PHUNZIRO 06
Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
Mulungu ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Kodi mumakhulupirira zimenezi? Anthu ena amaganiza kuti zamoyo zinangokhalapo zokha. Ngati zimenezi ndi zoona, ndiye kuti anthufe tinangokhalako mwangozi. Koma ngati Yehova Mulungu ndi amene analenga zamoyo, ndiye kuti anali ndi cholinga. a Tiyeni tikambirane zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mmene moyo unayambira komanso chifukwa chake tingakhulupirire kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona.
1. Kodi zinthu zam’chilengedwechi zinakhalako bwanji?
Baibulo limanena kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Asayansi ambiri amavomereza kuti zinthu zam’chilengedwechi zili ndi chiyambi. Kodi Mulungu anazilenga bwanji? Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera, womwe ndi “mphamvu ya Mulungu” yogwira ntchito, kuti alenge zinthu zonse m’chilengedwechi, kuphatikizapo milalang’amba, nyenyezi ndi mapulaneti.—Genesis 1:2.
2. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi?
Yehova ‘sanalenge dziko lapansi popanda cholinga. Analiumba kuti anthu akhalemo.’ (Yesaya 45:18) Iye analenga dziko lapansi n’kuikamo zinthu zonse zofunikira kuti anthu akhalemo mpaka kalekale. (Werengani Yesaya 40:28; 42:5.) Asayansi amanena kuti dziko lapansili ndi lapadera kwambiri. Iwo sanapeze pulaneti lina loposa dzikoli lomwe lili ndi zinthu zofunika kuti anthu akhale ndi moyo.
3. Kodi n’chiyani chimasiyanitsa anthu ndi nyama?
Yehova atalenga dzikoli, analenganso zinthu zamoyo. Choyamba analenga zomera ndi nyama. Kenako “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake.” (Werengani Genesis 1:27.) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu azisiyana ndi nyama? Anthufe timatha kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi ndi chilungamo chifukwa chakuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Iye anatilenganso ndi luso lotha kuphunzira zinenero, kusangalala ndi nyimbo komanso zinthu zina zokongola. Ndipo mosiyana ndi zinyama, anthufe timatha kulambira Mlengi wathu.
FUFUZANI MOZAMA
Pezani umboni wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kulengedwa komanso wakuti nkhani ya m’Baibulo yofotokoza zoti zinthu zinachita kulengedwa ndi yoona. Onani mmene makhalidwe amene anthu ali nawo angatithandizire kudziwa zokhudza Mulungu.
4. Zamoyo zinachita kulengedwa
Anthu amatha kulemekezedwa chifukwa chopanga zinthu zokongola potengera zinthu zam’chilengedwe. Ndiye kodi ndi ndani amene ayenera kulemekezedwa chifukwa cha zinthu zam’chilengedwezo? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu apanga potengera zinthu zam’chilengedwe?
Kuti nyumba imangidwe, pamakhala winawake wolemba mapulani ndiponso woimanga. Ndiye kodi ndi ndani amene analemba mapulani komanso kupanga zinthu zam’chilengedwe? Werengani Aheberi 3:4, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi ndi zinthu ziti zam’chilengedwe zimene zimakusangalatsani?
-
Kodi ndi nzeru kukhulupirira kuti zinthu zonse zam’chilengedwe zinachita kulengedwa? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi mukudziwa?
Mukhoza kupeza nkhani komanso mavidiyo okhudza zinthu zachilengedwe pa jw.org pamitu yakuti,“Kodi Zinangochitika Zokha?” ndiponso “Zimene Ena Amanena Zokhudza Mmene Moyo Unayambira.”
“N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu”
5. Nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu ndi yoona
Mu Genesis chaputala 1, Baibulo limafotokoza mmene dziko lapansi komanso zinthu zamoyo zinayambira. Kodi inuyo mumakhulupirira nkhani imeneyi, kapena mumaona kuti ndi yongopeka? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
-
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti dziko lapansi ndiponso zamoyo zonse zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24?
-
Kodi inuyo mumaona kuti nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu ndi yomveka komanso yoona? N’chifukwa chiyani mukutero?
Werengani Genesis 1:1, kenako mukambirane funso ili:
-
Asayansi amanena kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi. Kodi zimene amanenazi zikugwirizana bwanji ndi zimene mwawerenga m’Baibulo?
Anthu ena amaganiza kuti polenga zinthu, Mulungu anangochititsa kuti zisinthe kuchokera ku zinthu zina. Werengani Genesis 1:21, 25, 27, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu anapanga zinthu zing’onozing’ono zomwe zinasintha n’kukhala nsomba, zinyama ndiponso anthu? Kapena kodi analenga zamoyo za “mitundu” yosiyanasiyana? b
6. Pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga, anthu analengedwa mwapadera
Anthufe ndife osiyana ndi zinyama zimene Yehova analenga. Werengani Genesis 1:26, kenako mukambirane funso ili:
-
Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, kodi tikamasonyeza chikondi ndi chifundo timasonyeza kuti Mulungu ndi wotani?
ZIMENE ENA AMANENA: “Nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu ndi yongopeka.”
-
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova analenga zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi.
Kubwereza
-
Kodi Baibulo limanena kuti zinthu zam’chilengedwe zinakhalako bwanji?
-
Kodi Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse kapena anangolola kuti zamoyo zina zizisintha kuchokera ku zamoyo zing’onozing’ono?
-
Kodi anthu amasiyana bwanji ndi zinyama?
ONANI ZINANSO
Onani zimene tingaphunzire kuchokera ku zinthu zam’chilengedwe.
“Kodi Zamoyo Zimatiphunzitsa Chiyani?” (Galamukani!, September 2006)
Onani mmene bambo angafotokozere mwana wake nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu.
Onani ngati nkhani yakuti zamoyo zinachita kusintha ikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena.
“Kodi Mulungu Anasintha Zamoyo Zina Polenga Mitundu Inanso ya Zamoyo?” (Nkhani yapawebusaiti)
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA