MUTU 6

Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?

Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?

“Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”​—1 AKORINTO 10:31.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala posankha zosangalatsa?

TIYEREKEZE kuti mukufuna kudya chipatso koma mwazindikira kuti n’chowola mbali imodzi. Kodi mungatani? Kodi mungadyebe chipatsocho, kapena mukhoza kungochitaya? Kapena kodi mungaganize zochotsa mbali yowolayo n’kudya mbali yabwinoyo?

2 Chipatso chimenechi tingachiyerekezere ndi zosangalatsa. Zosangalatsa zina ndi zabwino, koma zambiri ndi zoipa chifukwa zimasonyeza zinthu zachiwerewere, zachiwawa komanso zamizimu. Kodi inuyo mumaona kuti muli ndi ufulu wosankha zosangalatsa zilizonse zomwe mungakonde? Kapena mumaona kuti zosangalatsa zonse ndi zosayenera? Kapena kodi mumayesetsa kusankha zosangalatsa zabwino n’kumapewa zosangalatsa zosayenera?

3. Kodi tiyenera kuganizira chiyani tikamasankha zosangalatsa?

3 Tonsefe timafunikira zosangalatsa. Komabe tiyenera kusankha bwino. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimasankha zimakhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova?’

“CHITANI ZONSE KUTI ZIBWERETSE ULEMERERO KWA MULUNGU”

4. Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti imene ingatithandize posankha zosangalatsa?

4 Tikadzipereka kwa Yehova, timakhala kuti tamulonjeza kuti tizimutumikira ndi mtima wathu wonse. (Werengani Mlaliki 5:4.) Timalonjeza kuti tizichita “zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Zimenezi zikutanthauza kuti timakhala odzipereka kwa Mulungu nthawi zonse, ngakhale pamene tikupuma kapena kuchita zosangalatsa, osati tikakhala pamisonkhano kapena mu utumiki basi.

5. Kodi Yehova amafuna kuti tizimulambira bwanji?

5 Chilichonse chimene timachita pa moyo wathu chimagwirizana ndi kulambira kwathu. Paulo anafotokoza zimenezi pamene anati: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Nayenso Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Timafuna kuti tizipereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Aisiraeli akamapereka kwa Yehova nsembe ya nyama, ankayenera kupereka yathanzi. Nyamayo ikakhala ndi chilema, Mulungu sankailandira. (Levitiko 22:18-20) Masiku anonso, zinthu zina zingalepheretse kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

6, 7. Kodi ndi zosangalatsa ziti zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

6 Yehova amatiuza kuti: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.” (1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Yehova amavomereza kulambira kwathu pokhapokha ngati kuli koyera. (Deuteronomo 15:21) Kulambira kwathu sikungakhale koyera ngati timachita zinthu zimene Yehova amadana nazo. Izi ndi zinthu monga chiwerewere, chiwawa kapena zamizimu. (Aroma 6:12-14; 8:13) Koma tingakhumudwitsenso Yehova ngati timasangalala ndi zinthu zimenezi. Izi zingapangitse kuti kulambira kwathu kukhale kodetsedwa ndiponso kosavomerezeka. Komanso zingasokoneze kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova.

7 Ndiye kodi tingatani kuti tizisankha zosangalatsa mwanzeru? Nanga ndi mfundo ziti zomwe zingatithandize kudziwa zosangalatsa zoyenera ndi zosayenera?

MUZIDANA NDI ZOIPA

8, 9. Kodi ndi zosangalatsa ziti zimene tiyenera kupewa, ndipo n’chifukwa chiyani?

8 Masiku ano pali zosangalatsa zosiyanasiyana. Zina ndi zoyenera kwa Akhristu koma zambiri ndi zosayenera. Choyamba tiyeni tione zosangalatsa zosayenera zomwe tiyenera kupewa.

9 Mafilimu ambiri, mawebusaiti, mapulogalamu a pa TV, masewera a pa kompyuta komanso nyimbo zimasonyeza zinthu zachiwerewere, zachiwawa komanso zamizimu. Nthawi zambiri zinthu zoipa zimaonetsedwa ngati zabwinobwino komanso zosangalatsa. Koma Akhristu amapewa zosangalatsa zonse zomwe sizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10) Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timadana ndi zoipa.​—Salimo 34:14; Aroma 12:9.

10. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tayamba kukonda zosangalatsa zolakwika?

10 Komabe anthu ena amaona kuti zosangalatsa zachiwawa, zachiwerewere kapena zamizimu zilibe vuto lililonse. Iwo amaganiza kuti: ‘Sikuti ineyo ndingachite zinthu zimenezi.’ Koma kumeneku n’kudzinamiza. Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yeremiya 17:9) Ngati timasangalala ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo, kodi tinganene kuti timadana ndi zoipa? Tikayamba kusangalala ndi zinthu zimenezi, m’pamenenso timayamba kuziona kuti zilibe vuto lililonse. Kenako chikumbumtima chathu chimafooka ndipo chimasiya kutichenjeza tikafuna kuchita zinthu zolakwika.​—Salimo 119:70; 1 Timoteyo 4:1, 2.

11. Kodi lemba la Agalatiya 6:7 lingatithandize bwanji posankha zosangalatsa?

11 Baibulo limati: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Choncho ngati timasangalala ndi zinthu zoipa, pakapita nthawi tikhoza kudzazichita. Mwachitsanzo, anthu ena amene ankakonda zosangalatsa zosonyeza anthu akuchita chiwerewere, anachita chiwerewere. Koma Yehova amatipatsa malangizo othandiza kuti tizisankha zosangalatsa zoyenera.

MUZIGWIRITSA NTCHITO MFUNDO ZA M’BAIBULO POSANKHA ZOCHITA

12. N’chiyani chingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani ya zosangalatsa?

12 Monga taonera, pali zosangalatsa zina zimene Yehova amadana nazo, ndipo tiyenera kuzipewa. Koma bwanji ngati sitikudziwa bwinobwino ngati zosangalatsa zinazake zili zoyenera kapena ayi? Yehova sanatipatse mndandanda wa malamulo okhudza zoyenera ndi zosayenera kuonera, kumvetsera kapena kuwerenga. M’malomwake amafuna kuti tizigwiritsa ntchito chikumbumtima chathu chomwe tachiphunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Werengani Agalatiya 6:5.) Yehova anatipatsa mfundo za m’Baibulo ndipo zimatithandiza kudziwa maganizo ake pa nkhani zosiyanasiyana. Mfundo zimenezi zimatithandiza kuphunzitsa chikumbumtima chathu komanso kudziwa “chifuniro cha Yehova.” Choncho tingathe kusankha zinthu zimene zingamusangalatse.​—Aefeso 5:17.

Mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kuti tizisankha zosangalatsa zoyenera

13. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu amasankha zinthu mosiyana pa nkhani ya zosangalatsa? (b) Kodi Akhristu onse ayenera kuchita chiyani?

13 Nthawi zambiri zosangalatsa zimene Mkhristu wina angasankhe, zingasiyane ndi zomwe wina angasankhe. Zili chonchi chifukwa choti anthufe timakonda zinthu zosiyana. Komanso zimene munthu wina angaone kuti n’zoyenera zingakhale zosayenera kwa wina. Komabe Akhristu onse ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti azisankha zinthu moyenera. (Afilipi 1:9) Zimenezi zingatithandize kuti tizipewa zosangalatsa zimene Mulungu amadana nazo.​—Salimo 119:11, 129; 1 Petulo 2:16.

14. (a) Kodi ndi mfundo iti yofunika kuiganizira yokhudza mmene timagwiritsira ntchito nthawi? (b) Kodi Paulo anapereka malangizo otani kwa Akhristu?

14 Mfundo ina yofunika kuiganizira, ndi kuchuluka kwa nthawi imene timachita zosangalatsazo. Ngati nthawi yambiri timakhala tikuchita zosangalatsa, ndiye kuti timaona kuti zosangalatsa n’zofunika kwambiri pa moyo wathu. Koma Akhristufe tiyenera kuona kuti chofunika kwambiri ndi kutumikira Yehova. (Werengani Mateyu 6:33.) Ngati titapanda kusamala, tingawononge nthawi yambiri pochita zosangalatsa. Paulo analangiza Akhristu kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.” (Aefeso 5:15, 16) Choncho tiyenera kudziikira malire pa kuchuluka kwa nthawi imene timachita zosangalatsa ndipo tizionetsetsa kuti kutumikira Yehova kuli pamalo oyamba pa moyo wathu.​—Afilipi 1:10.

15. Kodi tingadziteteze bwanji ku zosangalatsa zomwe zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

15 Taona kuti tiyenera kupewa zosangalatsa zonse zimene tikudziwa kuti Yehova amadana nazo. Koma bwanji zosangalatsa zimene zikutikayikitsa ngati zilidi zabwino? Tiyeneranso kusamala kwambiri ndi zosangalatsa zoterozo. Tiyerekezere kuti mukuyenda mumsewu wa m’mbali mwa phiri. Kodi mungamayende m’mbali mwenimweni kufupi ndi phedi? Ayi. Simungachite zimenezo chifukwa mukudziwa kuti mukhoza kugwera kuphediko. N’chimodzimodzinso ndi zimene tiyenera kuchita tikamasankha zosangalatsa. Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Chotsa phazi lako pa zoipa.” (Miyambo 4:25-27) Choncho sikuti timangopewa zosangalatsa zomwe tikudziwa kuti n’zoipa. Timapewanso zosangalatsa zomwe tikukayikira kuti mwina zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.

KODI MAGANIZO A YEHOVA NDI OTANI PA NKHANIYI?

16. (a) Kodi zinthu zina zimene Yehova amadana nazo ndi ziti? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadana ndi zimene Yehova amadana nazo?

16 Wamasalimo ananena kuti: “Inu okonda Yehova danani nacho choipa.” (Salimo 97:10) Baibulo limatithandiza kudziwa maganizo a Yehova komanso zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikuphunzirazi zingandithandize bwanji kuti ndiziona zinthu ngati mmene Yehova amazionera?’ Mwachitsanzo, Baibulo limati Yehova amadana ndi ‘lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzera ena ziwembu komanso mapazi othamangira kukachita zoipa.’ (Miyambo 6:16-19) Limanenanso kuti tiyenera kupewa ‘dama, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, nsanje, kupsa mtima, kaduka, kumwa mwauchidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotero.’ (Agalatiya 5:19-21) Kodi mukuganiza kuti mfundo zimenezi zingakuthandizeni bwanji kuti muzisankha zosangalatsa zoyenera? Tiyenera kutsatira mfundo za Yehova pa chilichonse chimene timachita, kaya tili pagulu kapena tili kwatokha. (2 Akorinto 3:18) Nthawi zambiri zimene timachita tikakhala tokha ndi zomwe zimasonyeza khalidwe lathu lenileni.​—Salimo 11:4; 16:8.

17. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa tisanasankhe zosangalatsa?

17 Choncho mukamasankha zosangalatsa muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zikhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova? Nanga zikhudza bwanji chikumbumtima changa?’ Tiyeni tikambiranenso mfundo zina zimene zingatithandize tikamasankha zosangalatsa.

18, 19. (a) Kodi Paulo anapereka malangizo otani kwa Akhristu? (b) Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize posankha zosangalatsa?

18 Tikamasankha zosangalatsa, timakhala tikusankha zinthu zomwe tikufuna kuika m’maganizo mwathu. Paulo analemba kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.” (Afilipi 4:8) Mumtima mwathu mukakhala zabwino ngati zimenezi, tingathe kunena kuti: “Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweretseni, inu Yehova.”​—Salimo 19:14.

19 Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimaika zinthu zotani m’maganizo mwanga? Ndikamaliza kuonera filimu inayake, kodi ndimakhala ndi maganizo abwino komanso ndimasangalala? Kodi ndimakhala ndi mtendere wa mumtima ndiponso chikumbumtima chabwino? (Aefeso 5:5; 1 Timoteyo 1:5, 19) Nanga kodi ndimamasuka kupemphera kwa Yehova, kapena ndimaona kuti ndine wosayenera kupemphera? Kodi zosangalatsazo zimachititsa kuti ndiziganizira zinthu zachiwawa komanso zachiwerewere? (Mateyu 12:33; Maliko 7:20-23) Nanga kodi zosangalatsa zimene ndimasankha zikundichititsa kuti ndizitengera maganizo a anthu a m’dzikoli?’ (Aroma 12:2) Mayankho a mafunso amenewa angatithandize kudziwa zoyenera kuchita kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Mofanana ndi wamasalimo, ifenso timapempha Yehova kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” *​—Salimo 119:37.

ZIMENE TIMASANKHA ZIMAKHUDZANSO ENA

20, 21. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira chikumbumtima cha ena tikamasankha zosangalatsa?

20 Mfundo ina yofunika kuikumbukira ndi yakuti: “Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa. Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:23, 24) Kukhala ndi ufulu wochita chinachake sikutanthauza kuti tiyenera kuchita chinthucho. Tiyenera kuganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire abale ndi alongo athu.

21 Anthufe timasiyana pa nkhani ya chikumbumtima. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti chikumbumtima chanu chikukulolani kuonera pulogalamu inayake ya pa TV. Koma kenako mwazindikira kuti chikumbumtima cha m’bale kapena mlongo wina sichikumulola kuonera pulogalamuyo. Kodi mungatani? Ngakhale kuti muli ndi ufulu woonera pulogalamuyo, mungachite bwino kusankha kuti musaionere. Mungachite zimenezi chifukwa choti simukufuna ‘kuchimwira abale anu komanso Khristu.’ (1 Akorinto 8:12) Sitifuna kuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse Akhristu anzathu.​—Aroma 14:1; 15:1; 1 Akorinto 10:32.

22. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera ngati Akhristu ena asankha zosiyana ndi zimene tasankha?

22 Nanga bwanji ngati chikumbumtima chanu sichikukulolani kuonera, kuwerenga kapena kuchita zinthu zina zimene wina akuona kuti zilibe vuto? Chifukwa choti mumakonda komanso kulemekeza m’bale wanuyo, simungamukakamize kuti nayenso asankhe zofanana ndi inuyo. Munthu akamayendetsa galimoto amaona madalaivala ena akuthamangitsa galimoto kapena kuyendetsa pang’onopang’ono kuposa iyeyo. Koma amadziwa kuti umenewo si umboni wakuti anthuwo si madalaivala abwino. Mofanana ndi zimenezi, inuyo ndi m’bale wina mungasiyane pang’ono pa nkhani yokhudza zosangalatsa zoyenera, ngakhale kuti nonse mumatsatira mfundo za m’Baibulo.​—Mlaliki 7:16; Afilipi 4:5.

23. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani ya zosangalatsa?

23 Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zosangalatsa zoyenera? Tizigwiritsa ntchito chikumbumtima chathu chomwe timachiphunzitsa mfundo za m’Baibulo. Komanso tiziganizira chikumbumtima cha abale ndi alongo athu. Tikatero, tizisangalala chifukwa chodziwa kuti tikuchita “zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”

^ ndime 19 Mfundo zina zimene zingatithandize kusankha bwino zosangalatsa tingazipeze pa Miyambo 3:31; 13:20; Aefeso 5:3, 4 ndi Akolose 3:5, 8, 20.