PHUNZIRO 04

Kodi Mulungu Ndi Ndani?

Kodi Mulungu Ndi Ndani?

Kuyambira kalekale, anthu akhala akulambira milungu yosiyanasiyana. Koma Baibulo limanena kuti pali Mulungu mmodzi yemwe “ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.” (2 Mbiri 2:5) Kodi Mulungu ameneyu ndi ndani? Nanga n’chifukwa chiyani ndi wamkulu kuposa Milungu ina yonse imene anthu amalambira? M’phunziroli tiona zimene Mulungu wachita kuti mumudziwe bwino.

1. Kodi dzina la Mulungu ndi ndani, nanga tingatsimikizire bwanji kuti amafuna kuti tilidziwe?

Mulungu amafuna kuti timudziwe, ndipo amatiuza dzina lake m’Baibulo. Iye anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Werengani Yesaya 42:5, 8.) Dzina lakuti “Yehova” analimasulira kuchokera ku dzina la Chiheberi ndipo zikusonyeza kuti limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Yehova amafuna kuti tidziwe dzina lake. (Ekisodo 3:15) Tikudziwa bwanji zimenezi? Iye anachititsa kuti dzina lake lilembedwe m’Baibulo maulendo oposa 7,000. a Dzina lakuti Yehova ndi la “Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.”​—Deuteronomo 4:39.

2. Kodi Baibulo limatiuza zotani zokhudza Yehova?

Baibulo limatiuza kuti pa milungu yonse imene anthu amailambira, Yehova yekha ndiye Mulungu woona. N’chifukwa chiyani tikutero? Pali zifukwa zambiri. Yehova ndi wolamulira wamkulu, ndipo iye yekha ndi “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Werengani Salimo 83:18.) Iye ndi “Wamphamvuyonse,” kutanthauza kuti ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene wasankha. Iye ndi amene ‘analenga zinthu zonse,’ zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Chivumbulutso 4:8, 11) Mosiyana ndi wina aliyense, Yehova alibe chiyambi komanso alibe mapeto.​—Salimo 90:2.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kusiyana pakati pa mayina audindo a Mulungu ndi dzina lake lenileni lomwe ndi lapadera. Kenako phunzirani zimene Mulungu anachita kuti mudziwe dzina lake ndiponso chifukwa chake anatero.

3. Mulungu ali ndi mayina audindo ambirimbiri, koma dzina lake lenileni ndi limodzi lokha

Kuti muone kusiyana pakati pa dzina la udindo ndi dzina lenileni, onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili.

  • Kodi dzina laudindo ngati lakuti “Ambuye,” ndi losiyana bwanji ndi dzina lenileni?

Baibulo limavomereza kuti anthu amalambira milungu ndi ambuye ambirimbiri. Werengani Salimo 136:1-3, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi “Mulungu wa milungu” ndi “Mbuye wa ambuye” ndi ndani?

4. Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake n’kumaligwiritsa ntchito

N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi inuyo mumaona kuti Yehova amafuna kuti anthu adziwe dzina lake? N’chifukwa chiyani mukutero?

Yehova amafuna kuti anthu azigwiritsa ntchito dzina lake. Werengani Aroma 10:13, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova n’kofunika bwanji?

  • Kodi inuyo mumamva bwanji munthu wina akakumbukira dzina lanu n’kulitchula?

  • Ndiye mukuona kuti Yehova amamva bwanji mukamagwiritsa ntchito dzina lake?

5. Yehova amafuna kuti inuyo mukhale mnzake

Mayi wina wa ku Cambodia dzina lake Soten ananena kuti palibe “chinthu chosangalatsa kwambiri” ngati kudziwa dzina la Mulungu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

  • Muvidiyoyi, kodi Soten anamva bwanji atadziwa dzina la Mulungu?

Munthu asanakhale mnzathu timayamba tadziwa kaye dzina lake. Werengani Yakobo 4:8a, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yehova akufuna kuti inuyo muchite chiyani?

  • Kodi kudziwa dzina la Mulungu ndiponso kuligwiritsa ntchito kungakuthandizeni bwanji kuti muzimuona kuti ndi mnzanu?

ZIMENE ENA AMANENA: “Mulungu alipo mmodzi yekha, ndiye zilibe kanthu kuti ukumutchula pogwiritsa ntchito dzina liti.”

  • Kodi inuyo mumakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova?

  • Kodi mungafotokoze bwanji zoti Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito dzina lake?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Dzina la Mulungu woona ndi Yehova. Iye amafuna kuti tilidziwe dzinali ndiponso tiziligwiritsa ntchito n’cholinga choti akhale mnzathu.

Kubwereza

  • Kodi Yehova amasiyana bwanji ndi milungu ina yonse imene anthu amalambira?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?

  • N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti inuyo mukhale mnzake?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zifukwa 5 zotsimikizira kuti Mulungu alipo.

“Kodi Mulungu Alipodi?” (Nkhani yapawebusaiti)

N’chifukwa chiyani ndi zomveka kukhulupirira kuti Mulungu alipo?

“Kodi Ndani Analenga Mulungu?” (Nsanja ya Olonda, August 1, 2014)

Dziwani chifukwa chake tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, ngakhale kuti sitidziwa mmene ankalitchulira kalekale.

“Kodi Yehova Ndi Ndani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Kodi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu n’kofunika bwanji? Onani chifukwa chake tinganene kuti dzina lake lenileni ndi limodzi lokha.

“Kodi Mulungu Ali Ndi Mayina Angati?” (Nkhani yapawebusaiti)

a Kuti mumve zambiri pa nkhani ya tanthauzo la dzina la Mulungu komanso chifukwa chake anthu analichotsa m’Mabaibulo ena, onani Mutu 1 mu Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu.