsopano?’ Tingachite bwino kuyesetsa kuti tizitsatira lamulo la Mulungu lakuti: “Thawani dama.”—1 Akorinto 6:18.
KODI DAMA N’CHIYANI?
7, 8. Kodi dama n’chiyani, nanga ndi loopsa bwanji?
7 Anthu ambiri masiku ano ali ndi khalidwe lotayirira ndipo amachita kuonetseratu kuti salemekeza malamulo a Mulungu okhudza kugonana. M’Baibulo, mawu akuti dama amanena za kugonana kwa pakati pa anthu amene sanakwatirane motsatira Malemba. Zimenezi zikuphatikizapo kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha komanso kugonana ndi nyama. Zikuphatikizaponso kugonana m’kamwa, kumatako, komanso kuseweretsa maliseche a munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wako.—Onani Mawu Akumapeto 23.
8 Baibulo limanena momveka bwino kuti ngati munthu atapitiriza kuchita dama, sangaloledwe kukhalabe mumpingo. (1 Akorinto 6:9; Chivumbulutso 22:15) Komanso munthu amene amachita dama amadzichotsera ulemu ndipo anthu samukhulupirira. Nthawi zonse dama limabweretsa mavuto. Mwachitsanzo, limachititsa kuti munthu asakhale ndi chikumbumtima chabwino komanso atenge mimba yosakonzekera. Limayambitsanso mavuto a m’banja, matenda komanso imfa. (Werengani Agalatiya 6:7, 8.) Ngati munthu ataganizira kaye mavuto amene amabwera chifukwa chochita dama, n’zodziwikiratu kuti sangachite zinthu zomwe zingachititse kuti achite dama. Koma kawirikawiri munthu amachita zimenezi chifukwa choti akungoganizira zokwaniritsa chilakolako chake. Kuonera zolaula n’kumene nthawi zambiri kumachititsa kuti munthu achite dama.
KUONERA ZOLAULA KUMACHITITSA KUTI MUNTHU ACHITE DAMA
9. Kodi kuonera zolaula n’koopsa bwanji?
9 Zithunzi zolaula zimakonzedwa m’njira yoti zizipangitsa munthu kukhala ndi chilakolako chogonana. Masiku ano zinthu zolaula zili ponseponse. Zimapezeka m’magazini, m’mabuku, mu nyimbo, m’mapulogalamu a pa TV komanso pa intaneti. Anthu ambiri amaganiza kuti kuonera zolaula kulibe vuto lililonse koma zoona ndi zoti kuonera zolaula ndi koopsa kwambiri. Zolaula zingachititse kuti munthu azingoganizira zogonana komanso kuti azilakalaka zinthu zina zoipa. Munthu akafika poti sangathenso kukhala osaonera zolaula, angayambe khalidwe loseweretsa maliseche. Munthu wotereyu angakhalenso ndi mavuto a m’banja, mwinanso banja lake lingathe.—Aroma 1:24-27; Aefeso 4:19; onani Mawu Akumapeto 24.
10. Kodi mfundo ya pa Yakobo 1:14, 15 ingatithandize bwanji kupewa dama?
10 Tiyenera kudziwa zimene zingachititse kuti tikopeke n’kuchita dama. Palemba la Yakobo 1:14, 15 pali chenjezo lakuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo. Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” Choncho mukangoyamba kuganizira zinthu zoipa, muziyesetsa kusiya nthawi yomweyo. Mukaona mwangozi chithunzi cholaula pakompyuta kapena pa TV, muziyang’ana kumbali nthawi yomweyo. Muzizimitsa kompyutayo kapena kusintha tchanelo cha TV yanuyo. Musamalole kuti maganizo oipa akhazikike mumtima mwanu chifukwa maganizowo angakule n’kuchititsa kuti muchite zoipa.—Werengani Mateyu 5:29, 30.
11. Kodi Yehova angatithandize bwanji ngati tili ndi maganizo olakwika?
11 Yehova amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziwira. Choncho amadziwa kuti si ife angwiro. Koma amadziwanso kuti tingathe kupewa zilakolako zoipa. Iye amatiuza kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.” (Akolose 3:5) Ngakhale kuti kuchita zimenezi si kophweka, Yehova amatilezera mtima ndipo amatithandiza. (Salimo 68:19) Mwachitsanzo, mnyamata wina anayamba kuonera zolaula komanso kuseweretsa maliseche. Anzake a kusukulu ankaona kuti kuchita zimenezi kulibe vuto ndipo ndi chizindikiro chakuti akukula. Komabe mnyamatayu anati: “Zimene ndinkachitazi zinachititsa kuti chikumbumtima chizindivutitsa komanso kuti ndiyambe khalidwe lachiwerewere.” Iye anazindikira kuti sankayenera kumangotsatira zofuna za mtima wake ndipo ndi thandizo la Yehova anasiya makhalidwe ake oipawa. Ngati nanunso mumakhala ndi maganizo olakwika, muyenera kupempha Yehova kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti musamaganize zolakwika.—2 Akorinto 4:7; 1 Akorinto 9:27.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kuteteza mtima wathu’?
12 Solomo analemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) Mawu akuti “mtima” akutanthauza umunthu wathu wamkati, kapena kuti mmene Yehova amationera. Zinthu zimene timaona zikhoza kukhudza kwambiri mmene timaganizira. Yobu, yemwe anali wokhulupirika, ananena kuti: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Mofanana ndi Yobu, tiyenera kusamala ndi zimene timaona komanso kuganiza. Potengera chitsanzo cha munthu wina amene analemba nawo buku la Masalimo, tizipemphera kwa Mulungu kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.
DINA SANASANKHE ZOCHITA MWANZERU
13. Kodi Dina ankacheza ndi anthu otani?
13 Anzathu angatichititse kuti tizichita zabwino kapena zoipa. Ngati mumacheza ndi anthu amene amatsatira mfundo za Mulungu angakuthandizeni kuti inunso muzitsatira mfundozi. (Miyambo 13:20; werengani 1 Akorinto 15:33.) Zimene zinachitikira Dina zingatithandize kudziwa kufunika kosankha bwino anthu ocheza nawo. Dina anali mwana wa Yakobo, choncho anakulira m’banja la anthu olambira Yehova. Dina sanali munthu wachiwerewere koma anayamba kucheza ndi atsikana a ku Kanani omwe sankalambira Yehova. Akanani ankaona nkhani yogonana mosiyana kwambiri ndi mmene anthu a Mulungu amaionera ndipo ankadziwika ndi khalidwe lachiwerewere. (Levitiko 18:6-25) Nthawi ina Dina akucheza ndi anzake a ku Kananiwo, anakumana ndi mnyamata wina dzina lake Sekemu. Mnyamatayu anakopeka naye kwambiri. Sekemu ankaonedwa kuti “anali wolemekezeka kwambiri” m’banja lakwawo koma sankakonda Yehova.—Genesis 34:18, 19.
14. Fotokozani zimene zinachitikira Dina.
14 Sekemu anachita zimene iyeyo ankaona kuti n’zoyenera. Atakopeka ndi Dina, “anamutenga n’kumugwiririra.” (Werengani Genesis 34:1-4.) Zimene Sekemu anachitazi zinabweretsa mavuto ambiri kwa Dina ndi banja lawo lonse.—Genesis 34:7, 25-31; Agalatiya 6:7, 8.
15, 16. Kodi tingatani kuti tikhale anzeru?
15 Tisadikire kuti mpaka tidzakumane ndi zimene Dina anakumana nazo kuti timvetse mfundo yoti tikamatsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino zinthu zimatiyendera bwino. Paja Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Yesetsani kuti muzidziwa “njira yonse ya zinthu zabwino” ndipo mukatero mudzapewa mavuto ambiri.—Miyambo 2:6-9; Salimo 1:1-3.
16 Kuti tikhale anzeru tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu, kupemphera tisanasankhe zochita komanso kutsatira malangizo amene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa. (Mateyu 24:45; Yakobo 1:5) Anthufe timadziwa kuti si ife angwiro moti nthawi zina timalakwitsa zinthu. (Yeremiya 17:9) Koma kodi mumatani munthu wina akakuchenjezani kuti zimene mukuchita zingachititse kuti muchite dama? Kodi mumakhumudwa kapena mumadzichepetsa n’kutsatira malangizowo?—2 Mafumu 22:18, 19.
17. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti malangizo ochokera kwa Mkhristu mnzathu angatithandize.
17 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mlongo wina amagwira ntchito ndipo mnyamata wina wa kuntchitoko wayamba kusonyeza kuti akumufuna. Kenako akumupempha kuti apitire limodzi kukayenda kumalo enaake. Mnyamatayo satumikira Yehova koma amaoneka kuti ndi wabwino komanso wokoma mtima. Mlongo wina wawaona ali limodzi ndipo akumuchenjeza kuti zimene akuchitazo si zabwino. Kodi mlongo wochenjezedwayo adziikira kumbuyo kapena aona kuti mnzakeyo wachita bwino kumuchenjeza? N’kutheka kuti iye amakonda Yehova ndipo amafuna kuchita zabwino. Koma ngati atapitiriza kuyenda ndi mnyamatayo, kodi tingati ‘akuthawa dama’ kapena ‘akudalira mtima wake’?—Miyambo 22:3; 28:26; Mateyu 6:13; 26:41.
YOSEFE NDI CHITSANZO CHABWINO
18, 19. Kodi Yosefe anatani mkazi wa abwana ake atamukakamiza kuti achite dama, nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti achite zimenezi?
18 Yosefe ali mnyamata, anali kapolo ku Iguputo. Tsiku lililonse mkazi wa abwana ake ankamuuza kuti agone naye. Koma Yosefe ankadziwa kuti kuchita zimenezi n’kulakwa. Iye ankakonda kwambiri Yehova ndipo ankafuna kumusangalatsa. Choncho nthawi zonse mkaziyo akayamba kumukopa kuti agone naye, Yosefe ankakana. Popeza anali kapolo, sakanatha kuchoka panyumbapo. Tsiku lina akugwira ntchito m’nyumba, mkazi wa abwana akeyo anayamba kumukakamiza kuti agone naye. Koma Yosefe ‘anathawira panja.’—Werengani Genesis 39:7-12.
19 Yosefe akanavutika kwambiri kukana mayeserowa akanakhala kuti ankaganizira zinthu zoipa kapena ankawafuna ndi kale akazi a abwana akewo. Koma Yosefe ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kuposa chilichonse, moti anauza mkazi wa abwana akeyo kuti: “Mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”—Genesis 39:8, 9.
20. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova ankasangalala ndi zimene Yosefe ankachita?
20 Ngakhale kuti Yosefe anali kutali ndi anthu a m’banja lake, anakhalabe wokhulupirika ndipo Yehova anamudalitsa. (Genesis 41:39-49) Yehova ankasangalala kwambiri poona kuti Yosefe anali wokhulupirika. (Miyambo 27:11) Nthawi zina kuthawa dama kumakhala kovuta. Koma muzikumbukira mawu awa: “Inu okonda Yehova danani nacho choipa. Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.”—Salimo 97:10.
21. Kodi m’bale wina wachinyamata anatsanzira bwanji Yosefe?
21 Tsiku lililonse atumiki a Yehova amasonyeza molimba mtima kuti ‘amadana ndi choipa’ ndipo ‘amakonda chabwino.’ (Amosi 5:15) Kaya muli ndi zaka zingati, mungathe kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, m’bale wina wachinyamata anakumana ndi mayesero kusukulu. Mtsikana wina anamuuza kuti amuuzire mayeso ndipo akamuuzira agona naye. Ndiye kodi m’baleyu anatani? Anatsanzira Yosefe ndipo anakana kugona ndi mtsikanayo. Iye anati: “Ndinakana nthawi yomweyo. Chifukwa choti ndimayesetsa kukhala wokhulupirika, anthu amandilemekeza.” Munthu akachita dama, amapeza ‘chisangalalo chosakhalitsa’ ndipo nthawi zambiri zotsatira zake zimakhala zopweteka. (Aheberi 11:25) Koma munthu amene amamvera Yehova amakhala wosangalala nthawi zonse.—Miyambo 10:22.
MUZILOLA KUTI YEHOVA AKUTHANDIZENI
22, 23. Kodi Yehova amatithandiza bwanji ngakhale pamene tachita tchimo lalikulu?
22 Satana akhoza kugwiritsa ntchito dama pofuna kuti atikole ndipo amenewa angakhale mayesero ovuta kwambiri. Tonsefe nthawi zina timakhala ndi maganizo olakwika. (Aroma 7:21-25) Koma Yehova amatimvetsa ndipo “amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Koma bwanji ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu la dama? Kodi zikatero ndiye kuti palibenso chimene angachite? Ayi. Ngati walapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova angamuthandize. Mulungu ndi “wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5; Yakobo 5:16; werengani Miyambo 28:13.
23 Komanso Yehova anatipatsa “mphatso za amuna,” omwe ndi akulu amene amatisamalira. (Aefeso 4:8, 12; Yakobo 5:14, 15) Iye anatipatsa akuluwa kuti azitithandiza kuti tikhalenso naye pa ubwenzi.—Miyambo 15:32.
MUZICHITA ZINTHU MWANZERU
24, 25. Kodi kuchita zinthu mwanzeru kungatithandize bwanji kupewa dama?
24 Kuti tizitha kusankha bwino zochita, tiyenera kukhulupirira kuti malamulo a Yehova ndi othandiza. Sitingafune kukhala ngati mnyamata wotchulidwa pa Miyambo 7:6-23. Mnyamatayu anali “wopanda nzeru” moti anachita chiwerewere. Munthu amene ali ndi nzeru zimene zatchulidwa palembali amayesetsa kumvetsa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana ndipo amayesetsa kuti nayenso azikhala ndi maganizo omwewo. Baibulo limati: “Munthu amene wapeza mtima wanzeru akukonda moyo wake. Wopitiriza kusonyeza kuzindikira amapeza zabwino.”—Miyambo 19:8.
25 Kodi inuyo mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti mfundo za Yehova ndi zabwino? Nanga mumakhulupirira kuti kutsatira mfundozi kungakuthandizeni kukhala wosangalala? (Salimo 19:7-10; Yesaya 48:17, 18) Ngati mukukayikirabe, kumbukirani zabwino zonse zimene Yehova wakuchitirani. Baibulo limati: “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.” (Salimo 34:8) Mudzaona kuti mukamachita zimene lembali likunena, mumayamba kumukonda kwambiri Yehova. Yesetsani kuti muzikonda zimene amakonda n’kumadana ndi zimene amadana nazo. Yesetsaninso kuti nthawi zonse muziganizira zinthu zoona, zolungama, zoyera, zachikondi komanso khalidwe labwino lililonse. (Afilipi 4:8, 9) Mukatero mudzakhala ngati Yosefe amene anadalitsidwa chifukwa choti ankatsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu.—Yesaya 64:8.
26. Kodi tikambirana chiyani m’mitu iwiri yotsatira?
26 Kaya muli pa banja kapena ayi, Yehova amafuna kuti muzisangalala. Mitu iwiri yotsatira ikufotokoza zimene tingachite kuti tikhale ndi banja labwino.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA
Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa
Kodi zitsanzo za m’Baibulo zingatithandize bwanji kukhala odziletsa? N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuyesetsa kukhala odziletsa?
KODI MUNGATANI KUTI MULUNGU AZIKUKONDANI?